Ndi Motani Mmene Mungakhalire Osangalala Ngakhale Mukudwala?
Ndi Motani Mmene Mungakhalire Osangalala Ngakhale Mukudwala?
DZIŴANI ndithu kuti n’kwachibadwa ndiponso n’koyenera kuvutika m’maganizo choncho. Ngakhale kuti mwina vuto lanu n’lokhudza kulemala kwathupi, maganizo anu amakana zoti musinthe mogwirizana ndi matendawo. Zingaoneke ngati kuti muli pampikisano wokokerana chinthu ndi matenda anuwo; inu mukufuna kuti mukhale monga poyamba, matenda akufuna kuti musinthiretu. Ndipo pakali pano mungaone ngati kuti matendawo ndiwo akupambana. Komabe, zinthu zingathe kusintha? Zingasinthe bwanji?
“Munthu akawonongeka thupi chifukwa cha matenda aakulu amangoona ngati wafa kale,” anatero Dr. Kitty Stein. Motero, ngati simungathenso kukhala athanzi monga mmene mumafunira, n’kwachibadwa kukhala ndi nthaŵi yodandaula ndi kulira, monga mmene mungachitire munthu amene mumakonda atamwalira. Kwenikweni, si thanzi lokha limene lingakhale litawonongeka. Mayi wina analongosola kuti, “Ndinakakamizika kusiya ntchito yanga. . . . Sindinathenso kudziyang’anira ndekha monga ndinkachitira kalelonse.” Ngakhale zitakhala choncho, musaganize kuti palibenso chanu. “Muyenera kudandaula chifukwa cha zimene simungathenso kuchita, koma muyeneranso kuzindikira zinthu zimene mungathebe kuchita,” anatero Dr. Stein, amenenso akudwala matenda okhudza ubongo otchedwa multiple Sclerosis. Zoonadi, mukathana ndi mavuto oyamba, mudzaona kuti zilipobe zinthu zofunika zimene mungathe kuchita. Chachikulu, n’chakuti mungathe kusintha.
Woyendetsa chombo sangathe kuthetsa namondwe, koma angathe kulimbana naye posintha mathanga a chombo chake mogwirizana ndi kumene kukuloŵera mphepo. N’chimodzimodzinso inuyo, mwina simungathe kuthetsa matenda amene angokupezeketsani monga namondwe, koma mungathane nawo posintha “mathanga” anu, amene ali mphamvu zanu, nzeru zanu, ndiponso maganizo anu. N’chiyani chimene chathandiza anthu ena odwala matenda aakulu kuchita zimenezo?
Phunzirani za Matenda Anuwo
Anthu ambiri akaiŵala madandaulo amene anali nawo poyamba atangowapeza ndi matenda, amaona kuti kudziŵa zoonadi kumawawa, koma ndi bwinobe kusiyana ndi kumangoopa matenda osawadziŵa. Kuchita mantha kungakulepheretseni kuchitapo kanthu koma kudziŵa zimene zikukuchitikirani kungakuthandizeni kuganizira zimene mungachite, ndipo kutero pakokha n’kothandiza. “Taonani mmene mumamvera bwino mukapeza njira yothana ndi chilichonse chimene chimakudandaulitsani,” anatero Dr. David Spiegel wa ku yunivesite ya Stanford. “Mukakonzeka kwa nthaŵi yaitali musanachite chilichonse, mumachepetsa mavuto anu mwa kulinganiza zochita.”
Mungaone kuti n’kofunika kudziŵa bwino matenda anuwo. Paja mwambi wina wa m’Baibulo umati “munthu wodziŵa ankabe nalimba.” (Miyambo 24:5) Wodwala wina amene amangokhala chigonere analangiza kuti, “Muzikabwereka mabuku ku laibulale. Dziŵani zonse zimene mungathe zokhudza matenda anuwo.” Mukadziŵa za mankhwala amene alipo ndiponso njira zothana ndi matendawo, mwina mungaone kuti matenda anuwo si odetsa nkhaŵa kwambiri monga munali kuwawopera. Mwina mpaka mungathe kupeza zifukwa zingapo zoziziritsira mtima.
