Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulimbana ndi Mavuto mwa Kukhala N’zolinga

Kulimbana ndi Mavuto mwa Kukhala N’zolinga

Kulimbana ndi Mavuto mwa Kukhala N’zolinga

MBALI ya nyumba ina yoyandikana ndi bwalo landege la ku New York lotchedwa LaGuardia ndiyo nyumba ya William (Bill) Meiners ndi mkazi wake, Rose. Kumeneko, Rose, mayi wodziŵa kulandira anthu, wazaka zokwana cha m’ma 75, akulandira mlendo wake mwachimwemwe. M’kati mwanyumbayo munthu sangalephere kuona mmene balaza losangalatsalo likusonyezera kuti mayiyu n’ngwosangalala. Maluŵa oyalidwa mochititsa kaso amene ali pafupi ndi khomo ndiponso zojambulajambula zopachikidwa pazipupa n’zosonyeza kuti anthuwa n’ngachimwemwe ndiponso osangalala nawo moyo.

Moyandikana ndi balaza pali chipinda chowala bwino, chimene Bill, yemwe ali ndi zaka 77, wagonamo pabedi, atayedzamira ndi msana wake pa matilesi ochita kusintha. Poona mlendo wakeyo, akumuyang’ana mosonyeza chifundo ndiponso chimwemwe ndipo akumwetulira kuti mwee! Angakonde atadzuka, kugwirana chanza ndi mlendoyo, ndi kukupatirana naye, koma sangathe kutero. Bill anafa thupi lonse kuchokera m’khosi kupita kumunsi kupatulako dzanja lake lamanzere basi.

Pakuti Bill wakhala akudwala kuyambira ali ndi zaka 26, akumufunsa kuti anene chomwe chamuthandiza kulimbana ndi matendawo kwa zaka zopitirira 50. Bill ndi Rose akuyang’anana mokhala ngati kuti zawaseketsa. “Sitikudziŵa zakuti pali wina amene akudwala!” akutero Rose uku akuseka chikhakhali n’kumveka m’chipinda monsemo. Maso a Bill ali phethiphethi n’chimwemwe; akuseka chapansipansi ndipo akugwedeza mutu wake movomereza. “Inde palibe akudwala muno,” akutero mokayika ndi mawu akukhosi. Rose ndi Bill akunena mawu angapo ongosereula, ndipo pasanathe nthaŵi, chipindacho chikudzaza ndi phokoso lakuseka. N’zoonekeratu kuti chikondi chimene Bill ndi Rose anali nacho pamene anakumana mu September 1945 chidakalipo chonse. Bill akufunsidwanso kuti: “Tsopano nenani zoona, kodi ndi mavuto otani amene mwakumana nawo? Ndipo kodi n’chiyani chimene chinakuthandizani kuti mulimbane nawo n’kukhalabe osangalala ndi moyo?” Atam’chonderera, Bill anavomera kusimba nkhani yake. Mfundo zili pansipa n’zimene atolankhani a Galamukani! anapeza pokambirana nthaŵi zingapo ndi Bill ndi mkazi wake.

Mavuto Ayamba

Mu October 1949—patatha zaka zitatu chikwatirireni Rose ndipo patatha miyezi itatu chibadwireni mwana wawo Vicki—Bill anauzidwa kuti ali ndi chotupa cha matenda a kansa pa kapaipi kena ka m’kholingo lake, ndipo chotupacho anakachichotsa. Patangotha miyezi ingapo, dokotala wa Bill anamuuza za vuto linanso—matenda a kansawo anali atagwira kholingo lonse. “Anandiuza kuti ndikapanda kuchitidwa opaleshoni yochotsa kholingo, ndiye kuti ndikhala ndi moyo kwa zaka ziŵiri zokha basi.”

Bill ndi Rose anawauziratu zotsatirapo za opaleshoni imeneyi. Kholingo, la mawu limachokera kutsinde la lilime n’kufika poyambira pa kum’mero. M’kati mwa kholingo mumakhala timapaipi tiŵiri totulutsa mawu. Mpweya wochokera m’mapapo ukayenda modutsa timapaipiti, timanjenjemera n’kutulutsa mawu amene timamva tikamalankhula. Akachotsa kholingo, pamwamba pa m’mero pamalumikizidwa pabowo lina lake lopezeka kumaso kwakhosi limene limangokhala pululu. Opaleshoniyo ikatha, wodwalayo amapuma kudzera pabowo limeneli—koma salankhulanso.

