Kodi Tsogolo la Chipembedzo N’lotani?
Kodi Tsogolo la Chipembedzo N’lotani?
M’MAYIKO amene kale anali mu Soviet Union chipembedzo chayambiranso mwamphamvu. Ku Russia kokha, theka la anthu amati ndi atchalitchi cha Orthodox, ndipo anthu mamiliyoni ambiri amatsatira zipembedzo zina molimba. Zina mwa zipembedzo zakale ndizo Chisilamu, Chiyuda, ndi Chibuda, ndipo Mboni za Yehova nazo n’zakale ndithu kumeneku.
Kale mu 1891, nthumwi za Ophunzira Baibulo, dzina la Mboni za Yehova isanafike 1931, zinayendera mzinda wa Kishinev ku Russia (tsopano ndi Chisinau, ku Moldova). Kumeneko anachita misonkhano ndi okhulupirira anzawo. Mu 1928, George Young, amene anali nthumwi yapadera ya Ophunzira Baibulo, anakumana ndi akuluakulu a boma la Soviet Union mumzinda wa Moscow ku Russia, pofuna chilolezo chofalitsira mabuku a Baibulo. Pambuyo pake Mboni zinadziŵika kwambiri chifukwa cha zimene a Soviet Union amayesa kuchita kuti azithetseretu.
Pamene Soviet Union inatha mwadzidzidzi zaka pafupifupi khumi zapitazo, anthu anayamba kufunsa kuti, ‘Kodi n’chifukwa chiyani boma la Soviet Union limafuna kuthetsa chipembedzo?’ Anthu ambiri amene anaphunzitsidwa kwa zaka zambiri kuti kulibe Mulungu anayamba kufuna kudziŵa ubwino wa chipembedzo. Kodi Baibulo, buku limene analiletsalo, lingathandize pamavuto amene anthu amakumana nawo? Anthu a ku Russia anayamba kudzifufuzira paokha.
Vuto Lina la Chipembedzo
Chifukwa chakuti anthu ambiri anachita chidwi ndi Baibulo, ku Soviet Union wakale kunabuka vuto lina. Nyuzipepala ina ya ku London, England yotchedwa The Guardian, chaka chatha inati: “Mwina ‘kukangana ndi Mulungu’ kunathadi, koma patha zaka khumi zokha dziko lokana Mulungu poyerali litagonja mochititsa manyazi ndipo mwina tsopano ku Russia kwayambika kukangana kwa zipembedzo.” Kodi kukangana kwa zipembedzo kumene nyuzipepalayi ikunena ndi chiyani?
Monga tanenera m’nkhani ya m’mbuyo ija, tchalitchi cha Russian Orthodox chinali paubwenzi wa ponda apa m’pondepo ndi boma la Soviet Union n’cholinga choti lisachiletse komanso kuti lizichikondera. Magazini ya The Guardian ikulongosola mmene ubwenziwo ukuyendera ponena kuti: “Pa zaka khumi zapitazi tchalitchichi chakhala paubwenzi wonyanyira ndi boma lomwe linkachipondereza lija, ndipo nthaŵi ndi nthaŵi chimathandiza boma la Russia (monga pankhondo ya ku Chechnya) ndipo potero chimapeza mphamvu pandale.”
Nyuzipepala ya Los Angeles Times ya pa February 10, 1999, inasonyeza mmene tchalitchichi chinagwiritsira ntchito mphamvu zake pandale ponenapo za Lamulo la Ufulu wa Chikumbumtima ndi Chipembedzo. Nyuzipepalayi inati lamuloli, limene pulezidenti wapanthaŵiyo Boris Yeltsin anasaina mu September 1997, “amene analilimbikitsa ndi a tchalitchi cha Russian Orthodox.” Lamulolo linakondera tchalitchichi pamodzinso ndi Chisilamu, Chiyuda ndi Chibuda ponena kuti zinali zipembedzo “zodziŵika.” Ina mwa mfundo za m’lamuloli inali yakuti magulu achipembedzo a ku Russia ayenera kulembetsanso kuboma.
