Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Akristu Ayenera Kupita ku Tchalitchi?

Kodi Akristu Ayenera Kupita ku Tchalitchi?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Akristu Ayenera Kupita ku Tchalitchi?

“NDINKAKONDA kupita kutchalitchi, koma ndinasiya.” “Ndimaona kuti n’zotheka kulambira Mulungu paliponse, osati kutchalitchi kokha.” “Ndimakhulupirira Mulungu ndi Baibulo, koma sindiona kuti kupita kutchalitchi n’kofunika.” Kodi munamvapo mawu ngati ameneŵa? Anthu ambiri, masiku ano amatero, makamaka m’mayiko a Azungu. Amene poyamba ankapita kutchalitchi saonanso kuti n’kofunika kutero. Kodi Baibulo limanenapo chiyani pankhani yopita kutchalitchi?

Mawu akuti “tchalitchi” ndiponso “matchalitchi” amapezeka koposa ka 110 mu Baibulo la King James Version. Mabaibulo enanso amagwiritsa ntchito mawu ameneŵa. Mawu achigiriki amene amawatembenuza kuti “tchalitchi” tanthauzo lake lenileni ndi “kuitana,” kapena, tingati msonkhano. Mwachitsanzo, pa Machitidwe 7:38, mu Baibulo la King James Version, amanena za Mose kuti anali “m’tchalitchi kuchipululu,” kapena kuti, pakati pa mtundu wosonkhana wa Israyeli. Pankhani ina, Malemba amanena kuti “anayamba kuzunza tchalitchi kwambiri,” kutanthauza Akristu a ku Yerusalemu. (Machitidwe 8:1, The Jerusalem Bible) M’kalata yake ina, Paulo anapereka moni “kwa tchalitchi cha m’nyumba mwa [Filemoni],” kutanthauza mpingo umene unkakumana m’nyumbayo.—Filemoni 2, Revised Standard Version.

N’zoonekeratu kuti mawu akuti “tchalitchi” m’Baibulo satanthauza malo olambiriramo koma gulu la anthu olambira. Pozindikira zimenezi, mphunzitsi wina wa zachipembedzo wa m’zaka za zana lachiŵiri, dzina lake Clement wa ku Alexandria, analemba kuti: “Mpingo wa anthu osankhidwa ndiwo ndimautcha kuti Tchalitchi osati malo ayi.” Komabe, kodi Akristu ayenera kupezeka pa malo kapena nyumba inayake kuti Mulungu aziwamvera akamamulambira?

Mmene Mtundu wa Israyeli Unkalambirira

Chilamulo cha Mose chinkati amuna onse achiyuda ayenera kupezeka pamalo enaake kukachita mapwando atatu apachaka. Amayi ndiponso ana ambiri analinso kupezekapo. (Deuteronomo 16:16; Luka 2:41-44) Pazochitika zina ansembe ndi Alevi ankaphunzitsa makamu a anthu osonkhana, poŵerenga Chilamulo cha Mulungu. ‘Ankachiŵerenga momveka, natanthauzira nawazindikiritsa choŵerengedwacho.’ (Nehemiya 8:8) Pa zaka zasabata, lamulo la Mulungu linati: “Sonkhanitsani anthu, amuna ndi akazi ndi ana aang’ono, ndi mlendo wokhala m’midzi mwanu, kuti amve, ndi kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, ndi kusamalira kuchita mawu onse a chilamulo ichi.”—Deuteronomo 31:12.

Ndi kukachisi kokha ku Yerusalemu kumene munthu akanatha kupereka nsembe kwa Mulungu ndi kulangizidwa ndi ansembe. (Deuteronomo 12:5-7; 2 Mbiri 7:12) M’kupita kwa nthaŵi anakhazikitsa nyumba zina zolambirira ku Israyeli, ndizo masunagoge. Aŵa anali malo oŵerengera Malemba ndiponso opempherera. Komabe, kachisi wa ku Yerusalemu ndiye anali malo ofunika kwambiri olambirira. Zimene wolemba Baibulo Luka anasimba zikusonyeza mfundo imeneyi. Iye ananena kuti panali mayi wina wachikulire dzina lake Anna, amene “sanachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.” (Luka 2:36, 37) Chofunika kwambiri kwa Anna chinali kulambira koona pamodzi ndi anthu ena odzipereka. Ayuda ena oopa Mulungu anachita zomwezi.

Kulambira Koona Kristu Atafa

Yesu atafa otsatira ake anasiya kutsata Chilamulo cha Mose ndiponso sanafunikirenso kukalambirira m’kachisi. (Agalatiya 3:23-25) Komabe, anapitiriza kukumana kuti azipemphera ndi kuphunzira Mawu a Mulungu. Analibe nyumba zambambande, m’malo mwake ankagwiritsa ntchito nyumba za anthu ndiponso malo ogwiritsidwa ntchito ndi aliyense. (Machitidwe 2:1, 2; 12:12; 19:9; Aroma 16:4, 5) Misonkhano yachikristu ya m’zaka za zana loyamba imeneyi inalibe zamiyambo kapena kudzionetsera, motero inali yabwinobwino.

Mu ufumu wa Roma, makhalidwe anaipa kwambiri mwakuti mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo zinalidi zapadera zedi. Osakhulupirira ena akapita ku misonkhano nthaŵi yoyamba sankalephera kunena kuti: “Mulungu ali ndithu mwa inu.” (1 Akorinto 14:24, 25) Inde Mulungu analidi pakati pawo. “Kotero Mipingoyo [“matchalitchi,” RS, JB] inalimbikitsidwa m’chikhulupiriro, nachuluka m’chiŵerengo chawo tsiku ndi tsiku.”—Machitidwe 16:5.

Kodi Mkristu panthaŵiyo akadayanjidwa ndi Mulungu ngati akanalambirira mu akachisi achikunja kapena payekha? Baibulo limapereka malangizo omveka bwino pa nkhani imeneyi. Mfundo yake n’njakuti: Olambira amene Mulungu anawavomereza anayenera kukhala m’tchalitchi, kapena kuti mpingo woona wokha, umene ndi “thupi limodzi” la olambira enieni. Ameneŵa anali ophunzira a Yesu, otchedwa kuti Akristu.—Aefeso 4:4, 5; Machitidwe 11:26.

Nanga Bwanji Masiku Ano?

M’malo motilimbikitsa kuti tizilambirira m’nyumba imene amati tchalitchi, Baibulo limatilimbikitsa kuti tizilambirira pamodzi ndi tchalitchi, chomwe ndi “Eklesia [“mpingo,” NW] wa Mulungu wamoyo,” anthu amene ‘amalambira mumzimu ndi m’choonadi.’ (1 Timoteo 3:15; Yohane 4:24) Misonkhano yachipembedzo imene Mulungu amavomereza iyenera kulangiza anthu ‘mayendedwe opatulika ndi chipembedzo.’ (2 Petro 3:11) Iyenera kuthandiza opezekapo kukhala Akristu aakulu misinkhu, omwe angathe “kusiyanitsa chabwino ndi choipa.”—Ahebri 5:14.

Mboni za Yehova zimayesetsa kutsanzira Akristu a m’zaka za zana loyamba. Mipingo yopitirira 91,400 padziko lonse imakumana mokhazikika n’kumaphunzira Baibulo ndi kulimbikitsana, ndipo imatero m’Nyumba za Ufumu, nyumba za anthu, ndi m’malo ena. Zimenezi n’zogwirizana ndi mawu a mtumwi Paulo akuti: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi.”—Ahebri 10:24, 25.