Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Maloto Ndi Mauthenga Ochokera kwa Mulungu?

Kodi Maloto Ndi Mauthenga Ochokera kwa Mulungu?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Maloto Ndi Mauthenga Ochokera kwa Mulungu?

AKUTI Elias Howe, munthu woyamba kupanga makina osokera anachita kuwalota. Wolemba nyimbo wotchedwa Mozart ananena kuti nyimbo zake zambiri anachita kulota. Komanso wa sayansi ya mankhwala Friedrich August Kekule von Stradonitz anati anatulukira mpangidwe wa molekyu ya benzene m’maloto. Zinthu ngati zimenezi si zachilendo ayi. M’mbiri yonse anthu ambiri akhala akunena kuti maloto amachokera kwa milungu. Anthu ena amakhulupirira kuti zimene timalota monganso zimene timachitadi zimakhala zenizeni.

M’Baibulo muli nkhani zambiri zosonyeza kuti maloto anali ofunika kwambiri podziŵitsa anthu zinthu, anali njira yolankhulana ndi Mulungu. (Oweruza 7:13, 14; 1 Mafumu 3:5) Mwachitsanzo, Mulungu analankhula ndi Abrahamu, Yakobo ndi Yosefe m’maloto. (Genesis 28:10-19; 31:10-13; 37:5-11) Mulungu analotetsa mfumu ya ku Babulo Nebukadinezara maloto onena za m’tsogolo. (Danieli 2:1, 28-45) Choncho kodi pali zifukwa zokhulupiririra kuti masiku anonso maloto ena ndi mauthenga ochokera kwa Mulungu?

Maloto Ochokera kwa Mulungu

M’Baibulo, nthaŵi zonse Mulungu akalotetsa anthu pankakhala chifukwa chodziŵika bwino. N’zoona kuti nthaŵi zina wolotayo samazindikira tanthauzo la lotolo nthaŵi yomweyo. Komabe, nthaŵi zambiri, ‘Wovumbula zinsinsi’ amatanthauzira n’cholinga chakuti akhulupirire tanthauzo la lotolo. (Danieli 2:28, 29; Amosi 3:7) Maloto ochokera kwa Mulungu sanali osalongosoka monga amakhalira maloto amene timalota nthaŵi zonse.

Nthaŵi zina, Mulungu ankagwiritsa ntchito maloto poteteza anthu ofunikira kuti zofuna zake zichitidwe. Amene amalotetsedwawo sanali kwenikweni atumiki a Mulungu. Mwachitsanzo, openda nyenyezi amene anakaona Yesu ali khanda sanapitenso kwa Herode wachiwembuyo monga mwa pempho lake. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Chifukwa anachenjezedwa m’maloto. (Mateyu 2:7-12) Izi zinathandiza Yosefe, bambo a Yesu om’lera kukhala ndi nthaŵi yokwanira yothaŵira ku Igupto ndi banja lake, pomvera malangizo amene iyenso analandira m’maloto. Motero Yesu ali khanda, anapulumuka.—Mateyu 2:13-15.

Zaka mazana angapo m’mbuyomo izi zisanachitike, farao wina ku Igupto analota ngala za tirigu zonenepa zisanu ndi ziŵiri ndi ng’ombe zamaonekedwe okoma komanso ngala za tirigu zopsyerera zisanu ndi ziŵiri ndiponso ng’ombe zisanu ndi ziŵiri zoonda. Mulungu anamuthandiza Yosefe kumasulira malotowo molondola ponena kuti: dziko la Igupto lidzakhala ndi chakudya chochuluka kwa zaka zisanu ndi ziŵiri ndipo kenako lidzakhala ndi zaka zisanu ndi ziŵiri za chilala. Kudziŵiratu zimenezi kunapatsa mpata Aigupto kukonzekera ndi kusunga chakudya. Iyi inali njira yopulumutsira mbadwa za Abrahamu ndi kuziloŵetsa m’dziko la Igupto.—Genesis, chaputala 41; 45:5-8.

Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo nayonso inalota maloto. Inalosera za kukwera ndi kugwa kwa maulamuliro am’tsogolo apadziko lonse zimene zinadzakhudza kwambiri anthu a Mulungu. (Danieli 2:31-43) Kenako, inalotanso maloto amene ananeneratu kuti iyenso adzachita misala ndipo adzachira. Maloto a ulosi ameneŵa anadzakwaniritsidwanso m’njira ina yoposa apa chifukwa ankanena za kukhazikitsa Ufumu wa Umesiya umene Mulungu adzagwiritse ntchito pokwaniritsa chifuno chake.—Danieli 4:10-37.

Nanga Bwanji Masiku Ano?

Inde, Mulungu analankhulapo ndi anthu ena m’maloto. Koma Baibulo limasonyeza kuti zimenezi zinkachitika kamodzikamodzi. Maloto sanali njira yaikulu yolankhulana ndi Mulungu. Panali atumiki ambiri okhulupirika a Mulungu amene sanalandireko uthenga wochokera kwa Mulungu m’maloto. Zimene Mulungu ankachita polankhulana ndi anthu m’maloto tingaziyerekezere ndi nthaŵi imene anagaŵa Nyanja Yofiira. Timadziŵa kuti anaigaŵa kamodzi kokha, koma nthaŵi zonse sachita choncho ndi anthu ake.—Eksodo 14:21.

Mtumwi Paulo anasonyeza kuti m’nthaŵi yake mzimu wa Mulungu unali kugwira ntchito pa atumiki ake m’njira zambiri zodabwitsa. Pauloyu anati: “Kwa mmodzi kwapatsidwa mwa Mzimu mawu a nzeru; koma kwa mnzake mawu a chidziŵitso, monga mwa Mzimu yemweyo: kwa wina chikhulupiriro, mwa Mzimu yemweyo; ndi kwa wina mphatso za machiritso, mwa Mzimu mmodziyo; ndi kwa wina machitidwe a mphamvu; ndi kwa wina chinenero; ndi kwa wina chizindikiro cha mizimu; kwa wina malilime a mitundu mitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime.” (1 Akorinto 12:8-10) Ngakhale maloto ouziridwa ndi Mulungu satchulidwa mwachindunji, n’zachidziŵikire kuti Akristu ambiri analota maloto otere monga mphatso ina ya mzimu pokwaniritsa Yoweli 2:28.—Machitidwe 16:9, 10.

Komabe, pankhani ya mphatso zapaderazi mtumwiyo anati: “Koma kapena zonenera zidzakhala chabe, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzakhala chabe.” (1 Akorinto 13:8) Ndi umboni umene ulipo, zina mwa mphatso zodzayenera ‘kukhala chabe’ ndizo njira zosiyanasiyana zolankhulana ndi Mulungu. Atumwi atatha kufa, Mulungu analeka kupatsa atumiki ake mphatso zimenezi.

Lerolino akatswiri akuyesetsa kuzindikira m’mene maloto amachitikira ndiponso ngati amathandiza. Baibulo silimanena kanthu pankhani zimenezi. Komabe, Baibulo limachenjeza amene amalimbikira kulankhula ndi Mulungu m’maloto. Pa Zekariya 10:2, limati: “Aula awona bodza; nafotokoza maloto achabe.” Mulungu amachenjezanso za kuopsa kwa kuwombeza. (Deuteronomo 18:10-12) Ndi machenjezo ameneŵa, lerolino Akristu sayembekezera kuti Mulungu angawauze zochita kudzera m’maloto. M’malo mwake, amaona maloto monga zakutulo basi.