Kupenda Njira Zochiritsira Zosagwiritsidwa Ntchito Masiku Onse
Kupenda Njira Zochiritsira Zosagwiritsidwa Ntchito Masiku Onse
“Kuyamba kukambirana n’cholinga chofuna kugaŵana nzeru pakati pa madokotala omwe amagwiritsa ntchito njira zochiritsira zamasiku onse ndi madokotala omwe amagwiritsa ntchito njira zochiritsira zosagwiritsidwa ntchito masiku onse, n’kofunika kwambiri kaamba ka umoyo wabwino kwa odwala amene amasankha njira zochiritsira zosagwiritsidwa ntchito masiku onse.”
MAWU ameneŵa analembedwa m’kope la pa November 11, 1998, la magazini yotchedwa The Journal of the American Medical Association (JAMA). Nkhaniyo inanena kuti: “Kufunika [kwa kukambirana] kumeneku, kungayembekezereke kukula malinga ndi kugwiritsidwa ntchito kwa njira zochiritsira zosagwiritsidwa ntchito masiku onse, makamaka pamene ma inshuwalansi a zaumoyo akukonza zoti njira zochiritsira zamtunduwu zizilipiridwanso ndi inshuwalansi.”
Odwala ambiri amagwiritsa ntchito njira zochiritsira zosagwiritsidwa ntchito masiku onse komanso panthaŵi yomweyo amagwiritsa ntchito njira zochiritsira zogwiritsidwa ntchito masiku onse. Ngakhale zili choncho, anthu ena amalephera kudziŵitsa dokotala wawo zomwe iwo akuchita. Choncho, chikalata chotchedwa Tufts University Health & Nutrition Letter cha April 2000 chinalangiza kuti: “Muyenera kugwirizana ndi dokotala wanu mukamachita zinthu zomwe mukuona kuti n’zokupindulitsani m’malo mongodzichitira nokha.” Chikalatacho chinalangizanso kuti: “Kaya dokotalayo avomereza malingaliro anu, komabe inu mumapindula mwa kukambirana naye nkhaniyo.”
Zimenezi zinanenedwa chifukwa cha ngozi zomwe zingakhalepo ngati mankhwala ena ake azitsamba ataphatikizidwa
ndi mankhwala ochiritsira omwe amagwiritsidwa ntchito masiku onse. Pozindikira kuti ena mwa odwala awo akusankha kugwiritsa ntchito njira zochiritsira zosagwiritsidwa ntchito masiku onse, akatswiri ambiri a zamankhwala amayesetsa kuti zomwe iwo akulingalira pankhani zaumoyo zisawalepheretse kugwira ntchito limodzi ndi madokotala omwe amagwiritsa ntchito njira zochiritsira zosagwiritsidwa ntchito masiku onse n’cholinga chofuna kuthandiza wodwala.Kuti tipatse oŵerenga athu chithunzithunzi cha njira zochiritsira zosagwiritsidwa ntchito masiku onse zimene tsopano anthu ambiri akuzigwiritsa ntchito m’mayiko ambiri, tsopano tilongosola mwachidule njira zochepa chabe mwa njira zimenezi. Komabe, dziŵani kuti Galamukani! sikuikira kumbuyo chithandizo china chilichonse mwa zithandizo zamankhwala zimenezi kapenanso chithandizo chamankhwala cha mtundu wina uliwonse.
Mankhwala Azitsamba
Njira imeneyi mwinamwake ndiyo njira yochiritsira yofala kwambiri pa njira zochiritsira zosagwiritsidwa ntchito masiku onse. Ngakhale kuti zitsamba zagwiritsidwa ntchito popanga mankhwala kwazaka mazana ambiri, pali mitundu yochepa kwambiri ya zomera yomwe asayansi aiphunzira mosamala kwambiri. Ndiponso n’chiŵerengero chochepa kwambiri cha mitundu ya zomera ndi magawo ake zimene zaphunziridwa mozama kwambiri kwakuti pali chidziŵitso cha ubwino wake ndiponso mphamvu zake. Chidziŵitso chochuluka chokhudza mankhwala azitsamba n’chochokera pa zinthu zomwe zinachitikapo m’mbiri ya mmene amagwiritsidwira ntchito.
