Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ntchito Yamaphunziro Yofala Kwambiri

Ntchito Yamaphunziro Yofala Kwambiri

Ntchito Yamaphunziro Yofala Kwambiri

“Anthu ophunzira ndiwo okha amakhala paufulu.”—Anatero Epictetus m’chaka cha 100 C.E.

WILLIAM H. Seward amene anali mdani waukapolo ankakhulupirira kuti “anthu angayembekezere kupita patsogolo pokhapokha ngati atapitiriza kutsatira Baibulo.”

Mboni za Yehovanso zimalemekeza kwambiri Baibulo. Zimakhulupirira kuti anthu amene amagwiritsa ntchito mfundo zake amakhala amuna abwino, akazi abwino, ana abwino,—inde, amakhala anthu abwino kwambiri m’dziko. Choncho zimamvera lamulo la Yesu Kristu lakuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse.”—Mateyu 28:19, 20.

Pokwaniritsa cholinga chimenechi chophunzitsa anthu Baibulo, Mboni za Yehova zikuchita ntchito yophunzitsa imene ingakhale yofala kwambiri m’mbiri ya anthu. Kodi ndi yofala motani?

Ntchito Yapadziko Lonse Yopanga Mabuku

Mu utumiki wawo wapoyera, Mboni zimagwiritsa ntchito mabaibulo opezeka m’zinenero zambirimbiri. Koma zafalitsanso Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures m’zinenero 21 ndi la New World Translation of the Christian Greek Scriptures (lija amalitcha Chipangano Chatsopano) m’zinenero zina 16. Ndiponso, pakalipano ali m’kati motembenuza Baibulo limeneli m’zinenero zina 11. Mboni zimasindikizanso mabuku amene amathandiza kuyamikira Baibulo ndi kulimvetsetsa bwino.

Mwachitsanzo, magazini ino, yotchedwa Galamukani! imasindikizidwa m’zinenero 82, ndipo pa avareji kope lililonse amasindikiza makope oposa 20,380,000. Magazini inzake, yotchedwa Nsanja ya Olonda pafupifupi kope lililonse amasindikiza makope 22,398,000 m’zinenero 137. Ndiye kuti chaka chilichonse amasindikiza makope oposa biliyoni imodzi a magazini ameneŵa! Komanso, Nsanja ya Olonda imatuluka nthaŵi imodzi m’zinenero 124 mwa zinenero zimenezi, ndipo Galamukani! m’zinenero 58. Choncho, anthu a zinenero zosiyanasiyana padziko lonse amaŵerenga nkhani za m’magazini ameneŵa m’zinenero zawo panthaŵi imodzi.

Komanso, m’zaka makumi angapo zapitazi Mboni za Yehova zasindikiza miyandamiyanda ya mabuku othandizira kuphunzira Baibulo. Buku lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya analisindikiza makope oposa 107 miliyoni. Kenako, buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi analisindikiza makope oposa 81 miliyoni, ndipo posachedwapa buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, alisindikiza makope oposa 75 miliyoni m’zinenero 146. Komanso, asindikiza makope oposa 113 miliyoni m’zinenero 240 a bulosha la masamba 32 la Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?

Asindikizanso mabuku ena n’cholinga chapadera. Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, lopangidwa kaamba ka ana, lasindikizidwa makope oposa 51 miliyoni. Mabuku aŵiri opangidwa moganizira achinyamata otchedwa, Your Youth— Getting the Best Out of It ndi Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza, onse pamodzi anasindikizidwa makope oposa 53 miliyoni. Ndipo buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, limene lathandiza mabanja miyandamiyanda kuthana ndi mavuto awo, lasindikizidwa m’zinenero 115.

Mabuku ena anayi amene anatulutsidwa kuyambira 1985 amene kwenikweni amalimbikitsa kukulitsa chikhulupiriro mwa Mlengi, mwana Wake, ndiponso Baibulo onse pamodzi anasindikizidwa makope oposa 117 miliyoni. Mabukuwa ndi Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation?, Munthu Wamkulu Koposa Onse Amene Anakhalako, Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?, ndi Is There a Creator Who Cares About You?

