Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuona Mbalame N’kosangalatsa Kwambiri

Kuona Mbalame N’kosangalatsa Kwambiri

Kuona Mbalame N’kosangalatsa Kwambiri

DZIKO lopanda mbalame silingasangalatse! Kulira kwake, nyimbo zake, mitundu yake yosiyanasiyana ndiponso kuuluka kwake—zonsezi n’zosangalatsadi. Koma kodi n’kangati pamene timamvetsera kapena kuyang’ana mbalame? Ngati m’makhala mumzinda umene anthu amakhala piringupiringu tsiku n’tsiku komanso waphokoso la magalimoto, ndiye kuti simungadziŵe n’komwe mbalame zomwe m’makhala nazo pafupi. Ngakhale ngati m’makhala kumidzi, n’kwapafupi kusachita nazo chidwi. Koma kodi mungakonde kuzionera pafupi mbalame za m’dera lanu?

Mungachite zimenezi mwa kuziwazira chakudya kuseri kwa nyumba yanu pafupi ndi zenera. Kenako, tengani chipangizo choonera zinthu patali kapena imani pazeneralo—ndipo khalani phee! Tengani kamera yamphamvu ndiponso filimu yokwanira yonjambulika mofulumira. Tenganinso buku lofotokoza mbalame ngati muli nalo kuti muthe kuzidziŵa bwinobwino. Kenako, yang’anitsitsani, mvetserani, ndipo sangalalani!