Mukadwala Kwambiri
Mukadwala Kwambiri
“Zinandisokoneza maganizo kwabasi.”Anatero John atadziŵa kuti ali ndi matenda oopsa.
“Ndinagwidwa nthumanzi.”Anatero Beth atazindikira kuti matenda ake afika podetsa nkhaŵa.
KUDZIŴA kuti muli ndi matenda aakulu ndiponso owononga thupi kapena kudziŵa kuti mupunduka chifukwa cha zilonda zimene munavulala pangozi ndi china cha zinthu zoŵaŵa kwambiri m’moyo. Kaya matendawo mwawadziŵira mu ofesi ya dokotala kuli zii kapena ngati mwazindikira kukula kwa vuto lanulo m’chipinda cha kungozi poona madokotala ali yakaliyakali, mungalephere kumvetsa. Si zinthu zambiri m’moyo zimene zimakukonzekeretsani kudzathana ndi chisoni chimene mumakhala nacho matenda oopsa akakusokonezani.
Pofuna kudziŵa zimene zingathandize anthu amene adwala kwambiri posachedwapa, atolankhani a Galamukani! analankhula ndi anthu ambiri m’mayiko osiyanasiyana amene kwa zaka zambiri athana nawo matenda aakulu owononga thupi. Anawafunsa kuti anenepo maganizo awo pamafunso onga akuti: Kodi zinakukhudzani bwanji? Kodi n’chiyani chinakuthandizani kupirira ndiponso kulimba mtima? Kodi munachita zinthu zotani kuti mukhaleko ndi mphamvu yochitanso zinthu bwino? Zimene anapeza pa kufufuzaku komanso mfundo zina zimene ofufuza zotsatira za matenda anthaŵi yaitali apeza tazilemba kuti zithandize anthu amene akusauka ndi matenda pakali pano. *
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 5 Nkhani ino talembera makamaka anthu odwala kapena olumala, koma nkhani zamutu wakuti “Nthenda Yaikulu” (Galamukani! ya June 8, 2000) zinali ndi chidziŵitso chokhudza makamaka anthu amene akusamalira odwalawo.