Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ngakhale Ndili Wolumala Ndine Wosangalala

Ngakhale Ndili Wolumala Ndine Wosangalala

Ngakhale Ndili Wolumala Ndine Wosangalala

YOSIMBIDWA NDI KONSTANTIN MOROZOV

Pamene ndinabadwa pa July 20, 1936, ndinalibe mafupa okhwima m’thupi mwanga kupatula chibade ndi fupa la msana. Mafupa anga onse anali osalimba kuposa khutu la munthu wamkulu. Ndinkalemera osafika ndi theka lomwe la kilo imodzi. Zizindikiro zimene zimaonetsa kuti ndili moyo zinali chabe kugunda kwa mtima kwa pansipansi, kupuma pang’onopang’ono, ndi kutakataka pang’ono.

NDINALI mwana wachisanu ndi chiŵiri m’banja lokhala ndi ana asanu ndi anayi limene linkakhala m’mudzi wa Sara, ku Ul’yanovsk Oblast, m’kati mwenimweni mwa dziko la Russia. Ndili ndi masabata atatu, makolo anga anapita nane kutchalitchi kuti ndikabatizidwe. Wansembe anafulumira kundiwaza madzi n’kuuza makolo anga kuti afulumize kwambiri kupita nane kunyumba, popeza kuti iye anati ndimwalira patangotha maola ochepa okha.

Mu January 1937, makolo anga anapita nane ku mzinda wa Kazan’, likulu la dziko la Tatarstan la chitaganya cha Russia, kuti madokotala akandione. Panthaŵi imeneyo ndinkatha kutchula kuti “Amama,” “Ababa,” ndiponso “Babushka” (Agogo), komanso ndinkawadziŵa mayina a achimwene anga. Madokotala atandiyeza, anauza makolo anga kuti ndimwalira m’kati mwa chakacho. Iwo ananena kuti akanakonda kuti andiphe ndi cholinga choti andiike m’chibotolo kuti ophunzira zamankhwala azidzathandizika kuphunzirira pa ine. Ndikuthokozatu kwambiri makolo anga kuti anakana kwamtuwagalu!

Ubwana Wamavuto

Ndikukumbukira bwino ndithu, kuti nthaŵi zonse thupi langa lakhala mu ululu wamtima bi. Komabe, ngakhale pamene ndinali mwana, ndinayesetsa kukhala ndi malingaliro oti zagwa zatha ndipo ndinali kuyesako kuseka nthaŵi zina n’kumasangalala ndi moyo. Limeneli ndilo khalidwe limene ndalisunga mpaka pano. Mafupa anga anayamba kulimba pang’onopang’ono, ndipo ndinayamba kutha kukhala tsonga ndi kukwaŵa pang’ono. Sindinakule ngati mmene ana ena onse amakulira ndipo ndinalumaliratu. Koma ndinali wanzeru kusukulu, ndipo pofika zaka zisanu, ndimatha kuŵerenga ndi kulemba.

Mu May chaka cha 1941, amayi anapita nane kutchalitchi kachiŵirinso. Kunali anthu ambiri kumeneko, ndipo onse ankapemphera chogwada. Wolandira alendo wina wachikazi anafikira amayi kuti awafunse chifukwa chake sanagwade. Amayi atandisonyeza kwa iye, iye anapita kukauza wansembe. Pobwerera, wolandira alendoyo anatiperekeza kupita panja n’kuwauza amayi kuti kunali bwino kuti andisiye kunjako ndipo iwo aloŵe okha m’kati. Iye anawauza kuti ati chifukwa cha machimo a makolo angawo, ndinaperekedwa kwa iwo ndi “wodetsedwayo.” Amayi anabwerera kunyumba ali ndi misozi m’maso mwawo. Ndinakhala ndikuganiza zimenezi kwa nthaŵi yaitali. Ndinadabwa kuti, ‘Kodi “wodetsedwayo” ndi ndani?’

