Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthana ndi Ziyeso Mwamphamvu ya Mulungu

Kuthana ndi Ziyeso Mwamphamvu ya Mulungu

Kuthana ndi Ziyeso Mwamphamvu ya Mulungu

YOSIMBIDWA NDI STEPAN KOZHEMBA

Tsiku lina usiku, kumayambiriro kwa mwezi wa April chaka cha 1951, magalimoto aakulu odzaza ndi asilikali a dziko la Soviet anali kudutsa pa mudzi wathu wotchedwa Stenyatyn ku Ukraine. Asilikali okhala ndi mfutiwo anazungulira nyumba zimene anali atasankhiratu ndipo anatengamo mabanja onse a Mboni za Yehova n’kuwapititsa ku Siberia. Ndinali n’zaka 12 ndipo chilichonse chimene ndinkaona chinkandikhudza kwambiri, motero sindinkamvetsa kuti n’chifukwa chiyani anali kuwazunza choncho ndiponso kuti iwo ankatha bwanji kupirira mavuto amenewo.

NDINABADWIRA m’mudzi wa Stenyatyn m’mwezi wa October 1938. Mayi anga anafa patangotha masabata aŵiri ine nditabadwa, ndipo Bambo anga anaphedwa mu 1944 ali m’gulu la nkhondo la dziko la Soviet pomenyana ndi dziko la Germany. Alongo awo a bambo anga, Olena ndi Anna, ananditenga ndipo ndiwo anandilera.

Ndili mnyamata, ndinkadziŵa Amboni za Yehova ambiri m’tauni imene tinkakhala. Nthaŵi iliyonse akapeza mpata anali kundiuza ineyo ndiponso anthu ena za Ufumu Waumesiya. M’kupita kwa nthaŵi ndinapalana ubwenzi ndi Amboni za Yehova ena achinyamata. Ndinadabwa kwambiri pamene iwo anagwidwa ndi asilikali a dziko la Soviet n’kuwathamangitsira ku Siberia.

Koma si kuti Amboni onse anawathamangitsira kuukapolo. Stepan, anali Wamboni amene ankakhala pafupi ndi kwathu, ndipo analoledwa kukhala chifukwa m’banja mwawo sanali Amboni. Anali ndi zaka zisanu ndi zitatu kundiposa ine, ndipo nditasiya sukulu, ndinagwira naye ntchito ya ukalipentala. Ankaphunzira nane Baibulo, pogwiritsa ntchito magazini alionse a Nsanja ya Olonda amene analipo. Stepan, amene tsopano amatumikira Mulungu woona, Yehova, ku Estonia, anali ndi chimwemwe chodzaza tsaya pamene ndinabatizidwa mu July 1956.

Kutsutsidwa kunangosanduka moyo wa mtumiki aliyense wa Yehova ku Ukraine. Apolisi anali kufufuza m’manyumba pofunafuna mabuku olongosola Baibulo, motero ine ndinali ndi malo angapo obisapo mabuku. Azakhali anga aja, Olena ndi Anna, amene anali Akatolika achigiriki, sankavomereza kuti ndizichezerana ndi Amboni. Mpaka anayesa kundichititsa kuti ndisiye kuyanjana nawo. Mofanana ndi mmene anachitira mtumwi Paulo nthaŵi zina, ndinkamva ‘kuthodwa kwakukulu koposa mphamvu yanga’. Koma ubwenzi wanga ndi Yehova Mulungu unandilimbikitsa kupirira chiyeso chilichonse.—2 Akorinto 1:8; Afilipi 4:13.

Khama Langa Kuti Ndisaloŵerere Nkhondo

Afune kaya asafune, anyamata azaka 18 anayenera kulembedwa usilikali m’gulu lankhondo la dziko la Soviet. Chifukwa cha zimene ndinkadziŵa m’Baibulo, ndinatsimikiza mtima kuti sindiloŵerera zochitika za dziko, kutanthauza kuti ndinakana kuloŵa m’gulu la nkhondo la ku Soviet. (Yesaya 2:4; Yohane 17:14-16) Olena ndi Anna anandilimbikitsa kuti ndikhale msilikali, ngakhale kuti achimwene awo, omwe anali bambo anga, anaphedwa pankhondo.

