Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Ndili Wochepa Thupi Chonchi?

N’chifukwa Chiyani Ndili Wochepa Thupi Chonchi?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

N’chifukwa Chiyani Ndili Wochepa Thupi Chonchi?

JUSTIN n’ngwochepa thupi ndipo n’ngwathanzi koma sasangalala ndi thupi lake. “Ndikuyesetsa kuti ndinenepeko,” iye anavomereza motero. Choncho pakali pano amadya kasanu patsiku, chakudya chopereka mphamvu zambiri zokwana ma calorie 4,000. Komabe, chimene iye akufuna kuwonjezera ndicho kujintcha kwa thupi lake. Chotero ananenanso kuti: “Masiku ena ine ndi mnzanga timadzuka m’mamaŵa kupita ku nyumba yochitiramo maseŵera osiyanasiyana olimbitsa thupi kukanyamula zitsulo zolemera tisanayambe kugwira ntchito.”

Vanessa nayenso n’ngwochepa thupi kwabasi. Koma iye amakhutira ndi thupi lakelo. “Pamene ndinali wam’ng’ono, ana ankakonda kundiseka n’kumandiitana kuti kangawonde,” anakumbukira motero Vanessa. “Komabe sindidandaula nazonso masiku ano. Ndimangovomera kuti ndi mmene thupi langa lilili.”

‘Kuvomereza kuti ndi mmene thupi lako lilili,’ kukuoneka ngati malangizo abwino ndithu. Komano mwina malangizoŵa amakuvutani kuwagwiritsa ntchito. Monga wachinyamata, mwina muli pa “unamwali.” (1 Akorinto 7:36) Makamaka nyengo ya kutha msinkhu ndiyo yovuta kwambiri popeza kuti thupi limasintha mofulumira. Panthaŵi yoti mwatha msinkhu, ziŵalo za thupi lanu zimakula pamlingo wosiyanasiyana; manja anu, miyendo yanu, ndiponso ziŵalo zanu zina zakumaso zingaoneke kuti sizikukula mofanana. * Izi zingakuchititseni kumadzimva wopanda pake ndiponso wosakongola. Ndiye palinso nkhani yakuti si achinyamata onse amene amakula pamlingo wolingana. Choncho, ngakhale kuti anyamata anzanu angakule mojintcha kapena atsikana anzanu angakhale ndi mbina monga akazi, inuyo mungaonekebe wochepa thupi poyerekeza ndi iwowo.

Ngakhale kuti pali nkhani zambiri zokhudza achinyamata amene amadziona kuti n’ngonenepa kwambiri, nthaŵi zambiri achinyamata amene amadziona kuti n’ngochepa thupi kwabasi satchulidwa n’komwe. Zimenezi zimachitika makamaka ku mitundu ina komanso m’mayiko ena kumene kuchepa thupi sakuona monga chizindikiro cha kukongola. Kumadera ngati ameneŵa mtsikana wochepa thupi angamasekedwe kwabasi chifukwa choti “n’ngwoonda.”

Bwanji nanga za anyamata? Malinga ndi zomwe wofufuza wina wotchedwa Susan Bordo ananena, “kufufuza kokhudza mmene akazi amaonera kaonekedwe kochitidwa m’zaka makumi angapo pambuyo pa m’ma 1980, kunasonyeza kuti mkazi akaona pagalasi, amangoona mbali zimene sakuoneka bwino basi.” Bwanji amuna? Bordo anapitiriza kunena kuti: “Amuna akaona pagalasi, m’maganizo mwawo amaona chithunzi chabwino kapena ngakhale choposa chimene amaganizira.” Komabe m’zaka zaposachedwapa zimenezi zayamba kusintha. Bordo ananena kuti chiŵerengero cha amuna ochititsa opaleshoni yodzikongoletsa chaposa gawo limodzi mwa magawo anayi a anthu ofuna chithandizo chamtunduwu. Iye akuona kuti anyamata ambiri akufuna kuoneka olimba chifukwa cha zithunzi zamatupi a amuna “ojintcha” zimene akhala akuzionetsa potsatsa malonda a zovala zam’kati ku United States ndi m’mayiko ena Akumadzulo. Mosadabwitsa, zimenezi zakhudza anyamata kwambiri. Iwo amadziona kuti sakukwanira ngati alibe thupi lojintcha ngati la amunawo.

Choncho, ngati ndinu wochepa thupi, mungadzifunse kuti, “Kodi vuto langa n’chiyani? Chosangalatsa n’chakuti n’kutheka kuti vuto palibe.

