Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Njira Zochiritsira Zosagwiritsidwa Ntchito Masiku Onse—Chifukwa Chomwe Anthu Ambiri Amazigwiritsira Ntchito

Njira Zochiritsira Zosagwiritsidwa Ntchito Masiku Onse—Chifukwa Chomwe Anthu Ambiri Amazigwiritsira Ntchito

Njira Zochiritsira Zosagwiritsidwa Ntchito Masiku Onse—Chifukwa Chomwe Anthu Ambiri Amazigwiritsira Ntchito

NJIRA zochiritsira zosagwiritsidwa ntchito masiku onse, kapena kuti chithandizo chochiritsira chokomera aliyense, zili ndi njira zambiri zochiritsira kapena zothandizira munthu. Zambiri mwa njirazi zili m’njira yochiritsira yaikulu kwambiri yotchedwa naturopathy, yomwe imadalira pa zinthu zachilengedwe kapena njira zina kuti zikonzekeretse thupi ndi kulipangitsa kuti lidzichiritse lokha. Zingapo mwa njira zimenezi, zomwe zakhala zikugwiritsidwa ntchito mofala kwambiri kwa zaka mazanamazana, zinasiyidwa kalekale kapena kunyalanyazidwa ndi njira zamakono zochiritsira.

Mwachitsanzo, magazini yotchedwa Journal of the American Medical Association, ya pa August 27, 1960, inanena kuti kugwiritsa ntchito zinthu zozizira pa zilonda zamoto kunali “kodziŵika kwa anthu akale koma kukuoneka ngati kuti kwakhala kukunyalanyazidwa ndi madokotala ndiponso anthu wamba. Chithandizo chamtunduwu sichigwiritsidwa ntchito kaŵirikaŵiri lerolino, ngakhale kuti maumboni a apo ndi apo a m’mabuku ndi ogwirizana polimbikitsa chithandizo chimenechi. N’zoonadi, madokotala ambiri amati ‘palibe munthu amene amagwiritsa ntchito chithandizochi,’ ngakhale kuti palibe munthu yemwe amadziŵa bwinobwino chifukwa chake.”

Komabe, m’zaka makumi angapo zapitazi, njira zochiritsira zimene zimagwiritsidwa ntchito masiku onse zinayambanso kulimbikitsa kugwiritsa ntchito madzi ozizira pochiritsa zilonda zamoto kapena kumanga chilonda chamoto ndi nsalu yoviikidwa m’madzi ozizira. Magazini yotchedwa The Journal of Trauma, ya September 1963, inati: “Chidwi chogwiritsa ntchito madzi ozizira pa chithandizo choyambirira pochiza zilonda zamoto chinakula kuchokera pamene Ofeigsson ndi Schulman analemba malipoti awo mu 1959 ndi mu 1960. Chaka chathachi takhala tikuchiza odwala motsatira njira imeneyi; ndipo zotsatirapo za chithandizo chamankhwala athu zakhala zolimbikitsa.”

Chithandizo chogwiritsa ntchito madzi ozizira sichivulaza, ndipo chimatonthoza mtima kwambiri. Njira zochiritsira zosagwiritsidwa ntchito masiku onse zimagwiritsa ntchito hydrotherapy, komwe ndi kugwiritsa ntchito madzi m’njira zosiyanasiyana pochiritsa matenda, ndipo pakali pano njira zosiyanasiyana za chithandizo chamtunduwu zikugwiritsidwa ntchito ndi njira zamakono zochiritsira. *

Mofananamo, nthaŵi zambiri akatswiri a njira zochiritsira zosagwiritsidwa ntchito masiku onse amagwiritsa ntchito zitsamba kuti achize matenda. Zimenezi zakhala zikuchitika kwa zaka mazana ambiri—ngakhale kwa zaka zikwi zambiri—m’madera ena a dziko lapansi. Mwachitsanzo, ku India, kugwiritsa ntchito zitsamba ndiko kumene kwanthaŵi yaitali kwakhala chithandizo chamankhwala chodalirika kwambiri. Lerolino, pafupifupi kwina kulikonse, akatswiri a zaumoyo ambiri akudziŵa za mphamvu yochiritsa ya zitsamba zina ndi zina.