Masiku ano mabuku onena za m’Baibulo amene Mboni za Yehova zimapanga amapezeka m’zinenero 353, ndipo posachedwapa ena mwa mabuku ameneŵa adzasindikizidwa m’zinenero zina 38. Ndithudi, Mboni za Yehova zasindikiza mabuku, timabuku, mabulosha, ndi magazini oposa 20 biliyoni kuyambira 1970! Komanso, aphunzitsi ngati 6,000,000 ndi otanganidwa kufesa chidziŵitso cha Baibulo m’mayiko oposa 230. Koma kodi zonsezi zatheka bwanji, ndipo kodi zakhudza motani miyoyo ya anthu?

Chifukwa Chake Amasindikiza M’Zinenero Zawo

Mungaone nokha kuti pamafunika kugwira ntchito mogwirizana kwambiri posindikiza mabuku abwino nthaŵi imodzi m’zinenero zoposa 100. Magulu a anthu otembenuza, amene apereka nthaŵi yawo ndi maluso awo, amagwiritsa ntchito makompyuta, kuti apange mabuku abwino zedi, olondola, komanso mofulumira. N’chifukwa chake ngakhale zinenero zimene zili ndi anthu otembenuza ochepa, mabuku amapezeka mofulumira. Pakalipano, amuna ndi akazi oposa 1,950 padziko lonse akugwira ntchito imeneyi, yomwe cholinga chake sichopanga ndalama. Nanga amachitiranji ntchito yaikulu choncho? Kodi n’koyenera kudzivuta motero popeza kuti anthu ambiri amene amalankhula zinenero zing’onozing’ono amadziŵanso zinenero zikuluzikulu?

Mboni za Yehova zaona kuti n’koyenera kutero pa chifukwa chimene William Tyndale, wotembenuza Baibulo wotchuka kwambiri m’zaka za m’ma 1500 anatchula. Iye analemba kuti: “Ndazindikira pa zimene ndaona kuti n’kosatheka kuphunzitsa anthu wamba chiphunzitso choona cha m’Baibulo, pokhapokha ngati apatsidwa Malemba m’chinenero chawo, kuti athe kuona mfundo zake, kugwirizana kwake, ndi tanthauzo lake.”

Ndi zoona kuti sizikhala zotheka nthaŵi zonse kuti anthu akhale ndi zofalitsa za m’Baibulo m’zinenero zawo. Koma ngati zatheka, choonadi cha m’Baibulo chimawafika msanga pamtima komanso chimawakhudza kwambiri. Taona zimenezi m’mayiko amene kale anali mu ulamuliro wa Soviet Union kumene mafuko amalankhula zinenero zosiyanasiyana. Kumayambiriro kwa m’ma 1900, ambiri mwa anthu ameneŵa anaphatikizidwa mu ulamuliro wa Soviet Union ndipo anaphunzitsidwa komanso kulimbikitsidwa kuti azilankhula Chirasha. Chotero, amaŵerenga ndi kulemba Chirasha koma amalankhulanso zinenero zawo.

Makamaka kuyambira pamene ulamuliro wa Soviet Union unatha mphamvu mu 1991, ambiri mwa anthu ameneŵa akufuna kuti azilankhula zinenero zawo. Izi zili choncho kwa anthu amene chinenero chawo ndi chi Adyghe, Altai, Belorussia, Georgia, Kirghiz, Komi, Ossetia, Tuvinia, kapena chilichonse mwa zinenero zawo zina zambiri. Ngakhale kuti ambiri angalankhule Chirasha, mabuku onena za m’Baibulo achirasha sawafika pamtima mofulumira. Koma, mabuku am’chinenero chawo amakhala ochititsa chidwi kwambiri. “Zili bwino kuti mwayamba kupanga mabuku m’chinenero chathu,” ananena choncho munthu wina amene anapatsidwa thirakiti lonena za m’Baibulo la m’chinenero cha Altai.

