Kulimbikitsa Mtendere M’malo mwa Nkhondo
Kulimbikitsa Mtendere M’malo mwa Nkhondo
YOSIMBIDWA NDI DOROTHY HORLE
Ndinabadwa mu 1919, m’banja la chitaliyana la chikatolika mumzinda wa Wilmington, m’boma la Delaware, ku America. Makolo anga sankapita kutchalitchi, koma ankatumizako ine ndi achemwali anga aŵiri. Ndinkachita chidwi ndi kukula kwa matchalitchiwo ndiponso mamangidwe ake apamwamba, mafano ake ndi zina zochitika kumeneko.
M’KUPITA kwa nthaŵi ndinalibenso chidwi ndi Chikatolika. Tchalitchichi sichimalemekeza Baibulo, limene bambo anga ankalilemekeza ndi kuliŵerenga nthaŵi zonse. Ku tchalitchi ndinkanyansidwa akamalengeza anthu amene apereka ndalama ndiponso ndalama zimene apereka. Panalinso mbiri zambiri zochititsa manyazi zokhudza ansembe. Pamene ndimakwanitsa zaka 15, n’kuti nditasiya Chikatolika. Motero ndinapeza nthaŵi yokwanira yophunzira luso lojambula.
Ntchito Yojambula
Mu 1940, ndili ndi zaka 21, ndinakwatiwa ndi William Horle, mnyamata wokonda kujambula zithunzi zilizonse zokhudza nkhondo, monga ndege, asilikali, mfuti ndi sitima. Mwamuna wanga amene tinkamutchanso kuti Bill anasangalala kuti ndinkadziŵa kujambula, ndipo anandigulira penti yojambulira. Aka kanali koyamba kukhala ndi penti yangayanga. Ndinayamba kuphunzira maluso a ojambula a akatswiri akale.
Titatha zaka ziŵiri m’banja, Bill anayamba kupanga ziboliboli za asilikali zamtovu. Kodi zinali zidole wamba? Ayi ndithu! Anali kuzipanga mwaukatswiri zedi. Ena ankapanga ziboliboli za pulasitiki, za mitengo, kapena za pulasitala, koma Bill ankapanga za mtovu chifukwanso chakuti anaphunzira kugwiritsa ntchito makina.
Ankajambula chimene akufuna kupanga, n’kupanga zikombole zooneka choncho, kenako amathira mtovuwo atausungunula m’zikombolezo. M’kupita kwa nthaŵi, anakhala waluso zedi polumikiza mbali zake, kuwotcherera, kusalalitsa, ndi kuŵalitsa. Kenako anasiya kupangira ziboliboli m’zikombole za pulasitala n’kumazipangira m’zikombole zosalala kwambiri. Izi zinam’pangitsa kugwira ntchito yake mwaukatswiri.
Akatha kupanga chitsulo chilichonse, ntchito yanga inali yomalizitsa. Mwa kufufuza kwambiri, tinapeza nkhani zofotokoza maonekedwe a mayunifolomu akale a asilikali—kuphatikizapo mabatani ake, zokongoletsera zake, nyota zake, ndi mitundu yake.
Pogwiritsa ntchito makina oonetsa zinthu ngati zazikulu kwambiri, ndinkapaka zitsulozo mafuta ndi penti yopaka zitsulo. Izi zimapangitsa ziboliboli zathu kuoneka ngati zenizeni. Mu chipinda chathu chaching’ono ku Philadelphia, Pennsylvania, tinali kupangiramo ziboliboli zoonetsa amwenye a ku America, asilikali ankhondo ya pachiŵeniŵeni, asilikali apanyanja a America, akavalo ndi okwerapo ake a m’nthaŵi ya Napoleon, asilikali omwe ankalamulira dziko ku Igupto, a Zouave a ku Algeria ndi zinanso!
Kenako gulu la asilikali apanyanja a ku America linam’pempha Bill kuti apange chiboliboli cha kagulu koyamba ka asilikali apakavalo kamene kanatumizidwa ku Peking (kumene tsopano ndi
Beijing), m’dziko la China, isanafike 1939. Tinagwira ntchito mosapumira kuti tichimalize, ndipo mu 1954 tinachipereka ku bungwe la Smithsonian Institution ku Washington, D.C. Patapita zaka, Pulezidenti Lyndon Johnson anafunsa ngati tingachisamutsire ku White House. Sitinakane.Sitinkagulitsa ziboliboli zathu, koma zambiri Bill ankangopatsa anthu. M’mabuku ambiri amatiyamikira pankhani yopanga ziboliboli za asilikali. Ziboliboli zathu anazionetsa mu 1965 ku Flushing Meadow, ku Queens, New York pamene kunali chionetsero cha zinthu zopangidwa m’mayiko osiyanasiyana. Oyang’anira nyumba zoonetseramo zinthu zakale anapempha ziboliboli zathu. Mkulu wina wolemba mbiri ya nkhondo za pachiŵeniŵeni wa ku America, wotchedwa Bruce Catton, anajambula zithunzi za ziboliboli zathu zosiyanasiyana m’mabuku ake.
