Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kuzemba Panyumba N’kulakwa?

Kodi Kuzemba Panyumba N’kulakwa?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Kuzemba Panyumba N’kulakwa?

“Tinkazemba panyumba pakati pa usiku n’kupita kukantini kukakhala ndi anthu ena. Kenaka tinayamba kukhala pa phiri linalake kumangocheza. Onsewo anali kusuta fodya, ngakhale kuti ineyo sindinasutepo. Tinkakhala pamodzi n’kumakambirana zinthu zambirimbiri, tikumvera nyimbo zogunda kwambiri za heavy metal. Kenaka tinkapita kunyumba 5 koloko m’maŵa makolo anga asanadzuke,” anatero Tara. *

“Bambo anga akapita kuntchito ndipo amayi akagona, ndinkazembera kukhomo lakumaso. Ndinkalisiya lotseguka kuchitira kuti amayiwo asamve ndikamatseka chitseko chomwe chinali chachitsulo. Ndinkangocheza ndi anzanga usiku wonse. Kenaka m’mamaŵa dzuŵa likatuluka, ndinkaloŵanso m’nyumba mozemba. Nthaŵi zina ankazindikira kuti ndachokapo ndipo ankanditsekera panja,” anatero Joseph.

KUZEMBA PANYUMBA—kumaoneka ngati n’kosangalatsa. Ndi nthaŵi yosangalala ndi moyo wanuwanu kwa maola angapo, nthaŵi yochita zimene mukufuna ndi kukhala ndi amene mukufuna popanda kuopa aliyense. Komanso, mwina munamvapo anzanu akudzitamandira ndi zinthu zimene achita, komanso zosangalatsa zimene amakhala nazo akazemba panyumba usiku. Motero zingakukopeni kwambiri kuti muyese kugwirizana nawo.

Ana 110 ongoyamba kumene ndiponso otsala pang’ono kumaliza maphunziro awo a kusekondale ku North America atafunsidwa, 55 anavomera kuti anazembapo panyumba mwina kamodzi. Ambiri anayamba kuzemba ali ndi zaka 14. Vutoli n’lalikulu mwakuti akatswiri ena alimbikitsa makolo kuika ma alamu m’nyumba zawo kuchitira kuti ana awo asamachoke iwo osadziŵa. Kodi n’chifukwa chiyani achinyamata ambiri akuputa ukali wa makolo awo pozemba panyumba?

Chifukwa Chake Ena Amazemba Panyumba

Nthaŵi zina achinyamata amazemba panyumba chabe chifukwa chakuti amanyong’onyeka ndipo amangofuna kuti akasangalale ndi anzawo. Buku lakuti Adolescents and Youth limafotokoza kuti achinyamata angazembe panyumba “chifukwa chowaletsa zinthu zina, monga kuwauza kuti asachoke panyumba madzulo dzuŵa likangoloŵa kapena kuwaletsa kuti asapite kukakhala ndi anzawo pamacheza ena ake. Wachinyamatayo angangochoka ndipo mwina n’kubwerera makolo osadziŵa.” Mtsikana wina wa zaka 16 anafotokoza zimene zimam’pangitsa kuzemba panyumba. “Ndimangoona ngati ndine khanda komanso kuti ndilibe ufulu wochita zofuna zanga m’moyo,” anatero. “Nthaŵi imene anandiikira kuti ndizipezeka panyumba ndi masanasana poyerekeza ndi ya ena onse. Ndipo makolo anga salola kuti ndizipita kumene anzanga amapita . . . Ndiye kunena zoona ndimapitabe n’kudzanama” Joseph uja tam’tchula poyamba paja, anayamba kuzemba panyumba ali ndi zaka 14 pamene anapita kukamvera nyimbo za rap kumene makolo ake anam’letsa kupezekako.