Nditalandira mapepala ondikakamiza kulembetsa usilikali, ndinapita ku likulu la asilikali lam’dera lathu ndi kukalongosola chikhulupiriro changa. Nthaŵi yomweyo anandimanga ndi kundiika m’ndende uku akukonza milandu yodzandizenga. Mlanduwo anauzenga mwachinsinsi; ngakhale azakhali anga aŵiri aja sanauzidwe tsiku lodzauzenga. Ndinalalikira mokwanira bwino kwa woweruzayo, wozenga mlandu, ndiponso kwa anthu aŵiri opereka chigamulo. Patatha mphindi 20, zonse zinatha. Chilango changa chinali chakuti ndimangidwe zaka zisanu ndiponso ndikhale zaka zina zisanu ndili wopanda ufulu wina woyenera nzika.

Ukaidi Wanga

Mlanduwo utazengedwa ndinaikidwa m’ndende ku Lviv. Kwa miyezi itatu, kuchokera pamene ndinamangidwa mpaka pamene ndinasamutsidwa kupita ku msasa kokagwira ntchito ya kalavula gaga, ndinalibe anzanga alionse achikristu oti n’kucheza nawo, ndinalibe Baibulo, ndiponso ndinalibe mabuku olongosola Baibulo. Koma ndinalimbabe mwauzimu polalikira kwa akaidi anzanga, amene sankamvetsa chifukwa chimene ndinakanira kukhala msilikali. Pamiyezi imeneyo, ndinapulumukira phunziro laumwini limene ndinali kuchita ndisanamangidwe. Zimene ndinakumana nazozi zinandipatsa phunziro lofunika kwambiri lakuti: Phunziro laumwini la Baibulo limatithandiza kukhomereza nkhokwe yauzimu imene imatipulumutsa pakabwera ziyeso.—Yohane 14:26.

Mu April 1958, ndinatumizidwa ku msasa wachibalo wa 21 kuti ndikamalizire kumeneko ukaidi wanga. Msasawu unali pafupi ndi mzinda wa Dnepropetrovsk, omwe uli pamtunda wa makilomita 700 kuchokera kwathu. Kumeneku tinkadzuka sikisi koloko m’maŵa, ndipo tikadya chakudya cham’maŵa ankatiika m’magalimoto aakulu n’kutipititsa kumalo athu antchito omwe anali pamtunda wa makilomita 50 kunja kwa msasawo. Tinkagwira ntchito maola asanu ndi atatu pa malo omangapo nyumba, ndipo kenako ankakatitula ku msasa kunja kukada.

Tinkagona m’nyumba zogonamo asilikali ndipo nyumba iliyonse munkakhala akaidi okwana 100. Chakudya chake chinali chosakwanira ndiponso chosalongosoka, ndipo kukhala kwake kunali kovutikira zedi; koma mwayi wake ndinali ndi anzanga aŵiri Amboni m’chinyumba chimene ndinkakhala. Aliyense payekhapayekha anali kuyesetsa kwambiri kulimbikitsa anzake aŵiriwo. Iyinso ndi njira ina imene Yehova amaperekera mphamvu kwa atumiki ake amene akuvutika, njira ya kugwirizana ndi anzathu okhulupirira.—2 Akorinto 7:6.