Nyuzipepala ya The New York Times ya pa February 11, 1999, inanena kuti atakhazikitsa lamulo limeneli, “tchalitchi cha Orthodox chinayamba kuvutitsa matchalitchi omwe chimawayesa adani ake.” Nyuzipepalayi inapitiriza kunena kuti: “Mwezi wa August wapitawu,
Aleksei II, mtsogoleri wa tchalitchi cha Russian Orthodox, anati zipembedzo zonse zosintha anthu mitima, makamaka zimene zimayesa kunyengerera anthu kuchoka ‘m’zipembedzo za makolo awo’ aziletse.” Kuyambira nthaŵi imeneyo, ayesabe kuletsa zipembedzo zimene akuti n’zosintha anthu mitima, ndipo zimenezi zayambitsa khalidwe limene ena akuti “mkangano wa zachipembedzo.”Ena mwa Ozondedwa
Gulu la Mboni za Yehova ndi gulu lina limene a tchalitchi cha Russian Orthodox aliukira kwambiri. Pa June 20, 1996, ofesi ya ku Moscow yozenga milandu inayamba kuzenga mlandu woperekedwa ndi Komiti Yoteteza Ana ku Zipembedzo Zonyenga yomwe imadana ndi zipembedzo zosadziŵika bwino. Ngakhale kuti mlanduwu ankauimitsa nthaŵi ndi nthaŵi chifukwa chakuti panalibe umboni uliwonse wakuti Mboni zinaphwanya lamulo, nthaŵi zonsezo amauyambitsanso.
Zili chomwecho, anayamba kufalitsa mabodza osaneneka onamizira Mboni. Nyuzipepala ya ku Russia ya Komsomolskaya Pravda, yomwe amaifalitsa makope 1,200,000, inanena m’kope lake la pa November 21, 1998 kuti: “Pa zaka ziŵiri zokha, tchalitchi cha Russian Orthodox chatulutsa mabuku opitirira khumi komanso mabulosha, ndi timabuku zofotokoza makamaka gulu la okhulupirira Yehova ameneŵa.” N’chifukwa chiyani tchalitchichi chikulimbikira kunyoza Mboni?
Nyuzipepala ya Komsomolskaya Pravda inapitiriza kunena kuti “mosakayika, chifukwa chachikulu kwambiri n’chakuti anthu m’gululi achulukana moŵirikiza nthaŵi khumi patangotha zaka zisanu ndi ziŵiri, koma tchalitchi cha Russian Orthodox, sichikonda opikisana nacho monganso amachitira magulu onse odziona ngati apamwamba koposa.”
Mlandu wa Mboni unadziŵika padziko lonse pamene anayambanso kuuzenga kumayambiriro kwa 1999. Mutu wina wa nkhani m’nyuzipepala ya The New York Times ya pa February 11 unati: “Khoti la ku Moscow Lipenda Lamulo Loletsa Mboni za Yehova.” Nkhani yake inati: “Mlanduwu umene akuuzenga m’khoti laling’ono ku Moscow, m’kachipinda kakang’ono, magulu achipembedzo ndiponso olimbikitsa ufulu wachibadwidwe akuutsatira mwachidwi pakuti aka n’koyamba kuti [Lamulo la Ufulu wa Chikumbumtima ndi Chipembedzo] ayese kuligwiritsa ntchito poletsa kupembedza.”
Pulezidenti wa gulu la International Helsinki Federation loona za ufulu wachibadwidwe, Lyudmila Alekseyeva, analongosola chimene chinachititsa kuti mlandu wa Mboniwu ena aziutsatira mwachidwi chonchi. Iye anati ngati amene akuyesa kupondereza Mboni za Yehova“atapambana pamlanduwu,” ndiye kuti “adzapeza mphamvu zolimbana ndi magulu enanso” amene amawaona ngati si zipembedzo zodziŵika. Komabe mlanduwu anauimitsanso pa March 12, 1999. Koma mwezi wotsatira, pa April 29, Unduna wa Zachilungamo wa ku Russia unapereka chikalata cholembetsa “Ofesi Yoyang’anira Mipingo ya Mboni za Yehova mu Russia.”