Komabe, si kuti cholinga chanu chachikulu ndicho kumvetsa bwino matenda anuwo ayi. Dr. Spiegel analongosola kuti: “Kufufuza kumene mumachitaku n’kongofunika kuti muwazoloŵere matendawo, kuwamvetsa, ndiponso kudziŵa mmenedi akukukhudzirani.” Kuvomereza kuti tsopano moyo wanu wasintha koma sunathe n’kovuta ndipo nthaŵi zambiri kumatenga nthaŵi ndithu. Koma inuyo mukhoza kuchita zimenezi—pomvetsa matenda anuwo mpaka powavomereza mumtima mwanu. Kodi mungatero bwanji?
Kuona Zinthu Mosamala
Muyenera kusintha malingaliro anu patanthauzo la mawu akuti kuvomereza matenda anu. Ndipotu,
kuvomereza kuti mukudwaladi si kugonja ayi, monga mmenenso zingakhalire kwa woyendetsa chombo kuti si kugonja kuvomereza kuti wapezeketsedwa ndi namondwe. M’malo mwake, kuvomereza kuti akukanthidwa ndi namondwe kumam’pangitsa kuti achitepo kanthu. Moteronso, kuvomereza matenda anu si kugonja ayi, koma “n’kutulukira njira ina yatsopano,” monga mmene mayi wina wodwala matenda aakulu ananenera.Ngakhale mutafooka m’zochita zina, muyenera kudzikumbutsa kuti nzeru zanu, maganizo anu, ndiponso makhalidwe anu auzimu siziyenera kukhudzidwa kwenikweni. Mwachitsanzo, kodi mudakali ndi nzeru ndiponso mungathebe kulinganiza zinthu ndi kulingalirabe bwinobwino? Mwina mukuthabe kumwetulira mosangalatsa, kufuna kusamalira ena, ndiponso mukutha kumvetsera bwino ndi kukhala bwenzi lenileni. Ndipo chofunika kwambiri, n’chakuti mudakakhulupirirabe Mulungu.
Kuwonjezera apo, kumbukirani kuti ngakhale kuti simungasinthe mavuto anu onse, mungathebe kuona mmene mungachitire. Irene Pollin wa m’bungwe loona za matenda a kansa lotchedwa National Cancer Institute ananena kuti: “Muli ndi udindo woyang’anira mmene matenda anuwo akukukhudzirani. Muli ndi mphamvu zimenezi ngakhale matendawo atakuvutitsani motani.” Helen, yemwe ndi mayi wazaka 70 amene matenda ake a multiple sclerosis okhudza ubongo afika poipa, anatsimikizira zimenezi mwakunena kuti: “Kuti maganizo anu akhazikikenso si zidalira mtundu wa matenda amene mukudwala koma mmene matendawo akukukhudzirani. Mwamuna wina amene wapirira kulumala kwake kwa zaka zoposa makumi awiri ananena kuti: “Maganizo abwino ali ngati chida chothandizira bwato kuti lisapendame.” N’zoonadi, Miyambo 18:14 amanena kuti: “Mtima wa munthu um’limbitsa alikudwala; koma ndani angatukule mtima wosweka?”
Kukhazikikanso Maganizo
Maganizo anu akayambanso kukhazikika, mungasiye kumadzifunsa mafunso onga akuti ‘N’chifukwa chiyani zimenezi zinachitikira ine?’ n’kuyamba kudzifunsa kuti ‘Pakuti zandichitikira, kodi ndidzatani nazo?’ Zinthu zikafika potere mungafune kutsatira njira zinanso kuti mufike patali kuposa mmene zililimo. Tiyeni tione njira zingapo.