Chifukwa Chimene Mulili Wochepa Thupi

Kwa achinyamata ambiri, kuchepa thupi n’kwachibadwa. Nthaŵi zambiri kumachitika chifukwa cha mavuto ena okhudza kakulidwe ndiponso kupukusika kofulumira kwa zakudya m’thupi komwe kumadza m’zaka za kusinkhuka. Kaŵirikaŵiri zimenezi zimamka zichepa munthu akamakalamba. Komabe, ngati muli woonda modetsa nkhaŵa ngakhale ngati m’madya bwino, ndibwino kukaonana ndi dokotala kuti akatsimikizire ngati mulibe matenda alionse monga matenda a shuga amene angakuondetseni.

Steven Levenkron, yemwe ndi katswiri wa matenda akadyedwe, anauza atolankhani a Galamukani! kuti: “Ndikukumbukira mkazi wina wachitsikana wochepa thupi kwabasi amene anamubweretsa kwa ine kuti akudwala matenda odana ndi zakudya otchedwa anorexia, ndipo ankaonekadi kuti akudwala matendaŵa. Koma mwamsanga ndinazindikira kuti vuto lake linali matenda ena osati matenda amaganizo odana ndi zakudyaŵa. Dokotala wa banjalo analephera kutulukira kuti anali ndi matenda oopsa a m’matumbo otchedwa Crohn. Kulakwitsa kumeneko kukanaphetsa mtsikanayu.” Ngati inuyo mukudwala matenda a shuga kapena matenda ena alionse amene amawondetsa, n’kwanzeru kutsatira mosamalitsa malangizo a dokotala.

N’zoona kuti kuwonda kungakhale chizindikiro cha kuvutika maganizo. M’buku lake lotchedwa Anatomy of Anorexia, Dr. Levenkron anatchulamo zomwe ofufuza ena anena, zakuti ambiri mwa “anthu odwala matenda a shuga ali ndi matenda osiyanasiyana okhudza kudya monga matenda a kudya kwambiri otchedwa compulsive overeating, matenda osanza zakudya otchedwa bulimia, ndipo mpakanso matenda odana ndi chakudya otchedwa anorexia.” Dokotala wodziŵadi ntchito yake angadziŵe ngati inuyo muli ndi mavuto akadyedwe amenewa. *

Malangizo Othandiza

Tiyerekeze kuti mwaonana ndi dokotala wanu ndipo wapeza kuti n’zoona ndinu wochepa thupi koma ndinu wathanzi. Ndiyeno mungatani? Pa Yobu 8:11, Baibulo limati: ‘Kodi gumbwa aphuka popanda chinyontho? Kodi manchedza amera popanda madzi?’ Monga mmene mbewu imakulira bwino ikakhala pamalo abwino ndiponso pachakudya chokwanira, n’chimodzimodzinso inuyo mumafunikira chakudya chamagulu onse ngati mukufuna kudzakhala munthu wachikulire wathanzi. Zimenezi n’zofunikabe kaya mukufuna kunenepa kapena kuchepetsako thupi.

Komabe, musatengeke mtima n’kuyamba kudya zakudya zochuluka zamafuta ambiri n’cholinga chofuna kunenepa msanga. Pakafukufuku wa zakudya za anthu ochita maseŵera olimbitsa thupi, katswiri wa zakudya wotchedwa Susan Kleiner anaona kuti anthu otereŵa amadya chakudya chopatsa mphamvu zokwana ma calorie 6,000 patsiku! Komabe malinga ndi kunena kwa Kleiner, “chodetsa nkhaŵa kwambiri pa kufufuzako n’chakuti anthuŵa amadya zakudya zamafuta okwana magilamu 200 patsiku. Mafutaŵa n’ngwochuluka mofanana ndi amene amakhala m’batala olemera magilamu 125! Kudya mafuta onseŵa kwa nthaŵi yochepa anthu ambiri angadwale nako. Kudya zakudya zamafuta kwambiri nthaŵi yaitali kumayambitsa matenda a mtima.”

Malinga ndi zomwe bungwe la zaulimi lotchedwa U.S. Department of Agriculture (USDA) linanena, zinthu zofunika kwambiri pa chakudya chamagulu onse ndizo chakudya chopatsa mphamvu monga buledi, chimanga, mpunga, ndipo chachiŵiri ndicho ndiwo zamasamba ndi zipatso. Bungwe la USDA linalimbikitsa kuti nyama ndi mkaka ziyenera kudyedwa mwapang’ono pokha.

Kuti muone kuchuluka ndi mtundu wa chakudya chomwe m’madya mungayese kumalemba m’kabuku zomwe mwadya, tsiku ndi tsiku. Ikani kabukuko m’thumba kuli konse komwe mukupita kwamlungu umodzi, ndipo lembani chakudya chilichonse chimene mwadya ndi nthaŵi imene mwachidya. Mungadabwe kupeza kuti simudya kwambiri monga mmene m’maganizira, makamaka ngati nthaŵi zonse mumakhala mukuchita zinthu mothamanga. Monga wachinyamata wojijirika, thupi lanu lingagwiritse ntchito chakudya chopatsa mphamvu zokwana ma calorie 3,000 patsiku kapena kuposerapo! Mungapezenso kuti chakudya chomwe m’madya si chamagulu onse monga chiyenera kukhalira. Mungapeze kuti m’madya zakudya zamafuta ambiri monga nyama ndi zinanso koma popanda zipatso zokwanira komanso ndiwo zamasamba.

