Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ntchito Yofunika ya Anamwino

Ntchito Yofunika ya Anamwino

Ntchito Yofunika ya Anamwino

“Namwino ndi munthu amene amadwazika ndi kuteteza ndipo amakhala wokonzeka kusamalira odwala, ovulala, ndi okalamba.”—Limatero buku lotchedwa Nursing in Today’s World—Challenges, Issues, and Trends.

NGAKHALE kuti kusadzikonda n’kofunika, iko pakokha si kokwanira kuti munthu akhale katswiri wa unamwino. Anamwino abwino amafunikanso kuphunzitsidwa zedi ndi kuzoloŵera ntchito yawo kwambiri. Chinthu chimodzi chofunika kwambiri n’chakuti ayenera aphunzire ndiponso kuyesera ntchitoyo kwa chaka chimodzi mpaka zaka zinayi. Koma kuti namwino akhale wabwino kodi ayenera kukhala ndi khalidwe lotani? Pano pali mayankho angapo operekedwa ndi anamwino odziŵa amene anafunsidwa funsoli ndi atolankhani a Galamukani!

“Dokotala amachiritsa, koma namwino amasamalira wodwalayo. Kuti atero nthaŵi zambiri amayenera kulimbikitsa odwala amene asokonezeka maganizo ndiponso amene akumva ululu. Mwachitsanzo odwala angatero pamene auzidwa kuti akudwala matenda aakulu kapena kuti afa. Uyenera kukhala ngati mayi wake wa munthu wodwalayo.”—Anatero Carmen Gilmartin, wa ku Spain.

“Kumva nawo ululu ndiponso nkhaŵa imene wodwala akumva ndiponso kufuna kumuthandiza n’kofunika. Chifundo ndi kuleza mtima n’zofunika. Nthaŵi zonse uzifunabe kudziŵa bwino unamwino ndiponso kuchiza matenda.”—Anatero Tadashi Hatano, wa ku Japan.

“M’zaka zaposachedwapa anamwino anafunikira kudziŵa zinthu zambiri zokhudza ntchito yawo. Motero, kukhumba kuphunzira ndiponso kutha kumvetsa zinthu zophunziridwazo n’kofunika. Chinanso n’chakuti anamwino ayenera kudziŵa chochita mwamsanga ndi kuthandiza anthu zinthu zikafika pofuna zimenezo.”—Anatero Keiko Kawane, wa ku Japan.

“Pokhala namwino, uyenera kukhala wansangala. Uyenera kulolera ndiponso kuganizira ena.”—Anatero Araceli García Padilla, wa ku Mexico.

“Namwino wabwino ayenera kukonda kuphunzira, kukhala woonetsetsa bwino zinthu, ndiponso wodziŵa ntchito yake bwino zedi. Ngati namwino sali wodzimana ndipo ngati ali ndi khalidwe linalake lodzikonda kapena ngati amadana ndi malangizo amene madokotala ena ophunzira kwambiriko akumupatsa, angathe kukhala wosayenera kwa odwala ndiponso kwa anzake amene amagwira nawo ntchito.”—Anatero Rosângela Santos, wa ku Brazil.

“Pali mikhalidwe ingapo imene ili yofunika kwambiri: kukhala wokonzeka kusintha maganizo, kulolera, ndiponso kuleza mtima. Uyeneranso kukhala wokonzeka kumva za ena, n’kumatha kukhala bwino ndi anzako ndi akuluakulu a ku chipatala. Uyenera kuphunzira mwamsanga maluso atsopano kuti ukhalebe katswiri.”—Anatero Marc Koehler, wa ku France.

“Uyenera kukonda anthu ndiponso kukhala wofunitsitsadi kuthandiza ena. Uyenera kukhala wokhoza kuthana ndi vuto la kutopa pantchito chifukwa chakuti ntchito yaunamwino siifuna kutayirira ngakhale pang’ono pokha. Uyenera kukhala wotha kuzoloŵera zinthu mwamsanga kuti nthaŵi zina zinthu zikavuta uzitha kugwira ntchito mulipo anamwino ochepa, moti ntchito n’kuyendabe bwino.”—Anatero Claudia Rijker-Baker, wa kuti Netherlands.

