Kodi N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kudziŵana ndi Agogo Anga?
Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kudziŵana ndi Agogo Anga?
“Ine ndi amayi tikayambana agogo ankatiyanjanitsa,” anatero Damaris.
“KUYAMBIRA kalekale, agogo ndiwo akhala othandiza pogwirizanitsa mabanja ndi kuwapatsa mwambo wa zachikhalidwe.” Dr. Arthur Kornhaber analemba choncho m’buku lake lakuti Grandparent Power! Ananenanso kuti: “Pokhala aphunzitsi, ochirikiza makolo, odziŵa bwino mbiri ya banja, osamala ndi kuteteza ana, olangiza, komanso osangalatsa, nzeru zawo, makhalidwe awo, ndi uzimu wawo zinali zofunika kwambiri. Ndinadzifunsa kuti, kaya zinatheka bwanji kuti mbadwo wathu uzinyalanyaza ntchito yaikuluyi imene agogo amachita?”
Kalekale, agogo amakhala nsanamira yabanja, makamaka kwa anthu olambira Yehova Mulungu. Baibulo linalamula Aisrayeli kuti achitire ulemu anthu okalamba ndi kuwaona monga ofunika. (Levitiko 19:32) Agogo ankaonedwa kuti ndiwo makamaka ali ofunika kulandira ulemu.—1 Timoteo 5:4.
N’zomvetsa chisoni kuti zinthu zasintha masiku ano. Nthaŵi zambiri anthu a mbumba imodzi amakhala motalikirana, ndipo achinyamata ambiri amaonana ndi agogo awo mwa apo ndi apo. Nawonso makhalidwe asintha. M’madera ambiri padziko lonse, anthu okalamba, ngakhale a pachibale, sakulandiranso ulemu wowayenera. (2 Timoteo 3:1-3) Kusamvana kumene ankati n’kochititsidwa chifukwa cha kusiyana mbadwo, kwafika poipiratu. Achinyamata ambiri amaona agogo awo ngati achikale osadziŵa zinthu za masiku ano. Sazindikira n’komwe kuti achikulire ameneŵa angathe kumvetsetsa zovuta zimene achinyamata amakumana nazo masiku ano.
Ngati mumaganiza choncho, konzekani kuganizapo mofatsa! Chifukwatu kudziŵa agogo anu, makamaka ngati amaopa Mulungu, n’kopindulitsa kwambiri. Ndipo ngati simuwadziŵa, mukumanidwa ndithu. Kodi mukumanidwa bwanji?
Anzeru Ndiponso Olangiza
Achinyamata ambiri azindikira kuti agogo angakhale ngati m’dambo mozimira moto panthaŵi ya zaka zovuta zaunyamata. Magazini yotchedwa Seventeen inanena kuti: “Chifukwa chokhala ndi moyo kwa zaka zambiri, nthaŵi zambiri agogo ndiwo amathandiza kwambiri pothetsa mavuto kuposa anzanu a msinkhu wanu, amene akuvutika ndi zovuta ngati zanu zomwe. Inu ndi anzanuwo mukuvutika ndi zinthu zinazake chifukwa n’kuyamba kuzichita m’moyo wanu, pamene agogo anu apyola mavuto Miyambo 16:31.
otero kambirimbiri. Nthaŵi zambiri amachita zinthu mwanzeru komanso modziŵa.” Malangizowa akungobwereza zimene Baibulo linanena zaka zambiri zapitazo kuti: “Imvi ndiyo korona wa ulemu, idzapezedwa [ikapezeka, NW] m’njira ya chilungamo.”—N’zoonadi kuti agogo anu anakulira m’moyo wosiyana ndi umene mukukhala panopo. Koma ndithudi nthaŵi inayake nawonso anavutikapo maganizo ngati mmene mukuvutikira panopo. Mungakhale musakudziŵa zochita kuti muthetse mavuto otero, koma agogo anu anadutsa momwemo n’kufika podziŵa kuthana nawo kwake. (Miyambo 1:4) “Kwa okalamba kuli nzeru, ndi kwa a masiku ochuluka luntha,” anatero Yobu munthu wolungamayo. (Yobu 12:12) Inde, ndipo pa chifukwa chimenecho agogo angakhaledi ofunika kwambiri ngati wachinyamata akufuna malangizo abwino, kum’limbikitsa, kapena kum’chirikiza.
Mwachitsanzo, Damaris ankakhala m’tauni inayake m’nyumba imodzi ndi agogo ake aakazi pamodzi ndi amayi ake. Damaris akukumbukira kuti, “Ine ndi amayi tikayambana, agogo ankatiyanjanitsa. Ankandithandiza kuganizapo mofatsa.”
Alexandria anali ndi vuto ngati lomwelo pamene kwawo anasamuka ndipo anafunika kusintha sukulu. “Mphunzitsi wanga watsopano anali wovuta ndipo ankangokwiyakwiya,” anatero Alexandria. Choncho zinali zovuta kuti Alexandria asinthe mogwirizana ndi sukulu yatsopanoyo. Komabe, agogo ake anakhaladi mnzake wom’thandiza. Anam’thandiza Alexandria kusintha mwa kum’limbikitsa kuona kuti panalibe vuto lenileni. “Tsopano sukulu ndimasangalala nayo ndiponso mphunzitsi wangayo ndikum’konda,” akutero Alexandria.
Wachinyamata wina ku Brazil dzina lake Rafael anafotokoza motere mmene agogo ake anam’thandizira atamaliza kosi yake: “Anandilangiza kwambiri za anthu ogwirizana nawo ndiponso mmene ndingapeŵere mavuto a mankhwala osokoneza bongo.” Tsopano Rafael ndi mlaliki wa nthaŵi zonse.
