Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kusinthadi Ambanda N’kotheka?

Kodi Kusinthadi Ambanda N’kotheka?

Kodi Kusinthadi Ambanda N’kotheka?

“Palibe munthu yemwe angaumirize mnzake kuti asinthe khalidwe. Munthu ayenera kusintha yekha mwakufuna kwake,” anatero VIVIEN STERN M’BUKU LAKUTI A SIN AGAINST THE FUTURE—IMPRISONMENT IN THE WORLD.

NJIRA yofunika kwambiri yosinthiradi akaidi yagona pa kuwaphunzitsa ndi kuwasintha maganizo ndiponso mmene amaonera zinthu. Mosakayikira, pali anthu ena oona mtima amene akuyesetsa kuphunzitsa ndi kuthandiza akaidi. Akaidi ambiri amayamikiradi ntchito yabwino yoganizira ena imene anthuwa amachita.

Anthu ena angatsutse kuti ndende pazokha zili ndi vuto losati n’kukonzeka motero sizingasinthe n’komwe makhalidwe a anthu. N’kutheka kuti kungotsekeredwa m’ndende sikungachititse munthu kusintha, komabe malangizo a m’Baibulo athandiza anthu ena kusintha. Zimenezi zikusonyeza kuti anthu ena angasinthe.

Masiku ano, chifukwa chothandizidwa ndi Baibulo akaidi ena akusintha kukhala ndi maganizo ndi makhalidwe abwino. Akutero motani? Pomvera uphungu wa m’Baibulo wakuti: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Kodi zimenezi zikuchitika motani?

Ntchito ya Baibulo

Anthu ambiri amaganiza kuti chipembedzo chingagwire ntchito yaikulu pothandiza akaidi kuti alape n’kusiya zochita zawo zakale. Inde, vuto lake la zimenezi n’lakuti khalidwe lililonse labwino limene munthu angapeze ali m’ndende angalisiye atam’tulutsa m’ndendemo. Mkaidi wina ananena chonchi: “Anthu ambiri amam’landira Yesu ali kundendeko, koma akamachoka amam’siya komweko!”

Zochitika zasonyeza kuti kusintha kwenikweni kumayenera kuchitika m’kati mwa munthu, momwe ndi mumtima ndiponso m’maganizo a mkaidiyo, ndipo azisintha makamaka chifukwa cholapa zolakwa zake zakale kuchokera pansi pamtima. Kuphunzira Baibulo kungathandize munthu kudziŵa mmene Mulungu amaonera zinthu zoipa ndi kudziŵa chifukwa chake zili zolakwika. Motero angapeze zifukwa zokwanira zolekera kuchita zinthu zolakwikazo.

Mboni za Yehova zikuchita ntchito yophunzitsa Baibulo imeneyi m’ndende zambiri padziko lonse, ndipo zinthu zikuyenda bwino kwambiri. (Onani tsamba 10.) Mkaidi wina anati: “Atithandiza kuona zimene Baibulo limanena zokhudza cholinga cha moyo ndi madalitso amene anthu angapeze m’tsogolomu.” Anapitiriza kunena kuti: “Ameneŵa ndi maphunziro othandiza kwambiri!” Mkaidi winanso ananena kuti: “Tikuchita zinthu mogwirizana ndi zimene Mulungu amalangiza. . . . Tikuona kuti tayamba kusintha ndithu. Tayamba kudziŵa zinthu zofunika kwambiri m’moyo.”

Inde, sikuti anthu amayenera kusintha khalidwe kundende kokha. Njira yeniyeni yothetsera mavuto a ndende ndiyo kuthetsa kufunika kwa ndendezo. Choonadi china cha m’Baibulo chosangalatsa kwambiri chimene chakhudza mitima ya akaidi ambiri ndicho lonjezo la Mulungu lakuti: “Ochita zoipa adzadulidwa . . . Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:9, 29.