Namwino Akakhala Woyang’anira Wodwala

Magazini yotchedwa Nursing in Today’s World inanena kuti “ntchito ya unamwino imakhudza kusamalira munthuyo m’njira zosiyanasiyana zokhudza umoyo wake. N’chifukwa chake, pochiza wodwala timaganiza za chithandizo cha mankhwala ndipo posamalira odwalayo timaganiza za unamwino.”

Motero namwino ndiye woyang’anira wodwala. Choncho, n’zoonekeratu apa kuti namwino ayenera kusamalira bwino anthu. Nthaŵi ina m’mbuyomo anamwino ovomerezeka 1,200 anawafunsa kuti, “Kodi chinthu chofunika kwambiri kwa inu pantchito yanu ya unamwino n’chiyani?” Anamwino 98 mwa anamwino 100 anayankha kuti ndicho kuthandiza anthu bwino.

Nthaŵi zina anamwino amadziona ngati osafunika kwenikweni kwa anthu odwala. Carmen Gilmartín amene tam’tchulapo kale uja, wakhala ali namwino kwa zaka 12, ndipo anauza atolankhani a Galamukani! kuti: “Panthaŵi ina ndinamuuza chilungamo mnzanga wina kuti sindinali kuthandizapo kwambiri pamatenda akayakaya. Ndinkadziona ngati “wongoperekeza”. Koma kenaka mnzangayo anayankha kuti “woperekeza” wake waphindu chifukwa chakuti munthu akamadwala, iweyo umakhala wofunika koposa china chilichonse poti ndiwe namwino woganizira anthu.”

N’zoonekeratu kuti kuthandiza m’njira imeneyi kungavutitse kwambiri namwino amene tsiku lililonse amagwira ntchito kwa maola khumi kapena kuposerapo! Kodi n’chiyani chimene chinalimbikitsa odwazika okhala ndi mzimu wodzimana ameneŵa kuti akhale anamwino?

N’kukhaliranji Namwino?

Atolankhani a Galamukani! anafunsa anamwino padziko lonse funso lakuti, “Kodi chinakuchititsani kuti mukhale namwino n’chiyani?” Mayankho awo ena nawa.

Terry Weatherson wakhala namwino kwa zaka 47. Panopa akugwira ntchito ya unamwino wodwazika matenda mwachindunji mu dipatimenti yoona za matenda okhudza chikhodzodzo pa chipatala china cha ku Manchester, ku England. Iye anati, “Ndinakulira m’Chikatolika ndipo ndinkapita kusukulu ya Chikatolika yogonera konko. Ndili mtsikana ndinasankha kuti ndidzakhala sisitere apo ayi namwino. Ndinkafunitsitsa kuthandiza ena. Mwina munganene kuti chinali chikhumbo changa. Mmene zililimu ndiye kuti ndinasankha unamwino.”

Chiwa Matsunaga wa ku Saitama, ku Japan, wakhala zaka zisanu ndi zitatu akuyang’anira chipatala chakechake. Iye anati: “Ndinamvera maganizo a bambo anga akuti ‘ndibwino kuphunzira ntchito imene ungadzagwire mpaka moyo wako wonse.’ Choncho ndinasankha ntchito ya unamwino.”

Etsuko Kotani wa ku Tokyo, ku Japan, yemwe ndi namwino wamkulu yemwe wagwira ntchito kwa zaka 38, anati: “Ndidakali pasukulu, bambo anga anakomoka ndipo anataya magazi ambiri. Ndikuyang’anira bambo angawo kuchipatala, ndinaganiza zodzakhala namwino kuti ndizidzathandiza anthu odwala.”