Dziŵani kuti mukupezako bwanji, ganizirani zochita zimene muyenera kusintha, ndipo sinthani zimene mungathe. “Nthaŵi imene mukudwala ndi nthaŵi yoti mupendenso moyo—n’kukugalamutsani osati pothera pa zonse,” anatero Dr. Spiegel. Dzifunseni kuti, ‘N’zinthu zotani zimene zinali zofunika kwa ine matenda anga asanayambe? Nanga zimenezi zasintha motani?’ Musadzifunse n’cholinga chofuna kudziŵa zinthu zimene simungathenso kuchita, koma kuti mudziŵe zimene mungathebe kuchita, mwina pochita zinthu mosiyana ndi poyamba. Mwachitsanzo, ganizani za Helen amene tam’tchula poyamba paja.
Kwa zaka 25 zapitazo, matenda a multiple sclerosis akhala akum’foola. Poyamba ankayendera ndodo za olumala. M’kupita kwa Mateyu 28:19, 20) Helen akulongosola mmene amachitira zimenezi:
nthaŵi, dzanja lake lamanja linafa ndipo anayamba kugwiritsa ntchito lamanzere. Kenaka lamanzere lija linafanso. Ndiyeno zaka zisanu ndi zitatu zapitazo, anafa miyendo. Pakali pano amachita kusambitsidwa, kudyetsedwa, ndiponso kuvekedwa. Zimenezi zimam’dandaulitsa, koma ngakhale zili choncho, iye amati: “Mfundo yanga ndi yomweyobe yakuti, ‘Ganizira zimene ungathe kuchita osati zimene unkatha kuchita.’” Ndipo mothandizidwa ndi mwamuna wake ndi anamwino odzamuzonda ndiponso kuganiza kwake kwaluntha, amathabe kuchita zinthu zina zimene wakhala akusangalala nazo nthaŵi zonse. Mwachitsanzo, mbali yofunika ya moyo wake kuyambira ali ndi zaka 11 ndiyo kuuza ena lonjezo la m’Baibulo la dziko lamtendere limene likubwera, ndipo masiku ano amachitabe zimenezi mlungu uliwonse. (“Ndimafunsa namwino amene wabwera kudzandizonda kuti andigwirizire nyuzipepala. Akatero timaŵerengera limodzi pamene pakunena za anthu amene amwalira n’kusankhanso nkhani zina. Kenaka ndimamuuza namwinoyo mfundo zimene ndikufuna kulemba m’kalata yopita kwa abale a munthu womwalirayo, ndipo namwinoyo amataipa kalatayo. Ndimatumiza kalatayo pamodzi ndi bulosha ya Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, * imene imalongosola chiyembekezo cha m’Baibulo chotonthoza chachiukiriro. Ndimachita zimenezi Lamlungu lililonse madzulo. Zimandisangalatsa kuti ndikuthabe kuuza ena uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.”
Khalani ndi zolinga zabwino komanso zotheka kuchita. Chifukwa chimodzi chimene Helen amayesetsera kusintha zochita zimene angathe n’chakuti akatero zimam’thandiza kukonza ndiponso kukwaniritsa zolinga. Zimenezi n’zofunikanso kwa inu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti kukhala ndi cholinga kumapititsa maganizo m’tsogolo, ndipo kukwaniritsa zolinga kumakukhutiritsani. Kungathenso kukuchititsani kuyambanso kudzidalira. Komabe, onetsetsani kuti cholinga chimene mwakonza n’chotsimikizika. Mwachitsanzo, mungakhale n’cholinga chakuti: ‘Lero ndiŵerenga chaputala chimodzi cha m’Baibulo.’ Ndiponso khalani ndi zolinga zimene mungathe kukwaniritsa. Pakuti thupi lanu ndiponso maganizo anu n’ngosiyana ndi a anthu ena odwalanso matenda aakulu, mwina simungathe kuchita zolinga zimene iwo angathe kuchita.—Agalatiya 6:4.