Inde, achinyamata ambiri sakhala ndi malingaliro oipa pozemba panyumba. Tara, wachinyamata wina amene wagwidwa mawu pachiyambi pa nkhani ino, anati: “Sikuti poyamba tinali kuganiza kuti ‘Tiyeni tikachite zinthu zoipa.’ Ndinkangofuna kuti ndikhale ndi achemwali anga, ndipo iwo ankafuna kupita kwina kwake kuti akasangalale ndi anzawo.” Joseph ananena kuti: “Tinali kungocheza basi. Ndinkafuna kucheza ndi kuti ndikhale pamodzi ndi anzanga.” Ngakhale kuti wina sangakhale pangozi yaikulu chifukwa chongocheza ndi anzake, achinyamata ambiri amagwa m’mavuto aakulu.

Kuopsa Kwake

Katswiri wa zamaganizo Dr. Lynn E. Ponton akusonyeza kuti: “Si zachilendo kwa achinyamata kuchita zosimbwa.” Dr. Ponton akupitiriza kufotokoza kuti si zachilendo ndiponso mwina n’zabwinobwino kwa achinyamata kufuna kukhala odziimira paokha, kuyesa zinthu zatsopano, kuona zinthu zatsopano ndiponso zosangalatsa. N’kukulanso kumeneko. Koma achinyamata ambiri amanyanyira kusimbwa—makamaka akakhala kutali koti makolo awo sakuwayang’anira. Magazini onena za achinyamata a Teen amati: “Mawu a anzawo, kunyong’onyeka, kusoŵa zochita ndiponso mwina zinthu zina ngati moŵa . . . zingachititse achinyamatawo kudziika pangozi pochita zolakwika—n’kutaya moyo wawo.” Nthaŵi inayake ofufuza ena analemba zoopsa zina zimene achinyamata amachita, kuphatikizapo kuthamangitsa galimoto mopitirira muyeso, kuwononga zinthu, kuyendetsa galimoto ataledzera, komanso kuba.

Mukangoyamba kusamvera, n’zosavuta kuti muyambe kuchita zolakwa zikuluzikulu. Zili ngati mmene Yesu ananenera pa Luka 16:10 kuti: “Iye amene akhulupirika m’chaching’onong’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu.” Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti kuzemba panyumba ndi anzanu kungakuchititseni machimo aakulu. Tara anachita dama. Joseph anayamba kugulitsa mankhwala osokoneza bongo, ndipo anagwidwa n’kuikidwa m’ndende. Mkristu wachinyamata dzina lake John anayamba kumwa mankhwala osokoneza bongo ndi kuba magalimoto. N’zomvetsa chisoni kuti achinyamata ambiri amatutanso mavuto chifukwa cha khalidwe lotero—mimba za patchire, matenda opatsirana mwa kugonana, uchidakwa kapena kukonda mankhwala osokoneza bongo.—Agalatiya 6:7, 8.

Kuwononga Kwake

Zodetsa nkhaŵa kwambiri kuposa kuwonongeka kwa thupi lanu n’kusoŵa mtendere. Zimapweteka kwambiri ngati mtima wako suli pamtendere. (Salmo 38:3, 4) Joseph anati: “Pali mawu akuti munthu suzindikira kufunika kwa chinthu chinachake mpaka chitakusoŵa. Nthaŵi zina ndimakumbukira zakale ndipo sindikhulupirira kuti ndinali wosazindikira choncho.”

Komanso musaiŵale kuti zimenezi zingawonongetse mbiri yanu. Mlaliki 10:1 amati: “Ntchentche zakufa zinunkhitsa moipa nizioletsa mafuta onunkhira a sing’anga; chomwecho kupusa kwapang’ono kuipitsa iye amene atchuka chifukwa cha nzeru ndi ulemu.” Kalekale mafuta apamwamba kapena zonunkhiritsa zinkaipitsidwa ndi chinthu chaching’onong’ono ngati ntchentche yakufa. Mofananamo, mbiri yanu yabwino ingaipitsidwe chabe ndi “kupusa kwapang’ono.” Ndipo ngati ndinu Mkristu, mosakayika konse makhalidwe oipa ngati amenewo angakulepheretseni kukhala ndi maudindo mumpingo. Ndiponsotu, kodi mungalimbikitse bwanji ena kutsatira mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo pamene iwo akudziŵa kuti inuyo panokha simutero?—Aroma 2:1-3.