“Nditamva zimenezi, ndinapsa mtima,” anatero Bill. “Tinali ndi kamwana kakakazi, ndinali pantchito, tinkaganiza zodzachita zinthu zambiri m’moyo wathu, koma tsopano zonse zimene ndinali kuyembekeza zinathera pompo.” Koma chifukwa chakuti opaleshoni yochotsa kholingoyo inali yopulumutsa moyo wake, Bill anagwirizana nazo zakuti amuchite opaleshoni. Bill akusimba kuti, “Atandichita opaleshoniyo sindinkathanso kumeza kanthu. Sindinkathanso kulankhula chilichonse. Ndinasanduka bububu.” Pamene Rose anakam’zonda Bill, anali kulankhulana naye polemba mawu papepala basi. Inali nthaŵi yowawa zedi. Kuti athetse vuto limeneli anapanga zolinga zina.

Osalankhula Ndiponso Osagwira Ntchito

Opaleshoni ya kholingo inachititsa kuti Bill asathenso kulankhula komanso asakhale pantchito. Poyamba anali kugwira ntchito mushopu yolumikiza makina, koma pakuti tsopano ankangopumira pa bowo lapakhosi lake, fumbi ndiponso utsi ukadawononga mapapo ake. Anafunikira kupeza ntchito ina. Adakali bububu choncho analembetsa kusukulu ina kuti aphunzire kukonza mawatchi. Bill anati, “Inali yofanana ndi ntchito yanga yapoyamba, ndinkadziŵa kulumikiza zitsulo za makina ndipo popanga mawatchi timalumikizanso tizitsulo. Kungoti tizitsulo take sitinali tolemera mapaundi 50!” Atangomaliza sukuluyo, anapeza ntchito yokonza mawatchi. Ndiye kuti anakwanitsa cholinga chimodzi.

Panthaŵiyi n’kuti Bill atayambanso kupita kusukulu kukaphunzira kulankhulira kukhosi. Polankhulira kukhosi mawu samveka kuchokera m’timapaipi tiŵiri totulutsa mawu tija ayi koma kuchokera kukhosi kukamanjenjemera, m’njira imene chakudya chimadzera chikamapita m’mimba. Munthuyo amayamba kuphunzira kumeza mpweya ndi kuukakamiza kuti utsikire kukhosi. Kenaka, amautulutsa mwapang’onopang’ono. M’pweyawo ukamatuluka, umachititsa kuti kukhosi kunjenjemere. Zimenezi zimapangitsa kuti kukhosiku kumveke mawu apansipansi, amene munthu angathe kuwasintha ndi pakamwa ndiponso milomo yake kuti asanduke mawu odziŵika tanthauzo lake.

“Poyamba, ndinkageya pokhapokha ndikadya kwambiri, koma tsopano ndinafunikira kuphunzira kugeya mosalekeza”, anatero Bill. Poyamba ndinakhoza kungotchula liwu limodzi limodzi. Mwachitsanzo, potchula kuti ‘Kodi muli bwanji?’, ndinkakoka mpweya, n’kuumeza, n’kugeya potchula liwu lililonse. Sizinali zophweka. Kenaka, mphunzitsi wanga anandiuza kuti ndizimwa kwambiri zakumwa zinazake zoziziritsa kukhosi chifukwa chakuti mpweya wake ungandithandize kuti ndizigeya. Motero nthaŵi iliyonse Rose akapita panja kukawongola miyendo ndi Vicki, ndimangokhalira kumwa ndi kugeya. Ndinalimbikira kwambiri kutero!”

Ngakhale kuti odwala 60 mwa 100 alionse ochotsedwa kholingo amakanika kuphunzira kulankhulira kukhosi, Bill anayamba kudziŵa. Vicki, amene panthaŵiyi anali ndi zaka pafupifupi ziŵiri, anali kumulimbikitsa mosadziŵa. Bill analongosola kuti: “Vicki anali kundilankhula kenaka n’kumandiyang’ana, kudikirira kuti ndimuyankhe. Koma sindinkatha kumuyankha ngakhale liwu limodzi. Ndiye anali kupitiriza kulankhula, koma sindinali kumuyankhabe. Popsa mtima, Vicki anali kuuza mkazi wanga kuti: ‘Tawauzani bambo kuti andilankhule!’ Mawuwa anandikhudza kwambiri ndipo anandipangitsa kufunitsitsa kwambiri kuyambiranso kulankhula.” Bill atakwanitsa kulankhula, Vicki, Rose, ndi ena anasangalala. Apa anakwanitsanso cholinga chake china.

Kukumana ndi Vuto Linanso

Kumapeto kwa 1951, Bill ndi Rose anakumana ndi vuto lina. Poopa kuti matenda a kansa angamuyambenso, madokotala anamulangiza Bill kuti alandire chithandizo chogwiritsa ntchito mphamvu ya kuwala. Bill anavomera. Atalandira chithandizocho, anali wofunitsitsa kubwereranso mwakale. Sanadziŵe kuti posakhalitsa adzadwalanso matenda ena!