Pamsasa wonsewo panali Amboni 12. Ena anali ndi abale awo kunja kwa msasawo amene anali kutizembetsera masamba a Nsanja ya Olonda powabisa m’maphukusi a chakudya. Maphukusi ambiri anali kuonedwa kaye ndi asilikali olondera, amene ankayamba aona zomwe zilimo asanatipatsire. Koma poopa kutulukiridwa, masamba a Nsanja ya Olonda ankawakuta m’mapulasitiki ndi kuwaika m’zitini za jamu, zimene asilikaliwo sankazitsegula poona kuti angodzivutitsa. Tinkati tikalandira nkhanizo, tinkazikopera pamanja ndi kugawana pagulu pathupo.

Tinayesetsanso kwambiri kulalikira Ufumu wa Mulungu, ndipo Yehova anadalitsa khama lathu. Mwachitsanzo ndinadziŵana ndi mkaidi mnzanga wina wotchedwa Sergei, amene anali kugwira ntchito yoŵerengera ndalama pa kampani ina ya boma kum’maŵa kwa Ukraine. Kuntchito kwake anatulukira kuti kunkachitika zachinyengo, ndipo iyeyu anamuzenga mlanduwu ndipo anamulamula kuti akhale m’ndende zaka khumi. Amboni angapo m’ndendeyi anali kuphunzira naye, pogwiritsa ntchito magazini alionse amene analipo. Sergei anamvera ndipo pomaliza pake anandiuza kuti: “Ndikangomasulidwa ku msasa kuno, ndikufuna ndidzabatizidwe n’kukhala Wamboni za Yehova!” Sergei anasungadi mawu ake ndipo anabatizidwa mwamsanga atangotulutsidwa, m’ndende ndipo anatumikira Yehova mokhulupirika mpaka pamene anafa.

Kusamvetsetsa Aroma Chaputala 13

Ndinatulutsidwa m’ndende mu January 1963 ndipo ndinabwerera kumudzi kwathu, ku Stenyatyn. Nditangokhala pang’ono chabe ndinazindikira kuti mumpingo wa kumeneko ku Sokal, zinthu sizinali bwino penapake. Abale sanali kumvetsetsana. Kodi vuto linali chiyani? Kodi chinachititsa kuti abale agwire njakata n’chiyani?

Kwa zaka zambiri boma la Soviet linali kuyesa kuyambitsa udani pakati pa anthu a Yehova pogwira abale n’kumakawafunsa ndi kuwauza kuti Amboni anali kugwiritsidwa ntchito n’cholinga chopititsa patsogolo zofuna za dziko la United States of America. Abomawo anati ndibwino kuti Amboni a ku Soviet Union apange gulu lawolawo ndipo ananenanso kuti ngati atatero ndiye kuti angathe kugwirizana ndi boma ndipo angaloledwe kupembedza osaletsedwa. Abomawo ananena zimenezi m’njira yokopa zedi.

Kenaka mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 1962, imene m’chilankhulidwe cha ku Ukrane inatulutsidwa mochedwa pa July 1, 1964, munalongosoledwa tanthauzo latsopano la Aroma chaputala 13. M’mbuyo monsemo, tinkati “maulamuliro a akulu” amene anatchulidwa pa vesi 1 anali kunena za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu, koma Nsanja ya Olonda inatchulapo kuti mawu akuti “maulamuliro a akulu” kwenikweni akuimira maboma apadziko lapansi ndipo kuti maboma ameneŵa “aikidwa ndi Mulungu.”—Aroma 13:1.

Ena mwa Amboniwo anaona kuti n’kovuta kwambiri kukhulupirira lingaliro latsopanoli, chifukwa chakuti atsogoleri a boma la Soviet Union anachita nkhanza zadzaoneni n’cholinga chofuna kuchotseratu kulambira Mulungu koona. Choncho, Mboni zimenezi zinaganiza kuti Nsanja ya Olonda imene munali chidziŵitso chatsopanoyi siinachokere kugulu lenileni la Mboni za Yehova. Mmalo mwake, iwo anaganiza kuti nkhaniyo inali itakonzedwa ndi ena ogwirizana ndi boma n’cholinga chakuti Mbonizo zikhale zomvera kwambiri boma la Soviet.

