Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufuna Kuchotsa Boma la Vatican M’bungwe la UN

Kufuna Kuchotsa Boma la Vatican M’bungwe la UN

Kufuna Kuchotsa Boma la Vatican M’bungwe la UN

BUNGWE lofalitsa nkhani lomwe lili ku Rome lotchedwa Inter Press Service (IPS) linanena kuti “mgwirizano wa mabungwe omwe si a boma (NGO) a pa dziko lonse opitirira 70 wayamba ntchito yapadziko lonse yofuna kuchotsa boma la Vatican m’bungwe la United Nations.” Padakali pano, boma la Vatican lili ndi udindo wachikhalire woyang’anira zochitika m’bungweli kapena kuti limakhala monga dziko lomwe si membala wa bungwe la UN. Boma la Vatican linakhala pa udindowu kuchokera mu 1964.

N’chifukwa chiyani gulu la mabungwe omwe si a boma limeneli lomwe kumapeto kwa April chaka chatha linali litakula kufika pa mabungwe 100 padziko lonse, silikugwirizana ndi udindo umene boma la Vatican lili nawo m’bungwe la UN? N’chifukwa chakuti mabungwe omwe si a bomawa anati Vatican ndi boma lachipembedzo osati dziko landale. Frances Kissling yemwe ndi pulezidenti wa bungwe la ufulu wodzisankhira wa akatolika lotchedwa Catholics for a Free Choice, anauza atolankhani a bungwe la IPS kuti mgwirizano wa mabungwe ameneŵa sikuti sukugwirizana ndi ufulu wa boma la Vatican wolankhula maganizo ake, koma nkhani yagona pa ufulu umene bomali, lomwe si dziko landale, lili nawo womachita zinthu pamodzi ndi mayiko.”

Anika Rahman, yemwe ndi mkulu wa Mapulogalamu Apadziko Lonse m’bungwe la Centre for Reproductive Law and Policy, anavomereza zimenezi. Bungwe la IPS linalemba mawu omwe iye ananena kuti “ngati bungwe la UN limaona Holy See (boma lolamulidwa ndi papa) monga dziko loyenera mwayi wokhala ndi udindo woyang’anira wachikhalire chifukwa cha mphamvu zake zachipembedzo, ndiye kuti bungweli likuyambitsa zoti zipembedzo zina nazonso ziyambe kufuna mwayi wofananawo.” Iye anawonjezera kuti: “Pofuna kutsimikiza kuti bungwe la United Nations silichirikiza chipembedzo china chilichonse, magulu achipembedzo monga ngati la Tchalitchi cha Roma Katolika sayenera kuloledwa kukhala nawo pa zokambirana za bungweli pomati iwo ndi dziko lomwe si membala.”

Koma bwanji nanga za mfundo yakuti Vatican ndi dziko kotero kuti n’loyenerera udindo womwe lili nawo? “Zimenezo n’zosamveka ndipo kutero n’kulankhula mosokoneza anthu,” anayankha motero Ms. Kissling pomwe ankamufunsa mafunso. “Mfundo yathu n’njakuti, Vatican linali dziko, m’zaka za m’ma 1400 malinga ndi tanthauzo la panthaŵiyo la mawu akuti dziko, koma zoona zake n’zakuti, Holy See ndi bungwe lolamulira chipembedzo. Iye ananenanso kuti, mawu onse aŵiri akuti “Vatican” ndiponso “Holy See” ali mawu ofanana ndi mawu akuti Tchalitchi cha Roma Katolika.”

Kuipidwa kwa mabungwe omwe si a boma pankhani ya udindo umene boma la Vatican lili nawo m’bungwe la UN kunayamba chifukwa cha maganizo a boma la Vatican pankhani ya kuchulukana kwa anthu. Mwachitsanzo, boma la Vatican lagwiritsa ntchito misonkhano ikuluikulu ya bungwe la UN monga umene unachitikira ku Cairo m’1994 wotchedwa International Conference on Population and Development (Msonkhano Wapadziko Lonse Pankhani ya Chiŵerengero cha Anthu ndi Chitukuko) ndiponso womwe unachitikira ku Beijing m’1995 wotchedwa Women’s Conference (Msonkhano Waukulu wa Amayi) kulankhulira maganizo ake otsutsa kwabasi njira za kulera. Popeza kuti mfundo zambiri za bungwe la UN zimadalira kuti ambiri azivomereze,” inatero IPS, “maganizo otsutsa a boma la Vatican asokoneza zokambirana zokhudza nkhani ya kuchulukana kwa anthu, njira za kulera, ufulu wa amayi, ndiponso chithandizo chamankhwala chokhudza kubereka.”

Malinga ndi zomwe ananena Ms. Kissling “udindo wa boma la Vatican n’ngwoyenera mabungwe omwe si a boma, mofanana ndi mabungwe ena otereŵa omwe amaimira Asilamu, Ahindu, Abuda, Abahai ndiponso magulu ena achipembedzo.” Mgwirizano wa mabungwe umenewu ukufuna kuti Mlembi Wamkulu wa bungwe la UN a Kofi Annan pamodzi ndi gulu lonse lotchedwa General Assembly lomwe limayendetsa bungweli, aonenso bwino udindo wa boma la Vatican m’bungwe landale lalikulu kwambiri padziko lonse limeneli.

[Chithunzi patsamba 31]

Mkulu wa ku Vatican akulankhula pamsonkhano wa UN

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi cha UN/DPI chojambulidwa ndi Sophie Paris

Chithunzi cha UN 143-936/J. Isaac