Kuyang’anitsitsa Tsitsi Lanu
Kuyang’anitsitsa Tsitsi Lanu
BUKU lina la maumboni limati, “tsitsi limavumbula umunthu wa anthu kaya ndi a msinkhu wanji kapenanso a mtundu wanji.” Choncho, sizodabwitsa kuti anthu ambiri amafunitsitsa kuti tsitsi lawo lizioneka bwino ndiponso lokongola.
Atolankhani a Galamukani! anafunsa akatswiri anayi osamalira tsitsi mafunso otchuka okhudza tsitsi ndiponso kulisamalira kwake. Anapeza kuti tsitsi lili ndi zambiri koposa zimene timaona.
Kukula ndi Kuthothoka kwa Tsitsi
Funso: Kodi tsitsi limapangidwa ndi chiyani?
Yankho: Tsitsi lili ndi puloteni yokhala ndi nkhosi. Tsitsi lililonse limamera kuchokera pakabowo. Pansi pa kabowo kalikonse pamakhala kachisa katsitsi, kamene kamasunga magazi ambiri. Kachisaka kamatulutsa maselo a tsitsi amene amakwera n’kufika pa kabowo kaja ndipo zikatere tsitsi limapangidwa.
Funso: Anthu ambiri amakhulupirira kuti tsitsi limakula msanga likadulidwa. Kodi zimenezi n’zoona?
Yankho: Ayi. Anthu ena amaganiza kuti tsitsi limapeza chakudya kuchokera m’thupi, monga mmene nthambi za mtengo zimapezera chakudya kuchokera m’thunthu la mtengowo. Koma tsitsi likaphuka n’kutulukira panja, basi limasiya kumera.
Choncho, kudula tsitsilo, sikukhudzana ndi kukula kwake.Funso: N’chifukwa chiyani tsitsi limachita imvi?
Yankho: M’kati mwa tsitsi muli zinthu zimene zimalisintha mtundu. Ndipo zinthu zimenezi zikafa, tsitsi limachita imvi; ndipo nthaŵi ya imvi ndiyo ukalamba. Kumera imvi usanafike msinkhu wokalamba chingakhale chibadwa kapena matenda. Komabe, si zoona kuti tsitsi limachita imvi mwadzidzidzi. Zinthu zimene zimasintha mtundu wa tsitsi zimakhala pansi pa khungu lam’mutu. Choncho pamatenga nthaŵi kuti imvi zitulukire (zimakula pafupifupi masentimita 1.25 pamwezi) kenako zimayamba kuonekera m’mutu.
Funso: N’chifukwa chiyani tsitsi limathothoka?
Yankho: Tsitsi limathothoka mwachibadwa. Pa avareji, munthu aliyense patsiku amathothoka tsitsi 50 kapena 80. Koma dazi la amuna limakhala la kumtundu ndipo zikuoneka kuti limachitika chifukwa cha kupereŵera kwa mahomoni ena m’thupi, zimene zimapangitsa tsitsi *
kuthothokeratu. Matenda othothoka tsitsi kwambiri amatchedwa alopecia.Funso: Ena amati tsitsi limasonyeza thanzi la munthu. Kodi inuyo munaona kuti n’zoona?
Yankho: Inde. Pansi pa khungu, magazi amapereka chakudya ku tsitsi. Choncho tsitsi lathanzi lingasonyeze kuti munthu ali ndi magazi athanzi. Komabe, munthu amene amadya mopereŵera kapena amene ali chidakwa angaone kuti tsitsi lake limakhala lonyetchera ndi losachedwa kuduka, chifukwa magazi ake sapititsa chakudya chokwanira ku tsitsi lake. Tsitsi likamathothoka kapena likamangodukaduka chingakhale chizindikiro cha matenda kapena pathupi.
Kusamalira Khungu la M’mutu Ndiponso Tsitsi Lanu
Funso: Fotokozani mmene mumasamalilira tsitsi ndiponso khungu la m’mutu.