Chitsanzo china cha zimenezi ndi chilumba cha Greenland, chomwe chili m’dera la Artic ndipo chili ndi anthu pafupifupi 60,000 okha. Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zimasindikizidwa m’Chigirinilandi, ndipo magazini ameneŵa ndi otchuka kwambiri monganso zofalitsa zina zimene Mboni za Yehova zimasindikiza m’chinenero cha Chigirinilandi. Ndipotu, mabuku ameneŵa amapezeka m’nyumba zambiri m’midzi yakutali ndi chilumbachi.

Ku South Pacific, anthu pafupifupi 7,000 amalankhula Chinauru, 4,500 amalankhula Chitokelauni, ndipo 12,000 amalankhula Chirotuma. Tsopano Mboni zikupanga mathirakiti ndi mabulosha onena za m’Baibulo m’zinenero zimenezi komanso zikutulutsa Nsanja ya Olonda kamodzi pamwezi m’chi Niue, chinenero chimene amalankhula anthu pafupifupi 8,000, ndiponso m’Chituvalu chimene amalankhula anthu pafupifupi 11,000. Ndipotu, Mboni za Yehova zili m’gulu la anthu amene amafalitsa kwambiri mabuku m’zinenero zing’onozing’ono, ndipo amasindikiza mabuku ofotokoza za m’Baibulo m’zinenero ngati chi Bislama, Hiri Motu, Papiamento, Mauritian Creole, New Guinea Pidgin, Seychelles-Creole, Solomon Islands Pidgin, ndi zina zambiri.

Nthaŵi zambiri chinenero chikakhala cha anthu ochepa, anthuwo amakhala kwaokhaokha komanso amakhala osauka. Koma, m’madera otere anthu odziŵa kuŵerenga ndi kulemba amakhala ambiri. Ndipo nthaŵi zambiri Baibulo la m’chinenero chawo ndilo chimodzi mwa zofalitsa zina zimene anthu am’madera ngati ameneŵa amakhala nazo. Ndipo, palibe ngakhale nyuzipepala yosindikizidwa m’zinenero zinazi, chifukwa kutero kungakhale kungoluza ndalama.

Chifukwa Chake Ntchitoyi Ili Yoyamikirika

Chifukwa chakuti Mboni za Yehova zimapanga mabuku amene amasintha miyoyo ya anthu, anthu ambiri amayamikira ntchito yawo yotembenuza mabuku. Linda Crowl, amene amagwira ntchito ku bungwe la Institute for Pacific Studies, limene lili pa Yunivesite ya South Pacific mumzinda wa Suva, ku Fiji, ananena kuti ntchito yotembenuza mabuku imene Mboni zimagwira ndi “chinthu chosangalatsa zedi chimene chikuchitika ku Pacific kuno.” Amayamikira zofalitsa zawo chifukwa n’zabwino kwambiri.

Atayamba kusindikiza Galamukani! kamodzi m’miyezi itatu m’chinenero cha Chisamoa, nyuzipepala za kumeneko komanso nkhani za pawailesi yakanema yam’dzikolo zinaulutsa nkhaniyi. Poulutsa nkhaniyi anaonetsanso chikuto cha Galamukani! ndipo anatsegula magaziniyo n’kuonetsa nkhani iliyonse. Kenako anafotokoza nkhani iliyonse payokha.

Chosangalatsa n’chakuti m’mayiko ena otembenuza zofalitsa za Mboni nthaŵi zambiri amafikiridwa ndi mabungwe a komweko oona za chinenero pankhani zokhudza galamala, malamulo a kalembedwe, kapangidwe ka mawu, mawu achilendo, ndi zina zotero. Ndithudi, ntchito yamaphunziro aulere imene Mboni za Yehova zikuchita yakhudza miyoyo ya anthu ambiri zedi osati amene ali achangu m’mipingo yawo okha.

