Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndiyenera Kufotokozera Munthu Wina Kuti Ndikuvutika Maganizo?

Kodi Ndiyenera Kufotokozera Munthu Wina Kuti Ndikuvutika Maganizo?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndiyenera Kufotokozera Munthu Wina Kuti Ndikuvutika Maganizo?

“Ndikavutika maganizo, sindifuna kaye kumafotokozera anthu kuopera kuti angamaganize kuti ndine mwana wovutitsa. Koma kenaka ndimazindikira kuti ndifunika kufotokozera munthu wina kuti andithandize.”—Anatero Alejandro, amene ali ndi zaka 13.

“Ndikavutika maganizo, sindifotokozera anzanga chifukwa ndimaganiza kuti iwo sangandithandize. Iwo atha kungondiseka basi.”—Anatero Arturo, amene ali ndi zaka 13.

PAFUPIFUPI munthu aliyense amavutika maganizo nthaŵi zina. * Komabe, chifukwa chakuti mudakali aang’ono ndiponso kuti simunakumane ndi zinthu zambiri, mungathe kuthedwa nzeru kwambiri ndi mavuto a m’moyo. Zofuna za makolo anu, za anzanu, ndiponso za aphunzitsi anu; kusintha kwa thupi ndi maganizo anu mukatha msinkhu; kapenanso kudandaula kuti ndinu wolephera kuchita zinthu chifukwa choti munaphonyetsa pang’ono—zinthu zonsezi zingakuchititseni kukhala ovutika maganizo ndiponso okhumudwa.

Ngati zimenezi zitachitika, ndi bwino kupeza munthu wina woti akuthandizeni maganizo. “Ndikadapanda kufotokozera munthu wina mavuto anga, ndiganiza kuti ndikanachita zoopsa kwambiri,” anatero mtsikana wina wazaka 17 wotchedwa Beatriz. Komabe, n’zomvetsa chisoni kuti achinyamata ambiri amasungira mavuto awo mumtima ndipo nthaŵi ndi nthaŵi amangozindikira kuti ataya mtima kwambiri. María de Jesús Mardomingo yemwe ndi pulofesa pa sukulu ina ya zamaphunziro a mankhwala yotchedwa Medical Faculty of Madrid, ananena kuti achinyamata amene amafuna kudzipha nthaŵi zambiri amakhala osukidwa kwambiri. Achinyamata ambiri amene apulumuka kufuna kudzipha amanena kuti iwo sanapeze wachikulire ngakhale ndi m’modzi yemwe woti akadakambirana naye ndiponso woti awathandize maganizo.

Nanga inuyo mumatani? Kodi muli naye munthu amene mungamuuze zakukhosi ngati mutavutika maganizo? Ngati mulibe, kodi mungapite kwa ndani?

Fotokozerani Makolo Anu

Alejandro yemwe mawu ake alembedwa koyambirira kuja, akulongosola motere zomwe iye amachita akavutika maganizo: “Ndimafotokozera amayi anga chifukwa chakuti chibadwireni, amayi akhala akundichirikiza ndipo amandilimbitsa mtima. Ndimafotokozeranso abambo anga chifukwa chakuti iwo anakumana ndi zinthu monga zomwe ndimakumana nazo ine. Ngati zinazake zandikhumudwitsa kwambiri ndipo sindinafotokozere munthu wina, ndimakhumudwa koposa.” Mnyamata wina wazaka 11 wotchedwa Rodolfo anakumbukira kuti: “Nthaŵi zina aphunzitsi akandinyoza ndiponso kundikalipira, ndinkakwiya kwambiri moti ndinkapita m’chimbudzi n’kukalira. Ndiyeno kenako, ndinkafotokozera amayi ndipo iwo ankandithandiza kuthetsa vutolo. Ndikadapanda kumawafotokozera, ndikanamakwiya koposerapo.”

