Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Nyenyezi Zolosera za M’tsogolo Ziyenera Kulamulira Moyo Wanu?

Kodi Nyenyezi Zolosera za M’tsogolo Ziyenera Kulamulira Moyo Wanu?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Nyenyezi Zolosera za M’tsogolo Ziyenera Kulamulira Moyo Wanu?

“ACHINYAMATA NDI ACHIKULIRE AMENE AMAPENDA ZIZINDIKIRO ZA M’NYENYEZI KUTI ADZIŴE TSOGOLO LAWO ALIPO AMBIRIMBIRI.”—PAPA YOHANE PAULO WACHIŴIRI.

KAUNDULA wina wasonyeza kuti munthu m’modzi mwa anthu anayi alionse a ku America amapenda kaye nyenyezi posankha zoti achite. Sikuti, kupenda zizindikiro za m’nyenyezi kumachitika m’dziko lokhali ayi. Pafupifupi kulikonse padziko lapansi anthu amapenda nyenyezi kuti apeze malangizo pankhani za chuma, kukonzekera ulendo, mwayi wantchito, masiku aukwati ndiponso njira zomenyera nkhondo. Akuti chizindikiro cha m’nyenyezi cha munthu chingam’sonyeze omwe angakwatirane nawo ndiponso ngakhale amene sangagwirizane ngati atakwatirana nawo. Kuchokera Kum’maŵa mpaka Kumadzulo kukhulupirira nyenyezi kwakopa anthu miyandamiyanda. Koma kodi kupenda nyenyezi zolosera za m’tsogolo zimenezi kunayamba bwanji?

Mbiri ya Kuyamba Kwake

Nyenyezi zamitundu yosiyanasiyana zolosera za m’tsogolo zinaliko ngakhale kale kwambiri m’magulu a anthu okhala pamodzi amakedzana. Ngakhale Baibulo limatchula za “nthanda.” (2 Mafumu 23:5) Zikuoneka kuti kalelo kupenda nyenyezi kunkachitidwa ndi Ahindu, Atchaina, Aigupto, Agiriki ndiponso mitundu ina ya anthu. Komabe, mabuku akale kwambiri onena za kupenda nyenyezi anapezeka m’Babulo wakale.

Ababulo anayambitsa kukhulupirira nyenyezi pofuna kudziŵa za m’tsogolo. Ankati akadziŵa kayendedwe ka zinthu zakuthambo, iwo ankapanga matchati ndiponso ndandanda za nyenyezi. Pogwiritsa ntchito zinthu zimenezi, zochitika za anthu ndiponso zakuthambo zinali kuloseredwa. Nthaŵi zambiri, sankasankha kuchita chilichonse pankhani zandale kapena zankhondo pokhapokha openda nyenyezi akaperekapo malangizo awo. Motero, panakhala gulu la ansembe odzinenera kuti ali ndi nzeru ndiponso mphamvu zaumulungu ndipo gululi linali ndi matama adzaoneni moti linakopa anthu ambiri. Ndiponsotu akachisi ofunika kwambiri a m’Babulo anali ndi gawo lina lopendera zakuthambo.

Masiku ano zizindikiro za m’nyenyezi zikupitirizabe kugwira ntchito m’miyoyo ya anthu ambiri. Ngakhale anthu ena amene amati sakhulupirira ndandanda ya nyenyezi zolosera za m’tsogolo, amaigwiritsabe ntchito pofuna kungosangalala kapena pofuna kungoiona chabe. N’zoona kuti zachitikapo kuti zinthu zina zomwe openda nyenyezi alosera zakhala zoona. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti kukhulupirira nyenyezi n’kopindulitsa? Iyayi, kodi atumiki akale a Mulungu anaiona motani nkhani yokonda kukhulupirira nyenyezi?

Ngozi Zobisika

Mosiyana ndi Ababulo, Ayuda okhulupirika sankakhulupirira nyenyezi ndipo ankachita zimenezo pachifukwa chomveka. Mulungu anawachenjeza mosapita m’mbali kuti: ‘Asapezeke mwa inu munthu . . . wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa. Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.’ *Deuteronomo 18:10-12.

