Kusintha Dera Louma Kukhala Lachonde
Kusintha Dera Louma Kukhala Lachonde
YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU INDIA
Kodi madera ouma a ku Ladakh, lomwe ndi boma la kumpoto kwa India, angakhale bwanji achonde? Ili ndi funso limene ankadzifunsa Tsewang Norphel, yemwe anapuma pa ntchito ya zomangamanga. Madzi oundana a m’mapiri a Himalaya amayamba kusungunuka n’kumapita kuderali, mu June, osati mu April. Komatu mu April mpamene mvula imakhala yochepa ndiponso mpamene alimi amafuna madzi othirira mbewu zawo. Norphel anapeza njira yanzeru yothetsera vutoli: Anaganiza zopanga dziŵe la madzi oundana pamalo otsikirapo, loti lizisungunuka kumayambiriro kwa chaka.
Malinga ndi nyuzipepala ya The Week ya ku India, akuti Norphel ndi anzake anaganiza zopatutsa kamtsinje kena m’phirimo pokumba ngalande yotalika mamita 200 ndiponso yokhala ndi njira 70 zotulukira madzi. Madzi akafika mu njira zimenezi amayenda pang’onopang’ono pamlingo wabwino ndipo amauma asanafike pamakoma otetezera madzi kuti asapyole amene anamanga m’munsi mwa phirilo. Ndiyeno pang’onopang’ono madzi oumawo amakwera, mpaka kuyamba kusefukira. Popeza malowo ali pa mthunzi wa phirilo, dziŵe loumalo lingathe kusungunuka mu April kukatentha, ndipo zikatere madzi othiririra mbewu ofunika kwambiri panthaŵiyi amayamba kupezeka.
Kodi njira yochita kupanga dziŵe lamadzi oumali inali yothandiza? Kwenikweni malingaliro a Norphel, anali othandiza kwambiri mwakuti pano ku Ladakh kuli maiŵe khumi otereŵa, ndipo akuganiza zopanga ena. Dziŵe limodzi lotere, lili pa chitunda cha mamita 1370, limasunga malita a madzi okwana 34 miliyoni. Nanga linadya ndalama zingati? “Kuchita kupanga dziŵe la madzi ouma kumatenga miyezi pafupifupi iŵiri ndiponso ndalama zokwana madola 1,860, ndipo zambiri amalipirira antchito,” inatero magazini ya The Week.
Nzeru za munthu, zitagwiritsidwa ntchito moyenera, zingathandizedi kwambiri. Tangolingalirani zinthu zimene anthu adzapange mu Ufumu wa Mulungu wakumwamba! Baibulo limalonjeza kuti: ‘Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti se lidzasangalala ndi kuphuka ngati duŵa. . . . M’chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m’dziko loti se.’ (Yesaya 35:1, 6) Si mmene tidzasangalalira kugwira nawo ntchito yokongoletsa dziko lathu!
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.
Arvind Jain, The Week Magazine