Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chosankha Chanu pa Chithandizo Chamankhwala

Chosankha Chanu pa Chithandizo Chamankhwala

Chosankha Chanu pa Chithandizo Chamankhwala

M’BUKU lake lonena za njira zochiritsira zosagwiritsidwa ntchito masiku onse, Dr. Isadore Rosenfeld anagogomezera mfundo iyi: “Chithandizo chilichonse chamankhwala kapena chinthu chilichonse chongolingaliridwa kuti ndi mankhwala choperekedwa kwa gulu la anthu osankhidwa mwachisawawa omwe auzidwa motsimikiza kuti chithandizocho ‘chidzagwira ntchito,’ chingachititsedi kuti theka la anthuwo lipeze bwino.”

Zimenezi zimatchedwa kuti kuchiritsa kwa chikhulupiriro, zomwe zikutanthauza kuti ngakhale m’bulu wa shuga ungachiritse ngati munthuyo akukhulupirira kuti udzam’chiritsa. Kuchiritsa kwa chikhulupiriro kungathetse matenda a m’maganizo, kuphatikizapo kupweteka m’thupi, nseru, kufooka, chizungulire, nkhaŵa, komanso kuvutika maganizo. Kodi mfundo imeneyi ikuvumbula chiyani?

Choyamba, mfundo imeneyi ikusonyeza kuti, kaŵirikaŵiri kudalira chithandizo chilichonse chamankhwala chomwe munthu angalandire, ndiko chinthu chofunika kwambiri kuti munthu achire. Komanso, n’kwanzeru kupenda kuti uone ngati mtundu wa chithandizocho ukulimbana ndi gwero la vutolo osati zizindikiro zake zokha. Zimenezi zingachitike poona zotsatira zake pambuyo pogwiritsa ntchito chithandizocho mwa kukapimitsa ku malaboletale ndiponso kupima kogwiritsa ntchito makina a X ray.

Komabe, pali zinthu zambiri zomwe munthu angachite posankha mtundu wa chithandizo chamankhwala.

Njira Yofunika Kutsatira

N’kwanzeru kuchita kafukufuku musanasankhe chithandizo chilichonse. Dzifunseni mafunso. Kodi n’zotsatirapo zotani zomwe ndingayembekezere? Kodi ubwino wake wa chithandizocho ndi wotani, nanga kuipa kwake, ndipo chingadzawononge ndalama zingati ndiponso chidzakhala chautali wotani? Lankhulani ndi anthu amene analandirapo chithandizo chomwe mukuchilingaliracho. Afunseni ngati chinawathandiza. Komabe, kumbukirani kuti mukhoza kusokeretsedwa ndi umboni wochepa chabe wokhudza chithandizocho.

Sikungakhale kwanzeru kulandira chithandizo chamankhwala chomwe sichigwiritsidwa ntchito masiku onse chomwe chingachititse munthu kusiya kulandira chithandizo chinachake chomwe chakhala chikumuchiza kwanthaŵi yaitali, ngakhale ngati chithandizo cha masiku onsecho sichichiritsa mokwanira. Umboni wa zinthu zoopsa zomwe zingatsatirepo unalembedwapo mu lipoti la m’magazini yotchedwa The New England Journal of Medicine. Magaziniyo inafotokoza za kupitirira kwa matenda a kansa mwa odwala aŵiri achinyamata omwe anakana kulandira chithandizo chamankhwala ogwiritsidwa ntchito masiku onse pomwe ankagwiritsa ntchito chithandizo chamankhwala chomwe sichigwiritsidwa ntchito masiku onse. Mmodzi wa odwalawo anamwalira.

Anthu amene akudwala matenda aakulu kapena matenda akupha mwanzeru amakhalabe atcheru podziŵa mfundo yakuti atha kupusitsidwa mosavuta ndi akathyali amene amalimbikitsa njira zochiritsira zachinyengo. Chenjerani ndi mankhwala ena alionse amene akuti amachiza matenda osiyanasiyana. Chitsanzo cha posachedwapa ndi cha mavitamini atsopano omwe ankanena kuti “athandiza kuthetsa vuto lililonse kuyambira pa kuvutika kupuma ndiponso kusoŵa mphamvu mpaka pa matenda oika moyo pangozi.” Kupenda “mavitamini” ameneŵa kunasonyeza kuti mavitaminiwo anali madzi amchere basi opanda kanthu kena kalikonse.

Mosakayikira, njira zina zochiritsira zosagwiritsidwa ntchito masiku onse zingathandize kukhala ndi thanzi labwino. Komabe, musayembekezere zinthu mopambanitsa. N’kwanzeru kungoyesetsa kudya chakudya chopatsa thanzi, kugona mokwanira, kuchita mokwanira bwino maseŵera olimbitsa thupi, ndiponso kukhala wochenjera posankha chithandizo chamankhwala.

Mankhwala Ofunikawo Apezeka

N’zodziŵikiratu kuti palibe chithandizo chamankhwala opangidwa ndi anthu chimene chingathetseretu matenda onse ndiponso imfa. Izi zili choncho chifukwa chakuti zimenezi ndi zochokera kwa kholo lathu loyambirira, munthu woyamba kulengedwa, Adamu. (Yobu 14:4; Salmo 51:5; Aroma 5:12) Zambiri mwa zithandizo zamankhwala, kaya zikhale za mtundu wanji, mwinamwake zingasonyeze kukhala zamphamvu kwambiri, komabe zimenezi ndi njira zongoyembekezera zomwe zingatalikitseko moyo ndi kuupangitsa kukhala wosangalatsa kwambiri kwa kanthaŵi kochepa chabe. Komabe, pali mankhwala odalirika othetsera matenda, ndipo anthu miyandamiyanda apeza kale mankhwala ameneŵa.

Mankhwala ameneŵa aperekedwa ndi Mlengi wathu, Yehova Mulungu, Dokotala Wamkulu. Mwa kusonyeza chikhulupiriro mwa iye ndi kugwiritsa ntchito nsembe yadipo yowombola ku machimo ya Mwana wake, Yesu Kristu, mudzatha kusangalala ndi thanzi langwiro ndiponso moyo wosatha m’dziko lopanda matenda! (Mateyu 20:28) Baibulo limalonjeza kuti m’dziko lapansi latsopano limenelo, “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”—Yesaya 33:24.

[Mawu Otsindika patsamba 12]

Anthu miyandamiyanda apeza chiyembekezo chodalirika cha kukhala ndi thanzi langwiro