Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anawapulumutsa Lokumbakumba

Anawapulumutsa Lokumbakumba

Anawapulumutsa Lokumbakumba

Yolembedwa ndi Mtolankhani wa Galamukani! ku BENIN

“CHIPANDA Mboni za Yehova kuwapulumutsa bwenzi anthu atatuwo pano titaiwalako!” Lachitatu, pa April 19, 2000, nkhani imeneyi inawanda paliponse mum’zinda wa Calavi, m’dziko la Benin lomwe lili kumadzulo kwa Africa. Kodi anthu atatuwo anali ndani, ndipo kodi Mboni za Yehova zinawapulumutsa motani?

Nthaŵi ili pafupifupi hafu pasiti sikisi m’mamaŵa, Philippe Elegbe ndi Roger Kounougbe anali pakalapakala kukonzekera kukagwira ntchito pamalo okachitira msonkhano waukulu wa Mboni za Yehova omwe ali moyandikana ndi ofesi yanthambi ya Watch Tower Society ya ku Benin. Madzulo ake ankayembekeza kuti pafika anthu ambiri odzachita Chikumbutso cha pachaka cha imfa ya Yesu Kristu. * Unali m’maŵa kunja kuli bata ndipo mwadzidzidzi kunamveka chiphokoso choti phwaa! Nthaŵi yomweyo, Philippe ndi Roger anazindikira kuti kumsewu kwachitika ngozi.

Pasanapite nthaŵi anangomva munthu akufuula kuti: “Anzanga atatu ondithandiza akwiriridwa pansi pa matumba a simentiwa!” Philippe ndi Roger anathamangira kumsewuko. Poyang’ana, anaona kuti kuli galimoto yaikulu ya matani 20 itagudubuka. Matumba ambirimbiri odzaza ndi simenti anali tololo pambali pa galimotoyo.

Josué Didolanvi, amenenso anali kugwira ntchito pa bwalo la msonkhanolo, anali atafika kale pamalopo, ndipo anali kukoka munthu kum’solola pakati pa mutu wa galimotoyo ndi matumba a simentiwo. Dalaivalayo anadzitulutsa yekha m’galalimotoyo ndipo apa n’kuti ali njenjenje. Komabe anadzilimbitsa n’kukuwa, amvekere: “Patsala anthu aŵiri pansi pa matumba a simentiwa!” Anthu ena oonerera anayamba kuchotsapo matumbawo, koma anasiya mwamsanga chifukwa anali kutentha koopsa. Simentiyo anali atangoiphula kumene kuchokera m’mauvuni a kufakitale kumene amaipangira!

Kuwapulumutsa

Philippe, Roger, ndi Josué anagundika nayo ntchito yochotsa matumba aja limodzilimodzi. Manja awo anali kupweteka kwambiri chifukwa cha kutentha ndiponso kulemera kwa matumbawo omwe anali a makilogalamu 50. Chinawonjezeranso vuto n’chakuti simentiyo inali kutayikira kuchoka m’matumba ophulikawo n’kumawachititsa matuza m’manja ndiponso kubanika. “Manja anga anali kumva kutentha kwambiri, makamaka zala zanga,” anatero Josué itatha ntchitoyo. “Komabe ndinali kuganiza kuti mwamwayi tingathe kupulumutsa winawake amene anali atakwiriridwa pamenepo.”

Atachotsa matumba pafupifupi 40, anthu atatuwo anangoona lona. Modabwa kwambiri, anapeza kuti anthu aŵiriwo ali pamenepo, pansi palonayo. Anali amoyo eti! Pamene ngoziyo inkachitika, anthu ameneŵa n’kuti ali kumbuyo kwa galimotoyi atagona palona imene anaphimbira matumba a simentiwo. Pamene ankagwa kuchoka m’galimotoyo, lonayo inawaphimba, ndipo inawatetezera kuti asatenthedwe ndi matumba a simenti amene anawakwirirawo.

Panthaŵi yomwe ankawapulumutsa ndiponso pambuyo pake, gulu lalikulu ndithu la anthu linasonkhana n’kumaonerera. Onse anadabwa kwambiri kuona kuti Philippe, Roger ndi Josué anatha kuchotsa mulu wa matumba a simenti wokwana matani aŵiri mwamsanga choncho komanso movutikira zedi. Ndiponso anadabwa nawo kwambiri anthu atatu ameneŵa chifukwa chodzivutitsa motero pofuna kuthandiza anthu amene sankawadziŵa n’komwe. Posapita nthaŵi anthu onse a ku Calavi zikuoneka kuti anadziŵa za ntchito yawo yachamuna imeneyo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Pomvera lamulo la Yesu, Mboni za Yehova zimachita chikumbutso chimenechi chaka chilichonse.—Luka 22:19.

[Chithunzi patsamba 18]

Roger atanyamula lona pambuyo populumutsa anthuwo