Pafupifupi chaka chathunthu chinadutsa. Kenaka tsiku lina zala zakumanja a Bill zinachita dzanzi. Kenaka anayamba kulephera kukwera masitepesi. Kenaka pasanapite nthaŵi yaitali, anagwa akuyenda ndipo analephera kuimirira. Atakamuyesa anapeza kuti chithandizo cha mphamvu ya kuwala chija (chimene panthaŵiyo sichinali cholondola kwenikweni monga masiku ano) chinawononga fupa lamsana wake. Anauzidwa kuti matenda ake adzaipiraipira. Ndipo mpaka dokotala wina anamuuza kuti zoti apulumuka “zinali zosadziŵika.” Bill ndi Rose anasokonezeka maganizo kwambiri.

Ngakhale zinali choncho, poyesa kuthana ndi vuto limeneli, Bill anakakhala m’chipatala akulandira chithandizo kwa miyezi isanu ndi umodzi. Ngakhale kuti chithandizochi sichinam’pangitse kukhalanso wabwinobwino, kukhala kwake m’chipatalamo kunam’pangitsa kusintha moyo wake—kusintha kumene m’kupita kwa nthaŵi kunam’chititsa kuti adziŵe Yehova. Kodi zimenezo zinachitika bwanji?

Alimbitsidwa Pozindikira Chochititsa Mavutowo

Kwa miyezi isanu ndi umodzi imeneyo, Bill anali m’chipinda chimodzi ndi anthu 19 ofa ziwalo pachipatala cha Ayuda, ndipo onse anali achipembedzo chachiyuda cha Jewish Orthodox. Madzulo alionse anthu ameneŵa anali kukambirana za m’Baibulo. Bill yemwe anali kupita ku tchalitchi cha Baptist, ankangomvetsera. Koma pomwe ankachoka kuchipatalako, anali atamva zinthu zambiri ndithu mwakuti anavomereza zakuti Mulungu Wamphamvuyonse ndi munthu m’modzi basi ndi kuti chiphunzitso cha Utatu n’chotsutsana ndi Baibulo. Motero, Bill sanapitenso kutchalitchi chake. Komabe, iye anaona kuti m’pofunika kutsogozedwa mwauzimu kuti alimbane nawo mavuto a m’moyo. “Ndinali kum’mpemphabe Mulungu kuti andithandize, ndipo iye anayankha mapemphero anga,” anatero Bill.

Tsiku lina Loŵeruka mu 1953, munthu wina wachikulire, Roy Douglas, amene nthaŵi ina ankakhala naye moyandikana amenenso anamva za mavuto a Bill, anam’chezera. Roy amene ali wa Mboni za Yehova, anapempha Bill kuti aphunzire naye Baibulo, ndipo Bill anavomera. Zimene Bill anaŵerenga m’Baibulo ndi m’buku lakuti “Mulungu Akhale Woona” * zinatsegula maso ake. Anamuuza Rose zimene anali kuphunzira, ndipo naye anayamba kuphunzira nawo. Rose anakumbukira kuti: “Kutchalitchi ankatiphunzitsa kuti matenda anali chilango chochokera kwa Mulungu, koma phunziro lathu la Baibulo linasonyeza kuti izi sizinali zoona. Mitima yathu inakhala pansi.” Bill anawonjezera ponena kuti: “Kuphunzira m’Baibulo chimene chimayambitsa mavuto onse, kuphatikizapo matenda angawa, ndiponso kudziŵa kuti tsogolo labwino likubwera posachedwapa kunatithandiza kuti tipirire mavuto angawa.” Mu 1954, Bill ndi Rose anakwanitsa cholinga china. Onse anabatizidwa n’kukhala Mboni za Yehova.

Kupitiriza Kusintha

Panthaŵiyi n’kuti ziwalo za Bill zitaferatu mwakuti sakanathanso kuchita ntchito yake. Kuti athe kupeza zofunika m’moyo, Bill ndi Rose anasinthana ntchito: Bill anali kukhala panyumba ndi Vicki, ndipo Rose anayamba kugwira ntchito kukampani yokonza mawatchi ija, ndipo ntchitoyi anaigwira kwa zaka 35!

Bill akusimba kuti: “Kusamalira mwana wathu wamkazi, Vicki, kunandisangalatsa kwabasi. Nayenso mwanayo anali kusangalala nazo. Anali kuuza monyadira munthu aliyense amene anali kukumana naye kuti: ‘Inetu ndimasamalira Bambo anga!’ Kenaka pamene anayamba kupita kusukulu ndinali kumuthandiza akapatsidwa ntchito yoti achitire kunyumba, ndipo nthaŵi zambiri tinali kuseŵera maseŵera. Ndiponso ndinapeza mwayi waukulu kwambiri womulangiza za m’Baibulo.”