Yankho: Odziŵa bwino zatsitsi akuona kuti anthu ambiri amene khungu la m’mutu mwawo lili louma mosowetsa mtendere amasamba tsitsi lawo pafupipafupi kwambiri. Ndi zoona kuti mafuta a m’mutu mwanu amasunga fumbi ndiponso litsiro zimene zingatsekereze mitsempha yopita ku timabowo tija. Choncho n’kofunika kusamba tsitsi pafupipafupi. Koma mafuta achibadwa ameneŵa amatetezanso khungu lanu ku mabakiteriya oipa ndiponso amasunga chinyontho chofunikira. Mukamasamba pafupipafupi mumachotsa mbali yoteteza imeneyi pakhungu lanu ndipo mumaputa matenda monga kuuma khungu. Anthu ambiri odziŵa bwino zatsitsi amaona kuti ndi bwino kusamba tsitsi pamene m’mutu muli mwakuda kwambiri. Anthu a tsitsi lokhala ndi mafuta ambiri ayenera kusamba tsitsi lawo kaŵirikaŵiri kusiyana ndi amene ali ndi tsitsi labwinobwino kapena amene ali ndi tsitsi louma.
Posamba tsitsi, tikitani khungu lanu. Izi zimachotsa maselo akufa pakhungulo ndipo zimathandiza kuti magazi amene amaperekera zakudya ku tsitsi lanu aziyenda bwino. Kumbukirani kulitsukuluza bwinobwino! Ngati simunatsukuluze m’manja mwanu mutatha kusambamo ndi sopo, m’manjamo khungu limatha kuuma ndiponso kukakala. Mofananamo, ngati simuchotsa bwinobwino mankhwala otsukira tsitsi, khungu la m’mutu lingathe kuuma ndiponso kukakala.
Funso: Kodi tingatani nalo khungu lokakala?
Yankho: Imwani madzi ambiri, ndipo idyani chakudya chopatsa thanzi. Izi zimafeŵetsa khungu lanu ndipo mumakhala ndi magazi athanzi. Gwiritsani ntchito mankhwala otsukira tsitsi amphamvu pang’ono ndipo tikitani khungu lanu nthaŵi zonse. Ena amagwiritsa ntchito mankhwala ena a tsitsi amene amaumira m’mutu momwemo ndiponso mafuta ofeŵetsa khungu.
Kukonza Tsitsi Lanu
Funso: Kodi tiyenera kukumbukira chiyani popita kokakonzetsa tsitsi?
Yankho: Ngati mukufuna kusintha sitayilo ya tsitsi lanu, tengani chithunzi chosonyeza sitayilo imene mukufuna kapenanso imene simukufuna. Nenani moona mtima malingaliro anu ndi nthaŵi imene mukufuna kuti muzithera pokonza tsitsi lanu tsiku lililonse, popeza masitayilo ena amafuna nthaŵi yambiri kusiyana ndi ena. Kumbukirani kuti pamafunika maulendo aŵiri kapena atatu okakonzetsa tsitsi kwa munthu mmodzi kuti azoloŵere tsitsi lanu ndiponso kuti muzimasuka naye. Choncho osafulumira kusintha kumene mumakonzetsa tsitsi lanu!
Zimene Tsitsi Lanu Limavumbula
Mmene munthu amasamalira tsitsi ndiponso sitayilo imene amalichita zimasonyeza mmene amaganizira. Anthu amameta tsitsi, kulitalikitsa, kuliwongola, kulipinda, kulisintha mtundu, ndi masitayilo ena osiyanasiyana kuti ligwirizane ndi mafashoni otchuka, zikhulupiriro zachipembedzo, chikhalidwe ndiponso ndale. Liyang’anitsitseni tsitsi lanu. Kodi likuvumbula kuti mumaganiza zotani? Tsitsi la thanzi limene lili lokonzedwa bwino limakongoletsa munthu ndipo ena amalisirira.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 12 Kuti mumve zambiri, onani nkhani yakuti “Alopecia—Living in Silence With Hair Loss,” mu Galamukani! yachingelezi ya April 22, 1991.
[Chithunzi patsamba 26]
Kudya zakudya zopatsa thanzi ndiponso kumwa madzi ambiri zimathandiza kufeŵetsa khungu lokakala
[Chithunzi patsamba 26]
Kusamba tsitsi pafupipafupi kwambiri kumachotsa mafuta oteteza khungu lanu la m’mutu
[Chithunzi patsamba 26]
Kumera imvi munthu akamakalamba n’kwachibadwa