Kusokonezeka Maganizo
Kusokonezeka Maganizo
“ATANDIUZA kuti ndili ndi matenda oopsa, ndinayesa kudzilimbitsa mtima, koma ndinafooka kwambiri posadziŵa chomwe chindichitikire,” anakumbukira motero munthu wina wachikulire. Mawu ake akugogomezera mfundo yakuti matenda akagwira thupi, amasokonezanso maganizo. Ngakhale zili choncho pali anthu amene akuthana nawo bwino lomwe mavuto oterewo. Ambiri a iwo angafune kukutsimikizirani kuti njira zothandiza zolimbana ndi matenda aakulu zilipo. Koma tisanayambe kulongosola zimene mungachite, tiyeni tiyambe taona mofatsa mavuto ena a m’maganizo amene mungakhale nawo poyambirira.
Kusamvetsa, Kukana, Kusasangalala
Mavuto anu a m’maganizo angasiyane kwambiri ndi a ena. Komabe, akatswiri a zaumoyo ndiponso odwala ena anenapo kuti anthu odwala kwambiri nthaŵi zambiri amakhala ndi mavuto ofala osiyanasiyana a m’maganizo. Poyamba amakhumudwa ndiponso samvetsa kuti zili choncho ndipo kenaka amakana kuti zawachitikira ponena kuti: ‘Si zoona zimenezi.’ ‘Alakwitsa basi.’ ‘Mwina asokoneza zimene apeza atandiyeza ndi za munthu wina.’ Mayi wina ananena mawu awa polongosola mmene anamvera atam’peza ndi matenda a kansa: “Umalakalaka utangodzifunditsa zofunda mpaka kumutu, ndiye ukadzivundukula ungozindikira kuti basi wachira.”
Komabe, mukayamba kuona kuti n’zoonadi, mumayamba kusoŵa mtendere, ndiko kuti mumakhala osasangalala ngati kuti china chake choopsa chichitika nthaŵi ina iliyonse. ‘Kodi ndikhala ndi moyo mpaka liti?’ ‘Kodi ndizingovutika ndi ululu kwa moyo wanga wonse?’ ndiponso mafunso ena ngati ameneŵa angakuvutitseni maganizo. Mungalakelake mutabwerera m’masiku am’mbuyo asanakupezeni ndi matendawo, koma simungathe. Mosachedwa mungangozindikira kuti mwathedwa nzeru chifukwa cha mavuto enanso a m’maganizo opweteka ndiponso osautsa. Kodi ena mwa iwo ndi ati?
Kukayika, Nkhaŵa, Mantha
Matenda aakulu amakuchititsani kukayikira ndiponso kudera nkhaŵa kwambiri moyo wanu. “Chifukwa chakuti matenda anga amasinthasintha nthaŵi zina ndimakhumudwa kwambiri ndi moyo,” anatero bambo wina wodwala matenda otchedwa Parkinson. “Tsiku lililonse sindidziŵa kuti kaya kugwa zotani.” Matenda anu angathenso kukuchititsani mantha. Ngati anangokuyambani mwadzidzidzi, mungagwidwe nthumanzi kwambiri. Koma ngati matendawo awapeza mutavutika kwa zaka zambiri asakudziŵika, mwina mantha ake angakule mwapang’onopang’ono zedi. Poyamba, mwinanso mungakhazike mtima pansi poganiza kuti tsopano anthu adzakhulupirira kuti mukudwaladi osati mukungonamizira. Komabe, posapita nthaŵi, mungayambenso kuda nkhaŵa poganizira zotsatira zake za matendawo.
Chingakudandaulitseninso ndicho mantha akuti simungathenso kudziyang’anira nokha.
Makamaka ngati mumakonda kukhala panokha, mungaipidwe kwambiri mukamaganiza kuti muyamba kudalira kwambiri anthu ena. Mungadandaule kuti matenda anu akuyamba kulamulira moyo wanu ndiponso chilichonse chimene mumachita.Ukali, Manyazi, Kusukidwa
Kuzindikira kuti simungaimenso panokha kungakuchititseninso ukali. Mungadzifunse kuti, ‘n’chifukwa chiyani matendawa agwira ineyo? N’dalakwa chiyani ine kuti nditere?’ Simungamvetse ndiponso mungadandaule kwambiri ndi matenda osautsawa. Manyazi ndiponso kutaya mtima zingakuthetseni nzeru. Munthu wina wofa ziwalo anakumbukira kuti: “Ndinachita manyazi kwambiri poganiza kuti chinandichititsa zonsezi ndi ngozi yachabechabe!”
Tsopano mungakakamizike kukhala nokha. Mukamakhala nokha m’posavuta kuti musiye kuyanjana ndi ena. Ngati matenda anu amakukhazikani panyumba, simungathenso kuchezerana ndi anzanu. Komatu, nthaŵi imeneyi m’pamene mumafuna kwambiri kukhala ndi anthu. Poyamba odzakuzondani ndiponso mafoni sati afika liti, koma kenaka amayamba kuchepa.
Popeza kuti zimawawa kuona anzako akukutaya, mwina zoterezi zitakuchitikirani munangodzipatula. N’zoona kuti payenera kukhala nthaŵi yopumula kaye musanakumane ndi anthu ena. Koma mukangolola pa nthaŵi imeneyi kuti mudzipatuliretu kwa anthu ena, mungachoke m’vuto losayanjidwa ndi ena (pamene anthu sakudzakuonani) n’kuloŵa m’vuto losafuna kuyanjidwa (pamene inuyo simukufuna kuonana ndi anthu). Mulimonsemo, mungavutikebe kwambiri chifukwa cha kusukidwa. * Nthaŵi zina, mungathenso kukayika zoti tsiku lotsatira lingadzaloŵe mudakali moyo.
Kuphunzirira pa Ena
Komabe, pali chiyembekezo. Ngati posachedwapa munadwalapo nthenda yaikulu, pali njira zokuthandizani zimene mungachite kuti muthe kumadzidalirako ndithu.
N’zoona kuti nkhani zotsatizana zino sizikuthetserani matenda anu aakulu, alionsewo. Koma mfundo zimene zalembedwamo zingakuthandizeni kupeza njira zokuthandizani kuthana nawo. Mayi wina wodwala matenda a kansa analongosola mmene ankamvera m’maganizo ake motere: “Nditatsimikizira zakuti ndikudwaladi ndinakwiya kwambiri kenaka ndinayamba kufunafuna thandizo.” Inunso mungafunefune thandizo mwa kupeza anthu amene anadwalapo inu musanadwale ndi kuphunzira kwa iwo mmene mungathandizikire ndi zinthu zimene mungathe kupeza.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 12 N’zoona kuti anthu ambiri amakumana ndi mavuto osiyanasiyana ameneŵa kumlingo wosiyanasiyana ndiponso mwanjira zosiyanasiyana.
[Mawu Otsindika patsamba 5]
Mungadzifunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani matendawa agwira ine? N’dalakwa chiyani ine kuti nditere?’