Motero mtumiki aliyense wa Yehova ku Ukraine anayenera kudziyankha funso lakuti, Kodi gulu limene lalondola ndi liti, ndipo lasochera ndi liti? Ndinali kungoyang’ana Mbonizo zikuchirikiza mbali ziŵirizo ndipo ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi cholinga chawo n’chiyani?’ Mwamsanga ndinatulukira kuti panali kusiyana kooneka bwino pakati pa mbali ziŵirizo.

Mboni za Yehova zochuluka, ngakhalenso ena amene sankamvetsetsa tanthauzo latsopano lija la Aroma chaputala 13, ankafuna kukhala okhulupirikabe kwa Yehova ndi gulu lake. Koma, ena anali atayamba kukayikira ngati mabuku atsopano a Watch Tower Bible and Tract Society panthaŵiyo anali kuchokerabe ku gulu lenileni la Mboni za Yehova. Anthu otereŵa ankakondanso kukokomeza nkhani zina zambiri. Mwachitsanzo, ankaona kuti n’kulakwa kuti mkwatibwi azivala diresi loyera pa ukwati wake ndi kutinso anthu okwatirana azivala mphete yaukwati. Anthu angapo ndithu anachoka m’gululi. Komabe m’kupita kwa nthaŵi angapo anazindikira kulakwa kwawo ndipo anayambiranso kutumikira Yehova.

Ntchito Yam’chibisira

Ngakhale kuti ntchito yathu yachikristu inali italetsedwa, nthaŵi iliyonse ngati n’kotheka tinkachita misonkhano yathu ya mlungu ndi mlungu m’magulu aanthu 10 kapena mpaka 15. Tinkalimbikitsidwa mwauzimu ndi misonkhanoyi pophunzira Baibulo komanso pocheza pambuyo pa phunziroli. Tinkauzana zimene takumana nazo, ndipo zimenezi zinkatithandiza kuzindikira kuti aliyense m’gulu lathu anali ndi mavuto ofanana. Tinamvera zimene mtumwi Petro analemba zakuti: “Zinthu zimodzimodzizo zomwe muvutika nazo zikuchitika m’gulu lonse la abale anu m’dziko.”—1 Petro 5:9, NW.

Nkhani za mu Nsanja ya Olonda ndizo tinali kugwiritsa ntchito pokambirana. Kodi magazini ameneŵa ankatifika bwanji? Amboni omwe ankagwira ntchito yotumikira ankabweretsa mafilimu a magaziniŵa kudutsa nawo malire n’kuloŵa mu Ukraine. Mafilimu ameneŵa anali kupita kwa Mboni imodziimodzi motsatira ndondomeko imene anakhazikitsa. Kenaka Mboni iliyonse inkapanga makope okwanira mpingo wake. Nthaŵi zina ndinkapanga nawo makope otere. Ndinkagwira ntchito tsiku lonse ndipo ndinkakhala otanganidwa kutumikira Yehova usiku popanga magazini ndiponso kuchita zinthu zina. Kuchita ntchitoyi panthaŵi yake kunali kovuta, koma ife amene tinali ndi udindo m’gulu tinaphunzira kuti Yehova “alimbitsa olefuka.”—Yesaya 40:29.

Tinkachita zotheka kuti anthu amene tinali kukumana nawo tizikambirana nawo za Baibulo. Ambirife tinkachita zimenezi titakwera zinthu monga basi. Njira yofala kwambiri yoyambira nkhani inali kungoŵerenga nyuzipepala ya tsiku n’tsiku ndipo kenaka n’kumuuza mocheza munthu amene mwakwera naye nkhani zimene zangotuluka. Tikangoyamba kucheza, basi kenaka timaikhotetsera nkhani ija ku Baibulo. Tinafalitsa uthenga wabwino m’dera lathu mwanjira imeneyi.

