Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Njira Yodzawathetseratu Yapezeka!

Njira Yodzawathetseratu Yapezeka!

Njira Yodzawathetseratu Yapezeka!

TAGANIZIRANI dziko limene mwana aliyense wokhalamo ali wofunidwadi, wokondedwadi, ndiponso wodala mwakukhala ndi makolo osamala, achikondi olakalakadi moona mtima kutsogolera mwana wawo mmene angathere ndiponso kum’patsa malangizo abwino koposa. Taganizirani, dziko limene mwana aliyense wokhalamo ali ndi thupi lathanzi ndiponso maganizo abwino komanso limene kulibiretu ana okhala m’misewu ndiponso limene ana sakugwiritsidwanso ntchito akadali aang’ono chifukwa chosoŵa ndalama!

Kodi sizosilirika zimenezi? Inde. Koma kodi n’zotheka? Eetu, a Mboni za Yehova amati n’zotheka ndipo amatero pazifukwa ziŵiri.

Makolo Angathandizire Kuthetsa Mavutoŵa

Mosakayikira mungavomereze kuti makolo ali ndi mphamvu zothetsera ndipo nthaŵi zina ngakhale kupeŵera mavuto ena a ana. N’zoona kuti izi zimadalira ngati iwowo pokhala anthu aakulu, akufunitsitsa kutero. Inde, makolo enieniwo ndiwo ali ndi njira imodzi yothetsera vutoli.

Mwachitsanzo, anthu aakulu amene amatsatira malangizo a m’Baibulo akuti “mkazi asasiye mwamuna . . . ndipo mwamuna asalekane naye mkazi” sakhala ndi ana amene amavutika chifukwa chokhala m’nyumba imene makolo ananyanyalana kapena kusudzulana.—1 Akorinto 7:10, 11.

Anthu aakulu amene ali ofunitsitsa kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti ‘yendani moyenera, osati m’madyerero ndi kuledzera’ sakhala ndi ana amene amavutika maganizo chifukwa chokhala ndi makolo omwe ndi zidakwa za moŵa kapena za mankhwala osokoneza bongo.—Aroma 13:13; Aefeso 5:18.

Anthu aakulu amene ali ofunitsitsa kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti “mudzipatule ku dama” amathandiza kuchepetsa tsoka la kulera ana osafunidwa mwinanso m’banja la kholo limodzi.—1 Atesalonika 4:3; Mateyu 19:9.

Anthu aakulu amene ali ofunitsitsa kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti, “musaputa ana anu, kuti angataye mtima” ndiponso amene ‘amakonda ana awo’ sangadzakhale ndi ana amene angazunzidwe kapena kuvutika maganizo chifukwa cha kuchitidwa nkhanza m’njira ina iliyonse.—Akolose 3:21; Tito 2:4.

Mwachidule, tinene kuti kukadakhala kuti anthu onse achikulire ali ofunitsitsa kutsatira malangizo a m’Baibulo omwe Yesu ananena akuti, “Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero,” kodi kudakakhala ana miyandamiyanda osafunidwa ndiponso osakondedwa?—Mateyu 7:12.

N’zosangalatsa kuti pali anthu achikulire ambiri amene ali ofunitsitsa kuchita zonse zomwe zatchulidwa pamwambazo. Komabe, zomvetsa chisoni n’zakuti si onse amene ali ofunitsitsa ndipo pamenepo ndiye pagona vuto. Ndiponso ngakhale anthu amene ali ofunitsitsawo nthaŵi zambiri amasokonezedwa chifukwa cha kupanda ungwiro komanso zinthu zina zomwe iwo sangathe kuzipeŵa. Ngakhale kuti anthu angathandizire kuthetsa mavuto a ana, komabe n’zoonekeratu kuti iwo sangathetseretu mavutowa.