Chimene chinachititsa anthu ena kukhala anamwino n’kudwala kwawo komwe. Eneida Vieyra, amene ali namwino ku Mexico, anati: “Pamene ndinali ndi zaka zisanu ndi chimodzi, ndinagonekedwa m’chipatala kwa masabata aŵiri chifukwa cha matenda a mapapo otchedwa bronchitis, ndipo pamenepa m’pamene ndinaganiza zodzakhala namwino.”

N’zoonekeratu apa kuti unamwino umafuna kudzimana kwakukulu. Tiyeni tione mwachifatse zovuta ndiponso zokoma za ntchito yabwino imeneyi.

Kukoma Kokhala Namwino

Kodi kukoma kwa unamwino n’kotani? Yankho la funso limenelo lingadalire ntchito imene namwinoyo amachita. Mwachitsanzo, amzamba amasangalala kwambiri pamene mwana wabadwa bwinobwino. “Zimasangalatsa kukabadwa mwana wathanzi amene wakhala ukumuyang’anira asanabadwe,” anatero mzamba wina wa ku Netherlands. Jolanda Gielen-Van Hooft, wochokeranso ku Netherlands, anati: “Kuchira ndi chinthu chimene banjalo ndiponso wogwira ntchito m’chipatala amasangalala nacho kwambiri. Ndi chinthu chozizwitsadi!”

Rachid Assam wa ku Dreux, ku France, ndi namwino wovomerezedwa ndi boma wogoneka anthu tulo powachita opaleshoni ndipo ali ndi zaka zongopitirira 40. Kodi n’chifukwa chiyani ntchito ya unamwino imamusangalatsa? Iye anati n’chifukwa chakuti “umamva bwino podziŵa kuti wachirikiza opaleshoni imene yayenda bwino ndiponso podziŵa kuti ukuchita nawo ntchito yosangalatsa kwambiri ndiponso yopitabe patsogolo. Isaac Bangili, amenenso ali wa ku France anati” “Ndimakhudzidwa kwambiri pamene odwala ndiponso mabanja awo akutiyamikira, makamaka pakachitika ngozi ndiye n’kuchiza munthu titataya kale mtima.”

Terry Weatherson, amene tam’tchulapo kale uja anayamikiridwapo motero. Mayi wina wamasiye anamulembera mawu akuti: “Nthaŵi ino siingapite popanda kutchulaponso zakuti mitima yathu inakhala pansi chifukwa cha kuona inu musakutekeseka, komanso mukutilimbitsa mtima panthaŵi yonse imene Charles ankadwala. Chifukwa inu munali wansangala, chisoni chathu chinatha ndipo tinalimbikitsidwa.”

Kukumana ndi Zovuta

Koma ngakhale pali zokoma za unamwino palinso zovuta. Sayenera kutayirira ngakhale pang’ono! Kaya akupereka mankhwala kapena kutenga magazi kapena kuloŵetsa chida chinachake mu mtsempha ngakhalenso kungosuntha chabe wodwala, namwino ayenera kusamala kwambiri. Namwino sayenera kulakwitsa makamaka m’mayiko amene kudulira namwino chisamani kuli kotchuka. Koma nthaŵi zina namwino amasoŵa chochita. Mwachitsanzo, taganizirani kuti namwino akuganiza kuti dokotala wam’lembera wodwala mankhwala olakwika kapena kuti walamula kuchita zinthu zosam’thandiza wodwalayo. Kodi namwinoyo angatani? Angatsutse dokotalayo? Zimenezo zimafunika kulimba mtima, kusamala, ndi kudziŵa kulankhula monyengerera ndiponso zinthu zingathe kukuvuta. N’zomvetsa chisoni kuti madokotala ena sasangalala ndi malingaliro operekedwa ndi anthu amene iwo amawaona monga apansi pawo.