Mu 1948, ndili ndi zaka 12, amayi anapita nane kumudzi wa Merenki m’dziko lotchedwa Chuvash Republic, limene linali pafupifupi mtunda wofika makilomita 80 kuchokera kwathu. Kunali akasupe a madzi ochiritsa kumeneko, ndipo amayi anali ndi chikhulupiriro kuti ndikhoza kuchiritsidwa ndi madziwo. Mwa zina zimene ansembe ananena kuti ndichiritsidwe anati ndisadye kwa masiku atatu. Ndinafunikanso kuti ndilandire Ukalisitiya m’tchalitchi. Ngakhale kuti sindinali kukhulupirira kwambiri tchalitchicho, ndinangovomera zimene ananena. Kwa ineyo ulendowo unali wautali komanso wovuta kwabasi, koma ndinapirira, n’kumangodzitanganitsa ndi kuona kukongola kwa malo.

Tchalitchicho chinali chodzaza ndi anthu. Pamene amayi ankadutsa nane m’kati mwa gulu atandinyamula, mayi wina wokalamba anandipatsa switi. Ndinalandira n’kuiika m’thumba mwanga. Nthaŵi yanga yoti ndilandire Ukalisitiya itafika, mayi wokalambayo anakuwa amvekere: “Abambo, musam’patse Ukalisitiya ameneyo! Wangodya kumene switi!” Ndinafotokoza kuti switiyo inali m’thumba mwanga, koma wansembeyo anakalipa amvekere: “Wolumala wachipongwe iwe! Kodi ukunamanso? M’tulutseni m’tchalitchi muno!” Komabe, tsiku lotsatira, wansembe wina anachititsa mwambo wa Ukalisitiya n’kundisambitsa ndi madzi “ozizwitsawo.” Komabe, palibe chozizwitsa chinachitika. Ndinali wolumalabe.

Kukhoza pa Ntchito Zofuna Maphunziro

Ngakhale kuti ndinali wolumala kwambiri choncho, paunyamata wanga ndinalimbikira maphunziro ambiri pofuna kudziŵa zambiri. Mu 1956, ndinaloŵa nawo m’gulu la Komsomol (Gulu la Achinyamata la Chikomyunizimu) ndipo patapita nthaŵi, ndinaphunzitsa achinyamata mbiri ya Komsomol. Ndinali nawo m’bungwe lotchedwa Home and Cultural Commission panyumba ya anthu olumala, ndipo ndinagwiranso ntchito yotsogolera nyumba ya mphepo ndiponso muulutsi.

Komanso, ndinali woyang’anira laibulale ya pagalimoto ya mabuku a akhungu ojambulidwa pakaseti, ndipo anandisankha kukhala nawo m’bungwe lotchedwa Judge’s Commission for the Fight Against Alcohol Abuse. Ndinakhala nawonso m’gulu la anthu amaluso osiyanasiyana, kuimba, komanso kuliza zida zoimbira zosiyanasiyana.

Panyumba ya Anthu Olumala

Mu 1957, pamene ndinafika zaka 21, ndinakakamizika kukakhala panyumba ya anthu olumala chifukwa cha kulumala kwangaku. Komabe, sindinataye mtima. Mu October chaka cha 1963, ndinapita ku chipatala choona za olumala cha Prosthetic Science Research Institute of Moscow. Anandichita maopaleshoni 18 kumeneko kuti awongole miyendo yanga.

Poyamba, anakoka miyendo yanga kuiwongola. Ndiyeno patapita masiku asanu ndi atatu, anandichita opaleshoni. Atamaliza, anandimanga pulasitala pamiyendo yanga kuti ikhale m’malo mwake mpaka opaleshoni yotsatira. Nesi ankalira akaona mmene ndikuvutikira.

Miyezi inayi yotsatira, ndinaphunzira kuyendera ndodo. Ndikhoza kuimirira ndekha mpaka msinkhu wofika masentimita 110 chifukwa cha ndodozo. Ndimalemera kungoposa pang’ono makilogalamu 25. Nditadziŵa kuyendera ndodozo, ndinabwerera kunyumba ya anthu olumala mu 1964. Mwatsoka, mafupa ofooka a miyendo yangayi sanathe kunyamula thupi langa lolemerali, choncho posakhalitsa ndinakakamizikanso kumayenda chokwaŵa kapena kugwiritsa ntchito njinga ya olumala. Mpaka panopa kwakukulukulu ndimayendera njinga ya olumala.