Kodi munayamba mwaganizapo zokambirana ndi makolo anu moona mtima? Mwinatu m’maganiza kuti iwo sangamvetsetse mavuto anu. Koma kodi zimenezo n’zoona? N’kutheka kuti iwo sangamvetsetse bwino lomwe mavuto onse amene achinyamata akukumana nawo masiku ano; komabe, kodi si zoona kuti iwo ndiwo akukudziŵani bwino kwabasi kuposa mmene munthu wina aliyense amakudziŵirani padziko lapansi? Alejandro ananena kuti: “Nthaŵi zina pamakhala povuta kuti makolo anga andimvere chisoni ndiponso kuti amvetsetse mmene ndikumvera.” Komabe, iye anavomereza kuti: “Ndikudziŵa kuti ndithabe kufunsira chithandizo kwa iwo.” Nthaŵi zambiri achinyamata amadabwa pozindikira kuti makolo awo amamvetsadi mavuto awo! Popeza kuti iwo ndi achikulire ndiponso akumana ndi zinthu zambiri m’moyo, nthaŵi zambiri angapereke malangizo othandiza, ndipo zimatero makamaka ngati makolowo akudziŵa bwino kugwiritsa ntchito mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo.

“Ndikafotokozera makolo anga, ndimalimbikitsidwa ndiponso ndimalandira malangizo othandiza kuthetsa vutolo,” anatero Beatriz, yemwe mawu ake alembedwa koyambirira kuja. N’chifukwa chake Baibulo limalangiza kuti: “Mwananga, sunga malangizo a atate wako, usasiye malamulo a amako; tamvera atate wako anakubala, usapeputse amako atakalamba.”—Miyambo 6:20; 23:22.

N’zoona kuti kuulula zakukhosi kwa makolo n’kovuta ngati simugwirizana bwinobwino. Malinga ndi zimene Dr. Catalina González Forteza ananena, kufufuza komwe anakuchita pakati pa ophunzira akusekondale kwasonyeza kuti ophunzira amene ananena kuti anafunapo kudzipha ankadziona ngati osafunika ndiponso sankagwirizana kwenikweni ndi makolo awo. Mosiyana ndi zimenezo, achinyamata amene amapeŵa maganizo odzipha otereŵa kaŵirikaŵiri amakhala “omwe ali ndi unansi wabwino ndi mayi awo komanso bambo awo.”

Choncho, chitani mwanzeru mwakuyamba kugwirizana bwino ndi makolo anu. Khalani ndi chizoloŵezi cholankhula nawo nthaŵi ndi nthaŵi. Afotokozereni zomwe zikukuchitikirani m’moyo wanu. Afunseni mafunso. Kulankhulana momasuka koteroko kungachititse kuti muzitha kuwafikira mosavuta mukakhala ndi vuto.

Kufotokozera Mnzanu

Koma kodi chidule si ndicho kungofotokozera wachinyamata mnzako mavutowo? Eya, ndi bwino kukhala ndi mnzako amene ungamudalire. Miyambo 18:24 imanena kuti “koma lilipo bwenzi lipambana mbale kuumirira.” Ngakhale kuti anzanu angakumvereni chisoni ndiponso kukuthandizani, iwo sangakuuzeni malangizo abwino zedi nthaŵi zonse. Ndiponsotu, iwo nthaŵi zambiri sadziŵa zinthu zoposa zimene inuyo mukudziŵa. Kodi mukukumbukira zimene zinam’chitikira Rehabiamu? Iye anali mfumu m’nthaŵi za Baibulo. Mmalo momvera malangizo a anthu odziŵa zinthu ndiponso okhwima maganizo, iye anamvera achinyamata anzake. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Linali tsoka ladzaoneni! Rehabiamu analeka kuchirikizidwa ndi anthu ake ndiponso kuyanjidwa ndi Mulungu.—1 Mafumu 12:8-19.

Vuto linanso la kufotokozera anzanu zakukhosi lingakhale la kusasunga chinsinsi. Arturo yemwe mawu ake alembedwa koyambirira kuja ananena kuti: “Anyamata ambiri amene ndimawadziŵa, amafotokozera anzawo akakhumudwa. Koma kenaka, anzawowo amaulula zonse kwa anthu ena ndipo amawaseka.” Mtsikana wina wazaka 13 wotchedwa Gabriela zinam’chitikirapo zoterezi. Iye ananena kuti: “Tsiku lina ndinatulukira kuti mnzanga anali kuuza anzake ena nkhani zanga zachinsinsi, chotero sindinkamuuzanso nkhani zina. N’zoona kuti ndimacheza ndi anthu amsinkhu wanga, koma ndimayesetsa kuti ndisawauze zinthu zimene zingandikhumudwitse kwambiri ngati atauza anthu ena.” Choncho, pamene mukufuna chithandizo, n’kofunika kupeza munthu “wosaulula zinsinsi za mwini.” (Miyambo 25:9) Munthu woteroyo mwachionekere angakhale wachikulirepo kuposa inuyo.