Kodi anamwino ena aona chiyani pankhaniyi? Barbara Reineke wa ku Wisconsin, ku U.S.A., amene wakhala namwino wovomerezedwa ndi boma kwa zaka 34, anauza atolankhani a Galamukani! kuti: “Namwino ayenera kukhala wolimba mtima. Chifukwa choyamba n’chakuti, mwalamulo iye ndiye angafunsidwe pankhani ya mankhwala kapena chithandizo chilichonse chimene angapereke ndiponso pa vuto lililonse limene zinthu zimenezi zingabweretse. Ayenera kumakana kumvera lamulo la dokotala ngati akuona kuti silikugwirizana ndi ntchito yake kapena ngati akuganiza kuti lamulolo n’lolakwika. Unamwino si ulinso mmene unalili m’masiku aanthu ngati Florence Nightingale kapena zaka 50 m’mbuyomu. Masiku ano namwino ayenera kudziŵa kuti pano ndiyenera kum’kanira dokotala ndi kuti pano ndiyenera kunenetsa kuti dokotalayo ayenera kumuona wodwala, ngakhale patakhala pakati pa usiku. Ndiye ngati walakwitsa ndiwe namwino, uyenera kukonzeka kunenedwa ndi dokotalayo koma osakhumudwa.”

Vuto lina limene anamwino amakumana nalo ndilo chiwawa cha kuntchito. Nkhani yochokera ku South Africa inati ogwira ntchito ya unamwino “amadziŵika kuti ndiwo ali ndi tsoka lalikulu lovutitsidwa ndiponso kuchitidwa chiwawa kuntchito. Kwenikweni, n’kosavuta kuti anamwino avutitsidwe kuntchito kusiyana ndi olondera ndende kapena apolisi ndipo anamwino 72 mwa anamwino 100 alionse amakhala ndi mantha poopa kuvutitsidwa.” Ku United Kingdom nako akuti n’chimodzimodzi, anamwino 97 mwa 100 alionse amene anafunsidwa pa kufufuza kwaposachedwa ananena kuti anali kudziŵa namwino amene anavutitsidwako chaka cham’mbuyomo. Kodi chimachititsa chiwawa chimenechi n’chiyani? Nthaŵi zambiri vuto limabwera chifukwa cha odwala amene amamwa mankhwala osokoneza bongo kapena amene akhala akumwa mowa kapena amene akuvutika maganizo kapenanso amene ali ndi chisoni chachikulu.

Anamwino amayeneranso kudzilimbitsa akakhala kuti atheratu chifukwa cha kutopa. Kuchepa kwa ogwira ntchito kumapangitsanso zimenezi. Namwino wosamalira ntchito yake bwino akalephera kusamalira wodwala mokwanira chifukwa cha kuchuluka kwa ntchito, sachedwa kuvutika maganizo. Poyesa kuthetsa vutolo mwakugwirabe ntchito panthaŵi yopuma ndiponso kugwirabe ntchito ataŵeruka kale kukuoneka kuti kumangowonjezera vuto.

Zipatala zambiri padziko lonse zili ndi antchito osakwanira. Nkhani ya m’nyuzipepala ina ya ku Madrid yotchedwa Mundo Sanitario inati: “Tilibe anamwino okwanira m’zipatala zathu. Munthu aliyense amene anafunapo chithandizo kuchipatala amadziŵa kufunika kwa anamwino.” Kodi nkhaniyo inati chachepetsa anamwinowa n’chiyani? Eti kufuna kusawononga ndalama zambiri! Nkhani yomweyo inati zipatala za ku Madrid zikupereŵera anamwino odziŵa ntchito okwana 13,000!

Akuti chifukwa china chimene chikuchititsa anamwino kuvutika maganizo n’chakuti iwo amagwira ntchito nthaŵi yaitali kwabasi asanalandirane ndipo malipiro akuti n’ngwochepa kwambiri. Nyuzipepala yotchedwa The Scotsman inati: “Malingana n’zimene linanena bungwe la anthu antchito za boma lotchedwa Unison akuti namwino m’modzi aliyense mwa anamwino asanu alionse a ku Britain ndiponso wothandiza anamwino m’modzi aliyense mwa othandiza anayi alionse amagwiranso ntchito kwina kuti athe kudzisamalira.” Anamwino atatu mwa anamwino anayi alionse amaona kuti akulandira ndalama zochepa. Motero, anamwino ambiri aganiza zosiya ntchitoyo.

