Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tsopano Ndikhala Bwanji Pamene Abambo Atichokera?

Kodi Tsopano Ndikhala Bwanji Pamene Abambo Atichokera?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Tsopano Ndikhala Bwanji Pamene Abambo Atichokera?

“Kukula popanda abambo kunali kovuta. Ndinkangofuna wina wondiuzako nzeru.”—Henry. *

JOAN anali ndi zaka 13 pamene abambo ake anachoka panyumba. Pokhala chidakwa chotheratu ntchito, iwo anangoyesa pang’ono kuonana ndi ana awo atachoka. N’zachisoni kuti Joan sali yekha; achinyamata ambiri asiyidwa ndi abambo awo.

Ngati zimenezi zinakuchitikirani, ziyenera kuti zikukuvutani kuthana ndi vutolo. Mwina mtima umakuŵaŵani kapenanso mumakwiya nthaŵi ndi nthaŵi. Nthaŵi zina mungamve chisoni ndiponso kupsinjika maganizo. Mungafune ngakhale kupanduka. Monga mmene wolemba Baibulo Solomo ananenapo, “nsautso iyalutsa wanzeru.”—Mlaliki 7:7.

‘Kuyaluka’

James ‘anayaluka’ abambo ake atachoka panyumba. James ananena kuti: “Sindinamvere akulu alionse, ngakhale amayi anga enieni. Ndinkamenyana komanso kukangana ndi anthu ambirimbiri. Ndinkangonama ndi kuthaŵa panyumba usiku chifukwa panalibe woti n’kundidzudzula. Amayi anayesa kundiletsa, koma analephera.” Kodi kupanduka kwa James kunasintha moyo wake kukhala wabwino? Ndithudi ayi. James akuti posakhalitsa anayamba “kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kujomba kusukulu, komanso kulephera kusukuluko.” Posakhalitsa kupulupudza kwake kunakula. “Ndinkaba m’masitolo,” akuluakulu, “ndipo ndinkaberanso anthu. Ndinagwidwa kaŵiri ndi kutsekeredwa m’ndende kwa nthaŵi yochepa, koma sindinasiye.”

Atafunsidwa chimene chinam’pandutsa choncho, James anati: “Chifukwa chakuti abambo anga kunalibe, sindinalangidwe. Sindinaganize n’komwe mmene ndinali kuwapwetekera mtima amayi anga, mng’ono wanga ndi mchemwali wanga wamng’ono, komanso ine mwini. Ndinkafuna chisamaliro ndi chilango cha abambo.”

Koma kupanduka kumangoipitsiratu zinthu. (Yobu 36:18, 21) Mwachitsanzo, James sanangodzibweretsera mavuto komanso anavutitsa amayi ake ndi abale ake, amene sanafunikire kupsinjika maganizo ndi kupweteka mtima. Komanso choopsa kwambiri n’chakuti kupanduka kungam’chititse munthu kusamvana ndi Mulungu weniweniyo. Ndipotu, Yehova amalamula achinyamata kuti amvere amawo.—Miyambo 1:8; 30:17.

Kuthetsa Mkwiyo

Nangano, mungathetse bwanji mkwiyo ndi kuipidwa ndi abambo anu? Choyamba, muyenera kukumbukira kuti abambo anu sanachoke chifukwa cha inuyo. Komanso kuchoka kwawo sikutanthauza kuti sakukukondaninso kapena kuti sakusamalanso za inu ayi. Zoonadi, zingakhale zopweteka kwambiri ngati abambo sakulankhula nanu kaŵirikaŵiri kapena kukuchezerani. Koma monga mmene nkhani yapapitapo m’nkhani ngati ino inanenera, * abambo ambiri ochoka amalephera kuonana kapena kulemberana ndi ana awo osati chifukwa chakuti sawakonda, koma chifukwa chothedwa nzeru podziimba mlandu komanso manyazi. Ena, ngati abambo a Joan, amalephereratu kusiya mankhwala osokoneza bongo kapena uchidakwa, ndipo zimenezi zimawononga mphamvu yawo yochita zinthu bwinobwino.