Zikadzatero, boma losawonongeka lomwenso ndi lachikondi komanso lolimba lidzalimbikitsa miyezo yapamwamba ya Mulungu. Ilo ndilo Ufumu wakumwamba wa Mulungu wolamulidwa ndi Kristu, ndipo ndilo boma limene Akristu aphunzitsidwa kulipempherera. (Mateyu 6:10) M’dziko latsopano limenelo, aliyense wokhalamo adzamusintha khalidwe mwa kuphunzira malamulo apamwamba kwambiri a Mulungu. Ndiyeno zidzakhaladi zoona kuposa n’kale lonse kuti “dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.” (Yesaya 11:9) Zikadzatere nanga zidzatha bwanji? Anthu osunga malamulo okhala m’dziko latsopanolo ‘adzakondwera nawo mtendere wochuluka.’—Salmo 37:11.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 10]

Mwayi Wokhala N’chiyembekezo

Kwa zaka zoposa 20, atumiki odzifunira a Mboni za Yehova akhala akuphunzitsa mfundo za m’Baibulo m’ndende ya ku Atlanta mu mzinda wa Georgia, ku United States of America. Panthaŵi imeneyo, akaidi oposa 40 athandizidwa kukhala Mboni za Yehova zobatizidwa, ndipo akaidi enanso oposa 90 apindula pophunzira Baibulo nthaŵi zonse.

Posachedwapa, alembi a Galamukani! analankhula ndi ophunzitsa Baibulo osiyanasiyana amene anagwira ntchito modzipereka m’ndende imeneyo.

N’chifukwa chiyani kuphunzira Baibulo kwathandiza kwambiri akaidi ena kusintha miyoyo yawo?

David: Akaidi ambiri ndi anthu omwe sanakondedwepo, ngakhale paubwana wawo. Ndiye akadziŵa kuti Mulungu amawakonda ndipo akamuuza zakukhosi m’pemphero, Mulunguyo n’kuyankha mapemphero awo, amakhulupirira kuti alikodi. Nawonso amayamba kum’konda tsopano.

Ray: Mkaidi wina amene ndinaphunzira naye Baibulo ankamuzunza ali mwana. Nditam’funsa chimene anakopekera ndi Yehova, anayankha kuti ukaphunzira choonadi cha m’Baibulo, umazindikira kuti Yehova amakumvetsadi. Zimenezi zinam’chititsa kulakalaka kudziŵa bwino umunthu wa Mulungu wachikondi woteroyo.

Ena anganene kuti akaidi amayamba kupemphera mongonamizira pofuna kuti awakhululukire milandu yawo kapena kungoti nthaŵi ibapita. Kodi inuyo mwaonapo zotani pamfundoyi?

Fred: Akaidi akabwera kudzaphunzira nafe, sitichita zinthu mwakuti atengeke mtima. Timangophunzira nawo Baibulo. Posakhalitsa, amadziŵa kuti akuphunzitsidwa Baibulo ndipo n’zimene timachita basi. Akaidi ena anandipeza n’kundipempha kuti ndiwathandize maganizo pankhani ya milandu yawo ku khoti. Sindikamba nawo zimenezo. Mapeto ake, amene amabwerabe kugulu lophunzira Baibulo kwanthaŵi yaitali ndithu amafunadi kuphunzira zimene Baibulo limanena.

Nick: Chinthu chimodzi chimene ndimaona ndicho mmene akaidi ena amasinthira akakhala m’ndende. Ena akhala atumiki obatizidwa ndipo avutika kwambiri chifukwa cha zochita za akaidi anzawo. Zimenezo n’zowavuta kwambiri. Baibulo lidakapanda kukhudza mitima yawo, sakanakhalabe okhulupirika m’mavuto oterowo.

Israel: Kwenikweni, ndi anthu ofunitsitsa kudziŵa Yehova, ndipo amaonetsa chidwi chawo m’njira yogwira mtima kwambiri. Mutha kuona kuti n’zochokera mumtima wawo.

Joe: Akaidi amene akhala Akristu enieni azindikira chimene chinapangitsa kuti moyo wawo usayende bwino. Azindikiranso kuti chiyembekezo chilipo. Ali nawo mwayi wokhala n’chiyembekezo. Tsopano akhoza kudikirira mokhulupirika kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Yehova a m’tsogolo.

N’chifukwa Chiyani Ndende Pazokha Sizingasinthe Apandu?

Joe: Si kuti cholinga chokhala ndi ndende n’kufuna kuti apandu akhalenso anthu abwino, koma kuti atalikirane ndi anthu ena onse. Vuto lagona pa mfundo imeneyi yokhudza cholinga cha ndende posunga anthu ameneŵa.

Henry: Ndende zikulephera kusintha mitima ya olakwaŵa. Akaidi ambiri amakachitanso milandu yomweyo akatuluka m’ndende.

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Akaidi ambiri athandizidwa kuphunzira choonadi cha m’Baibulo