Komabe, monga taonera m’nkhani yoyamba ija, anthu achikulire pafupifupi biliyoni imodzi—pafupifupi munthu m’modzi mwa anthu asanu ndi m’modzi alionse padziko lonse lapansi ndi osaphunzira. Kodi achita chiyani pofuna kuthandiza anthu otereŵa kupindula ndi chidziŵitso chopezeka mwa kuŵerenga ndi kuphunzira?

Kuthetsa Vuto la Maphunziro Ofunika

M’mayiko ambiri Mboni zakonza ntchito yamaphunziro aulere, yophunzitsa anthu kuŵerenga ndi kulemba. Zasindikiza ngakhale mabuku awoawo amalangizo, monga buku lakuti Dziperekeni pa Kuŵerenga ndi Kulemba, limene lasindikizidwa m’zinenero 28. Anthu ambirimbiri, komanso amayi ndi anthu okalamba, aphunzitsidwa chifukwa cha makalasi ameneŵa.

Ku Burundi, Mboni za Yehova zachititsa makalasi amaphunziro amene athandiza anthu ambiri kudziŵa kuŵerenga ndi kulemba. Aunduna wa Sukulu ya Anthu Achikulire m’dzikomo ataona zotsatira zabwino za pulogalamu imeneyi, anapereka mphatso kwa alangizi anayi a Mboni pa Tsiku lokumbukira Maphunziro a Anthu Achikulire Padziko Lonse, pa September 8, 1999.

Lipoti ili linachokera ku Mozambique ndipo n’lonena za makalasi amaphunziro, m’mipingo pafupifupi 700 ya Mboni za Yehova: “M’zaka zinayi zapitazo, ophunzira 5,089 anatsiriza maphunziro awo, ndipo pakalipano tili ndi anthu 4,000 amene alembetsa.” Wophunzira wina anati: “Ndikuthokoza kwambiri sukulu imeneyi. . . Ndinali mbuli yeniyeni. Koma chifukwa cha sukuluyi, ndikutha kuŵerenga, ndipo ngakhale kuti ndikufunika kumapitirizabe kuphunzira, tsopano ndikutha kulemba.”

Ku Mexico, kuyambira 1946 pamene anayamba kusunga malipoti a sukulu imeneyi, anthu oposa 143,000 aphunzira kuŵerenga ndi kulemba m’masukulu apadera ophunzitsa maluso ameneŵa. Mayi wina wachikulire wazaka 63 analemba kuti: “Ndikuthokoza kwambiri a Mboni za Yehova, amene anandiphunzitsa kulemba ndi kuŵerenga. Moyo wanga unali wosasangalatsa. Koma tsopano nditha kupeza malangizo m’Baibulo, ndipo uthenga wake umandisangalatsa.”

M’dziko la ku South America la Brazil, Mboni zaphunzitsanso anthu ambiri kuŵerenga ndi kulemba. “Kuphunzira kuŵerenga kunali ngati kumasulidwa kuukapolo komwe ndakhala zaka zambiri,” anatero mayi wina wazaka 64. “Tsopano nditha kuŵerenga china chilichonse. Koposa zonse, kuŵerenga ndi kuphunzira Baibulo kwandimasula kuziphunzitso zonyenga.”

Kaŵirikaŵiri aphunzitsi a Baibulo amene ali a Mboni za Yehova amathandiza ophunzira awo aliyense payekha kudziŵa kuŵerenga. Ku Philippines, pamene Mboni zinafika panyumba ya Martina n’kuti ali ndi zaka zopitirira 80. Martina ankafuna phunziro la Baibulo lokhazikika, koma sankadziŵa kuŵerenga. Mothandizidwa ndi mphunzitsi wake wa Baibulo, Martina anapita patsogolo, ndipo chifukwa cha zina zimene ankaphunzira pampingo wakumeneko, anadziŵa kugwiritsa ntchito Baibulo pophunzitsa ena. Tikunena pano ndi mphunzitsi wa Baibulo wanthaŵi zonse wodziŵa kuŵerenga.

