Mbiri Yakale—Kodi Tiyenera Kuikhulupirira?
Mbiri Yakale—Kodi Tiyenera Kuikhulupirira?
“Kudziŵa mbiri yakale kumatichititsa . . . kuona kuti pali ubale ndithu kuyambira kalekale tisanabadwe mpaka mtsogolo tikadzamwalira.”—A Companion To The Study Of History, Lolembedwa Ndi Michael Stanford.
NGATI sitikudziŵa zimene zinachitika m’mbuyomu, tikusoŵa zinazake zofunika m’moyo wathu. Ngati simudziŵa mbiri yanu, ndiye kuti inuyo, abale anu, fuko lanu, ngakhale dziko lanu mungakhale ngati mulibe chiyambi, opanda kale lanu. Zinthu zingaoneke ngati zilibe maziko ndi tanthauzo lake lenileni.
Zochitika m’mbiri zingakhale nkhokwe yaikulu ya maphunziro a chikhalidwe. Zingatithandize kupeŵa kuchita zolakwika zimodzimodzi nthaŵi zonse. Zili ngati mmene wafilosofi wina ananenera mwamphamvu kuti anthu amene amaiŵala zakale salephera kubwereza zimodzimodzizo. Kudziŵa bwino lomwe mbiri kungatithandize kuzindikira zitukuko zakale, zinthu zodabwitsa zimene anazitulukira, anthu osangalatsa, ndi njira zosiyana zoonera zinthu.
Koma popeza kuti mbiri imakhudza anthu ndi zochitika zakale kwambiri, kodi tingadziŵe bwanji ngati anthu angaikhulupirire? Ngati mbiri ingatiphunzitse zinthu zofunika, ndiye kuti zinthuzo n’zoonadi. Ndipo pamene tazindikira choonadi, tifunika kuchivomereza, ngakhale ngati kuchita zimenezo kungavute. Kale la munthu lingakhale ngati mtengo wa malalanje. N’ngwabwino komanso uli ndi minga; umathandiza, koma minga yake imabaya.
M’nkhani zotsatira, tidzakambirana mfundo zina zokhudza mbiri yakale zimene zingatithandize kuzindikira kuti zimene timaŵerenga n’zolondola. Tidzakambirananso mmene mbiri yodalirika ingathandizire munthu woŵerenga womvetsetsa.
[Chithunzi patsamba 3]
Kodi mbiri yakale ingatiphunzitse zotani?
[Chithunzi patsamba 3]
Mfumukazi Nefertiti
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Nefertiti: Ägyptisches Museum der Staatlichen Museen Preußischer Kulturbesitz, Berlin
M’malire mwake: Chithunzi chojambulidwa mwa chilolezo cha a British Museum