“Ngakhale kuti cholinga chanu chikuoneka kuti n’chaching’ono bwanji, mukachikwaniritsa zimakulimbikitsani
kuti mupose pamenepo,” anatero Lex, amene akukhala ku Netherlands. Zaka zopitirira 20 zapitazo, ali ndi zaka 23, iye anachita ngozi imene inachititsa kuti ziwalo zake zife. M’kati mwa nthaŵi zambiri zimene anali kulandira chithandizo, anam’limbikitsa kuti akhale ndi zolinga, monga kusukusula nkhope yake ndi thaulo. Zinali zotopetsa, koma anakwanitsa. Atazindikira kuti wakwanitsa cholinga chimenecho anapanga cholinga china ndipo chinali chakuti azitsegula ndiponso kutseka yekha mankhwala otsukira mano. Cholinga ichinso anachikwanitsa. Lex ananena kuti: “Ngakhale kuti sizinali zophweka, ndinazindikira kuti ndingathe kuchita zinthu zambiri zimene ndinkaona ngati sindingathe.”Indedi, mothandizidwa ndi mkazi wake, Lex anakwanitsa zolinga zazikulu kuposa apa. Mwachitsanzo, motsagana ndi Tineke, tsopano iye amatha kuyenda khomo ndi khomo panjinga ya olumala kuti auze ena chidziŵitso cha m’Baibulo. Ndiponso sabata iliyonse amayendera munthu wina wolumala kwambiri amene akuchita naye phunziro la Baibulo kukamulimbikitsa. Lex anati: “Kuthandiza ena kumandikhutiritsa kwambiri.” Baibulo limatsimikizira zimenezi ponena kuti, “kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.
Kodi inunso mungathe kukhala ndi cholinga chothandiza ena? Matenda kapena kulemala zingakuthandizeni kukhala munthu wotonthoza kwambiri chifukwa chakuti mavuto anuwo amakuchititsani kuganizira kwambiri anthu ena akamamva ululu.
Gwirizananibe ndi anthu ena. Kufufuza kwa a zachipatala kumasonyeza kuti mukamagwirizana ndi anthu mumakhala athanzi. Koma mukapanda kutero ndiye kuti zathanzi iwalani. Wofufuza wina ananena kuti: “Kudzipatula pakati pa anthu kumapha . . . monga mmene kusuta fodya kumachitira . . . ” Anawonjezera kuti: “Motero kugwirizana ndi ena n’kofunika kuti mukhale athanzi monga mmene mungakhalirenso athanzi mukasiya kusuta fodya.” N’zosadabwitsa kuti akutchula mfundo yakuti maluso athu otitheketsa kukhala bwino ndi anzathu “n’ngofunika kuti tichire”!—Miyambo 18:1.
Komabe, muja tanenera m’nkhani yam’mbuyo ija, vuto lanu lingakhale lakuti anzanu ena anasiya kukuyenderani. Kuti zinthu zikuyendereni bwino, muyenera kuchepetsa kudzipatula kwambiri. Koma kodi mungatero motani? Mungayambe mwa kuitana anzanu kuti adzakuchezereni.
Pangitsani kuti kukuchezerani kuzikhala kosangalatsa. * Mungatero posachulukitsa nkhani zokhudza matenda anuwo kuti alendo anu asachite kutopa nazo. Mayi wina wodwala matenda aakulu anathetsa vuto limeneli poika malire a nthaŵi yokambirana za matenda ake ndi mwamuna wake. Iye ananena kuti, “Tinayenera kuchepetsa nkhani zimenezi basi.” N’zoona, sikuti matenda anuwa ayenera kukulepheretsani kuchita chilichonse chimene mungachite ndi ena. Wodwazika matenda wina atatha kukambirana ndi mnzake wodwala amene amangokhala chigonere, nkhani zokhudza luso lamanja, mbiri yakale, ndiponso zifukwa zimene amakhulupirira Yehova Mulungu, ananena kuti: “Iyeyo sanalole kuti matenda ake amusinthe. Ndinasangalala kwambiri polankhula naye.”