Komabe, m’zaka zaposachedwapa pakhala pakuchitika kafukufuku wasayansi yemwe akusonyeza phindu la mankhwala azitsamba pochiza matenda monga a kuvutika maganizo, kuiwalaiwala chifukwa cha ukalamba, ndiponso kutupa kwa ziŵalo zina zoberekera za amuna. Chitsamba chimodzi chimene chinafufuzidwa chimatchedwa kuti black cohosh, (chomwe ndi 3chofanana ndi chivumulo) chimene nthaŵi zina chimadziŵika ndi mayina akuti black snakeroot, bugbane, kapena rattleroot. Amwenye a ku America ankaphika muzu wake ndi kuugwiritsa ntchito pa mavuto a kusamba kwa akazi ndiponso mavuto ena a panthaŵi yobereka. Malinga ndi zomwe chikalata chotchedwa Harvard Women’s Health Watch cha April 2000 chinanena, kafukufuku wa posachedwapa akusonyeza kuti mankhwala okonzedwa bwino omwe amagulitsidwa m’dziko la Germany opangidwa kuchokera ku chitsamba chotchedwa black cohosh angathandize “kuchiza matenda ena omwe amadza chifukwa cha mavuto a kusamba kwa akazi.”
Zikuoneka kuti mankhwala achilengedwe oterowo akufunika kwambiri chifukwa chakuti anthu amadziŵa kuti mankhwalaŵa ndi abwinopo kusiyana ndi mankhwala omwe sapangidwa mwachilengedwe. Ngakhale kuti zimenezi zingakhale zoona, zitsamba zina zimayambitsa matenda ena, makamaka ngati zagwiritsidwa ntchito limodzi ndi mankhwala a mitundu ina opangidwa m’mafakitale. Mwachitsanzo, chitsamba chodziŵika bwino kwambiri chimene amati ndi mankhwala achilengedwe othandiza kuchiza matenda
monga nyamakazi ndiponso kuthandiza kuti munthu akhale wochepa thupi, chikhoza kuwonjezera BP ndiponso kugunda kwa mtima.Palinso zitsamba zina zomwe zingawonjezere mlingo wa mmene wodwala amatayira magazi akavulala. Ngati zitsamba zimenezi zitagwiritsidwa ntchito limodzi ndi mankhwala othandiza “kupepukitsa magazi”, pangakhale zotsatirapo zoopsa kwambiri. Anthu amene akudwala matenda aakulu, monga matenda a shuga kapena BP, kapena anthu amene akumwa mankhwala ena ake opangidwa m’mafakitale ayenera kukhala osamala kwambiri pankhani ya kugwiritsa ntchito mankhwala azitsamba.—Onani bokosi limene lili m’nkhani ino.
Chodetsa nkhaŵa china ponena za mankhwala azitsamba n’chakuti sakhala odalirika kwenikweni kuti apangidwa molongosoka. M’zaka zaposachedwapa pakhala pakumveka kuti mankhwalaŵa amakhala ophatikizika ndi michenga yambirimbiri ndiponso zinthu zina. Komanso, mankhwala ena azitsamba apezeka kuti amakhala ndi zinthu zochepa kwambiri zomwe zimasonyezedwa pa malebulo osonyeza zinthu zomwe apangira mankhwalawo mwinanso sakhala nazo n’komwe. Zitsanzo zimenezi zikusonyeza kufunika kogula mankhwala opangidwa kuchokera ku zitsamba ndiponso mankhwala ena alionse kuchokera kwa anthu odziŵika bwino ndiponso odalirika.
