Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Sayansi Ingabweretse Moyo Wosatha?

Kodi Sayansi Ingabweretse Moyo Wosatha?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Sayansi Ingabweretse Moyo Wosatha?

ZAKA ZAM’MBUYOMO, funso ngati limeneli likanaoneka ngati lopusa. Koma masiku ano, anthu ena akuyembekezeradi zimenezi. Tikunena pano, asayansi atha kuŵirikiza kutalika kwa moyo wa touluka tina tam’zipatso ndiponso kutalika kwa moyo wa nyongolotsi pogwiritsa ntchito njira zimene anthu ena akuona kuti zingagwirenso ntchito pa anthu.

Kufufuza kwasonyeza kuti maselo onse a munthu amafa, pakuti amaberekana pogaŵikana nthaŵi zoŵerengeka chabe. Kenaka amasiya kugaŵikanako. Akuti njira imeneyi ili ngati wotchi yathupi imene imatchula nthaŵi imene anthu ayenera kukalamba ndi kufa. Tsopano asayansi akuyesayesa kukokera wotchi imeneyi.

Chiphunzitso china chotchuka chimati chinsinsi cha kukalamba chagona kumapeto kwa nkhosi iliyonse ya molekyu yosunga chibadwa cha zamoyo yotchedwa DNA, ku kachigawo kotchedwa telomere. Ma telomere akuti ali ngati timapulasitiki timene timakhala kumapeto kwa zingwe za nsapato, tomwe ntchito yake ndiyo kutetezera kuti zingwezo zisapombosoke. Asayansi aona kuti nthaŵi iliyonse maselo akaberekana, ma telomere amafupika ngati chingwe choti chagwira moto. Zikuoneka kuti m’kupita kwanthaŵi, ma telomere ameneŵa amafupika zedi mwakuti seloyo imaleka kuberekana. Komabe, pakakhala mapuloteni enaake a m’thupi, ma telomere safupika. Motero, malingana ndi chiphunzitsochi, maseloŵa angakhale ndi mpata woberekana kosalekeza. Bwana wa m’kampani ina yomwe ikuchita ntchito imeneyi anati: “Aka n’koyamba kuti tilingalirepo zakuti anthu angathe kukhala ndi moyo wosafa.” Koma si asayansi onse amene akuvomereza zimenezi.

Mmene Imfa Inabwerera

N’zoonadi, kwa zaka zikwi zambiri, anthu amene amakhulupirira Baibulo akhala akukhulupirira kuti n’zotheka kuti anthu akhale ndi moyo kosatha. Iwo sadalira anthu asayansi koma amadalira Wasayansi Woposa Onse, amene analenga zinthu zonsezi, wotchedwa Yehova Mulungu.—Salmo 104:24, 25.

Baibulo limasonyeza kuti imfa ya anthu siinali mbali ya chifuno cha Mlengi. Anthu oyamba okwatirana analengedwa m’chifanizo cha Mulungu ndipo anaikidwa m’munda wa paradaiso. Anali angwiro ndipo analibe chilema chilichonse chamaganizo ngakhalenso chathupi. Motero, anali ndi chiyembekezo chokhala kosatha padziko lapansi. Mulungu ankawafunira zimenezo. Anawalangiza kuti abereke ana ndi kuti pang’onopang’ono afutukule Paradaiso padziko lonse.—Genesis 1:27, 28; 2:8, 9, 15.

Monga mmene anasonyezera pa Genesis chaputala 3, Adamu, anasankha dala kusamvera Mulungu akudziŵa bwinobwino kuti chilango chake ndi imfa. Kuphatikizanso apo, poyenda m’njira ya kusamvera, iye anapatsira uchimo ndiponso imfa mbadwa zake zimene zinali zisanabadwe. Mtumwi Paulo analongosola zimenezi motere: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Kapenanso tinganene kuti, chifukwa chakuti Adamu anachimwa, thupi lake silinali langwironso. Pang’onopang’ono anayamba kukalamba ndipo anafa. Mbadwa zake zinatengera chilema chimenechi.

Motero imfa ya anthu inabwera chifukwa cha kusamvera kwa Adamu ndiponso chiŵeruzo chimene Mulungu anapereka pambuyo pake. Anthu sadzakwanitsa kuletsa chiŵeruzo chimenecho. Ngakhale kuti sayansi yapita patsogolo kwambiri pa zachipatala, mawu ouziridwa aŵa a Mose, olembedwa zaka 3,500 zapitazo, adakali oona: “Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi aŵiri, kapena tikakhala nayo mphamvu ndi zaka makumi asanu ndi atatu; koma teronso kukula kwawo kumati chivuto ndi chopanda pake; pakuti kumapitako msanga ndipo tithaŵa ife tomwe.”—Salmo 90:10.

Zimene Yehova Wakonza Kuti Kukhale Moyo Wosatha

Mwayi wake ndi wakuti, pali chiyembekezo! Ngakhale kuti pakali pano anthu onse amafa, Yehova safuna kuti zinthu zikhale choncho mpaka kalekale. Ngakhale kuti Adamu ndi Hava anayenera kufa, Mulungu anadziŵa kuti pakati pa ana awo amene anali asanabadwe padzakhala anthu ambiri amene adzachite zinthu moyamikira kusamalira kwake zinthu kwachikondi. Anthu otereŵa iye anawakonzera moyo wosatha padziko lapansi. Wamasalmo analemba kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) Kodi izi zidzatheka bwanji?

Zimenezi sikuti zingadzatheke chifukwa chakuti anthu atulukira chinsinsi cha chibadwa cha zamoyo. M’malo mwake, moyo wosatha ndi mphatso imene Yehova adzapereke kwa omukhulupirira. Pozindikira kuti mbadwa za Adamu ndi Hava zinali kufunika kupulumutsidwa, iye anazikonzera njira yopezera moyo wosatha yomwe ndi nsembe yadipo ya Yesu Kristu. Yesu anatchula njira imeneyi pamene ananena kuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.”—Yohane 3:16.

Yesu anali munthu wangwiro monga analili Adamu. Mosiyana ndi Adamu, Yesu anali womvera Mulungu pa china chilichonse. Motero Yesu anatha kupereka nsembe moyo wake wangwiro kuti uloŵe m’malo mwa tchimo la Adamu. Chifukwa cha ntchito yachikondi imeneyi, yomwe inakwaniritsa chilungamo, ana a Adamu anapeza pomasukira ku mlandu wa imfa. Choncho, onse amene amakhulupirira Yesu adzalandira mphatso ya Mulungu ya moyo wosatha.—Aroma 5:18, 19; 1 Timoteo 2:5, 6.

Ngati anthu akanakwanitsa kuthetsa kupanda ungwiro ndi kudzibweretsera moyo wosatha, sikukanafunikiranso dipo. Baibulo limapereka malangizo anzeru otsatiraŵa: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. Mpweya wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika. Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti am’thandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake; amene analenga zakumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m’mwemo; ndiye wakusunga choonadi kosatha.”—Salmo 146:3-6.

Moyo wosatha sudzabwera ndi kufufuza kwa sayansi, koma ndi Yehova. Chinthu chilichonse chimene Mulungu wayamba kuchita, angathe kuchikwaniritsa ndipo adzaterodi. “Palibe mawu amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.”—Luka 1:37.

[Mawu a Chithunzi patsamba 26]

© Charles Orrico/SuperStock, Inc.