Kukhalabe anthabwala kungachititsenso anzanu kusangalala n’kudzakuzondani. Ndiponsotu, kuseka kumakuthandizani inuyo panokha. Munthu wina wodwala matenda ofoola ziwalo otchedwa Parkinson’s anati, “Nthabwala zimakuthandizani kuti mupirire mukakhala m’mavuto osiyanasiyana ndiponso pothetsa mavuto osiyanasiyana.” N’zoonadi kuti kuseka ndi mankhwala othandiza. Miyambo 17:22 amanena kuti: “Mtima wosekerera uchiritsa bwino.” Ngakhale kungoseka kwa mphindi zochepa chabe kungakupindulitseni. Ndiponso, “mosiyana ndi mankhwala ena, kuseka n’kosaopsa ngakhale pang’ono, sikukhala ndi poizoni, ndiponso n’kosangalatsa,” anatero wolemba wina Susan Milstrey Wells, amenenso akudwala matenda aakulu. “Palibe chimene timataya kupatulapo kudandaula.”
Pezani njira zothetsera kuvutika maganizo. Kufufuza kwasonyeza kuti kuvutika maganizo kumawonjezera ululu wa matenda, koma kuthetsa kuvutika maganizo kumathandiza kuwachititsa kuti akhale osavuta kupiririka. Motero, nthaŵi ndi nthaŵi muziganizirako zinthu zina. (Mlaliki 3:1, 4) Musamangoganiza za matenda anuwo basi. Ngati mumangobindikira m’nyumba, mungayese kuziziritsa mtima wanu pomvetsera nyimbo zapansipansi, kuŵerenga buku, kukhala nthaŵi yaitali mukusamba, kulemba makalata kapena ndakatulo, kujambula zithunzi zapamanja, kuimba chida chinachake chanyimbo, kulankhulitsana ndi mnzanu wokhulupirika, kapena kutangwanika ndi zochita zina zotere. Kuteroko si kuti kungathetseretu vuto lanulo, koma kungakuziziritseni chabe mtima.
Ngati mungathe kuyenda, wongolaniko miyendo, pitani kokagula zinthu, samalirani dimba, yendetsani galimoto, kapena ngati n’kotheka pitani kutchuthi. N’zoona kuti kupita paulendo kungavute kwambiri chifukwa cha matenda anu, koma mwakukonzekereratu ndiponso kupeza njira zongogwirizira, mavuto angathe kuthetsedwa. Mwachitsanzo, Lex ndi Tineke, amene tawatchula poyamba aja, anakwanitsa kupita kunja kwa dziko lawo. Lex anati, “Poyamba tinali ndi mantha ndithu, koma tchuthi chimenechi tinasangalala nacho kwambiri! N’zoona kuti matenda anu angakhudze moyo wanu, koma si ndiye kuti ayambe kuulamulira.
Dzilimbitseni ndi chikhulupiriro. Akristu amene athana ndi matenda aakulu amanena kuti chikhulupiriro chawo mwa Yehova Mulungu ndiponso kugwirizana ndi mpingo wachikristu nthaŵi zonse kumawakhazika mtima pansi ndiponso kumawalimbikitsa. * Nazi ndemanga zawo zina zokhudza kufunika kwa pemphero, kuphunzira Baibulo, kusinkhasinkha zam’tsogolo, ndiponso kupita kumisonkhano yachikristu ku Nyumba ya Ufumu.
● “Nthaŵi zina ndimavutikabe maganizo. Zinthu zikatero, ndimapemphera kwa Yehova, ndipo iye amandilimbikitsa kuti ndipitirize kuchita zimene ndingathe.”—Salmo 55:22; Luka 11:13.
● “Kuŵerenga Baibulo ndiponso kusinkhasinkha zimene ndaŵerenga kumandithandiza kwambiri kuti ndikhazikitse pansi maganizo.”—Salmo 63:6; 77:11, 12.