Mulimonse mmene zingakhalire, yesani kukumbukira kuti makolo anu n’ngopanda ungwiro. Baibulo limati: “Onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23; 5:12) Inde, sikuti zimenezi zimalola khalidwe lopweteketsa mtima kapena losasamala. Koma kuzindikira mfundo yakuti ife tonse tinabadwa opanda ungwiro kungakupeputsireni zinthu kuti musiye mkwiyo ndi kuipidwa kovulaza.

Zimene Mlaliki 7:10 amanena zingakuthandizeni kuthetsa mkwiyo ndi kuipidwa ndi makolo anu. Taonani mmene amatichenjezera kusayang’ana zam’mbuyo: “Usanene, Kodi bwanji masiku akale anapambana ano? Pakuti sulikufunsa mwanzeru pamenepo.” Choncho, m’malo moganizabe mmene zinthu zinalili kale, ndi bwino kuona zimene mungachite pa vuto lanulo.

Kuyamba Inuyo

Mwachitsanzo, mungaganize zoyamba inuyo kuonana kapena kulembera abambo anu. Inde, ndiwo amene anakuchokerani ndipo mungaganizedi kuti ndi udindo wawo kuyamba iwowo. Koma ngati alephera kutero ndipo ngati kusaonana kwanu kapena kulemberana nawo makalata kukukuchititsani chisoni, kodi sikungakhale bwino inuyo kuyesa kuwongolera zinthu ? Taganizani mmene Yesu Kristu anachitira pamene abwenzi ake ena anam’pweteketsa mtima. Usiku womaliza moyo wake waumunthu, atumwi ake anam’siya. Petro anali atadzitama kuti adzakhalabe ndi Yesu zivute zitani. Koma Petro anam’kana Yesu—osati kamodzi kokha koma katatu!—Mateyu 26:31-35; Luka 22:54-62.

Ngakhale zinali choncho, Yesu anam’kondabe Petro ngakhale Petroyo anali ndi zolakwa. Yesu ataukitsidwa, anayamba ndi iyeyo kuyesa kubwezeretsa ubale wawo mwa kukaonekera kwa Petro payekha. (1 Akorinto 15:5) Chofunika kudziŵanso n’chakuti pamene Yesu anafunsa Petro kuti, “Kodi undikonda ine?” Petro anayankha kuti “Inde, Ambuye; mudziŵa kuti ndikukondani Inu.” Ngakhale kuti Petro anachita zochititsa manyazi, anakondabe Yesu.—Yohane 21:15

Monga mmene zinalili kwa Petro ndi Yesu, vuto la abambo anu lingakhale losatayitsa mtima ngati mmene mungaganizire. Mwina angakuyankheni ngati mutayamba inuyo njira zina ngati kuwaimbira foni, kuwalembera kalata, kapena kuwachezera. Henry, uja tam’tchula poyamba paja, akukumbukira kuti: “Ndinalembera kalata abambo kamodzi, ndipo anandiyankha kuti amanyadira nane. Ndinaika kalatayo m’pikitcha feremu n’kuisunga pakhoma langa kwazaka zambiri. Ndilinayobe mpaka lero.”

Joan ndi abale ake nawonso anayamba iwowo kuchezera abambo awo achidakwawo. “Iwo sanalinso abwinobwino,” Joan akutero, “koma zinakhalabe bwino kuwaona.” Mwina kuyamba inuyo zingakuyendereni bwino. Ngati salabadira poyamba, mungakonde kuti papite nthaŵi kaye n’kuyesanso.

