Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kusankha Chithandizo cha Mankhwala—Kodi N’kofunikira?

Kusankha Chithandizo cha Mankhwala—Kodi N’kofunikira?

Lingaliro la Baibulo

Kusankha Chithandizo cha Mankhwala—Kodi N’kofunikira?

MATENDA, ndiponso kuvulala n’zofala kwambiri pakati pa anthu. Anthu ambiri akapezana ndi adani a thanzi ameneŵa amafuna chithandizo pofunafuna mankhwala. Yesu Kristu anazindikira kufunika kotero, ponena kuti “amene ali olimba safuna sing’anga; koma akudwala ndiwo.”—Luka 5:31.

Wolemba Baibulo Luka, amene analemba mawu amenewo analinso dokotala. (Akolose 4:14) N’kutheka kuti m’maulendo amene anali kuyendera pamodzi, mtumwi Paulo anapindula ndi luso la Luka pankhani ya zachipatala. Koma kodi Malemba amalangizapo pa za mtundu wa mankhwala umene uli woyenerera kwa Akristu? Kodi kusankha mankhwala n’kofunikira?

Malangizo A M’malemba

Baibulo lingathe kuthandiza munthu kusankha bwino mankhwala. Mwachitsanzo, Deuteronomo 18:10-12 amalongosola momveka bwino kuti zinthu monga kuombedza maula ndiponso matsenga ‘n’zonyansa’ kwa Yehova. Zinthu zoletsedwazi zili m’gulu la “nyanga,” zimene Paulo anachenjeza kuti zisachitidwe. (Agalatiya 5:19-21) Motero, Akristu oona amapeŵa kuyezedwa kulikonse kapena njira iliyonse yochiritsira imene imaphatikizapo kukhulupirira mizimu moonekeratu.

Baibulo limavumbulanso kuti Mlengi amaona kuti moyo ndi magazi ndi zinthu zopatulika kwambiri. (Genesis 9:3, 4) Pofunitsitsa kutsatira lamulo lakuti tiyenera ‘kusala mwazi,’ Mboni za Yehova zimakana njira zochiritsira zimene zimaphwanya lamulo la Baibulo lakuti tisale mwazi. (Machitidwe 15:28, 29) Kutero sindiye kuti amakana chithandizo chilichonse chamankhwala. Mmalo mwake, iwo pamodzi ndi ana awo amafuna mankhwala abwino kwambiri. Amapempha ogwira ntchito yazachipatala kuti awathandize mogwirizana ndi chikhulupiriro chawo cha chipembedzo.

Samalirani Mayendedwe Anu

Mfumu Solomo anachenjeza kuti “wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.” (Miyambo 14:15) Ngakhale ngati mankhwala amene munthu wasankha sakuphwanya mfundo za m’Baibulo mwachindunji, munthu ayenera ‘kusamalira mayendedwe ake.’ Sikuti njira zonse zochiritsira zimathandiza. Pamene Yesu ananena kuti “odwala amafunikira sing’anga,” sanali kuvomereza njira zonse zochiritsira zimene zinalipo m’nthaŵi yake. Iye anali kudziŵa kuti njira zina zochiritsira zinali zothandizadi ndipo kuti zina zinali zonyenga. *

N’chimodzimodzinso masiku ano, mankhwala ena n’ngopanda ntchito, mwinanso amakhala achinyengo. Ngati munthu atapanda kulingalira bwino angaike moyo wake pachiswe. Tiyeneranso kuzindikira kuti mankhwala amene wina angachire nawo angakhale osathandiza kwa wina, mwinanso angamuvulaze. Pofuna kusankha mankhwala, munthu wanzeru amayamba waonetsetsa mankhwalawo m’malo ‘mongokhulupirira mawu alionse,’ ngakhale ngati atalangizidwa ndi anzake omufunira zabwino. Iye angasonyeze kukhala “wodziletsa” pofuna chidziŵitso chodalirika kuti athe kusankha mankhwala atawadziŵa kaye bwino.—Tito 2:12.

Ganizani Moona Mtima Ndiponso Mwanzeru

Kuganizira za thanzi lanu n’koyenera. Kusamalira thupi moyenera kuti likhale lathanzi kumasonyeza kuyamikira mphatso ya moyo ndiponso kuyamikira Mulungu amene anaipereka. (Salmo 36:9) Ngakhale kuti Akristu amafuna kupeza mankhwala owayanja, iwo ayenera kulingalira bwino pankhani zaumoyo. Mwachitsanzo, ngati munthu wathanzi labwino ndithu atayamba kudzitangwanitsa kwambiri pofuna thanzi labwino ndiponso kulimbitsa thupi, zingam’pangitse kuti aiwale ‘kutsimikizira zinthu zofunika kwambiri.’—Afilipi 1:10; 2:3, 4, NW.

Mayi wina wodwala kwambiri m’nthaŵi ya Yesu “analipira zonse anali nazo” pofuna kuti madokotala amuchiritse matenda ake aakulu. Kodi chinachitika n’chiyani? M’malo mochira, matenda akewo anakulirakulira, ndipo zimenezi ziyenera kuti zinam’foola kwambiri. (Marko 5:25, 26) Anachita zonse zimene akanatha kuti apeze mpumulo, koma palibe chinathandiza. Zimene zinam’chitikirazi zimasonyeza kupereŵera kwa sayansi ya zachipatala ya m’nthaŵi yake. Masiku anonso, ngakhale kuti kufufuza kwa zachipatala ndiponso umisiri zapita patsogolo kwambiri, anthu ambiri amangozindikira kuti zoterezi zikuwachitikira. Motero n’kofunika kwambiri kuzindikira malire a zimene sayansi ya zachipatala ingakwanitse. Kukhala ndi umoyo wangwiro n’kosatheka pakalipano. Akristu amazindikira kuti nthaŵi ya Mulungu ‘yochiritsa amitundu’ idakali m’tsogolo. (Chivumbulutso 22:1, 2) Choncho, tiyenera kulingalira bwino pankhani ya chithandizo chamankhwala.—Afilipi 4:5.

Mwachionekere, kusankha n’kofunikira. Pachifukwa chimenecho, tikamafuna kusankha chithandizo chamankhwala, zomwe tasankhazo zizionetsa kuti tikufunitsitsa kukhala athanzi ndiponso kukhalabe ndi ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Potero, tingayembekezerebe ndi mtima wonse kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Yehova lakuti m’dziko latsopano laulemerero limene likubwerali, “wokhalamo sadzanena, ine ndidwala.”—Yesaya 33:24.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Mwachitsanzo, akuti buku lina lolongosola zamankhwala la m’zaka za zana loyamba lolembedwa ndi Dioscorides, linanena kuti njira yochiritsira matenda a chikasu ndiyo kumwa mankhwala opangidwa ndi vinyo osakanizidwa ndi ndoŵe zambuzi! N’zoona kuti masiku ano timadziŵa kuti mankhwala otereŵa ankangowonjezera matenda a wodwalayo.

[Chithunzi patsamba 30]

Chithunzi cha “Dokotala,” chojambulidwa m’chaka cha 1891, ndi Bwana Luke Fildes

[Mawu a Chithunzi]

Tate Gallery, London/Art Resource, NY