Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zoletsa Zida Zitha Bwanji M’tsogolo Muno?

Kodi Zoletsa Zida Zitha Bwanji M’tsogolo Muno?

Kodi Zoletsa Zida Zitha Bwanji M’tsogolo Muno?

M’ZAKA zaposachedwapa, mayiko a padziko lonse akambirana za njira zimene angathetsere katangale wa mfuti zazing’ono. A bungwe la United Nations General Assembly aganizira za nkhaniyi. Akonza malipoti, avomereza zinthu zina, ndipo agwirizana pa zinthu zina. Komabe, anthu osagwirizana nazo akunena kuti poti maboma ndiwo amagula ndi kugulitsa zida kwambiri, tikamangolimbana ndi akatangale ndiye kuti mabomawo sitiwafufuza.

Kwenikweni, n’kovuta kusiyanitsa pakati pa kugulitsa zida mwachilungamo ndi mwakatangale. Zida zambiri zakatangale anazigulitsapo mwachilolezo cha boma nthaŵi ina yake. Zida zimene poyamba anazigulitsa kwa asilikali kapena kwa apolisi nthaŵi zambiri amaziba ndi kuzigulitsa kwa akatangale. Chinanso n’chakuti, n’zosadabwitsa kuona mfuti zikugulitsidwanso kwa wina, mwiniwake amene anazigulitsa poyambayo asakudziŵa kapena asanavomereze. Nkhani ina ya m’magazini yotchedwa Arms Control Today inati: “Maboma ndiwo kwenikweni ayenera kuchitapo kanthu osati kungokhazikitsa chabe malamulo oletsa katangale wa mfuti zonyamulika komanso ayenera kuona mbali yawo pankhani yochirikiza malonda ovomerezeka a zida.” Ngakhale kuti anthu ambiri akuyembekeza kuti maboma aletsa malonda a mfuti zazing’ono, mtolankhani wina anati: “Popeza kuti mayiko asanu omwe ndi mamembala achikhalire a bungwe la [zachitetezo la United Nations] ndiwo amagulitsa zida zambiri padziko lonse, mwina ndi bwino kungosiya kuyembekeza kuti zimenezi zithekadi.”

Kuletsa zida zazing’ono ndi zonyamulika kuti zisafale kukuvutanso kwambiri chifukwa zida zimenezi sizivuta kwenikweni kupanga. Mayiko amene amapanga zida zapamwamba kwambiri monga akasinja, ndege ndiponso sitima zam’madzi alipo pafupifupi 12 okha, koma tsopano pali makampani 300 ochokera m’mayiko 50 amene akupanga zida zonyamulika. Kuchuluka kwa makampani opanga zida kumeneku sikuti kumangowonjezera zida za mayikowo koma kumachulukitsanso mpata wopereka zida kwa magulu ankhondo, oukira boma, ndiponso zigaŵenga.

Nkhani Zimene Akukangana Kwambiri

Zambiri zimene takambirana ndi nkhani ya kugwiritsa ntchito zida zazing’ono m’mayiko amene ali pankhondo. Komabe, m’mayiko osatekeseka amene alibe nkhondo akukangana kwambiri pa nkhani zoletsa mfuti. Anthu ofuna kuti malamulo oletsa mfuti akhale okhwima amanenetsa kuti mfuti zikachuluka, kupha anthu kumachulukanso. Iwo amati ku United States, kumene kulibe malamulo okhwima oletsa mfuti koma mfutizo ziliko zambiri, anthu ambiri amaphedwa. Ndipo ku England, kumene kuli malamulo okhwima oletsa mfuti, ndi anthu ochepa chabe amene amaphedwa. Osagwirizana ndi zakuti pakhale malamulo okhwima oletsa mfuti amafulumira kunena kuti ku Switzerland anthu ambiri amapeza mfuti mosavuta, koma anthu saphana kwambiri.

Chimene chasokonezanso zinthu n’chakuti, pofufuza kwapezeka kuti ku United States anthu ophedwa koma osati ndi mfuti ndi ochuluka kwambiri kuposa anthu onse ophedwa m’mayiko ambiri a ku Ulaya. Chikhalirechobe, mayiko ena alipo amene anthu ophedwa koma osati ndi mfuti aliko ochuluka kuposa anthu onse amene amaphedwa ku United States.

Kuŵerengetsera bwino, ndiponso kulakwitsa dala ziŵerengero pofuna kukometsa mfundo inayake, si zachilendo. Ndipo zikuoneka kuti pankhani yoletsa zidayi, mfundo iliyonse ili ndi mfundo inzake yoitsutsa komanso yooneka ngati yomveka. Nkhani zake n’zovuta zedi. Komabe akatswiri ambiri amavomereza, kuti pali zinthu zambiri zoyambitsa anthu umbanda osangoti kukhala ndi mfuti basi.

Bungwe lamphamvu loyang’anira zida ku United States la National Rifle Association nthaŵi zambiri limanena kuti: “Mfuti sizipha anthu, koma anthu ndiwo amapha.” Malingana ndi mfundo imeneyi, ngakhale kuti mfuti anaipanga kuti izipha, siipha payokha. Munthu amachita kuifwamphula mwadala kapena mwangozi. N’zoonadi kuti ena angatsutse ponena kuti mfuti zimathandizira anthu kuti aphane mosavuta.

Kusula Malupanga Kukhala Zolimira

Malingana ndi Baibulo, vuto la anthu lophana silidzathetsedwa polanda mfuti anthu amene cholinga chawo n’kupha. Inde, pamlingo winawake zida zayambitsa vuto la umbanda, koma anthunso ali ndi vuto. Kuti vutoli lithe, chofunika n’kungosintha maganizo a anthuwo. Mneneri Yesaya anauziridwa kulemba kuti: “[Mulungu] adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:4.

Ena angaganize kuti zimenezi n’zosatheka, koma n’zotheka ndithu. Ulosi wa Yesaya ukukwaniritsidwa masiku ano kwa Akristu oona padziko lonse. Mophiphiritsa kusula zida zawo n’kusanduka zida zogwirira ntchito yamtendere kwasonyeza chikhumbo chachikulu kwambiri chofuna kusangalatsa Mulungu ndi kukhala pamtendere ndi ena. Pamapeto pake aliyense padziko lapansi adzakhala pamtendere komanso wotetezeka kotheratu mu Ufumu wa Mulungu. (Mika 4:3, 4) Mfuti sizidzaphanso anthu. Anthu sadzaphanso anthu anzawo. Zida zophera anthu zidzakhala zosagwiranso ntchito.

[Chithunzi patsamba 18]

“Adzasula malupanga awo akhale zolimira”