Malonda Akale Kwambiri
Malonda Akale Kwambiri
Shopu ya John yopalira matabwa anaimanga bwino ndiponso inali ndi zida zokwanira bwino. Kunalibe ina yofanana nayo kwawoko. Iye ankainyadira kwambiri. Koma usiku wina kunabuka moto. Mu maola ochepa chabe, shopu yake yokongola ija inakhala phulusa lokhalokha.
POYAMBA, John anali kuganiza zodula inshuwalansi ya moto ndi ndalama zina zimene anamangira shopuyo. Komabe anaganiza kuti: ‘Ine ndine munthu wosamala kwambiri. Ndipo pakapanda kubuka moto, ndiye kuti inshuwalansiyo idzangondiwonongera ndalama zanga.’ Komatu moto unadzabuka. Shopu ya John ikanakhala ndi inshuwalansi, mosakayikira akanaimanganso. Koma popanda inshuwalansi sanakwanitse.
Kodi Inshuwalansi N’chiyani?
Kwenikweni inshuwalansi sibizinesi imene munthu amayembekeza kubwezeredwa ndalama zake. Ndipo sikutchova njunga. Wotchova njunga amaputa dala tsoka, pamene inshuwalansi imateteza munthu ku masoka amene alipo kale. Inshuwalansi ndi njira yothandizana ndi anthu ena pakagwa tsoka.
Kuyambira kale, anthu akhala akusonkherana chuma chawo kuti athandize ena amene ataya zinthu. Pafupifupi zaka 3,500 zapitazo, Mose analangiza mtundu wa Israyeli kuti nthaŵi ndi nthaŵi uzipereka gawo la zokolola zawo kuthandizira “mlendo, ndi ana amasiye, ndi mkazi wamasiye.”—Deuteronomo 14:28, 29.
Chiyambi cha Inshuwalansi
Inshuwalansi yakhalapo kwa zaka zikwi zambiri. Mtundu wa inshuwalansi ya ngongole unaliponso pandandanda ya Malamulo a Hammurabi achibabulo, omwe anthu ena amati anaperekedwa Chilamulo cha Mose chisanakhaleko. Kuti alipirire maulendo awo a zamalonda kalelo, enisitima zapanyanja anali kutenga ngongole kwa amalonda. Sitima ikasoŵa, eniakewo samakhala ndi udindo wobweza ngongolezo. Pakuti sitima zambiri zinali kubwerako bwino, chiwongoladzanja choperekedwa ndi enisitima ambiri chinali chokwanira kukhala chipukutira misozi kwa opereka ngongolewo.
Imodzi mwa makampani aakulu kwambiri a inshuwalansi padziko lonse yotchedwa Lloyd’s of London, inayamba ndi malonda apanyanja omweŵa. Chakuma 1688, Edward Lloyd anali ndi kantini imene amalonda a ku London ndiponso oyang’anira mabanki ankakumanapo
mosachita kupangana n’kumakambirana za malonda. Kumeneku anthu achuma amene anali kupangana za inshuwalansi ndi amalinyero, ankalemba mayina awo m’munsi mwa mawu onena za tsoka limene lingagwe limene iwo angavomere kudzathandizapo ngati atawapatsa malipiro ena ake. Potsiriza, mu 1769, gulu la Lloyd’s limeneli analivomereza kukhala lodulitsa inshuwalansi ndipo m’kupita kwanthaŵi linakhala bungwe lalikulu kwambiri lotetezera masoka a panyanja.Inshuwalansi Masiku Ano
Anthu akamadula inshuwalansi masiku ano, amakhalabe akuthandizana pa masoka. Makampani a inshuwalansi a masiku ano amapenda maumboni osonyeza kuti ndi kangati m’mbuyomo kamene makasitomala awo anatayapo zinthu, mwachitsanzo chifukwa cha moto wa m’shopu, pofuna kudziŵiratu zimene makasitomalawo angadzataye m’tsogolo. Kampani ya inshuwalansiyo imagwiritsa ntchito ndalama zimene makasitomala awo ambirimbiri analipira popereka chipukutira misozi kwa makasitomala amene ataya zinthu.
Kodi mukufunikira inshuwalansi? Ngati ndi choncho, ndi inshuwalansi yamtundu wanji imene ili yokuyenerani? Ndipo kaya muli ndi inshuwalansi kapena ayi, kodi ndi kusamala kotani kumene kungakuthandizeni kupirira ngozi pamoyo wanu?
[Chithunzi patsamba 21]
Imodzi mwa makampani aakulu kwambiri a inshuwalansi padziko lonse inayambira pa kantini
[Mawu a Chithunzi]
Mwa chilolezo cha a Lloyd’s of London