Palinso zifukwa zina zambiri zimene zimachititsa anamwino kuvutika maganizo. Tikayang’ana ndemanga zimene atolankhani a Galamukani! anauzidwa ndi anamwino padziko lonse, tingaone kuti kufa kwa wodwala kumafooketsa. Magda Souang, wochokera ku Egypt, amagwira ntchito ku Brooklyn, ku New York. Atamufunsa kuti chimachititsa ntchito yake kukhala yovuta n’chiyani, anayankha kuti: “Kuona imfa za odwala akayakaya pafupifupi 30 amene atsirizikira m’manja mwanga pa zaka zokwana 10. N’zofooketsa kwambiri.” N’zosadabwitsa kuti buku lina linati: “Kutanganidwa ndiponso kuganizira kwambiri zothandiza odwala amene amafa kungathe kukusokonezani maganizo ndiponso kukufooketsani.”

Tsogolo la Anamwino

Kupita patsogolo ndiponso kudalira njira zatsopano kukuchulukitsa mavuto pantchito ya unamwino. Vuto lagona pofuna kugwirizanitsa njira zimenezi ndi umunthu, kutanthauza njira za umunthu zothandizira odwala. Palibe makina amene angaloŵe m’malo mwa chisamaliro ndiponso chikondi cha namwino.

Magazini ina inati: “Ntchito ya namwino n’njamuyaya. . . . Malinga ngati anthu alipo, ndiye kuti pazifunikabe kuwasamala, kuwachitira chifundo, ndiponso kuwamvetsetsa.” Ntchito ya unamwino ndiyo imachita zinthu zimenezi. Koma chilipo chifukwa chachikulu kuposa apa choyembekezera kuti m’tsogolo tidzasamalidwa bwino. Baibulo limasonyeza kuti kukubwera nthaŵi imene palibe munthu adzanene kuti, “Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Madokotala, anamwino, ndiponso zipatala sizidzafunikanso m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza.—Yesaya 65:17; 2 Petro 3:13.

Baibulo limalonjezanso kuti “Mulungu . . . adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Koma pakali pano, tiziyamikira chisamaliro ndiponso kudzimana kwa anamwino mamiliyoni ambiri padziko lapansi. Chipanda iwowa bwenzi kukhala m’chipatala kuli kovuta mwinanso bwenzi kuli kosatheka n’komwe! Motero funso lakuti, “Chipanda anamwino bwenzi tikutani?” n’loyeneradi.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 22]

Florence Nightingale—Amene Anayambitsa Unamwino Wamakono

Florence Nightingale anabadwa m’chaka cha 1820 ku Italy ndipo makolo ake anali abritishi olemera motero anakulira pachinyezi. Florence ali mtsikana anakana amuna omwe ankafuna kum’kwatira ndipo anaphunzira za umoyo ndiponso za kusamalira osauka. Florence anayamba ntchito pasukulu ina yophunzitsa anamwino ku Kaiserwerth, m’dziko la Germany ngakhale kuti makolo ake anali kumuletsa. Kenaka anakaphunzira ku Paris, ndipo ali ndi zaka 33, anakhala woyang’anira wachipatala china cha akazi ku London.

Koma anakumana ndi vuto lake lalikulu kwambiri pamene anadzipereka kuti azisamalira asilikali ovulala ku Crimea. Kumeneko, iye ndi gulu lake la anamwino 38 anatsuka m’chipatala modzaza ndi makoswe chifukwa sadakachitira mwina. Inali ntchito yosautsa zedi, pakuti poyamba kunalibe sopo, kunalibe mabeseni osambira m’manja kapena mathawulo, ndiponso machira, matilesi, ngakhalenso mabandenji sanali okwanira. Florence ndi gulu lake anayesetsa kuthana ndi vutolo, ndipo pomwe nkhondoyo inkatha, iye anali ataisintha ntchito yaunamwino ndi yoyendetsa zipatala, padziko lonse. M’chaka cha 1860, anayambitsa sukulu yophunzitsa anamwino yotchedwa Nightingale Training School for Nurses pachipatala cha St. Thomas ku London. Imeneyi inali sukulu yaunamwino yoyamba yosakhudzana ndi chipembedzo. Asanafe m’chaka cha 1910, iye ankakhala chogona chifukwa anakhala kwa zaka zambiri ali ofa ziwalo. Komabe, anapitiriza kulemba mabuku ndi zinthu zina pofuna kupititsa patsogolo chithandizo cham’zipatala.