Sindinapitenso ku tchalitchi. Mawu akuti ndinabadwa kwa “wodetsedwa” anapitiriza kundipweteketsa mtima kwambiri. Ndinawakonda kwambiri abambo ndi amayi anga, ndipo ndinakaniratu kuti iwo komanso Mulungu ndi amene anachititsa kuti ndibadwe wotere. Ndinayesetsa kukhalabe wosangalala. Ndinkafuna kuchitira ena zabwino ndipo, makamaka, kutsimikiza ndekha kuti inenso ndikhoza kutero.

Kukhala Modzidalira

Mu 1970, ndinakwatira Lidia, amene ndi wopuwala pang’ono kuyambira ubwana wake. Tinapeza nyumba yaing’ono, imene tinakhalamo zaka 15. Tonse tinagwira ntchito kuti tipeze zofunika pamoyo nthaŵi imeneyo. Ndinaphunzira kukonza mawatchi ndi tinthu tina ting’onting’ono.

Kwa nthaŵi ndithu ndinagwiritsa ntchito galu wophunzitsidwa kugwira ntchito zingapo zofunika. Inde, ine ndi wophunzitsa agalu tinapanga chowongolera galu chapaderadera ndithu. Ndinali ndi agalu aŵiri—wina dzina lake Vulkan ndi winayo dzina lake Palma. Palma anali mnzanga wokhulupirika kwa zaka zambiri. Iye amandinyamulira zakudya m’sitolo. Chinthu chokha chimene iye sanafune kuchita n’kuima pamzera tikamalipira. Iye ankanyamula chikwama changa cha ndalama ndi mano ake, ndipo anali ndi kokolowekera chikwama changa chogulira zinthu m’khosi mwake.

Mu 1973, amayi anadwala kwambiri. Popeza kuti nthaŵi zonse ndimakhala panyumba, ine ndi mkazi wanga tinaganiza kuti tiwatenge kuti adzikhala nafe. Nthaŵi imeneyo n’kuti abambo anga ndi achimwene anga asanu atamwalira, ndipo abale anga ena atatu ankakhala kwina ndi kwina ku Russia. Pamene amayi anali kukhala nafe, ndinayesa kuwachitira zimene ndikanatha. Kenaka anamwalira ali ndi zaka 85.

Mu 1978, ndinaganiza zopanga ndekha galimoto langa. Nditayesa kupanga magalimoto ambirimbiri, pomaliza pake ndinatha kupanga linalake londiyenerera. Bungwe loona zapamsewu kwathu lotchedwa The State Automobile Inspectorate linavomereza kuti andiyese kuyendetsa galimoto komanso kuti ndilembetse galimoto langalo. Ndinalipatsa dzina loti Osa (Mavu). Ine ndi mkazi wanga tinalipangira telela imene imanyamula katundu wolemera makilogalamu 300. Timatha kukwera aŵirife galimotolo titanyamula katundu. Galimoto loyendera mota limeneli linatithandiza mpaka 1985.

Chapanthaŵi yomweyo diso langa lamanzere linachita khungu, ndipo diso lamanja linayamba kusaona bwino. Nayenso Lidia anayamba kudwala matenda a mtima. Mu May chaka cha 1985, tinakakamizika kukakhala kunyumba ya anthu olumala mumzinda wa Dimitrovgrad chifukwa cholephera kuchita zambiri.

Chifukwa Chimene Moyo Wanga Ulili Wokondwa Tsopano

M’chilimwe cha chaka cha 1990, Mboni za Yehova zinachezera nyumba yathu ya anthu olumala. Zimene anali kuphunzitsa zinandichititsa chidwi. Iwo anandisonyeza nkhani ya Uthenga Wabwino wa Yohane yonena za munthu amene anabadwa wakhungu. Kunena za iyeyu, Yesu anati: “Sanachimwa ameneyo, kapena atate wake ndi amake.” (Yohane 9:1-3) Ndinauzidwa kuti tinalandira uchimo ndi matenda kuchokera kwa kholo lathu Adamu.—Aroma 5:12.

Komabe, ndinakondwera kwambiri makamaka chifukwa cha mfundo yakuti pomaliza Mulungu adzachiritsa onse amene adzakhala ndi moyo mu Ufumu wolamulidwa ndi Mwana wake, Yesu Kristu, pamene Paradaiso adzabwezeretsedwa padziko lapansi. (Salmo 37:11, 29; Luka 23:43; Chivumbulutso 21:3, 4) Ndinatulutsa misozi chifukwa cha chisangalalo, ndipo ndinanong’ona kuti: “Ndapeza choonadi, choonadi, choonadi!” Ndinaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova kwa chaka chimodzi, ndipo mu 1991, ndinabatizidwa m’madzi kusonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova Mulungu.