Boma la Mulungu Ndilo Lidzathetseretu Mavutowa

Wolemba wotchedwa John Ruskin yemwe watchulidwa m’nkhani yangothayi ankakhulupirira kwambiri kuti “ntchito yoyamba ya Boma ndiyo kuonetsetsa kuti mwana aliyense wobadwa m’dzikolo akhale ndi nyumba yabwino, zovala, chakudya ndiponso maphunziro, mpaka atafika zaka zoti atha kudziimira payekha.” Komabe, Ruskin ananena poyera amvekere, “kuti zimenezi zitheke Boma liyenera kulamulira anthu m’njira imene padakali pano sitikulotako mpang’ono pomwe.”

Ndi boma lochirikizidwa ndi Mulungu lokha limene lingakhale ndi ulamuliro wabwino umene Ruskin ankanena. Ndipo boma loterolo lalonjezedwa, ndipo n’lomwe Yesu anatchula pa Mateyu 6:9, 10. Boma lopangidwa ndi Mulungu limeneli likadzatenga ulamuliro wonse pa zochitika zapadziko lapansi, lidzalamulira anthu onse, ndipo lidzapatsa anthu ake onse nyumba, zovala, chakudya, ndiponso lidzaphunzitsa nzika zake zonse kuphatikizapo ana. (Yesaya 65:17-25) Koma boma lolungama limeneli lidzachitanso zambiri.

Mu Ufumu wa Mulungu anthu adzatha kulera ana m’njira yabwino. (Yobu 33:24-26) Achinyamata adzaleredwa mumzimu wamtendere ndi wachibale chapadziko lonse chomwe ndicho cholinga cha Mfundo za UN za Ufulu Wachibadwidwe wa Mwana. (Salmo 46:8, 9) Sikudzafunikanso kuika Chaka Choganizira Mwana kapena Pangano la Ufulu Wachibadwidwe wa Mwana.

Kubwezeretsa thanzi langwiro kwa makolo ndiponso kwa ana opuwala idzakhala ntchito yosavuta kwa Kristu Yesu yemwe ndi Mfumu yaboma lakumwamba limeneli. Zozizwitsa zochiritsa anthu zomwe iye anachita akadali padziko lapansi ndizo zikutsimikiza zimenezi. (Luka 6:17-19; Yohane 5:3-9; 9:1-7) Ngakhale kuukitsa ana ndiponso makolo akufa sikudzamulephera!—Mateyu 9:18-25.

N’zosangalatsatu kwabasi kudziŵa kuti nthaŵi yoti Mulungu achitepo kanthu kuthandiza ana apadziko lapansi ili pafupi!

[Bokosi/Zithunzi patsamba 12]

Chithandizo kwa Ana

Mboni za Yehova zili ndi chidwi kwambiri pa kuthandiza ana kupeŵa mavuto komanso pa kuwasonyeza m’mene angapiririre bwino kwambiri mavuto osapeŵeka. Pachifukwa chimenechi, kwazaka zochuluka iwo afalitsa mabuku ndiponso zinthu zambiri zokonzedwa bwino kuti zithandize ana pamavuto awo. Mabuku ameneŵa ndi monga buku lotchedwa Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo ndiponso lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa Mayankho Amene Amathandiza komanso pali vidiyo yamutu wakuti Young People Ask—How Can I Make Real Friends? (Achinyamata Akufunsa Kuti—Kodi Ndingapeze Bwanji Anzanga Enieni?) Zinthu zimenezi mungazipeze kwa a Mboni za Yehova akwanuko kapena mwa kulembera kwa omwe amafalitsa magazini ino.

Tikanena za ana awo, Mboni za Yehova zimawasonyeza kuti amafunidwa ndiponso kukondedwa mwa kukambirana nawo nthaŵi ndi nthaŵi za mavuto awo. Makolo nthaŵi zambiri amagwiritsa ntchito nkhani za m’mabuku ndi mavidiyo zomwe zatchulidwa pamwambapa monga maziko a ntchito yanthaŵi zonse yokulirakulira yolangiza ana. Mwina inunsotu mungafune kutsatira njira yofananayo ndi ana anuwo.