Anthu ena sagwirizana nazo zomatchulatchula kuti Florence Nightingale anali munthu wololera kuvutikira ena, chifukwa amati aliponso anthu ena oyenera kuyamikiridwa chimodzimodzi chifukwa cha zomwe anayambitsa pantchito ya unamwino. Kuphatikizanso apo, anthu akhala akusiyana maganizo kwambiri pankhani ya mbiri yake. Malingana ndi buku lotchedwa A History of Nursing, (Mbiri ya Unamwino) anthu ena amati iye anali “wovuta maganizo, wokonda kulamulira, womva zayekha, wamtima wapachala, ndiponso wovutitsa ena,” koma ena amati ankam’gomera chifukwa cha “nzeru ndiponso nsangala zake, kujijirika kwake kodabwitsa, ndiponso poti anali munthu wovuta kumumvetsa.” Zilibe kanthu kuti kaya analidi wotani, mfundo yodziŵika n’njakuti: Njira zimene iye anayambitsa zochitira unamwino ndiponso zoyendetsera zipatala zinafalikira kumayiko ambiri. Iye amaonedwa kuti ndiye anayambitsa ntchito ya unamwino umene tikuudziŵa masiku anowu.

[Chithunzi]

Chipatala cha St. Thomas atakhazikitsapo kale sukulu yophunzitsa anamwino ya Nightingale Training School for Nurses

[Mawu a Chithunzi]

Mwachilolezo cha National Library of Medicine

[Bokosi/Chithunzi patsamba 24]

Ziyeneretso za Namwino

Namwino: “Munthu amene waphunzitsidwa bwino sayansi ya unamwino ndipo n’ngophunzira ndi kudziŵa ntchito yachipatala mokwanira.”

Namwino Wovomerezedwa ndi Boma: “Namwino amene anamaliza maphunziro apamwamba ndipo waloledwa kugwira ntchitoyi atayesedwa ndi komiti ya boma yoyesa anamwino . . . ndipo amene ali wovomerezeka mwalamulo kugwiritsa ntchito zilembo izi; R.N.”

Namwino Wapadera: “Namwino wovomerezeka ndi boma wodziŵa zedi, wokhoza ntchito, waluso, ndiponso wokhoza bwino mbali inayake yapadera yaunamwino.”

Namwino Komanso Mzamba: “Munthu amene anaphunzitsidwa ntchito yaunamwino ndiponso uzamba.”

Namwino Wothandiza Anthu: “Munthu amene wagwirapo ntchito ya kudwazika anthu koma amene sanamalize maphunziro alionse apamwamba kusukulu iliyonse ya unamwino.”

Namwino Wothandiza Anthu Wovomerezeka: “Munthu womaliza maphunziro kusukulu ya unamwino wothandiza anthu . . . amene waloledwa mwalamulo kuchita ntchitoyi ngati namwino wothandiza anthu kapena ngati namwino wophunzira ntchito.”