Mankhwala Opatsa Thanzi
Mankhwala opatsa thanzi, monga mavitamini ndi maminero, akuti athandiza kwambiri popewa ndiponso kuchiza matenda ambiri kuphatikizapo kusoŵa magazi m’thupi ndi kufooka kwa mafupa, ndiponso
ngakhale kupewa zilema zobadwa nazo. Mlingo wovomerezeka ndi boma wa mavitamini ndi maminero ofunika kumwa patsiku ndiwo amauona kukhala woyenerera ndi wothandiza kwambiri.Mosiyana ndi zimenezo, kumwa mankhwala amavitamini ochuluka kwambiri chifukwa cha matenda ena ake kungakhale kwangozi. Mankhwalawo angathe kusokoneza mosavuta kapukusidwe ka zakudya kapena mmene zakudya zina zomanga thupi zimagwirira ntchito ndiponso angachititse matenda ena oopsa kwambiri. M’posafunika kunyalanyaza mfundo yakuti pangakhale ngozi zoterozo komanso mfundo yakuti palibe umboni weniweni womwe umachirikiza kuti munthu ayenera kumwa mankhwala a mavitamini ochuluka.
Kufooketsa Tizilombo Toyambitsa Matenda
Kuchiritsa kogwiritsa ntchito mankhwala amene angayambitse matenda ena ake m’thupi la munthu yemwe sakudwala matendawo, n’cholinga chofuna kuti tizilombo toyambitsa matenda amene akudwalawo tifooke kunayamba m’zaka za m’ma 1700 monga njira yabwino yochiritsira, ndiponso yapamwamba kusiyana ndi njira zomwe zinkagwiritsidwa ntchito mofala kwambiri m’masiku amenewo. Kuchiritsa kwamtundu umenewu kumadalira pa mfundo yakuti “zinthu zofanana zimagonjetsana zokhazokha” ndiponso pa mfundo ya kumwa mankhwala mwapang’onopang’ono. Mankhwala ochiritsa mwanjira imeneyi amakonzedwa mwa kusukulutsa mobwerezabwereza mankhwala omwe amachiritsa matendawo, ndipo nthaŵi zina, amawasukulutsa kwambiri moti ngakhale kam’bulu kamodzi ka mankhwala oyambirirawo sikapezekanso m’mankhwala omwe akonzedwawo.
Komabe, poyerekeza ndi kugwiritsa ntchito mankhwala opha ululu, mankhwala ofooketsa tizilombo toyambitsa matenda anapezeka kuti angachiritseko matenda ena monga chifuwa cha mphumu, ziŵengo, ndi kutsekula m’mimba kwa ana aang’onoang’ono. Mankhwala ofooketsa tizilombo ameneŵa amaoneka kuti ndi otetezeka, chifukwa chakuti amakhala osukulutsidwa. Nkhani yosindikizidwa m’kope la pa March 4, 1998, la magazini yotchedwa JAMA inati: “Kwa odwala ambiri amene ali ndi matenda aakulu omwe sakudziŵika bwinobwino, kuchiritsa mwanjira yofooketsa tizilombo toyambitsa matendawo kungakhale kofunika ndiponso kwabwino kwambiri. Ngati atagwiritsidwa ntchito moyenerera, mankhwalaŵa angamagwirire ntchito limodzi ndi mankhwala amakono n’kukhala monga ‘chida chinanso pa zida zogonjetsera matenda.’” Komabe, pazochitika zadzidzidzi zoika moyo pangozi, n’kwanzeru kugwiritsa ntchito kwambiri chithandizo cha njira zochiritsira zomwe zimagwiritsidwa ntchito masiku onse.
Kuwongola Mafupa a Msana
Pali njira zambiri zochizira zimene sizigwiritsidwa ntchito masiku onse zomwe zimagwira ntchito mwa kusinikasinika ziŵalo zina m’thupi. Kuwongola mafupa a msana ndi imodzi mwa njira zochizira zimene sizigwiritsidwa ntchito kaŵirikaŵiri zomwe zili zofala kwambiri, makamaka ku United States. Kuwongola mafupa a msana kumagwiritsidwa ntchito chifukwa cha malingaliro akuti munthu angathe kuchira ngati mafupa a msana omwe anasemphana abwezeretsedwa m’malo mwake. N’chifukwa chake madokotala owongola mafupa amaika maganizo kwambiri pa kusinikasinika msana kuti abwezeretse fupa la msana m’malo mwake.