Ngakhale kuti akudziŵika ndi boma, Mboni pamodzi ndi magulu ena aang’ono achipembedzo akuwaukirabe ku Russia ndi kumayiko ena amene kale anali mu Soviet Union. Lawrence Uzzell, woyang’anira Keston Institute ku Oxford, England, anati “kuchita chidwi ndi nkhani zokhudza Mboni za Yehova kumathandiza” chifukwa zimene zimawachitikira zimakhala “chenjezo.” N’zoonadi kuti zimenezi zingalanditse anthu miyandamiyanda ufulu wawo wofunika wachipembedzo!
Awaukira Popanda Chifukwa Chomveka Bwino
M’zaka za zana loyamba, akulu a ansembe ndi atsogoleri ena achipembedzo anazunza otsatira a Yesu. (Yohane 19:15; Machitidwe 5:27-33) Motero, Chikristu anachinenera izi: “Pakuti za mpatuko uwu, tidziŵa kuti aunenera ponseponse.” (Machitidwe 28:22) Motero, sitiyenera kudabwa masiku ano Akristu oona akamadedwa, monga zachitikira kwa Mboni za Yehova.
Koma, Gamaliyele, Mfarisi wotchuka ndiponso mphunzitsi wa Chilamulo atapenda maumboni a mlandu wa Akristu oyambirirawo, analangiza kuti: “Lekani anthu ameneŵa, nimuwalole Machitidwe 5:38, 39.
akhale; pakuti ngati uphungu umene kapena ntchito iyi ichokera kwa anthu, idzapasuka; koma ngati ichokera kwa Mulungu simungathe kuwapasula; kuti kapena mungapezeke otsutsana ndi Mulungu.”—Masiku anonso anthu ofufuza apenda Mboni za Yehova mosamalitsa. Kodi apeza zotani? Sergey Blagodarov, amene amanena yekha kuti ndi watchalitchi cha Orthodox, ananena mawu aŵa m’nyuzipepala ya Komsomolskaya Pravda: “Pazaka zoposa [100], palibe dziko ngakhale limodzi limene lapereka umboni uliwonse wakuti anthu a m’gululi anaphwanya lamulo, kapena kuti malinga ndi malamulo gululi silifunikira kukhalapo.”
Kodi Tsogolo la Chipembedzo N’Lotani?
Baibulo limanenapo za “mapembedzedwe oyera ndi osadetsa.” (Yakobo 1:27a) Monga nkhani yam’mbuyo ija yasonyezera, Baibulo limatcha ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga “mkazi wachigololo wamkulu . . . amene mafumu a dziko anachita chigololo naye.” Hule wachipembedzo wophiphiritsayu wotchedwa ‘Babulo Wamkulu’ akuti ali “woledzera ndi mwazi wa oyera mtima.”—Chivumbulutso 17:1-6.
Mawu aŵatu akugwirizanadi ndi zipembedzo zimene zagwirizana mwathithithi ndi atsogoleri andale zadziko n’cholinga chofuna kuti zinthu ziziwakomera! Komatu zimene zichitikire hule wachipembedzoyu m’tsogolo muno n’zotsimikizika. Baibulo limati: ‘Miliri yake idzadza m’tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi njala; ndipo adzapserera ndi moto; chifukwa Ambuye Mulungu woweruza ndiye wolimba.’ N’chifukwa chake chenjezo la mngelo lakuti: “Tulukani m’menemo . . . kuti mungalandireko ya miliri yake” tiyenera kulilabadira mwamsanga!—Chivumbulutso 18:4, 7, 8.
Wophunzira Yakobo analongosola “mapembedzedwe oyera” kuti ndi ‘kusachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.’ (Yakobo 1:27b) Ndiponsotu, Yesu Kristu ananena za omutsatira kuti: “Siali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi.” (Yohane 17:16) Choncho kodi mukuona chimene Mboni za Yehova zimakanira kuloŵerera nkhani zodetsa zandale? Zimatero chifukwa zimakhulupirira ndi mtima wonse lonjezo la Baibulo lakuti: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.”—1 Yohane 2:17.
[Chithunzi patsamba 23]
Kuzenga Mlandu ku Moscow mu February 1999. Oimbidwa mlandu ndi loya wawo (kumanzere), woweruza (pakati), oimba mlandu ndi loya wawo (kumanja)
[Chithunzi patsamba 23]
Baibulo limalongosola tsogolo la zipembedzo zonse