Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupirira Mosangalala M’dziko Lotangwanitsa

Kupirira Mosangalala M’dziko Lotangwanitsa

Kupirira Mosangalala M’dziko Lotangwanitsa

ANTHU AMBIRI AMAPIRIRA ZOVUTA PAMOYO WAWO, KOMA NDI OCHEPA AMENE AMASANGALALA POPIRIRA. ZIMENEZO ZIMAFUNA NZERU YAPADERA.

POZINDIKIRA zimenezi, buku lakuti The 24-Hour Society limati: “Tifunika kukulitsa nzeru kuti titeteze zofuna za anthu ndi umunthu wawo m’dziko la zaumisiri limene tapangali.”

N’zosangalatsa kuti nzeru yothandiza ikupezeka m’buku lofala koposa padziko lonse lapansi—Mawu a Mulungu, Baibulo. Pokhala louziridwa ndi Iye amene amamvetsa bwinobwino zofuna za anthu ndi umunthu wawo, Baibulo lili ndi mfundo zabwino zachikhalidwe. Kugwiritsa ntchito mfundo zimenezi kungakuthandizeni kupezanso mphamvu yolamulira moyo wanu, kukupatsani chimwemwe pamene mukupirira m’dziko lotangwanitsa lamasiku anoli.—Yesaya 48:18; 2 Timoteo 3:16.

Mfundo zimenezi zikukhudza mbali zikuluzikulu zitatu. Yoyamba, zimasonyeza zinthu zosafunikira zimene mungangozisiya mwanzeru. Yachiŵiri, zingakuthandizeni kuika zinthu zofunika kwambiri pamalo ake. Yachitatu, zimakupatsani maganizo auzimu pa moyo amene amaposeratu maganizo a dziko. Tiyeni tsopano tipende mbali zitatu zimenezi.

Moyo Wanu Ukhale Wosalira Zambiri Ndiponso Wadongosolo

Tayerekezani kuti mukupita kukacheza kwinakwake masiku ochepa. Mukufuna kuti mukakhale motakasuka, ndiye mukunyamula tenti yaikulu pamodzi ndi zinthu zonse zimene mukuganiza kuti n’zofunika. Ndiponso mukutenga telela yodzaza mipando, ziwiya zophikira, firiji, jeneleta yaing’ono, nyali, wailesi ya kanema, ndi zinthu zina zambiri pamodzi ndi zakudya. Komatu kulongedza zinthu zonsezi kukutengerani maola ambiri! Kenaka tchuthi chanu cha nthaŵi yochepayo chitatha, mutenganso nthaŵi ina yolongedzanso—kuphatikizapo kusunga padera zina zonse zodzagwira ntchito m’tsogolo kunyumba. Poganizira za m’mbuyo, mukuona kuti munalibe nthaŵi yokwanira yosangalala kumene munakachezako! Ndiyeno mukudabwa ngati zimene munachitazo n’zopindula n’komwe.

Kwa anthu mamiliyoni masiku ano, moyo uli ngati ulendo wokachezawo. Amawononga nthaŵi yopitirira muyezo polimbikira kupeza ndi kusamalira zinthu zambirimbiri zimene dzikoli limafuna kuti tikhulupirire kuti n’zofunika kuti tikhale achimwemwe. Mosiyana ndi zimenezo, Yesu Kristu anati: “Moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.” (Luka 12:15) Inde, moyo suyerekezedwa n’kukhala ndi chuma. Kwenikweni, chuma nthaŵi zambiri chimawonjezera zopsinja ndi nkhaŵa za moyo. “Kukhuta kwa wolemera sikum’gonetsa tulo,” amatero Mlaliki 5:12.

Choncho ganizirani bwinobwino za zinthu zimene muli nazo, ndiye mudzifunse nokha kuti, ‘Kodi chinthu ichi n’chofunikadi, kapena chosafunika kwenikweni? Kodi chimawonjezera ubwino wa moyo wanga, kapena chimawononga nthaŵi yofunika?’ Mawu otsegulira a buku lakuti Why Am I So Tired? (N’chifukwa Chiyani Ndili Wotopa Chonchi?), lolembedwa ndi Leonie McMahon, anati: “Zipangizo zosiyanasiyana zimene azipanga kuti apeputse ntchito zapanyumba zachititsa akazi okwatiwa kusiya ntchito yapanyumba n’kukaloŵa kwina kuti azitha kugula zinthuzo ndi kuzikonzetsa.”

Moyo wanu utakhala wosafuna zambiri, mumakhala ndi nthaŵi yambiri yocheza ndi achibale ndi anzanu. Inunso mumakhala ndi nthaŵi yochuluka yochita zimene mukufuna. Mumafunika nthaŵi imeneyo kuti musangalale. Musakhale ngati anthu amene amazindikira mochedwa kuti mabwenzi ndi achibale ndiwo ofunika kwambiri m’moyo komanso osangalatsa kuposa ndalama ndi zinthu. Ndi anthu okha amene angakukondeni. Mabuku a kubanki, kukhala ndi zigawo m’makampani, makompyuta, mawailesi akanema, ndi zipangizo zina zamagetsi, ngakhale zili ndi ntchito yake, n’zosafunika kwenikweni pamoyo wa munthu. Amene amaika zinthu ngati zimenezi poyamba amapeputsa miyoyo yawo ndipo potsirizira pake amakhala osakhutira mwinanso osakondwa.—1 Timoteo 6:6-10.

