Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kutangwanitsa kwa Dzikoli

Kutangwanitsa kwa Dzikoli

Kutangwanitsa kwa Dzikoli

KODI MMENE MOYO UKUYENDERA ZIMAKUTHETSANI MPHAMVU NTHAŴI ZINA? KODI ZIMAKUKWIYITSANI, KUKUTOPETSANI, MOTI MUMALEPHERERATU KUTHANA NAZO? NGATI ZILI CHONCHO, SIMULI NOKHA.

KWA anthu ambiri, makamaka m’mizinda, moyo ndi wotangwanitsa kwambiri moti umawasokoneza mutu ndi kuwatopetsa. Izi zili choncho makamaka kumayiko a Azungu. Pamsonkhano wa zachipembedzo posachedwapa ku United States, wolankhula anafunsa anthu amene analipo kuti akweze manja awo ngati amakhala otopa nthaŵi zambiri. Nthaŵi yomweyo, ambiri anakweza manja awo m’mwamba.

Buku lakuti Why Am I So Tired? (N’chifukwa Chiyani Ndili Wotopa Chonchi?) limati: “Moyo wamakono uli ndi zopsinja zambirimbiri zomwe kale kunalibe—ndege zofuna kukwera panthaŵi yake, ntchito zofuna kumaliza panthaŵi yake, kutenga ana kupita nawo kusukulu ya mkaka ndi kubwerera nawo panthaŵi yake—mndandanda wake ndi wosatha.” N’zosadabwitsa kuti amati m’zaka zinozi kutopa kumayambitsa mavuto osatha. *

Kale, moyo unali wosavuta ndipo wosatangwanitsa. Anthu mochulukira amakhala mogwirizana ndi chilengedwe—usana unali wogwira ntchito ndipo usiku unali wokhala ndi banja lako ndi kugona. Masiku ano, pali zifukwa zambirimbiri zimene anthu amakhalira otopa ndi olema kwambiri.

Mwadzidzidzi, Usana Utalikirapo

Chifukwa china chingakhale chakuti anthu amagona pang’ono. Ndipo chitukuko chodziŵika kwambiri chimene chinaloŵerera nthaŵi yogona n’kufika kwa kuunika kwa magetsi. Mwa kungoyatsa magetsi, anthu anayamba kutha kuwonjezera utali wa “usana,” ndipo posakhalitsa anayamba kuchedwa kugona. Ndithudi, ambiri analibe chochita pankhani imeneyi chifukwa chakuti mafakitale anayamba kugwira ntchito usana ndi usiku ndipo makampani anawonjezera maola awo. Wolemba wina anati: “Chipani chogwira ntchito maola 24 chinabadwa.”

Zinthu zina zaumisiri zotsogola, ngati wailesi, wailesi yakanema, ndi kompyuta, zachititsanso anthu kulephera kugona panthaŵi yofunika. M’mayiko ambiri, mapulogalamu a pawailesi yakanema amagwira ntchito maola 24 patsiku. Si zachilendo kwa okonda mafilimu kapena maseŵera kupezeka kuti tulo tikuwagwira kuntchito ndipo ali otopa ataonerera kanema usiku kwa nthaŵi yaitali. Nazonso zinthu zosokoneza mutu zimene makompyuta akunyumba ali nazo, zimapusitsa mamiliyoni kuti agone mochedwa. N’zoonadi kuti zinthu zimenezi pazokha zilibe vuto; komabe zimasonkhezera anthu ena kunyalanyaza kufunika kopuma.

Moyo Ukuthamanga

Si usana wokha umene watalikirapo, moyonso ukuoneka kukhala wofulumira—ndipo zaumisiri n’zimene zachititsa zimenezi. Ngolo yokoka ndi mahatchi imene inkagwira ntchito zaka zosafika 100 zapitazo n’njosiyaniratu ndi magalimoto aliŵiro a masiku ano, sitima zapamtunda zaliŵiro, komanso ndege zaliŵiro. Inde, munthu wamalonda wamakono, mwina amene agogo ake anayendako kuntchito wapansi kapena pahatchi kapenanso panjinga, angathe kuuluka pandege kuwoloka nyanja ya Atlantic atadya chakudya cha masana ndi kukadyera cha madzulo tsidya linalo!

Nayonso ofesi yasinthiratu mwakachetechete kuti ntchito izigwirika mofulumira ndi kuti azipanga zinthu zambiri. Makompyuta, makina otumizira uthenga a fax, ndi mauthenga a pakompyuta zatenga malo a mataipilaitala ndi makalata. Makompyuta aang’onoang’ono, mafoni a mmanja, ndi zipangizo zina zamagetsi zachititsa kunyumba kungokhala ngati kuofesi komwe.

Inde, palibe aliyense angachepetse liŵiro la mmene dziko likuyendera. Komabe, tonse tingasinthe kukhala ndi moyo wabata ndithu ndiponso wapakati m’pakati. Koma tisanakambirane nkhani imeneyi, tiyeni tione zotsatira zake zina zimene moyo wotangwanitsa wa masiku ano ungakhale nazo pa ifeyo ndi anthu ena onse.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Kutopa kwa nthaŵi yaitali kungayambe kapena kukula ndi zinthu zingapo kuwonjezanso zopsinja za tsiku ndi tsiku. Kungayambe chifukwa chodwala, zakudya zopereŵera, mankhwala osokoneza bongo, kuipitsa dziko ndi makemikolo, kuvutika maganizo ndi mtima, ukalamba, kapena chifukwa cha zonse zimenezi.