Mkazi Waluso

M’chaka cha 1965, ndinakwatira Tamara, amene analeredwa monga mtumiki wa Mulungu woona ndipo ankadziŵa kuchirikiza chikhulupiriro chake pachiyeso. Mchimwene wake Sergei anamangidwa ndi kuzengedwa mlandu katatu chifukwa cha ntchito yake yokhala Mboni. Kotsiriza anam’peza ndi magazini a Nsanja ya Olonda ndipo anaikidwa m’ndende kwa zaka khumi. Tamara nayenso anagwidwa ndi apolisi n’kumupititsa kumalikulu awo kuti akamufunse ndipo anamuopseza kuti amumanga.

Zinali zovuta kuti tipeze malo okhala titakwatirana, koma banja lina limene linkakhala ku Sokal lomwe linkagwirizana ndi Amboni linatipatsa kachipinda m’nyumba mwawo koti tizilipira ndalama zochepa. Banja limeneli linatitsimikizira kuti Tamara angakhalebe m’chipindacho ngati ine nditamangidwa ndi kuikidwanso m’ndende. Mkazi wangayu ndi ine tinathokoza Yehova kwambiri kaamba ka madalitso ake ndiponso tinathokoza banjalo kaamba ka chifundo chawo. Kenaka banjalo litaferedwa, Tamara anapezerapo mwayi wom’longosolera mwana wawo wamkazi, Galina, chiyembekezo cha chiukiriro. Mbewu za choonadi cha Baibulo zimenezi zinabereka zipatso, ndipo Galina anayamba kukonda Mlengi wathu. Anabatizidwa ndipo tsopano iye ndi mwamuna wake amatumikira Yehova.

M’ma 1970, sabata iliyonse ikafika kumapeto, ndinkapita ku madera osiyanasiyana a ku Ukraine komanso kumadera a ku Moldavia (Moldova) ndi kumapiri a Carpathian. Kumeneko ndinkakumana ndiponso kulimbikitsa anthu amene anali kutsogolera m’gulu la Yehova. Nthaŵi zambiri ndinkanyamuka Lachisanu madzulo ndi kubwerera kunyumba madzulo lasabata. Nthaŵi zambiri Tamara sankadziŵa kumene ndinali kupita ndipo nthaŵi zina sankadziŵa n’komwe ngati ndibwereko. Zimenezi zinachitika kwa zaka zambiri ndithu. Sindingachitire mwina koma kukhulupirira zimene Baibulo limanena za mkazi waluso kuti: “Mtengo wake uposa ngale.”—Miyambo 31:10.

M’masiku amenewo ntchito iliyonse ya Mboni za Yehova inali yoopsa. Tinkatha kuigwirabe chifukwa cha mphamvu zimene Yehova amapereka basi. Nthaŵi zambiri ndinali kukumana ndi mavuto ndipo sindinkadziŵa chochita. Motero ndinali kunena pemphero lamumtima ndi kudalira kuti Yehova andipatsa mphamvu. Kuchita zimenezo kunangosanduka moyo wathu.—Machitidwe 4:29.

Zimene Zachitika Posachedwa

M’kupita kwa nthaŵi, zinthu zinayamba kuwayendera bwino atumiki a Yehova ku Ukraine. Chizunzo chinayamba kuchepa, ndipo anasiya zotsekera anthu m’ndende n’kuyamba kumangowalipiritsa. Cha m’ma 1980, aboma anayamba kumvetsa kuti n’zoona Mboni za Yehova ndi gulu lapadziko lonse. Motero poika m’ndende Mboni ku Ukraine ndiponso m’madera ena a ku Soviet Union, dzikolo linali kudziwonongera mbiri yake kumayiko akunja. Ndikukumbukira kuti nthaŵi ina ndinali kufunsidwa ndi mkulu waboma wina ndipo anandiuza kuti: “Tadziŵa tsopano kuti chipembedzo pachokha si kuti n’choipa. Nkhaŵa yathu yaikulu n’njakuti pasakhale gulu lachipembedzo lowononga boma.”

