Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ukwati ndi Mgwirizano wa Moyo Wonse?

Kodi Ukwati ndi Mgwirizano wa Moyo Wonse?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Ukwati ndi Mgwirizano wa Moyo Wonse?

N’KUFUNSIRANJI funsoli? Ndimayesa tikatengera malumbiro a ukwati a kumayiko a Azungu, ukwati uyenera kupitirizabe “pamtendere kapena pamavuto” “mpaka imfa”? Inde, malumbiro a ukwati amati mkwatibwi ndi mkwati amayamba mgwirizano wa moyo wonse. Koma ambiri saganiza kuti ali omangika ndi malumbiro amenewo. Maukwati ambiri akutha, ena patatha miyezi yochepa ndipo ena patatha zaka zambiri. N’chifukwa chiyani ambiri akusiya kulemekeza ukwati? Baibulo likuyankha.

Tikukupemphani kupenda 2 Timoteo 3:1-3, ndipo yerekezani ndi zimene mukuona m’dziko lerolino. Mbali ina ya mavesiŵa imati: “Masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, . . . osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, . . . osakhoza kudziletsa.” Kulondola kwa ulosiwo n’kodabwitsa. Mikhalidwe imeneyi yawononga ndi kufoola maukwati padziko lonse, tikaona kuchuluka kwa zisudzulo.

Ndithudi anthu ambiri sakulemekezanso ukwati. Poona zimenezi, tingafunse kuti: Kodi ukwati tiyenera kuuona kukhala nkhani yaikulu? Ndi iko komwe, kodi ukwati ndi wopatulika? Kodi Akristu ayenera kuuona motani ukwati? Kodi Baibulo likuwathandiza motani mabanja masiku ano?

Kodi Mulungu Anasintha Maganizo Ake?

Pachiyambi, Mulungu sananene kuti ukwati ndi mgwirizano wakanthaŵi kochepa. Zimene ananena pokwatitsa mwamuna woyamba ndi mkazi wake zafotokozedwa pa Genesis 2:21-24, ndipo pamenepa satchula n’komwe mpata wosudzulana kapena kupatukana. Komano, vesi 24 limati: “Mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.” Kodi lembali limatanthauzanji?

Talingalirani thupi la munthu, mmene minofu yake yosiyanasiyana imalukanira pamodzi popanda msoko ndi mmene mafupa ake amalumikizanira mwamphamvu m’mfundo zosapekesana. Sikugwirizana ndi kulimba kwake! Bwanji mmene zimaŵaŵira thupi labwino kwambiri limeneli likavulala koopsa! N’chifukwa chake, pa Genesis 2:24, mawu akuti “thupi limodzi” amagogomeza kugwirizana ndi kukhalitsa kwa ukwati. Komanso amasonyeza bwino zedi mmene zimapwetekera mgwirizanowo utathetsedwa.

Ngakhale kusintha kwa zinthu m’zaka masauzande apitawo kwaumba ndi kusintha malingaliro a anthu, Mulungu amaonabe ukwati kukhala mgwirizano wa moyo wonse. Zaka pafupifupi 2,400 zapitazo, amuna ena achiyuda anasiya akazi awo oyamba n’kukwatira atsikana. Mulungu anatsutsa zimenezi. Mwa mneneri wake Malaki anati: “Sungani mzimu wanu; ndipo asam’chitire monyenga mkazi wa ubwana wake ndi mmodzi yense. Pakuti ndidana nako kuleka kumene, ati Yehova Mulungu wa Israyeli.”—Malaki 2:15, 16.

Patatha zaka 400, Yesu anabwerezanso maganizo oyambirira a Mulungu pa ukwati pogwira mawu a pa Genesis 2:24 nati: “Chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Mateyu 19:5, 6) Patapita zaka mtumwi Paulo analangiza kuti “mkazi asasiye mwamuna” ndiponso “mwamuna asalekane naye mkazi.” (1 Akorinto 7:10, 11) Malemba ameneŵa akufotokoza bwino kwambiri mmene Mulungu amaonera ukwati.

Kodi Baibulo limalola ukwati kutha? Inde, ukwati umatha ngati wina wamwalira. (1 Akorinto 7:39) Chigololo chingathetsenso ukwati ngati wosalakwayo wasankha zimenezo. (Mateyu 19:9) Apo ayi, Baibulo limalimbikitsa okwatirana kukhalirabe limodzi.

Zothandiza Kuti Ukwati Ukhalitse

Mulungu amafuna kuti ukwati ukhalitse, osati wokhalira kulimbana, koma wosangalatsa. Amafuna kuti mwamuna ndi mkazi athetse mavuto awo n’kumasangalatsana. Mawu ake amapereka malangizo a ukwati wosangalatsa ndi wokhalitsa. Taonani malemba otsatiraŵa.

Aefeso 4:26: “Dzuŵa lisaloŵe muli chikwiyire.” * Mwamuna wina amene akusangalala ndi ukwati wake amakhulupirira kuti lembali limam’thandiza ndi mkazi wake kuthetsa mikangano mwamsanga. “Mukakangana, n’kusagona usiku, ndiye kuti zinthu sizili bwino. Simungafune vutolo kupitirira,” iye akutero. Nthaŵi zina iye ndi mkazi wake amakambirana mavuto awo mpaka usiku. Ndipo zimathandiza. Akutinso: “Kutsata mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo kumathandiza kwabasi.” Mwa kuchita zimenezi, mwamunayu ndi mkazi wake akhala ndi ukwati wosangalatsa kwa zaka 42.

Akolose 3:13: “Kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha.” Mwamuna wina akulongosola mmene iye ndi mkazi wake agwiritsira ntchito zimenezi: “Okwatirana angakwiyitsane popanda kulakwirana kwenikweni, popeza tonse tili ndi zophophonya ndi zizoloŵezi zimene zimanyansa anthu ena. Timakhululukirana mwa kusalola zinthu zimenezi kutidanitsa.” Ndithudi malingaliro amenewo athandiza banja limeneli zaka 54 zimene akhala m’banja!

Kutsata mfundo zachikhalidwe za m’Malemba zimenezi kumalimbitsa ubale umene umamanga pamodzi amuna ndi akazi awo. Choncho ukwati wawo ungakhale wachimwemwe, wokhutiritsa ndi wokhalitsa.

Ngati mungafune kudziŵa zambiri kapena kuti munthu wina aziphunzira nanu Baibulo panyumba panu kwaulere, lemberani ku Watch Tower, Box 30749, Lilongwe 3, Malaŵi, kapena ku adiresi yoyenerera pa maadiresi amene ali patsamba 5.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Malinga ndi nthaŵi ya ku Middle East m’zaka za zana loyamba, tsiku limatha dzuŵa likaloŵa. Chotero Paulo anali kulimbikitsa oŵerenga kukhala pamtendere ndi ena tsiku lisanathe.