Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kusefukira Kwa Anthu M’mizinda”

“Kusefukira Kwa Anthu M’mizinda”

“Kusefukira Kwa Anthu M’mizinda”

“Anthu ali yakaliyakali kuposa n’kale lonse, ndipo ambiri amene amachoka kumudzi pofunafuna moyo wabwinopo amasamukira kumzinda winawake.”

LINATERO buku lotchedwa Foreign Affairs poyamba nkhani ya mutu wakuti “Kusefukira kwa Anthu M’mizinda Yosatukuka.” Malinga ndi nkhaniyo, anthu ambiri akhala “akunyengeka ndi zinthu zotenga mtima, kapena akakamizika kuchoka kumidzi chifukwa cha ndale, umphaŵi, kuchuluka kwa anthu, ndiponso kuwonongeka kwa zinthu zachilengedwe.”

Komano kodi mizinda ikukula motani? Ena akuti anthu ochuluka kwambiri oposa miliyoni imodzi mlungu uliwonse akusamukira kumizinda! M’mayiko osatukuka, mizinda yoposa 200 tsopano ili ndi anthu oposa miliyoni imodzi. M’mizinda ina 20 anthu achuluka kuposa mamiliyoni khumi! Ndipo sizikuoneka kuti achepa. Mwachitsanzo, tione mzinda wa Lagos ku Nigeria. Malinga ndi lipoti lonenedwa ndi bungwe la Worldwatch Institute, akuti “podzafika mu 2015, ku Lagos kudzakhala kuli anthu pafupifupi 25 miliyoni, motero pamizinda ikuluikulu padziko lonse, mzindawu udzachoka pa nambala 13 n’kufika pa nambala 3.”

Akatswiri ambiri akuona kuti limeneli si tsogolo labwino. Federico Mayor yemwe anali woyang’anira wamkulu wa bungwe la United Nations Educational, Scientific, and Cultural Organization, anachenjeza kuti podzafika chaka cha 2035, “anthu enanso mamiliyoni 3000 azidzakhala m’matauni amene alipo pakalipanowa.” Kuti tisamalire anthu ambiri chonchi, “tidzayenera kumanga mizinda 1000 yokwana anthu mamiliyoni atatu m’zaka makumi anayi zikubwerazi. Ndiye kuti tizidzamanga mizinda 25 chaka chilichonse.”

Anthu odziŵa akutinso padziko lonse anthu akamachulukirachulukira m’mizinda, mizindayo imawonongeka. Ndipo zimenezi zikukhudzanso mizinda yotsogola yam’mayiko olemera. Ndiye kodi ndi mavuto otani amene ali m’mizinda, ndipo kodi angakukhudzeni bwanji? Kodi pali njira zilizonse zodzawathetsera? Nkhani zotsatira zifotokoza mfundo zofunika zimenezi.