Ndinali ndi Mafunso Ambiri Okhudza Moyo
Komabe pamene ndimafika zaka 40, zinthu zinayamba kusintha. Ndinayamba kufunsa za Mulungu. Pa Tsiku la Khirisimasi, ana asanu a akatolika anafa nyumba itapsa, makolo awo ali kutchalitchi. Ndinadzifunsa, kuti ‘Kodi Mulungu angalole bwanji zimenezi kuchitika patsiku limene anabadwa?’ Ndinaŵerenga buku limene linafotokoza nkhanza zimene anaona Ayuda pamene ankapululidwa ndi chipani cha Nazi. Izi pamodzi ndi zochitika zina zoipa zam’dziko zinandipangitsa kufunsa kuti, ‘Kodi Mulunguyo ali Kuti? Bwanji nanga sakugwira ntchito yake!’
Potsanzira zimene bambo anga ankachita ndidakali mwana, ndinaona kuti yankho lake liyenera kupezeka m’Baibulo. Choncho, ndinapita kwa mtsogoleri wa katolika wa kufupi ndi kwathu ku Philadelphia ndipo ndinagwirizana ndi wansembe kuti tidzakambirane za m’Baibulo. Ndinatopa n’kudikirira, koma sanabwerebe. Ndinkapita kunyumba kwake Mlungu uliwonse, mpaka milungu inayi, koma sindinakambirane naye m’pang’ono pomwe.
Tsiku lina madzulo, nditathedwa nzeru, ndinayang’ana kumwamba n’kupemphera kuti: Sindidziŵa kuti ndinu yani. Sindikudziŵanso kuti mumapezeka m’chipembedzo chiti, koma ndikudziŵa kuti muliko. Chonde ndiloleni kuti ndikudziŵeni!” Patangopita nthaŵi pang’ono, Mboni za Yehova zinafika panyumba yanga.
Nthaŵi zambiri, ndinkaona Mboni zikuimika magalimoto awo, kutulukamo, n’kumapita nyumba zosiyanasiyana. Ngakhale sindinkawadziŵa iwowo kapenanso chifukwa chimene ankayendera m’makomo a anthu, ndinkachita chidwi ndi ntchito yawo.
Tsiku limeneli mu 1961 pamene Mboni zinafika panyumba yanga, ndinali wokhumudwa chifukwa sindimaphula kanthu pofufuza za Mulungu. Ndikutsuka chitseko chakumaso kwa nyumba yanga, mayi wina wachikulire dzina lake Marge Brion anakwera sitepe la khonde langa n’kundipatsa moni. Poyamba sindinamuyang’ane pofuna kuti aziti sindinamuone. Koma atayamba kukamba zakuti dziko lapansi adzalisandutsa paradaiso wokongola, ndinamvetsera mwatcheru zonse zimene ankanena. Kenako anandifunsa kuti, “Kodi mukumvetsera?”
Ndinabwereza zonse zimene ananena, kuphatikizapo lemba la m’Baibulo la pa Yesaya 55:11 limene anaŵerenga. Ndiyeno ndinatembenuka, ndi kumugwira dzanja, ndipo ndinati, “Tiyeni m’nyumba!” Anandipatsa Baibulo loyamba kukhala nalo ndiponso buku lothandizira kuphunzira Baibulo lakuti Kucokera Ku Paradaiso Wotayika Kunka ku Paradaiso Wopezedwanso. Anandipemphanso kuti azikambirana nane Baibulo nthaŵi zonse. Ili ndilo phunziro limene ndinkafuna kuti azichita nane ku Tchalitchi cha Katolika kuja.
Chifukwa ndinkaphunzira kaŵiri pamlungu, ndinalimbikira kwambiri pophunzira Baibulo. Mosakhalitsa, ndinatsimikiza kuti ndapezadi choonadi. Ndinagwidwa nthumanzi kwambiri podziŵa dzina la Mulungu, Yehova. (Salmo 83:18) Tangoganizirani: ameneyu ndiye Mulungu amene ndinakhala ndikufuna kum’dziŵa kuyambira ndili wamng’ono! Ndinaphunziranso kuti Mwana wake, Yesu Kristu, sali mbali ya utatu wa Mulungu. (Yohane 14:28) Mosakhalitsa ndinayamba kupezeka pamisonkhano yachikristu ya Mboni za Yehova ndipo ndinkafunitsitsa kukhala wolengeza uthenga wa Baibulo nthaŵi zonse.
