Kodi N’kuti Kumene Mungapeze Maphunziro Abwino Kwambiri?
Kodi N’kuti Kumene Mungapeze Maphunziro Abwino Kwambiri?
“Maphunziro angasule munthu, monga mmene munthu wosema ziboliboli angasemere mwala kukhala chiboliboli chokongola kwambiri.”—Anatero Joseph Addison, m’chaka cha 1711.
KODI munapita kusukulu? Anthu ambiri angayankhe kuti inde—koma si aliyense amene angayankhe choncho. Pamene tikuloŵa m’zaka za m’ma 2000, mamiliyoni ankhaninkhani a ana sapita kusukulu. Izi zakhala zikuchitika kwanthaŵi yaitali, moti tikunena pano anthu achikulire pafupifupi biliyoni imodzi ndi osaphunzira.
Komabe, maphunziro abwino ndi ofunika kwambiri. M’malo moona maphunziro kukhala chinthu chapamwamba chosati n’kuchikwanitsa, anthu ambiri lerolino akuwaona kukhala ufulu wa ana ndi akulu omwe. Koma kodi maphunziro abwino angapezeke bwanji popanda zipangizo zofunika? Bwanji ngati palibe mabuku okwanira, palibe aphunzitsi odziŵa ntchito, ndiponso palibe masukulu okwanira?
Inde, kodi n’kuti kumene anthu angapeze maphunziro abwino amene amalimbikitsa aliyense kuchitapo kanthu, kuwonjezera zimene akudziŵa pa zochitika zimene zimawakhudza, ndiponso kuwaphunzitsa zinthu zauzimu zimene zingasinthe moyo wawo? Ndi maphunziro ati amene amalimbikitsa makhalidwe abwino, amene amasonyeza mmene tingapezere moyo wabwinopo, ndiponso amene amapereka chiyembekezo chodalirika cham’tsogolo? Kodi maphunziro otereŵa akupezekadi kwa aliyense?
Maziko a Maphunziro Abwino Kwambiri
Ngakhale kuti zingaoneke ngati zodabwitsa, tingayankhe ndi mtima wonse kuti inde, maphunziro abwino alipo kwa anthu onse. Zili choncho chifukwa chakuti pali chida champhamvu chophunzirira chimene chili maziko amaphunziro abwino. Ndi “buku lophunzirira” lakalekale limene limapezeka lathunthu kapena mbali yake chabe, m’zinenero zoposa 2,200 padziko lapansi. Kunena zoona munthu aliyense padziko lapansi ali nalo m’chinenero chimene angamve. Kodi ndi buku liti limeneli?
Ndi Baibulo, buku limene anthu ambiri anena kuti n’lofunika kwambiri kuposa buku lina lililonse. “Aliyense amene amalidziŵa bwino Baibulo angatchedwedi wophunzira,’ analemba motero katswiri wamaphunziro wa kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, wotchedwa William Lyon Phelps. “Palibe maphunziro kapena makhalidwe ena alionse amene . . . angafanane nalo, ngakhale atakhala otchuka kapena apamwamba bwanji.”
Baibulo ndi nkhokwe ya mabuku olembedwa m’zaka zoposa 1,600. Ponena za nkhokwe yamabuku yofunika imeneyi, Phelps ananenanso kuti: “Malingaliro athu, nzeru zathu, maganizo athu, mabuku athu, luso lathu, zolinga zathu, kwenikweni zimachokera m’Baibulo kuposa m’mabuku ena onse . . . . Ndimakhulupirira kuti kudziŵa Baibulo osapita kukoleji n’kopindulitsa kwambiri kulekana n’kupita kukoleji koma osadziŵa Baibulo.”
Masiku ano ntchito yaikulu yamaphunziro a Baibulo ikuchitika padziko lonse ndi Akristu a Mboni za Yehova. Maphunziro ameneŵo si ophunzitsa kuŵerenga ndi kulemba kokha. Amaphunzitsa kukula m’maganizo ndi m’makhalidwe abwino. Amakhudza m’mene anthu amaonera m’tsogolo, amapereka chiyembekezo chodalirika kuti zimene zili m’tsogolo zidzakhala zabwino kwambiri kuposa zam’mbuyomo.
Chonde dziŵani za ntchito yamaphunziro imeneyi yokuthandizani kwa moyo wonse poŵerenga nkhani yotsatira.