Mayiko a kum’maŵa kwa Ulaya anayamba kusiya kulamulira mwankhanza chakumapeto kwa m’ma 1980, ndipo kuyambira pamenepo takhala ndi ufulu wochulukirapo ku Ukraine. Mu 1991 ntchito yathu yolalikira inaloledwa mwalamulo. Kenaka mu September 1998, Watch Tower Society inakhazikitsa ofesi ya nthambi ku Lviv. Kumayambiriro kwa 1999 ntchito yomanga inayamba pamalo atsopano a ofesi yanthambi imene muzidzakhala ogwira ntchito okwana 170. Tsopano mu Ukraine muno tili ndi anthu okwana 112,000 amene akuchita nawo ntchito yolalikira, ndipo anthu oposa 250,000 anafika pa Chikumbutso m’chaka cha 2000. Chochititsa chidwi kwambiri ndicho chiŵerengero cha achinyamata amene ali m’gulu lathuli. Pamsonkhano wina waukulu ku Kiev m’chaka cha 1991, mtolankhani wina wamkazi wa nyuzipepala anandifunsa kuti:

Kodi anthu onsewa achokera kuti? Ine ndinkangoti mu Soviet Union mulibe Amboni, ndiye mwadzidzidzi mwangoti tulukiru masauzande ambiri chonchi!”

“Sikuti tangotulukira mwadzidzidzi,” ndinamuuza choncho. “Takhala tikutumikira Yehova kunoko kwa zaka zambiri.”

Kodi mumakopa bwanji achinyamata ambirimbiri kuti aloŵe m’chipembedzo chanu?” anatero pofuna kudziŵa.

“Njira yabwino ndiyakuti mungowafunsa achiyamatawo. Akuuzeni okha chifukwa chimene akufunira kutumikira Yehova.”

“Ndawafunsa kale,” anatero mtolankhaniyo. “Andiuza kuti zimawasangalatsa.”

“Ndiye kuti chifukwa chake n’chomwecho,” ndinathirira ndemanga. “Ngati zimenezo n’zimene achinyamata athu anena ndiye kuti chifukwa chake n’chomwecho.”

Achinyamata si okhawo amene amasangalatsidwa ndi kutumikira Yehova. Zaka zimene Tamara ndi ine takhala tikum’tumikira tikaziphatikiza zimakwana 80 ndipo sitingaganize zosinthanitsa chikhulupiriro chathu ndi chinthu china chilichonse. Ngakhale kuti ndife Mboni za Yehova, timakhalabe ndi mavuto. Timazindikira kuti ngati dongosolo lakale la zinthuli lilipobe, aliyense azikumanabe ndi mavuto. Koma ndife okonzekera bwino kuthana ndi ziyeso kuposa gulu lina lililonse la anthu padziko lapansi. Timakhala ofunitsitsabe kukumana ndi ziyeso zimenezi monga mmene tachitira m’mbuyomo, mwamphamvu ya Mulungu wathu wamphamvuyonse, Yehova. Timamva mmene ankamvera Mose pamene anali kuimba nyimbo yachipambano yakuti: “Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, ndipo wakhala chipulumutso changa.”—Eksodo 15:2.

[Chithunzi patsamba 22]

Ndili ndi Mboni zinzanga ku msasa wachibalo wa nambala 21

[Chithunzi patsamba 22]

Filimu ya Nsanja ya Olonda ya m’chiyukreniya (inali yaikulu momwe ikuonekeramu)

[Chithunzi patsamba 23]

Ndili ndi mkazi wanga Tamara

[Chithunzi pamasamba 24, 25]

Chithunzi chojambula pamanja cha ofesi yanthambi yatsopano imene ikumangidwa ku Lviv

[Chithunzi patsamba 25]

Kodi n’chifukwa chiyani achinyamata ambiri ku Ukraine akutumikira Yehova?