Pomaliza, taganizani mmene mtima wa makolo anu ungapwetekere atadziŵa za kuchoka kwanu. Mayi wina anafotokoza mantha ndi kuŵaŵidwa mtima kwake atadziŵa kuti mwana wake wamkazi wa zaka 15 sanali m’nyumba. Anafotokoza kuti iye ndi mwamuna wake anali ndi nkhaŵa kwambiri chifukwa chosadziŵa kumene mwana wawoyo anali atapita. Kodi mukufuna kuti makolo anu amve ululu ndi chisoni zoterozo?—Miyambo 10:1.

Kupeza Ufulu Wochuluka

N’zomveka ndithu kuti zingakhale zokhumudwitsa ngati mukuganiza kuti makolo anu amaletsa zinthu kwambiri. Koma kodi zikatero ndi bwino kungozemba panyumba? Mosakayika konse, adzakugwirani. Ngakhale muchenjere motani popusitsa makolo anu, Yehova Mulungu amaona zochita zanu, ngakhale zimene mungachite usiku kwambiri. (Yobu 34:21) Ndiye pamapeto pake nthaŵi ina adzakuonani ndithu, ndipo makolo anu angasiye kukukhulupirirani ngati mmene anali kuchitira asanakuoneni. Ndiyeno chingachitike n’chiyani? Ufulu umene munali kuufunawo simudzakhala nawotu!

Kumbukirani: Kuti mukhale ndi ufulu, makolo anu ayenera kukukhulupirirani. Ndipo njira yabwino kwambiri yochitira zimenezo n’kungowamvera basi. (Aefeso 6:1-3) Ngati mukuona kuti penapake makolo anu akunyanyira, auzeni moona mtima ndiponso mwaulemu. Angakumvereni ndithu zimene munganene. Komanso, mungaone kuti iwo ali ndi zifukwa zabwino zokuletserani zinazake. Ngakhale kuti simukuvomerezana nawo, musaiŵale kuti amakukondani ndi kuti akukufunirani zabwino. Pitirizani kukhala munthu wokhulupirikabe, ndipo panthaŵi yake mudzakhala ndi ufulu umene mumafuna. *

“Usayende Nawo”

Kale kwambiri, achinyamata oopa Mulungu ankakopeka n’kugwirizana ndi anzawo kuchita zamphulupulu. Pachifukwachi, Solomo analimbikitsa achinyamata kuti: “Mwananga, akakukopa ochimwa usalole. . . . Usayende nawo m’njira.” (Miyambo 1:10, 15) Tsatirani uphungu umenewo ngati amene mumati ndi anzanu akuyesa kukuuzani kuti muzembe panyumba. Solomo anapitiriza kuchenjeza kuti: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.”—Miyambo 22:3.

Ngati munayamba kale kuzemba panyumba, mulekeretu! Mapeto ake mungodziwononga nokha. Adziŵitseni makolo anu zimene mwakhala mukuchita, ndipo landirani chilango chilichonse chimene angakupatseni ndipo musachite chilichonse chimene angakuletseni. Ngati kuli kofunika, sankhani anzanu ena atsopano—anzanu amene angakuuzeni zabwino. (Miyambo 13:20) Funani zinthu zabwino kwambiri ndipo zosakuikani pangozi zimene mungasangalale nazo.

Chofunika kwambiri n’chakuti mulimbitse mkhalidwe wanu wauzimu poŵerenga Baibulo ndiponso kupezeka pamisonkhano yachikristu. Wamasalmo anafunsa kuti: “Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji?” Iye anayankha motere: “Akawasamalira monga mwa mawu [a Mulungu].” (Salmo 119:9) Mukayamba kusintha maganizo anu kuti muchite zoyenera, mudzaona kuti pamene kuzemba panyumba mwina kungakhale kosangalatsa, palibe chifukwa chodziikira pa ngozi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Tasintha mayina.

^ ndime 19 Kuti mudziŵe zambiri za kukhala ndi ufulu wochuluka, onani mutu 3 wa m’buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Mawu Otsindika patsamba 20]

“Makolo anga salola kuti ndizipita kumene anzanga amapita . . . Ndimapitabe n’kudzanama”

[Chithunzi patsamba 19]

Kuzemba panyumba kumayambitsa mavuto aakulu