Kaŵirikaŵiri njira zochiritsira zomwe zimagwiritsidwa ntchito masiku onse sizithetsa kupweteka kwa msana. Komabe, odwala ena amene amalandira chithandizo cha kuwongola mafupa a msana amanena kuti amapezako bwino kwambiri. Kupatula pa kusinikasinika msana n’cholinga chothetsa kupweteka kwa msana, pali umboni wochepa wochirikiza kugwiritsa ntchito njirayi kaamba ka matenda a mitundu ina.
Kusinikasinika msana n’cholinga chofuna kuwongola mafupa kungayambitse matenda ena ochepa zedi ngati kutachitidwa ndi katswiri. Komabe, munthu ayeneranso kuzindikira kuti kusinika fupa la pakhosi kungayambitse matenda oopsa kwambiri, kuphatikizapo stroko ndiponso kufooka kwa ziŵalo. Kuti achepetse ngozi yoti munthu atha kudwala pambuyo poti wasinikidwa msana, akatswiri ena amalangiza kuti munthu ayenera kuyamba wapimidwa kaye n’cholinga chofuna kuona ngati munthuyo ndi woyenera kusinikidwa kwa mtundu winawake.
Kutikita Minofu
Phindu la kutikita minofu lakhala likudziŵika kuyambira kalekale pafupifupi m’mitundu yonse ya anthu. Kugwiritsidwa ntchito kwake kwafotokozedwa ngakhale m’Baibulo. (Estere 2:12, NW) “Kutikita minofu kumathandiza kwambiri pa chithandizo chamankhwala cha miyambo ya anthu a ku China ndi ku India,” inatero magazini yotchedwa British Medical Journal (BMJ) ya pa November 6, 1999. “Kutikita minofu komwe kunkachitika ku Ulaya kunapangidwa kukhala kwadongosolo lapamwamba m’zaka za zana la 19 ndi Per Henrik Ling, amene anayambitsa kutikita komwe tsopano kumadziŵika ndi dzina lakuti Swedish massage.”
Anthu amanena kuti kutikita minofu kumathandiza kuti minofu ikhale yotakasuka, kuti magazi aziyenda bwino, ndiponso kuchotsa makemikolo oipa m’minofu. Madokotala masiku ano amatikita minofu chifukwa cha matenda monga kupweteka kwa msana, litsipa, ndiponso matenda ena okhudza kagayidwe ka chakudya m’thupi. Anthu ambiri amene amalandira chithandizo cha kutikita minofu amanena kuti chithandizochi chimawapangitsa kupeza bwino. Malinga ndi zomwe ananena Dr. Sandra McLanahan, “80 peresenti ya matenda a anthu amakhudzana ndi kufooka kwa thupi, ndipo kutikita minofu kumachepetsa vuto la kufooka kwa thupi.”
“Kutikita minofu kuli ndi ngozi yochepa ya kuyambitsa mavuto ena,” inatero magazini ya BMJ. “Kusagwiritsa ntchito njira yotikita minofu kumadalira kwambiri pa kuzindikira mtundu wa matenda (mwachitsanzo, n’kosayenera kutikita zilonda zamoto kapena kutikita mwendo kapena dzanja limene lili ndi mphuwa) . . . Palibe umboni wosonyeza kuti kutikita minofu ya anthu odwala matenda a kansa kungawonjezere vuto la kufalikira kwa matendaŵa ku ziŵalo zina.”
“Pamene kutikita minofu kukufala kwambiri, anthu amene amatikitidwawo akuyamba kuda nkhaŵa ponena za ziyeneretso za madokotala otikita minofuwo, ndipo ayenera kuterodi,” anatero E. Houston LeBrun, pulezidenti wakale wa bungwe loona za kutikita minofu lotchedwa American Massage Therapy Association. Magazini ya BMJ inalangiza kuti odwala angapewe kutikitidwa ndi anthu opanda luso lokwanira “mwa kuonetsetsa kuti owatikitawo ndi ovomerezeka ndi bungwe loyenerera.” Lipoti lina la chaka chatha linanena kuti madokotala a chithandizochi ankalandira chilolezo cha ntchito yawo m’maboma 28 a m’dziko la United States.
