Sakhulupirira Kwenikweni Koma Akufufuzabe
Sakhulupirira Kwenikweni Koma Akufufuzabe
M’kalata yopita ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya ku Slovenia, munthu wina yemwe anati anabatizidwa ku chikatolika anapempha kuti: “Chonde nditumizireni bulosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Ndikufunanso ndidziŵe mmene ndingamalandirire magazini ya Galamukani! nthaŵi ndi nthaŵi kunyumba kwanga.”
Munthuyo analongosola kuti: “Chonde mundimvetse. Sindikhulupirira kwenikweni nkhani zachipembedzo, koma ndinadabwa kwambiri nditaŵerenga Galamukani! chifukwa sinakambe zinthu moumirira koma momveka bwino zedi ndiponso molangiza.” Kenaka anatchula magazini ina yachipembedzo yodziŵika bwino ndipo anati kwenikweni imasokoneza anthu maganizo.
Munthuyo analongosola chifukwa chimene anasankhira kulemba kalata poitanitsa bulosha la Mulungu Amafunanji m’malo molemba pa kabokosi kamene kamakhala kuseli kwa Galamukani! kaja. Anati: “Sindinafune kuwononga magaziniyo, ndinafuna kuti ikhale yathunthu!”
Bulosha la masamba 32 lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? lili ndi maphunziro 16. M’maphunzirowa muli ziphunzitso zikuluzikulu za m’Baibulo ndipo muli mfundo za m’Baibulo zosonyeza zimene tiyenera kuchita kuti tiyanjidwe ndi Mulungu. Ngati inunso mungakonde kulandira bulosha limeneli, lembani zofunika m’kabokosi kali pamunsika, ndi kukatumiza ku adiresi imene yasonyezedwayi kapena sankhani adiresi yoyenera patsamba 5 la magazini ino.
□ Chonde nditumizireni bulosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
□ Chonde nditumizireni munthu kuti azichita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.
[Chithunzi patsamba 32]
Mabulosha 113 miliyoni m’zilankhulidwe 240