Ndithudi, tonse tili nawo mwayi woti tikhoza kukhala ophunzira. Koma tingafunse kuti, Kodi chidziŵitso cha m’Baibulo cha Mulungu ndi zifuno zake chingapindulitse anthu? Nkhani yomaliza m’nkhanizi iyankha funso limenelo.

[Bokosi patsamba 27]

“Sindikudziŵa Kuti Ndingathokoze Bwanji . . . ”

Akuluakulu a boma, anthu ophunzira, ndi anthu wamba onse achita chidwi ndi ntchito imene Mboni za Yehova zikugwira potukula maphunziro padziko lonse. Nazi zina zimene anena:

“Ine ndi boma langa tili osangalala kwambiri chifukwa buku ili [Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, la m’chinenero cha Chituvalu] ndi ‘chuma’ china chatsopano komanso chofunika m’chilumba cha Tuvalu muno. Muyenera kusangalala kwambiri ndi ntchito yabwino zedi imene mwagwira pomanga moyo wauzimu wa anthu adziko lino. Ndikukhulupirira kuti buku limeneli lidzalembedwa m’mbiri ya Tuvalu pankhani yosindikiza mabuku ophunzitsa.”Dr. T. Puapua, amene anali nduna yaikulu ya Tuvalu, lomwe ndi dziko la kumwera kwa nyanja ya Pacific.

“Mboni za Yehova zikuchita ntchito yachamuna yosindikiza mabuku, pogwiritsa ntchito njira zamakono kwambiri kumwera kwa nyanja ya Pacific. . . . Ntchito yosindikiza mabuku imeneyi n’njochititsa chidwi zedi tikaganiza za kusadalirika kwa njira zolankhulirana . . . pa zilumba za Pacific.”—Linda Crowl, wa pa Univesite ya South Pacific, mumzinda wa Suva, m’dziko la Fiji.

“Buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja la m’chinenero cha Chiisoko n’labwino ndiponso n’lothandiza zedi! Tikuthokoza anthu odzipereka amene akugwira ntchito yotembenuza m’chiisoko potithandiza kumvetsetsa bwino buku limeneli.”—C.O.A., Nigeria.

“Sindingathe kunena mmene ndikusangalalira chifukwa cha Baibulo limeneli [New World Translation m’Chiserbia], n’losavuta kulimvetsa. M’mbuyomu, ndakhala ndikuyesetsa kuŵerenga Baibulo lonse, koma nthaŵi zonse sindinkachedwa kugwa ulesi popeza sindinkamva chinenero chake. Tsopano nditha kuŵerenga Baibulo lapaderali ndi kulimvetsetsa!”—J.A., Yugoslavia.

“Zikomo kwambiri, chifukwa cha zofalitsa zanu zabwino, zothandiza, ndi zolimbikitsa zotembenuzidwa m’chinenero chotchedwa Tiv. Ndipotu, sindikudziŵa kuti ndingathokoze bwanji mapindu onse ndi chilimbikitso chonse chimene ndapeza m’mabuku ndi mabulosha ameneŵa. Anthu ambiri zedi apeza nawo zofalitsa zimenezi.”—P.T.S., Nigeria.

[Chithunzi]

Mabuku 36 miliyoni m’zinenero 115

[Zithunzi pamasamba 22, 23]

Mabaibulo oposa 100 miliyoni a “New World Translation” asindikizidwa m’zinenero 37

[Zithunzi patsamba 25]

Padziko lonse anthu pafupifupi 2,000 akugwira ntchito yotembenuza zofalitsa za Mboni za Yehova. (Gulu la otembenuza m’Chizulu ku South Africa, kumanzere; ndi wotembenuza m’Chijapanizi; m’munsi)

[Chithunzi patsamba 25]

Chaka chilichonse amasindikiza magazini a “Nsanja ya Olonda” ndi “Galamukani!” oposa biliyoni imodzi

[Zithunzi patsamba 26]

Mboni za Yehova zimachititsa makalasi ophunzitsa kuŵerenga ndi kulemba padziko lonse. (Ku Mexico, kumanja; ndi ku Burundi, m’munsi)