Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kusefukira kwa Madzi ku Mozambique—Momwe Akristu Anasamalira Anthu Ovutikawo

Kusefukira kwa Madzi ku Mozambique—Momwe Akristu Anasamalira Anthu Ovutikawo

Kusefukira kwa Madzi ku Mozambique—Momwe Akristu Anasamalira Anthu Ovutikawo

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU MOZAMBIQUE

KUMAYAMBIRIRO kwa chaka chatha anthu oonera wailesi yakanema anagwidwa nthumanzi ndi zithunzi za anthu ku Mozambique ali m’mitengo pothaŵa madzi osefukira. Mayi wina anaberekera mu mtengo ndipo anthu anamuona pakanemapo akum’nyamula pamodzi ndi mwana wakeyo kupita kotetezeka. Komabe anthu ambiri, anasoŵa chochita kwa masiku angapo—ena anakhala ndi njoka mpaka madzi ataphwera kapena helikoputala itawapulumutsa.

Vutoli linayamba ndi mvula yamvumbi imene inagwa ku Maputo, likulu la dziko la Mozambique. M’maola ochepa chabe madera onse oyandikana ndi mzindawu anali atasefukira. M’madera ena, madzi anafika mpaka kumadenga a nyumba. Misewu inasanduka mitsinje ikuluikulu. Madzi anakumba ngalande ndipo nyumba ndi galimoto tingoti chilichonse chinakokoloka. Koma zoopsa zinali zili m’njira.

Mvula inapitirira ndipo madzi anasefukira m’dera lonse la kumwera kwa dzikoli. Mvula inavumbanso m’mayiko oyandikana ndi dzikoli monga ku South Africa, Zimbabwe ndi Botswana. Chifukwa chakuti mitsinje ya Incomati, Limpopo, ndi Zambezi ya m’mayiko ameneŵa imadutsa m’Mozambique popita kunyanja, madera ambiri a Mozambique anawonongeka mitsinje imeneyi itasefukira. Njira yomwe Akristu anasamalirana nthaŵi ya vutoli ndi nkhani yolimbikitsa chikhulupiriro.

Kufufuza Zoyambirira Kuwonongeka

Chaka chatha pa February 9, anthu aŵiri oimira ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Maputo anapita kumpoto. Cha m’ma 9.00 koloko m’maŵa anadutsa mzinda wa Xinavane, kumene Mtsinje wa Incoluane unali utadzaza kwambiri. Anaganiza zokafika ku Xai-Xai, komwe ndi likulu la chigawo cha Gaza. Koma anapeza kuti pafupi ndi mzinda wa Chókwè, kumene kumakonda kusefukira kukagwa mvula ya mkuntho, kunalibe vuto lililonse. Choncho anaganiza zobwerera ku Maputo.

Komano pobwerera, atayandikira ku Xinavane apolisi anawaimitsa. Anawachenjeza kuti: “Madzi amene asefukira ku South Africa afika kuno ndipo atseka misewu yaikulu. Mabasi kapena galimoto zazikulu sizikudutsa.” Msewu womwe anadutsa tsikuli m’maŵa tsopano unali utamiriratu! Poti mitsinje ya kumpoto inalinso kudzaza, maloŵa anatalikirana ndi malo ena a dzikoli.

Aŵiriŵa anaganiza zogona ku Macia. Usiku umenewo zinthu sizinalinso bwino. Mzinda wonse wa Xinavane unali utasefukira madzi, ndipo zinthu zonse zinawonongeka. Anakonza zothandiza Mboni za m’derali kupita ku Nyumba ya Ufumu ya ku Macia, kumene kunali msasa wongoyembekezerapo. Mbonizo zinathamanga kukagula zinthu zofunika kwambiri monga mpunga, nyemba, fulawo ndi mafuta.

Tsopano anayamba kuganiza za Akristu anzawo a ku Chókwè komanso mizinda ina yapafupi. Oyang’anira mipingo a ku Chókwè anachita msonkhano ndipo anagwirizana zosamutsa anthu onse. Anafalitsa uthenga wakuti: “Thaŵani kuno, pitani ku Macia!” Ndipo, posapita nthaŵi analandira uthenga wakuti anthu ambiri a ku Xinavane anali asanafike. Choncho anatumako Mboni kukaona momwe zinthu zinalili. Anamvanso kuti mkulu wina wachikristu anamira m’nyumba yake. Anakonza zoika maliro, ndipo Mboni zonse anazipeza, zina zili padenga ndipo anapita nazo ku Macia.

Atatha kuyendetsa zimenezi, oimira nthambiwo anapita ku Bilene, mzinda waung’ono wakugombe, kumene anakakwera ndege kupita ku Maputo. Kulikonse kumene anthuŵa amaona kunali madzi okhaokha. Akuti chigawo cha Gaza chokha chinali ndi anthu 600,000 amene anali m’vutoli.

Vutoli Likula

Masiku angapo otsatira, mvula inalimbikira ndipo zigawonso za pakati ku Mozambique zinawonongeka. Kenako kunawomba mphepo yamkuntho yotchedwa Eline. Pa February 20 inabweretsa mvula yoopsa kuchigawo cha Inhambane, Sofala ndi Manica. Chifukwa cha kuchuluka kwa madzi, anthu ambiri anafa ndiponso zinthu zambiri zinawonongeka.