● “Phunziro la Baibulo limandikumbutsa kuti moyo weniweni udakali m’tsogolo ndi kutinso si kuti ndidzakhala wolemala mpaka kalekale.”—Yesaya 35:5, 6; Chivumbulutso 21:3, 4.
● “Kukhala ndi chikhulupiriro cha m’tsogolo mmene Baibulo linalonjeza kumandipatsa mphamvu zakuti ndisamakhale ndi nkhaŵa ya tsiku lotsatira.”—Mateyu 6:33, 34; Aroma 12:12.
● “Kupezeka kumisonkhano ya ku Nyumba ya Ufumu kumandithandiza kuika maganizo anga onse pa zinthu zolimbikitsa osati pa matenda angawa.”—Salmo 26:12; 27:4.
● “Kuchezerana kolimbikitsa ndi ena mumpingo kumandisangalatsa.”—Machitidwe 28:15.
Baibulo limatitsimikizira kuti: “Yehova ali wabwino, ndiye polimbikirapo tsiku la msauko; ndipo Nahumu 1:7) Kukhala ndi ubwenzi wapamtima ndi Yehova Mulungu ndiponso kugwirizana ndi Mpingo wachikristu kumakhazikitsa mtima pansi ndiponso n’kolimbikitsa.—Aroma 1:11, 12; 2 Akorinto 1:3; 4:7.
adziŵa iwo om’khulupirira iye.” (Dzipatseni Nthaŵi
Kuti mukhalebe osangalala muli ndi matenda aakulu kapena mutalemala “kumatenga nthaŵi yaitali osati kamodzin’kamodzi,” anatero munthu wina wantchito yothandiza anthu kulimbana ndi mavuto obwera chifukwa cha matenda aakulu. Katswiri wina anati muyenera kudzipatsa nthaŵi chifukwa chakuti apa mukuphunzira “luso latsopano: la kulimbana ndi matenda aakulu.” Zindikirani kuti ngakhale mutakhala ndi maganizo abwino, masiku ena kapena milungu ina zinthu sizingayendebe bwino chifukwa cha matenda anuwo. Komabe, m’kupita kwanthaŵi, mungayambe kuona kuti nkhasankoni. Zimenezi n’zimene zinachitikira mayi wina amene ananena kuti: “Ndinasangalala kwambiri n’tazindikira kuti tsiku lathunthu latha ndisanaganizeko za matenda anga a kansa. . . . M’mbuyomu sindikadaganizako kuti zimenezi zingatheke.”
Indedi, mantha amene mumakhala nawo poyambirira aja akangotha ndipo mukangopanga zolinga zatsopano, mungadabwe kuona kuti mukutha ndithu kupirira—monga mmene nkhani yotsatirayi ikusonyezera.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 17 Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
^ ndime 24 Malingaliro ameneŵa okhudza mmene muyenera kukhalira ndi alendo, kwenikweni amagwiranso ntchito pokhala ndi amene munakwatirana naye, ana anu, kapena wokusamalirani.
^ ndime 28 N’zochititsa chidwi kuti kufufuza kosiyanasiyana kwa a zachipatala kwasonyeza kuti chikhulupiriro chimawonjezera thanzi ndiponso kusangalala. Malingana ndi zimene ananena Pulofesa Dale Matthews wa ku yunivesite ya zamankhwala yotchedwa Georgetown University School of Medicine, “pali umboni wakuti chikhulupiriro chimathandiza.”
[Chithunzi patsamba 7]
Kuwaphunzira matenda anuwo kungakuthandizeni kuti mulimbane nawo
[Chithunzi patsamba 8]
Mothandizidwa ndi anthu ena, Helen akulemba makalata olimbikitsa
[Chithunzi patsamba 8]
“Zimandisangalatsa ndikamauza ena uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu”
[Chithunzi patsamba 9]
“Ndinazindikira kuti ngakhale ndili wakufa ziwalo, ndingathebe kuchita zinthu zambiri zimene ndinkaona ngati sindingathe,” anatero Lex