Ngakhale kuti ndinafunitsitsa kutumikira Yehova ndi kulalikira zolinga zake zodabwitsa, ndinakumana ndi zovuta zingapo. Kale, ndinalibe chifukwa chenicheni choyendera kutali, koma tsopano ndinafunika kupita kwina kukauzako ena za chikhulupiriro changa. Gawo langa loyamba kulalikira linali nyumba yathu yomweyo ya anthu olumala, kumene kumakhala anthu oposa 300. Ndinapempha kuti andipatse ntchito yogwira m’chipinda chosamalira za panyumbapo ndi cholinga choti ndithe kufikira anthu ambiri momwe ndingathere.

M’maŵa uliwonse ndimakhala pogwirira ntchito yanga n’kumasamala ntchitoyo. Pantchito yangayi, ndapeza anzanga ambiri amene ndakamba nawo nkhani zosangalatsa zokhudza Baibulo. Ambiri mwa iwo alandira mabuku ndi magazini amene awathandiza kumvetsa Baibulo. Alendo azoloŵera kuti ndidziwaŵerengera Baibulo ndi zofalitsa zokhudza Baibulo. Nthaŵi yopuma masana, kaŵirikaŵiri m’chipinda chimene ine ndi mkazi wanga timakhala m’madzaza anthu moti nthaŵi zina anthu ena satha kuloŵa.

Abale anga ndi alongo ochokera mumpingo wa Mboni za Yehova andithandiza kwambiri pantchito yolalikira. Amandibweretsera mabuku ofotokoza za m’Baibulo n’kucheza nane ndi mkazi wanga. Amandithandizanso kuti ndikafike ku Nyumba ya Ufumu pamisonkhano ya mpingo. Mboni ina inagula njinga yamoto yokhala ndi mpando wapadera pambali pake. Cholinga chachikulu chinali choti azindinyamula paulendo. Ena amene ali ndi magalimoto amakonda kubwera kudzandinyamula m’miyezi yachisanu.

Chifukwa cha chikondi choterocho, ndakhoza kusonkhana nawo pamisonkhano yachigawo yambirimbiri, kapena kuti misonkhano ya Mboni za Yehova yolandirira maphunziro. Msonkhano wanga woyamba unali msonkhano waukulu wa mayiko umene unachitikira ku Moscow mu July 1993, kumene kunasonkhana anthu 23,743, ochokera m’mayiko oposa 30. Ndinayenda mtunda wautali pafupifupi makilomita 1,000 kuti ndithe kukasonkhana nawo pamsonkhano umenewo. Kuyambira nthaŵi imeneyo sindinakhalepo osapita ku msonkhano uliwonse wachigawo wa anthu a Yehova.

Ndikuthokoza kwambiri chifukwa chakuti akuluakulu oyang’anira nyumba yathu ya anthu olumala amandilemekeza kwambiri. Mkazi wanga, Lidia amene ndakhala naye mogwirizana kwa zaka 30, amandilimbitsa ndiponso amandithandiza ngakhale kuti sitili chipembedzo chimodzi. Koma kwakukulukulu, Yehova amandichirikiza ndi dzanja lake lamphamvu ndipo amandipatsa madalitso ochuluka. Osati kale kwambiri, pa September 1, 1997, ndinaikidwa kukhala mpainiya, mmene atumiki a nthaŵi zonse a Mboni za Yehova amatchulidwira.

Panali nthaŵi zambiri m’moyo wanga zimene mtima wanga ukanaleka kugunda ndi kumwalira. Ndili wokondwatu kwabasi kuti zimenezo sizinachitike ndi kuti ndadziŵa ndi kukonda Gwero la moyo, Yehova Mulungu! Ndikufuna kupitiriza kum’tumikira pamodzi ndi abale ndi alongo anga auzimu a padziko lonse, malinga ngati ndikhalabe ndi moyo.

[Chithunzi patsamba 30]

Ndili ndi mkazi wanga, Lidia

[Chithunzi patsamba 31]

Kuphunzitsa wophunzira m’nyumba yathu ya anthu olumala