Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chimene Chaipitsa Khalidwe

Chimene Chaipitsa Khalidwe

Chimene Chaipitsa Khalidwe

MWEZI wa October wapitawu mtolankhani wina wa ku Loja, ku Ecuador, anayamikira ntchito ya Mboni za Yehova. Zina mwa zimene ananena n’zakuti:

“Chinthu chimodzi chimene chikusautsa anthu kwambiri ndicho kupanda khalidwe . . . Zikuoneka kuti anthu akuiŵala kutsatira Malamulo Khumi aja ndipo akunyalanyaza chikumbumtima chawo, ndipo zonsezi zimawalepheretsa kumvetsetsana. Kulikonse ndiponso tsiku lililonse, timamva za udani, chiwawa, umbanda, kuzembetsa mankhwala osokoneza bongo, uchigaŵenga, ndiponso kusapatsa anthu ulemu wawo. . . .

“Mosadzitamandira Amboni za Yehova, amagwira ntchito yawo mwamtendere ndiponso mwa phee, amayendera anansi awo khomo ndi khomo, n’kumapereka magazini awo okongola aŵiri aja, a Nsanja ya Olonda ndiponso Galamukani!, mmene mumakhala nkhani zosangalatsa kwambiri. Makamaka Galamukani! imasimba nkhani zosiyanasiyana zokhudza sayansi ndiponso chikhalidwe zosati n’kutsutsika. Nkhani zonsezi zimakhala zomveka bwino ndiponso zolondola kwambiri.”

Kupanda khalidwe komwe kulipo masiku ano n’kosabisika, koma monga mmene alembera pa tsamba 4 la magazini ino pa mbali yakuti “Chifukwa Chake Galamukani! Amafalitsidwa,” Galamukani! “amapenda zakuya ndi kusonyeza tanthauzo lenileni la zochitika zamakono.” Bulosha lakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi? limasonyeza kuti anthu akhala akuvutika kwambiri, koma sikuti limangonena zokhazo ayi. Limasonyezanso chimene chaipitsa khalidwe ndiponso zoipa zimene khalidwe loipali limabweretsa. Chinthu chofunika kwambiri n’chakuti limavumbula njira yodzatheketsa kuti posachedwapa anthu adzapumule.

Mungathe kuitanitsa bulosha lolimbikitsa la masamba 32 limeneli polemba zofunika m’kabokosi kali pamunsika ndi kukatumiza ku adiresi yosonyezedwapoyo kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa patsamba 5 la magazini ino.

□ Munditumizire bulosha lakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi?

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.