Bwanji nanga za zakudya zapamwamba zodula zowonjezera mavitamini? Zimenezo sizingakhale zofunika. Akatswiri ambiri amakhulupirira kuti mungapeze zakudya zonse zofunika m’thupi mwanu mwa kudya zakudya zabwino zawamba zomwezi. Chofunikanso koposa ndicho kupeŵa njira zachidule monga kumwa mankhwala opatsa thanzi kwakanthaŵi otchedwa ma steroids. N’zomvetsa chisoni kuti vuto la kugwiritsa ntchito mankhwalaŵa mwachisawawa silili ndi anyamata okha. Nyuzipepala yotchedwa The New York Times inanena kuti: “Atsikana amene akugwiritsa ntchito mankhwalaŵa akuchuluka, ndipo ofufuza ena akuona kuti n’chifukwa cha matenda a anorexia, a mtundu wina mwakuti tsopano atsikanaŵa n’ngochuluka mofanana ndi mmene anyamata analili m’ma 1980.” N’zodabwitsa kuti atsikana okwana 175,000 ku United States amavomereza kuti amamwa mankhwala opatsa thanzi mwamsangawa. Mankhwalawa akhala akuchititsa matenda ambiri ochititsa chisoni, monga kumera tsitsi losafunika kumaso, kulephera kupita kumwezi, kutsekeka kwa mitsempha ndiponso kansa yamaŵere kwa akazi ndi kansa yokhudza mphamvu ya umuna. Mankhwala a steroids sayenera kumwedwa popanda kuuzidwa ndiponso kulangizidwa ndi dokotala.

Khalani Wodzichepetsa ndi Woona Zinthu Moyenera

Baibulo limatiuza kukhala ‘modzichepetsa ndi Mulungu wathu.’ (Mika 6:8) Kudzichepetsa kumaphatikizapo kudziŵa zinthu zimene iweyo sungathe kuchita. Kudzichepetsa kudzakuthandizani kudziona moyenereradi. Inde, palibe cholakwika ngati m’mafuna kuoneka bwino. Komabe kudera nkhaŵa kwambiri za kaonekedwe kanu sikupindulitsa aliyense, mwina kupatulapo makampani okonza zinthu za fashoni ndi zakudya. Akatswiri a mphamvu ndi kulimba kwa thupi amavomereza kuti amuna ambiri alibe chibadwa choyenera kuti akhale ndi matupi ojintcha kwambiri, ngakhale atamadya bwino bwanji kapena kuchita maseŵera olimbitsa thupi. Ndipo ngati ndinu mtsikana, n’kutheka kuti thupi lanu silidzakula ngakhale mutamadya kwambiri motani.

Chochititsa chidwi n’chakuti, zovala zomwe muli nazo zingathandize kwambiri kuthetsa mavuto ena amene mungaganize kuti n’chilema. Pewani kuvala zovala zimene zimachititsa kuti muzioneka wowonda kwambiri. Ena amati ndibwino kuvala zovala zosawala kwenikweni, chifukwa zakuda zimachititsa anthu ochepa thupi kuoneka ngati owonda mopitirira.

Komanso, kumbukirani kuti chofunika kwambiri kuposa kaonekedwe kanu ndicho khalidwe lanu. Mkupita kwanthaŵi, kumwetulira kosangalatsa, ndiponso khalidwe loganizira ena powakomera mtima zidzakuthandizani kuoneka bwino kwambiri kwa anthu ena kuposa mmene kukhala ndi thupi lojintcha kapena kuvala zovala za saizi inayake kungachitire. Ngati anzanu nthaŵi zonse amakunyodolani chifukwa cha mmene m’maonekera, funani anthu amene amakukondani chifukwa cha khalidwe lanu, limene Baibulo limatcha kuti “munthu wobisika wamtima.” (1 Petro 3:4) Pomaliza, musaiŵale kuti “munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.”—1 Samueli 16:7.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Onani nkhani za “Achinyamata Akufunsa Kuti . . .” pamutu wakuti “Kodi Ndikukula Bwino Lomwe?” m’kope la Galamukani! wa October 8, 1993.

^ ndime 12 Onani nkhani za “Achinyamata Akufunsa Kuti . . .” pamutu wakuti “N’chifukwa Chiyani Ndimaopa Kunenepa?” ndiponso “Kodi Ndingathetse Bwanji Vuto Langa Loopa Kunenepa?,” m’magazini a Galamukani! a May 8 ndi June 8, 1999.

[Chithunzi patsamba 14]

Achinyamata ena amadzinyoza okha chifukwa choti n’ngochepa thupi