Kutema Mphini
Kutema mphini ndi njira yochiritsira yomwe yafala kwambiri padziko lonse lapansi. Ngakhale kuti mawu akuti “kutema mphini” amanena za njira zochuluka zosiyanasiyana, njirayi kaŵirikaŵiri imakhudzana ndi
kuboolaboola malo ena ake m’thupi mogwiritsa ntchito timasingano ting’onoting’ono n’cholinga choti munthu achire. Kafukufuku wochitika kwa zaka makumi angapo zapitazi akusonyeza kuti nthaŵi zina kutema mphini m’malo ena ake m’thupi kungathandize chifukwa chakuti kumatulutsa makemikolo a m’minyewa, monga endorphis, omwe angathandize kuthetsa ululu ndi kutupa.Kafukufuku wina akusonyeza kuti kutema mphini kungathandize kuchiza matenda a mitundu ingapo ndiponso kuti ili njira yabwinopo kusiyana ndi njira yochizira yochititsa dzanzi. Bungwe la Zaumoyo wa Anthu Padziko Lonse limavomereza kugwiritsa ntchito njira yochizira ya kutema mphini pochiza matenda amitundumitundu okwana 104. Ndipo komiti yokhazikitsidwa ndi bungwe la U.S. National Institutes of Health inapereka umboni wosonyeza kuti kutema mphini ndi njira yochiritsira yovomerezeka yothetsera ululu womwe umakhalapo pambuyo pochitidwa opaleshoni, kupweteka kwa minofu, kupweteka komwe akazi amamva panyengo yosamba, ndiponso nseru komanso kusanza chifukwa cha njira yochiritsira yogwiritsa ntchito mankhwala amakemikolo kapena chifukwa chakuti mayi ali ndi pakati.
Ngakhale kuti kutema mphini sikungayambitse matenda ena oopsa kwambiri, anthu amene amatemedwawo angathe kumva ululu, kuchita dzanzi, kapena kumva kulasalasa m’thupi. Kuŵiritsa bwino masingano, kapena kugwiritsa ntchito masingano omwe anapangidwa kuti akagwiritsidwa ntchito kamodzi azitayidwa, kungathandize kuchepetsa ngozi ya kupatsirana matenda. Madokotala ambiri ogwiritsa ntchito njira yochiritsira ya kutema mphini alibe luso lenileni lofunika kuti adziŵe matenda enieni kapena kupereka chithandizo china chowonjezera chomwe chingakhale choyenerera. Kungakhale kupusa kunyalanyaza mfundo yakuti iwo alibe luso lozindikirira matenda makamaka ngati mukusankha kutemedwa mphini n’cholinga chofuna kuchiza matenda ena obwera chifukwa cha matenda aakulu.
Pali Njira Zambirimbiri Zomwe Mungasankhe
Nkhani yomwe ikungothayi yapereka zitsanzo zochepa chabe za njira zambiri zomwe m’madera ena zafala monga njira zochiritsira zosagwiritsidwa ntchito masiku onse. M’tsogolo muno zina mwa njira zimenezi, kuphatikizanso zina zimene sizinafotokozedwe muno, zingathe kudzaonedwa monga njira zochiritsira zogwiritsidwa ntchito masiku onse, ngakhale kuti m’madera ena a dziko lapansi lino zakhala kale njira zogwiritsidwa ntchito masiku onse. Ndiponso, zina zingadzasiye kugwiritsidwa ntchito kapena ngakhalenso kuonedwa ngati zoipa.
Mwatsoka, kupweteka m’thupi ndiponso matenda ndi zina mwa zinthu zomwe munthu ayenera kukumana nazo, ngakhalenso Baibulo linaneneratu molondola kuti: “Tidziŵa kuti cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zoŵaŵa pamodzi kufikira tsopano.” (Aroma 8:22) N’zodziŵikiratu kuti anthu angafunefunedi mpumulo. Komano, kodi tingaloŵere kuti? Chonde, onani malingaliro ena omwe angakuthandizeni posankha chithandizo chamankhwala.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 8]
Kuphatikiza Mankhwala Azitsamba ndi Mankhwala Opangidwa M’mafakitale—KODI KUOPSA KWAKE N’KOTANI?