Ndiyeno ngati pazifukwa zina simukuthandizidwa kunyumba, palibe cholakwa kufotokozera mnzanu, komano wonetsetsani kuti mnzanuyo akhale wodziŵa zinthu ndiponso akhale ndi chidziŵitso cha mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo. Mumpingo wa Mboni za Yehova wakwanuko, mosakayikira muli anthu oyenerera oterowo. Mtsikana wina wazaka 16 wotchedwa Liliana ananena kuti: “Ndakhala ndikuuza zakukhosi alongo anzanga achikristu ndipo zimenezi zakhala zosangalatsa kwambiri. Popeza kuti iwo ndi achikulirepo kuposa ine, malangizo awo n’ngwothandizadi. Iwo angosanduka anzanga tsopano.”

Nanga bwanji ngati mwayamba kufooka mwauzimu? Mwinamwake mwakhala muli wokwiya kwambiri kwakuti mpaka mwayamba kunyalanyaza kupemphera ndiponso kuŵerenga Baibulo. Pa Yakobo 5:14, 15, Baibulo limapereka malangizo aŵa: “Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a Mpingo, ndipo apemphere pa iye, atam’dzoza ndi mafuta m’dzina la Ambuye: ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa.” Mpingo wa Mboni za Yehova wakwanuko uli ndi akulu amene athandizapo kale anthu ofooka ndiponso odwala mwauzimu. Khalani womasuka kulankhula nawo. Baibulo limanena kuti amuna otereŵa angakhale monga “pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo.”—Yesaya 32:2.

“Zopempha Zanu Zidziŵike kwa Mulungu”

Komabe, gwero la chithandizo chabwino koposa ndilo “Mulungu wa chitonthozo chonse.” (2 Akorinto 1:3) Pamene mwakhumudwa kapena kuvutika maganizo, tsatirani malangizo a pa Afilipi 4:6, 7 akuti: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” Yehova nthaŵi zonse amakhala wofunitsitsa kukumverani. (Salmo 46:1; 77:1) Ndipo nthaŵi zina pemphero ndilo limafunika kuti mukhazike mtima pansi.

Ngati mumakhumudwa kapena kuvutika maganizo nthaŵi zina, kumbukirani kuti achinyamata enanso ambiri ali ndi vuto lomwelo. M’kupita kwanthaŵi maganizo oterowo adzatha. Koma padakali pano, musamavutike nokha. Fotokozerani munthu wina kuti mukuvutika maganizo. Miyambo 12:25 imati: “Nkhaŵa iweramitsa mtima wa munthu; koma mawu abwino aukondweretsa.” Kodi mungawapeze bwanji “mawu abwino” olimbikitsa? Mwa kufotokozera munthu wina wodziŵa zinthu, wanzeru, ndiponso wanzeru zaumulungu kuti akutonthozeni komanso kukupatsani chithandizo chomwe mukufuna.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Ngati kuvutika maganizo kukupitirizabe, kungasonyeze matenda aakulu athupi kapena amaganizo. Motero, ndi bwino kupita kuchipatala msanga. Onani nkhani yakuti “Kupambana Nkhondo Yolimbana ndi Kuchita Tondovi” m’kope la March 1, 1990 la magazini inzake ya magazini ano yotchedwa Nsanja ya Olonda.

[Mawu Otsindika patsamba 14]

“Ndikafotokozera makolo anga, ndimalimbikitsidwa ndiponso ndimalandira malangizo othandiza kuthetsa vutolo”

[Chithunzi patsamba 15]

Nthaŵi zambiri makolo oopa Mulungu ndiwo angathe kukupatsani malangizo abwino kusiyana ndi a anzanu.