Gwiritsani Ntchito Nthaŵi Bwino ndi Kuika Zofunika Poyamba

Pa zinthu zina kugwiritsa ntchito nthaŵi bwino kuli ngati kukonza bajeti. Ngati muyesa kuchita zinthu zambiri pa maola ochepa amene muli nawo, simukugwiritsa ntchito nthaŵi yanu bwino. Mosakayikira, moyo woterowo umakhumudwitsa, kupsinja maganizo, ndiponso kutopetsa. Choncho muzidziŵa kuika zofunika poyamba.

Poyamba, onani zimene zili zofunika kwambiri, ndipo ikani nthaŵi yokwanira pa zimenezi. Nthaŵi zonse zinthu zauzimu zimakhala zoyambirira kwa Akristu. (Mateyu 6:31-34) Ngati muchita zinthu zofunika mothamanga kapena mwapatalipatali, nthaŵi zambiri pamatsatira mavuto aakulu. Choncho, mungafunike kuchotsa zina zonse zimene zimawononga nthaŵi koma zili zosapindulitsa kwenikweni.

Poika zofunika poyamba, kumbukiraninso kuti mumafunika nthaŵi yokhala panokha ya kusinkhasinkha kwaphindu ndi kupezanso mphamvu. Magazini ya Psychology Today ikuti: “Nthaŵi yaphindu yokhala panokha ndi yofunika komanso yotsitsimula m’dziko la masiku ano lotangwanitsali. . . . Nthaŵi yanu yokhala panokha imachirikiza moyo.” Anthu amene sapeza nthaŵi yosinkhasinkha angakhale ndi malingaliro opeputsa moyo.

Kudzichepetsa Ndiponso Mkhalidwe Wauzimu

Kudzichepetsa ndiponso mkhalidwe wauzimu ndi zinthu ziŵiri zabwino kwambiri zimene mungakhale nazo ngati mukufuna kukhala ndi moyo wabwino ndi wachimwemwe. Kudzichepetsa n’kofunika chifukwa kumakuthandizani kusalandira ntchito zina zambiri ndi maudindo. Ngati muli wodzichepetsa, mutha kudziŵa nthaŵi yokana ntchito ya ovataimu kapena zochita zina zimene zingasokoneze zinthu zofunika kwambiri. Anthu odzichepetsa sasirira zimene ena ali nazo ndi zimene amachita; choncho, amakhala okhutira kwambiri. Ndipotu, kudzichepetsa kwenikweni ndi mkhalidwe wauzimu. Ndi mbali inanso yofunika kwambiri kuti moyo wathu ukhale wolamulirika.—Mika 6:8; 1 Yohane 2:15-17.

Mkhalidwe wauzimu wozikidwa pa chidziŵitso cholondola cha Baibulo umakuthandizani kukhala munthu wozindikira kwambiri ndi woona patali—munthu amene sanyengeka ndi njira zopanda pake zimene dzikoli limafotokozera kupambana. Labadirani malangizo anzeru aŵa a pa 1 Akorinto 7:31: “Iwo akuchita nalo dziko lapansi, [akhale] monga ngati osachititsa; pakuti maonekedwe a dziko ili apita.” Akristu “akuchita nalo dziko lapansi” podzipezera zofunika pa moyo wawo ndi mabanja awo, koma salola dzikoli kuwapanikiza. Amadziŵa kuti silipereka chitetezo chenicheni, ndi kuti posachedwapa lidzawonongedwa, ndiponso kuti kupambana kwenikweni—chitetezo ndi moyo wosatha padziko lapansi laparadaiso—zimadalira mbiri imene munthu ali nayo kwa Mulungu. (Salmo 1:1-3; 37:11, 29) Choncho mverani chenjezo la Yesu, ndipo chitani mwanzeru mwa kukundika “chuma m’Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba.”—Mateyu 6:20.

Peŵani Nkhaŵa Ndipo Pezani Mtendere Weniweni

Pamene dongosolo ili likutha, mosakayika kupsinjika maganizo ndi zofuna nthaŵi yanu zidzachuluka. Ndiye n’kofunikatu kuti mumvere uphungu wa m’Baibulo wakuti: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” Mtendere woterowo sangaupeze wina aliyense wokonda za m’dziko amene saona kufunika kwake kwa pemphero.—Afilipi 4:6, 7.

Koma Yehova adzakuchitirani zambiri kuwonjeza pokupatsani mtendere wa maganizo. Adzakuthandizani kunyamula katundu wanu waudindo masiku onse ngati ‘mutaya pa Iye nkhaŵa yanu yonse.’ (1 Petro 5:7; Salmo 68:19) Choncho n’kwanzeru kumvera Mulungu tsiku ndi tsiku mwa kuŵerenga mbali ina ya Mawu ake. Ndaninso wina amene angathe kukupatsani malangizo abwino kuposa Mlengi wanu? (Salmo 119:99, 100, 105) Inde, zochitika zasonyeza kuti kwa awo amene Mulungu ali wofunika kwambiri athandizidwa kwambiri kupirira mosangalala m’dziko lotangwanitsali la masiku ano.—Miyambo 1:33; 3:5, 6.

[Mawu Otsindika patsamba 23]

Ikani zinthu zofunika poyamba, kuphatikizapo nthaŵi yanu yofunika yokhala panokha ndi mkhalidwe wauzimu

[Chithunzi patsamba 21]

Kodi moyo wanu ungakhale wosalira zambiri ndiponso wadongosolo?

[Chithunzi patsamba 22]

Kodi mumaona zinthu kukhala zofunika kuposa anthu?