Kusankha Zinthu Zofunika Kwambiri
Tsono ndinakumana ndi chiyeso chachikulu. Ndinkadzifunsa kuti, kodi ndisiye ntchito yanga yopanga ziboliboli limodzi ndi mwamuna wanga William? Kodi ndingatumikire bwanji Mulungu wamtendere ndi Mwana wake, Kalonga Wamtendere, ngati ndikulimbikitsa nkhondo m’ziboliboli? (Yesaya 9:6) Kodi si Yehova amene analonjeza kuti ‘adzaletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi’? (Salmo 46:9) Tsono ine n’kukakamiriranji chinthu chimene Mulungu adzachithetse? Ndiponso kodi Yesaya sananeneretu kuti anthu a Mulungu “adzasula malupanga awo akhale zolimira” ndipo sadzaphunziranso nkhondo? (Yesaya 2:4) Ndinasinkhasinkha ndiponso kupemphera kwanthaŵi yaitali. Kenaka ndinatsimikiza ndimvekere: “Sindidzapentanso ziboliboli!” Pa April 25, 1964, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova Mulungu mwa kubatizidwa m’madzi.
Kaŵirikaŵiri Bill ankanena kuti amamva chisoni kwambiri akaganiza kuti tsiku lina tidzasiyana tikadzamwalira. Nditayamba kuphunzira Baibulo, ndinkamuuza kuti: “Bill, tikhozatu kudzakhala ndi moyo kosatha m’dziko latsopano la Mulungu!” (Yesaya 25:8; Chivumbulutso 21:4, 5) Ankaona ngati ndayamba misala. N’tamufotokozera chifukwa chake sindimapentanso ziboliboli za asilikali, anakwiya ndipo anandiopseza kuti andisiya. Ndipo kenaka anandisiyadi.
Bill anapanga yekha ziboliboli kwa zaka zambiri. Koma sankakhala kutali ndipo nthaŵi zonse ankandipatsa chithandizo pamodzi ndi mwana wanga wamwamuna Craig, amene anabadwa mu 1942. Tinabwererana ndi Bill mu 1988, ndipo tinakhala limodzi kwa zaka khumi mpaka pamene anamwalira.
M’mbuyomo, mu 1966, ndinakwanitsa cholinga changa cha kukhala mpainiya. Kuyambira nthaŵi imeneyo, sindinabwererepo m’mbuyo ayi. Ndinali ndi mwayi wophunzira Baibulo ndi mkulu wanga. Anakhulupirira ziphunzitso zake, ndipo ndi Mboni yachangu mpaka pano. Bambo anga anamvetsera uthenga wa Baibulo ndipo patangotha milungu iŵiri anayamba kupezeka pamisonkhano pa Nyumba ya Ufumu. Anabatizidwa ali ndi zaka 75, ndipo anali wokhulupirika kwa Mulungu mpaka pamene anamwalira ali ndi zaka 81. Mayi anga anakhulupiriranso Yehova, ngakhale kuti anamwalira asanadzipatulire. Anamwalira ali ndi zaka pafupifupi 94.
Kwa zaka zonsezi Yehova, Mulungu wamtendere wandidalitsa kwambiri. Tsopano ndili ndi zaka 81, ndipo ndikuchitabe upainiya, ngakhale kuti ndimayenda movutikira. Ndimadziona monga mtumwi Paulo, amene analemba kuti: “Ndim’yamika iye wondipatsa ine mphamvu, ndiye Kristu Yesu, Ambuye wathu, kuti anandiyesa wokhulupirika, nandiika kuutumiki.” (1 Timoteo 1:12) Ndi utumiki wosangalatsa bwanji! Anthu ambiri amene ndaphunzira nawo Baibulo asiya zinthu zina zapamtima pawo kuti atumikire Mulungu wathu wachifundo.
Ndimamva chisoni kwambiri kuti si onse a m’banja langa amene alabadira choonadi cha Baibulo. Mwina mkupita kwanthaŵi ena adzalabadira. Koma kwa ine Mawu a Yesu ndi oona kuti atumwi ake ‘adzalandira makumi khumi tsopano nthaŵi ino, nyumba, ndi abale, ndi alongo, ndi amayi, ndi ana.’ (Marko 10:30) Ndithudi, Yehova wandilemeretsa. Ndimanyadira ndiponso kusangalala kwambiri kuti ndinakana kutchuka ndiponso nkhondo koma n’kusankha Mulungu ndiponso mtendere!
[Chithunzi patsamba 22]
Ndili ndi mkulu wa asilikali dzina lake L. C. Shepherd, Jr., mu 1954
[Mawu a Chithunzi]
Defense Dept. Chithunzi (Gulu la Asilikali Apanyanja)
[Chithunzi patsamba 23]
(M’mene chilili)
[Chithunzi patsamba 24]
Ndili ndi zaka 81, ndipo ndakhala mpainiya kwa zaka zoposa 30