Kaŵirikaŵiri anthu akhala akuchenjezedwa za kuopsa kwa kumwa mankhwala mophatikiza kapena kumwera zakumwa zoledzeretsa. Kodi kumwa mankhwala azitsamba limodzi ndi mankhwala opangidwa m’mafakitale kulinso ndi vuto lililonse? Kodi mchitidwe umenewu ndi wofala motani?
Nkhani ya m’magazini ya The Journal of the American Medical Association inanenapo za “kugwiritsira ntchito pamodzi mankhwala opangidwa m’mafakitale ndi mankhwala azitsamba.” Magaziniyo inanena kuti: “Mwa 44 peresenti ya anthu achikulire amene ananena kuti amamwa mankhwala opangidwa m’mafakitale nthaŵi zonse, pafupifupi m’modzi (18.4%) mwa anthu asanu ananena kuti panthaŵi imodzimodziyo amagwiritsanso ntchito pafupifupi mtundu umodzi wa mankhwala azitsamba, kapena kumwa mankhwala a mavitamini ochuluka, kapena zonse ziŵirizi.” M’pofunika kudziŵa za ngozi zomwe zingakhalepo chifukwa cha mchitidwe woterowo.
Anthu amene akumwa mitundu inayake ya mankhwala azitsamba ayeneranso kuda nkhaŵa akamalandira chithandizo chamankhwala chimene chimafunikira mankhwala ochititsa dzanzi. Dr. John Neeld, yemwe ndi pulezidenti wa bungwe la akatswiri odziŵa za dzanzi la American Society of Anesthesiologists, anati: “Pali malipoti a zinthu zomwe anthu ena zawachitikira zomwe sizikugwirizana ndi zomwe zili m’mabuku. Malipotiwo akunena kuti zitsamba zina zotchuka kwambiri, kuphatikizapo ginseng ndi St. John’s wort, zingapangitse kuti magazi azithamanga kwambiri kapena kuti azithamanga pang’onopang’ono. Zimenezi zingakhale zoopsa kwambiri panthaŵi yomwe munthu wachititsidwa dzanzi.”
Dokotala ameneyu ananenanso kuti: “Zitsamba zina monga ginkgo biloba, ginger, ndi feverfew, zingasokoneze magazi kuti asamatseke bala lomwe likutuluka magazi, zomwe n’zoopsa kwambiri panthaŵi yomwe minofu yomwe imaphimba bongo ndiponso fupa la msana yachititsidwa dzanzi, ndipo ngati pafupi ndi fupa la msana pakutuluka magazi munthu angathe kudwala matenda a kufa kwa ziŵalo. Chitsamba cha St. John’s wort nachonso chingawonjezere ziyambukiro zoipa za mankhwala ena omwe amapha ululu kapenanso mankhwala ochititsira dzanzi.”
Mwachionekere, n’kofunika kudziŵa za ngozi zomwe zingakhalepo chifukwa cha kulandira chithandizo cha mtundu winawake wa mankhwala azitsamba limodzi ndi mankhwala opangidwa a m’mafakitale. Makamaka amayi apakati ndiponso amayi omwe akuyamwitsa ana ayenera kudziŵa za ngozi yakuti ana awo angathe kudzadwala chifukwa cha kuphatikiza kwa zitsamba zinazake ndi mankhwala opangidwa m’mafakitale. Choncho, odwala akulimbikitsidwa kumakambirana ndi madokotala awo za mankhwala omwe akumwa, kaya akhale amene sagwiritsidwa ntchito masiku onse kapena omwe amagwiritsidwa ntchito masiku onse.
[Zithunzi patsamba 7]
Zitsamba zina zakhala zothandiza kwambiri pochiza matenda
Black cohosh
Saint-John’s-wort
[Mawu a Chithunzi]
© Bill Johnson/Visuals Unlimited
[Chithunzi patsamba 7]
Kuti pakhale zotsatirapo zabwino, odwala ndiponso akatswiri a zamankhwala afunika kugwira ntchito mogwirizana