Nkhani Yochititsa Chidwi

Zaka pafupifupi 100 zapitazo, Richard Willstätter, amene pambuyo pake anadzakhala wophunzira wa sayansi yamadzi osiyanasiyana a m’zomera, anakhudzidwa mtima kwambiri ndi zimene zinachitikira mnzake wapamtima wa zaka khumi, Sepp Schwab. Sepp anali ndi mwendo wovulala kwambiri kotero kuti dokotala ananena kuti m’pofunika kudula mwendowo kuti apulumutse moyo wake, koma makolo a Sepp anasintha tsiku la opaleshoniyo kuti idzachitike m’maŵa mwa tsiku lotsatira. Panthaŵiyo, makolowo anapita kwa mbusa wina wa ziŵeto amene anali wotchuka chifukwa cha mmene amagwiritsira ntchito mankhwala azitsamba. Mbusa wa ziŵetoyo anasonkhanitsa zitsamba zosiyanasiyana, ndiyeno anazidula m’tizidutswa ting’onoting’ono ngati mpiru wophikaphika, n’kuzithira pa chilondacho.

Pofika m’maŵa chilondacho chinali chitayamba kupola, ndipo opaleshoniyo inasinthidwiranso m’tsogolo. Anapitiriza kuthira mankhwalawo, ndipo m’kupita kwanthaŵi chilondacho chinapoleratu. Willstätter anapita kukaphunzira sayansi ya makemikolo ku Yunivesite ya Munich m’dziko la Germany ndipo kenako anapata mphoto ya Nobel chifukwa cha zinthu zomwe anatulukira mwa kafukufuku wake wa utoto wa m’zomera, makamaka mtundu wobiriŵira wotchedwa chlorophyll. Chodabwitsa n’chakuti pafupifupi 25 peresenti ya mankhwala opangidwa m’mafakitale omwe tsopano amagwiritsidwa ntchito, gawo lake lina kapena mankhwala onsewo amapangidwa kuchokera ku makemikolo achilengedwe a m’zomera.

Kufunika Kokhala Wosamala

Komabe, pankhani ya chithandizo chamankhwala m’pofunika kuzindikira kuti, chithandizo chomwe chimagwira ntchito bwino kwambiri kwa munthu wina sichingagwire ntchito mofananamo kwa wina. Kuti mankhwala agwire bwino ntchito zimadalira pa zifukwa zambirimbiri, kuphatikizapo mtundu wa matenda ndi ukulu wake ndiponso umoyo wa wodwalayo. Ngakhalenso nthaŵi ikhoza kukhala chifukwa china.

Kaŵirikaŵiri njira zochiritsira zosagwiritsidwa ntchito masiku onse zimagwira ntchito mwapang’ong’ono kusiyana ndi njira zochiritsira zomwe zimagwiritsidwa ntchito masiku onse. Choncho, nthenda yomwe mwinamwake ikanatha kugonjetsedwa ngati ikanapezeka ndi kuchizidwa mwamsanga ingakule kufikira pofuna mankhwala amphamvu kwambiri, mwinanso ngakhale kuchita opaleshoni n’cholinga chopulumutsa moyo. Choncho, kungakhale kupanda nzeru kukakamira pa mtundu umodzimodzi wa chithandizo chamankhwala ngati kuti ndi njira yokhayo yochizira matenda.

Njira zochiritsira zosagwiritsidwa ntchito masiku onse n’zosiyana ndi njira zochiritsira zamasiku onse pankhani ya mmene zimachitira ndi thanzi. Nthaŵi zambiri kachiritsidwe kake kamakhudzana kwambiri ndi kupewa, ndipo zimalimbana ndi makhalidwe a munthu ndiponso malo amene akukhala komanso mmene zimenezi zimakhudzira thanzi lake. M’mawu ena, madokotala a njira zochiritsira zosagwiritsidwa ntchito masiku onse, kwenikweni amaganizira za munthu yense m’malo mongoganizira za chiŵalo chomwe chikudwalacho kapena malo a nthendayo.

Mosakayikira, chikoka chachikulu cha njira zochiritsira zosagwiritsidwa ntchito masiku onse, chili chizindikiro chakuti anthu amadziŵa kuti njirazi zimagwiritsa ntchito bwino zinthu zachilengedwe, zimachiritsa bwino, ndiponso kuti n’zosavulaza kwambiri kuposa njira zochiritsira zimene zimagwiritsidwa ntchito masiku onse. Choncho, chifukwa cha chidwi chachikulu cha anthu chofuna kupeza chithandizo chamankhwala chomwe chili chotetezeka ndiponso chogwira mtima, m’nkhani yotsatirayi tifotokoza zitsanzo zochepa za njira zochiritsira zosagwiritsidwa ntchito masiku onse.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Onani Galamukani! yachingelezi ya June 22, 1988, masamba 25-6.