Atumiki a Mulungu anakana kwamtuwagalu kukhulupirira nyenyezi. Mwachitsanzo, Mfumu yokhulupirika Yosiya “analetsa ofukizira zonunkhira Baala, ndi dzuŵa, ndi mwezi, ndi nthanda.” Zomwe Yosiya anachita akuti zinali “zowongoka pamaso pa Yehova” ndipo Mulungu anam’dalitsa chifukwa cha zimenezi. (2 Mafumu 22:2; 23:5) Koma anthu ena angafunse kuti ‘Bwanji nanga zinthu zina zomwe openda nyenyezi amanena zimachitikadi?’

N’zochititsa chidwi kuti m’Malemba Achigiriki Achikristu timaŵerenga nkhani ya mtsikana yemwe “anapindulira ambuye ake zambiri pakubwebweta pake.” Zikuoneka kuti zinthu zina zimene mtsikanayo anali kulosera zinkachitikadi popeza kuti mbuye wake anapindula ndi kubwebweta kwa mtsikanayo. Koma kodi mtsikanayu mphamvu yolosera za m’tsogolo ankaipeza kuti? Baibulo limanena kuti iye anali kuthandizidwa ndi “mzimu wambwebwe.”—Machitidwe 16:16.

Baibulo limasonyeza kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo,” Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Mwakuchititsa zinthu zina kuti atheketse zolosera zina kuti zichitikedi, Satana ndi ziwanda akopa anthu miyandamiyanda.

Zoona zake n’zakuti kukhulupirira nyenyezi ndiwo amodzi mwa ‘machenjera a Mdyerekezi,’ amene amagwiritsa ntchito kulamulira ndiponso kukopera anthu kuti azitumikira zofuna zake. N’chifukwa chake n’zosadabwitsa kuti Baibulo limalangiza Akristu “kuchirimika” kukana nyambo za Satana zomwe zimaphatikizapo kukhulupirira nyenyezi. (Aefeso 6:11) Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti tinasiyidwa opanda chotitsogolera pa za m’tsogolo?

Baibulo Ndilo Chotitsogolera Chodalirika

Anthu miyandamiyanda aona kuti Baibulo ndilo chowatsogolera chodalirika posankha zoti achite. Monga ananenera wamasalmo Davide, “Mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru.” (Salmo 19:7; 119:105) Zimenezi sizikutanthauza kuti Baibulo limatchula mwatsatanetsatane zimene munthu ayenera kuchita pankhani iliyonse. Komabe Mawu a Mulungu ali ndi mfundo zimene zingaphunzitse mphamvu zathu za kuzindikira. Mphamvu zimenezi n’zimene zidzatitheketsa kudziŵa chabwino ndi choipa ndiponso zingatithandize kusankha mwanzeru zoti tichite.—Ahebri 5:14.

N’chifukwa chake zili zomveka kuti Akristu oona sagwiritsira ntchito ndandanda ya nyenyezi zolosera za m’tsogolo ngakhale pofuna kungosangalala kapena kufuna kungoiona chabe. Mmalo mwake, iwo mwanzeru amamvera machenjezo a m’Mawu a Mulungu oletsa mitundu yonse ya zinthu zokopa za ziwanda kuphatikizapo mitundu ina yovuta kuizindikira. Mwakulola Baibulo kulamulira moyo wanu kusiyana ndi kukopeka ndi kukhulupirira nyenyezi, mungathe kukhala ndi madalitso a Mulungu kwamuyaya.—Salmo 37:29, 38.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Kusamalira mitambo kumaphatikizapo zochita zonse zofuna kudziŵa zinthu makamaka zam’tsogolo kudzera m’mphamvu ya mizimu.

[Chithunzi patsamba 16]

Nyenyezi zolosera za m’tsogolo za ku mayiko akum’maŵa

[Chithunzi patsamba 16]

Nyenyezi zolosera za m’tsogolo za ku mayiko akumadzulo