Eda LeShan akukamba zimene anachita ngati gogo m’buku lake la Grandparenting in a Changing World. Analemba kuti: “Tsiku lina mdzukulu wanga anandiitana n’kunena kuti, ‘Agogo, ndikufuna mundithandize kuti ndisamatengeke maganizo ndi zochita za anzanga.’ Anzake ena a kusukulu ankamufunira zibwenzi zachinyamata, ndipo ena mwa anyamatawa ankamuimbira foni.” Chifukwa chakuti mdzukulu wawoyu anapempha thandizo, agogowo anam’patsa malangizo othandiza. Inunso mungaone kuti kucheza pang’ono chabe ndi agogo okukondani kungakuthandizeni pamakhalidwe abwino enieni.
Nthaŵi zambiri agogo ndiwo amathandiza kwambiri panthaŵi yamavuto ogwa m’banja, ngati matenda kapena imfa. Abambo a mtsikana wina dzina lake Lacey atamwalira chifukwa chodwala kwambiri, agogo ake anam’thandiza kuti aiŵale. “Ndife ogwirizana tsopano kuposa m’mbuyomu,” anatero Lacey.
Kukondana Kwambiri
Mwina mungakhale omasukirana kwambiri ndi agogo anu pa mavuto ena amene nthaŵi zina achinyamata amapeza pokambirana ndi makolo awo. Kodi n’chifukwa chiyani Miyambo 17:6, Today’s English Version.
zingatheke kutero? Chifukwa china n’chakuti nthaŵi zambiri agogo amakondana kwambiri ndi adzukulu awo. Baibulo limati: “Okalamba amanyadira chifukwa cha zidzukulu zawo.”—Kumbukiraninso kuti makolo anu ndiwo ayenera kukhala ndi udindo waukulu wokulerani inuyo ‘m’maleredwe ndi chilangizo cha Yehova,’ osati agogo anu ayi. (Aefeso 6:4) Chifukwa chakuti udindo wawo ndi wochepa, mwina agogo anu angamakulekerereni kwambiri kuposa makolo anu. Komanso nthaŵi zambiri agogo satanganidwa ndi zosamalira maudindo ena ndiponso zovuta za m’banja za tsiku ndi tsiku. Chifukwa angakhale alibe mavuto oterowo, sizingavute kuti akuthandizeni pamavuto anu kapena kukulabadirani. Tom yemwe ali ndi zaka 17 akukumbukira mmene agogo ake onse anam’labadirira. Ankam’tumizira “timphatso akakhoza bwino kusukulu”; ankam’lipiriranso maphunziro ake a piyano.
Zoonadi, si agogo onse amene angathe kupereka mphatso zoterozo, koma angasonyezebe kuti amakukondani, mwina pokuyamikani ndi kukulimbikitsani kapena pokumvetserani nthaŵi ndi nthaŵi. Zimenezi zingakugwirizanitseni kwambiri. Pankhani yokhudza agogo ake Damaris ananena kuti: “Amandichititsa kukhala womasuka, ndipo ndikhoza kucheza nawo nthaŵi iliyonse chifukwa chakuti nthaŵi zonse amamvetsera mwachidwi, ngakhale ndikamanena zinthu zosamveka kwa iwo panthaŵiyo.” Wachinyamata wina dzina lake Jônatas, nayenso amalankhula momasuka ndiponso amakambirana nkhani zachikulu ndi agogo ake.
Kuthandizana
Agogo angakukondeni ndi kukugaŵirani nzeru, koma nawonso angapindule ndi mphamvu zanu zaunyamata ndiponso ubwenzi wanu. Zingakhale choncho bwanji? Ndithudi, mungathandize ndi kuchirikiza agogo anu m’njira zambiri. Nthaŵi zambiri agogo amakhala ofooka. Kapena mwina angakhale akuvutika ndi matenda. N’zosakayikitsa kuti mungawalimbikitse ngati mutawathandiza pogula zinthu ndi kuwagwirira ntchito zapanyumba.
Agogo ambiri ndi amasiye, ofedwa amuna kapena akazi awo ndipo nthaŵi zina amasukidwa. Powasamalira mwachidwi, mungawathandize kwambiri kuti asamasukidwe n’kumasangalalabe ndi moyo. Kuchita zimenezo ndi njira ina yomvera lamulo la m’Baibulo lakuti muyenera ‘kubwezera agogo anu, pakuti ichi n’cholandirika pamaso pa Mulungu.’—1 Timoteo 5:4, NW.
Ndithudi, mungakhutire ndi moyo wanu ngati muli womasuka ndi agogo anu, ndipo nawonso angateronso! Mwina simunamasuke nawo mpaka pano. Ndiye n’kutheka kuti mumafuna mutamamasuka nawo koma mukusoŵa poyambira. N’kuthekanso kuti mwina agogo anu amakhala kutali kapena kuti makolo anu analekana ndiye munatalikirana ndi agogo anuwo. Nkhani yotsatira idzafotokoza mfundo zina zothandiza pothetsa mavuto oterowo.
Ngati mungafune kudziŵa zambiri kapena kuti munthu wina aziphunzira nanu Baibulo panyumba panu kwaulere, lemberani ku Watch Tower, Box 30749, Lilongwe 3, Malaŵi, kapena ku adiresi yoyenerera pa maadiresi amene ali patsamba 5.
[Chithunzi patsamba 31]
Agogo angakumvetseni mukamawalankhula ndiponso angakulangizeni ndi kukuchirikizani
[Chithunzi patsamba 32]
Muziwathandiza agogo anu