Kuthana ndi Ululu Wokanidwa

Solomo akutikumbutsa kuti pali “mphindi yakufunafuna ndi mphindi yakumwazika.” (Mlaliki 3:6) Nthaŵi zina wachinyamata ayenera kuvomereza mfundo yopweteka yakuti abambo ake sakufuna kuyanjana ndi ana awo. Ngati zili choncho ndi abambo anube, mwina tsiku lina adzazindikira mwayi waukulu umene akutaya polephera kuyanjana nanu.

Komabe, pakali pano tsimikizani kuti kukukanani kwawoko sikukutanthauza kuti ndinu wopanda pake. Wolemba salmo la Baibulo Davide analemba kuti: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.” (Salmo 27:10) Inde, ndinu wofunikabe kwambiri kwa Mulungu.—Luka 12:6, 7.

Choncho ngati mwagwa mphwayi kapena kupsinjika maganizo, yandikirani kwa Mulungu m’pemphero. (Salmo 62:8) Muuzeni mmene mukumvera kwenikweni. Dziŵani kuti adzakumverani ndi kukutonthozani. Wolemba salmo la Baibulo wina analemba kuti: “Pondichulukira zolingalira zanga m’kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.”—Salmo 94:19.

Kuyanjana bwino ndi Akristu anzanu kungakuthandizeninso kuthana ndi kukanidwa koteroko. Miyambo 17:17 imati: “Bwenzi limakonda nthaŵi zonse; ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.” Mungapeze mabwenzi oterowo m’kati mwa mpingo wachikristu wa Mboni za Yehova. Kungakhale kothandiza makamaka kudziŵa ena mwa oyang’anira a mpingo. Mchimwene wa Joan, Peter akupereka langizo ili: “Lankhulani ndi achikulire mumpingo, ndipo adzakuthandizani kwambiri. Ngati abambo anu anakusiyani, adziŵitseni mmene mukumvera.” Oyang’anira mpingo angaperekenso malingaliro othandiza posamalira maudindo ena amene abambo anu anali kusamalira, monga ngati kukonzanso nyumba.

Amayi anu angakhalenso okuchirikizani. Inde, iwo angakhale akuvutika ndi maganizo. Koma ngati mutafotokoza mwaulemu mmene mukumvera, mosakayikira adzayesetsa kulabadira.

Chirikizani Banja Lanu!

Kusakhalapo kwa abambo anu kungakhudze banja lanu m’njira zambiri. Amayi anu angayambe ntchito—mwina ntchito ziŵiri—kuti athe kupeza zosoŵeka panyumba. Inu pamodzi ndi abale anu mungakhale ndi ntchito zapanyumba zochuluka. Koma mungazoloŵere kusintha koteroko ngati mukulitsa chikondi chachikristu chopanda dyera. (Akolose 3:14) Zimenezi zingakuthandizeni kukhala ndi mzimu wololera komanso kulamulira mkwiyo. (1 Akorinto 13:4-7) Peter akuti: “Kuthandiza apabanja lathu ndicho chinthu chabwino kuchita, ndipo ndimamva bwino podziŵa kuti ndikuthandiza amayi ndi achemwali anga.”

Mosakayikira, abambo akachoka panyumba limakhala tsoka ndipo zimaŵaŵa kwambiri. Koma tsimikizani kuti mwa kuthandizidwa ndi Mulungu komanso anzathu achikristu ndi banja, inu ndi achibale anu mungathane nalo vutolo. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mayina asinthidwa m’nkhani ino.

^ ndime 11 Onani nkhani yakuti “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . Kodi N’chifukwa Chiyani Abambo Anatichokera?” m’kope lathu la December 8, 2000.

^ ndime 27 Kuti mudziŵe zambiri zokhudza kukhala m’nyumba mwa kholo limodzi, onani nkhani za “Achichepere Akufunsa Kuti. . . ”, m’makope a January 8, 1991, ndi April 8, 1991.

[Chithunzi patsamba 19]

Achinyamata ena ayamba iwowo kuonana kapena kulembera kalata abambo awo