Bill ndi banja lake ankasangalalanso popezeka pamisonkhano yachikristu ku Nyumba ya Ufumu. Amatha ola lathunthu akuyenda motsimphina kuchokera kunyumba kwake mpaka kukafika ku Nyumba ya Ufumu, koma sankaphonya misonkhano. Pambuyo pake, atasamukira kudera lina la mzindawo, Bill ndi Rose anagula galimoto laling’ono, ndipo Rose anali kuyendetsa banjalo popita ku Nyumba ya Ufumu. Ngakhale kuti Bill ankangolankhula kwa nthaŵi yochepa chabe, iye analembetsa kukhala wophunzira m’Sukulu Yautumiki Wateokalase. Bill analongosola kuti: “Ndinkalemba nkhani yanga, ndipo mbale wina ankaikamba. Akamaliza kuikamba, woyang’anira sukulu ankandipatsa uphungu wokhudza mfundo zimene ndinalemba.”

Anthu osiyanasiyana m’mpingo anamuthandizanso Bill kuti azichita nawo kaŵirikaŵiri ntchito yolalikira. Ndipo anthu oona kudzipereka kwake sanadabwe pamene Bill anaikidwa kukhala mtumiki wotumikira mumpingomo. Ndiye pamene miyendo yake inaferatu ndipo matenda a kufa ziwalowo atam’kulira, anangobindikirano m’nyumba mwake, ndipo m’kupita kwanthaŵi, anali kungokhala chigonere. Kodi vuto ilinso akadathana nalo?

Chotangwanitsa Chokhutiritsa

Bill anati: “Pakuti ndinkakhala panyumba kwatsiku lonse, ndinafunafuna chinthu choti chizinditangwanitsa. Ndisanafe ziwalo ndinkakonda kujambula zithunzi. Motero ndinaganiza zoyesa kujambula zithunzi zapamanja, ngakhale kuti ndinali ndisanajambuleko zithunzi zapamanja m’moyo mwanga. Komanso, ndimagwiritsa ntchito dzanja lamanja, koma dzanja langa lonse lamanja ndiponso zala zanga ziŵiri zakumanzere zinali zitafa. Komabe, Rose anagula mabuku ambiri onena za maluso osiyanasiyana ojambulira. Ndinali kuwaŵerenga ndipo ndinayamba kujambula ndi dzanja langa lamanzere. Zojambula zanga zambiri ndinali kukangoziotcha, koma m’kupita kwanthaŵi ndinayamba kudziŵa.”

M’nyumba ya Bill ndi Rose panopo muli zithunzi zokongola zojambula ndi utoto zimene zimasonyeza kuti Bill anakhoza kuposa mmene anali kuganizira. Bill anawonjezera kunena kuti: “Pafupifupi zaka zisanu zapitazo, dzanja langa lamanzere linayamba kunjenjemera kwambiri mwakuti ndinasiyira pompo kujambula, koma kwa zaka zambiri luso losangalatsali linkandikhutiritsa kwambiri.”

Cholinga Chimene Chinatsala

Bill akufotokoza bwinobwino kuti: “Tsopano patha zaka zoposa 50 chiyambireni kuvutika ndi matenda angawa. Kuŵerenga Baibulo kumandilimbikitsabe, makamaka ndikamaŵerenga Masalmo ndiponso buku la Yobu. Ndipo ndimakonda kuŵerenga mabuku a Watch Tower Society. Ndimalimbikitsidwanso pamene anthu a mumpingo mwathu ndiponso oyang’anira oyendayenda akamandiyendera ndi kundiuza nkhani zolimbikitsa zimene akumana nazo. Kuphatikizanso apo, ndimatha kumvetsera misonkhano kudzera patelefoni yolumikizidwa ku Nyumba ya Ufumu ndiponso ndimalandira matepi a vidiyo a misonkhano yaikulu.

“Ndimayamikira kwambiri kuti ndinadalitsidwa popeza mkazi wachikondiyu. Kwa zaka zonsezi, wakhala mnzanga wapamtima. Winanso amene ndimasangalala naye kwambiri ndi mwana wathu wamkazi uja, amene tsopano akutumikira Yehova pamodzi ndi banja lake. Makamaka ndimathokoza Yehova pondithandiza kupitiriza kumuyandikira. Panopo, pamene thupi ndiponso mawu anga zikufookerafookera, nthaŵi zambiri ndimaganizira mawu a mtumwi Paulo akuti: ‘Sitifoka koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wam’kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.’ (2 Akorinto 4:16) Inde, cholinga changa chidakali chakuti ndikhale wogalamuka mwauzimu kwa moyo wanga wonse.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 20 Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.; tsopano anasiya kulisindikiza.

[Mawu Otsindika patsamba 12]

“Atandichita opaleshoniyo sindinkathanso kumeza kanthu. Sindinkathanso kulankhula chilichonse. Ndinasanduka bububu”

[Chithunzi patsamba 13]

Bill ndi Rose, panopa