[Mawu a Chithunzi]

Zachokera m’buku la ku United States lotchedwa Dorland’s Illustrated Medical Dictionary

UN/J. Isaac

[Bokosi/Zithunzi patsamba 25]

‘Maziko a Zipatala’

Pamsonkhano wochitika pazaka 100 zilizonse wa bungwe la International Council of Nurses womwe unachitika mu June 1999, Dr. Gro Harlem Brundtland, yemwe ndi woyang’anira wamkulu wa bungwe la zaumoyo padziko lonse la World Health Organization, anati:

“Poti anamwino ndi anthu odziŵa ntchito yachipatala ofunika kwambiri, ndiwo okha angalimbikitse kwambiri dziko lonse lapansi kuti likhale lathanzi. . . . Popeza kuti anamwino ndiponso amzamba alipo 80 pa odziŵa ntchito yachipatala 100 alionse, ndiye kuti n’ngokwanira kusintha zinthu kuti cholinga chofuna kuti aliyense akhale wathanzi mu zaka za 2000 zino chitheke. N’zoona kuti ntchito zawo zothandiza pankhani ya zachipatala zimakhudza mbali zonse za chipatala . . . N’zodziŵikiratu kuti anamwino ndiwo maziko a magulu ambiri osamalira anthu m’zipatala.”

Pulezidenti wakale wa ku Mexico, Ernesto Zedillo Ponce de León anayamikira mwapadera anamwino a ku Mexico ponena kuti: “Tsiku lililonse inu nonse . . . mumagwiritsa ntchito nzeru zanu zonse, kumverana, ndiponso manja anu kuti muteteze ndiponso kuchiritsa anthu a ku Mexico. Tsiku lililonse mumathandiza odwala powadwazika komanso powalimbikitsa mwakuwasonyeza chifundo, kudzipereka ndiponso khalidwe lanu laumunthu . . . M’zipatala zathu inuyo ndiye munachuluka kwambiri . . . Moyo uliwonse ukapulumutsidwa, mwana aliyense akabaidwa katemera, mayi aliyense akabereka mothandizidwa, nkhani ya zaumoyo iliyonse ikakambidwa, munthu aliyense akachira, wodwala aliyense akasamalidwa ndi kuthandizidwa bwino, anamwino athu amakhala atathandizapo.”

[Mawu a Chithunzi]

UN/DPI Chithunzi chojambulidwa ndi Greg Kinch

UN/DPI Chithunzi chojambulidwa ndi Evan Schneider

[Bokosi/Chithunzi patsamba 27]

Dokotala Woyamikira

Dr. Sandeep Jauhar wa ku chipatala cha New York Presbyterian anavomereza kuti anathandizidwa kwambiri ndi anamwino odziŵa bwino ntchito. Namwino wina anam’khutiritsa mwaluso kuti ayenera kupereka mankhwala oletsa ululu a morphine kwa wodwala wina amene anali kutsirizika. Iye analemba kuti: “Anamwino odziŵa bwino ntchito amaphunzitsanso madokotala. Anamwino okhala m’mawodi apadera a anthu odwala mwakayakaya ali m’gulu la anthu odziŵa bwino zedi ntchito yawo m’chipatala. Pamene ndinali kuphunzira ntchitoyi nditangomaliza maphunziro, iwo anandiphunzitsa mmene amaloŵetsera zipangizo zinazake m’thupi la munthu ndiponso mmene amachunira zipangizo zothandiza munthu kupuma. Anandiuza mankhwala amene ndiyenera kupeŵa.”

Iye anapitiriza kunena kuti: “Anamwino amalimbitsa mtima anthu odwala, chifukwa chakuti iwo ndiwo amakhala nawo nthaŵi yambiri. . . . Nthaŵi zambiri ndimamvera msanga kwambiri ngati namwino amene ndimakhulupirira ndiye akundiuza kuti ndikaone wodwala nthaŵi yomweyo.”

[Chithunzi patsamba 23]

“Ndinkafunitsitsa kuthandiza ena.”—Anatero Terry Weatherson, wa ku England.

[Chithunzi patsamba 23]

“Ndikuyang’anira bambo anga kuchipatala, ndinaganiza zodzakhala namwino.”—Anatero Etsuko Kotani, wa ku Japan

[Chithunzi patsamba 23]

‘Kuchira ndi chinthu chimene amzamba amasangalala nacho kwambiri.’—Jolanda Gielen-Van Hooft, wa ku Netherlands.

[Chithunzi patsamba 24]

Amzamba amasangalala ndiponso kukhutira akamathandiza pa kubereka