Ndiyeno chakumapeto kwa February, mzinda wa Chókwè ndiponso chigawo chonse choyandikana ndi mzindawu madzi anasefukira kwambiri mwanjira imene sinachitikepo. Loŵeruka pa February 26 chapakati pa usiku, madzi osefukira anafika mwamkokomo, nakokolola chilichonse kumene amadutsa. “Anandidzutsa ndi mnansi wanga yemwe ankafuula pawindo,” akutero Luis Chitlango, Mboni ya zaka 32.

Chitlango anati: “Nditadzuka pabedi, ndinamva mkokomo wa madzi. Pothaŵa tinakumana ndi njoka zambiri. Cha m’ma sikisi koloko, tinafika pamtunda, koma pambuyo pake m’maŵa womwewu madzi atakwera mbali zonse, tinakwera mu mtengo. Tinalipo anthu 20.

“Amuna ndiwo anayamba kukwera m’mitengo. Ndiyeno azimayi anaperekera ana kwa amunawo, akatero amamangirira anawo kunthambi. Omalizira kukwera anali azimayi ndi makanda awo. Nthaŵi zambiri timatsika m’mitengomo ndi kumayambasa m’madzi kufunafuna mtedza, umene ankalima m’deralo.

“Patatha masiku atatu tonse tinaganiza zopita ku Chókwè. Madzi anali kufika m’chifuŵa, ndipo tinalimbana ndi mphamvu ya madzi othamangawo. Tili m’njira tinapeza anthu ambiri ali m’mitengo ndi padenga. Tsiku lotsatira madzi anali ataphwera moti galimoto zazikulu zimafika mu mzindawu kutenga anthu kupita nawo ku Macia.”

Msasa wa Mboni Zothaŵa Kwawo

Pa March 4 ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova inachita hayala ndege kukasiya oimira ake kudera losefukira madzilo. Anthu ambiri anali atathaŵira ku Macia, kumene kunali msasa waukulu wa othaŵa kwawo. Ambiri okhudzidwa ndi vutoli anadwala chimfine, matenda osoŵa chakudya m’thupi, malungo, ndi matenda ena.

Zinkaoneka ngati kuti kuli nkhondo. Mu mzindawu, mahelikoputala ochokera m’mayiko osiyanasiyana anali balalabalala mu mlengalenga ndipo ankatera pamalo omwe anakoza n’kumatsitsa katundu. Gulu la Mboni lopereka thandizo litafika ku Macia, sanangogaŵira anthuwo chakudya komanso anatsegula kachipatala. Koma, anayamba apempha kaye chilolezo kwa akuluakulu a boma amene anayamikira kwambiri zimenezo.

M’maŵa uliwonse nthaŵi ya 6.30 a.m. kumsasa wa Mboni, umene unali ndi Mboni 700 komanso ndi anthu ena, ankakambirana lemba la m’Baibulo. Alongo achikristu akakonza chakudya, amaitana mayina a mitu ya mabanja. Aliyense anali kukweza zala kusonyeza nambala ya mbale ya zakudya zimene akufuna ndiyeno anali kuwapatsa chakudyacho.

Mu msasawu zonse zofunika pa moyo wa munthu zinali kuyenda bwino. Anthu ena anapatsidwa ntchito yogula chakudya; ena yosamalira madzi akumwa, kuyeretsa zimbudzi ndi zina zotero. Akuluakulu a boma anachita chidwi ndi momwe zinthu zinali kuyendera, ndipo anati: ‘Malo ano ndiwo ofunika kukhalako. Palibe amapereŵera chakudya ndiponso sakangana.’ Nduna ina ya boma kumeneko inati: ‘Aliyense apite kumsasa wa Mboni kukaona mmene zinthu ziyenera kukhalira.’

Tsiku lina komiti yopereka chithandizo inasonkhanitsa akulu achikristu ndi kuwadziŵitsa kuti ofesi ya nthambi yakonza zomanganso nyumba ndi Nyumba za Ufumu komanso kupereka zinthu zina zofunika kwa anthu amene vutoli lawakhudza. Tsiku lotsatira pokambirana lemba la tsikulo la m’Baibulo, analengeza nkhaniyi. Anthu anaomba m’manja nthaŵi yaitali.

Ngakhale kuti boma linapereka matenti akuluakulu aŵiri, ambiri pamsasapo ankagona panja. Choncho anasankha anthu pa gululi oti amange Nyumba ya Ufumu yaikulu pamalo a mpingo wa m’deralo. Inamangidwa ndi mabango ndiponso malata—mmene amamangira nyumba za ku Mozambique—kuti muzikhala anthu 200. Inamangidwa masiku aŵiri okha!

Kufunafuna Anthu Akutali

Pa March 5, madzi ataphwera ndithu, anakhazikitsa gulu lopereka chithandizo kuti lipite ku tauni ya Aldeia da Barragem, kuchimodzi mwa zigawo zoyambirira kusefukira madzi. Kunali mpingo wa Mboni 90 koma sikunamveke zilizonse zokhudza abale ameneŵa.

Gululi lili paulendo linadutsa Chihaquelane, msasa waukulu wa anthu pafupifupi 100,000. Mu mzindawu mbali zonse za mseŵu, umene unali ndi malo ena okokoloka, kunali madzi okhaokha. Wina pagululi anati: “Titafika ku Chókwè, kunali bwinja. Madzi anali adakafikabe kudenga m’nyumba zambiri m’mphepete mwa tauni. Nyumba zambiri zinali zitamira. Kunayamba kuda koma kunali kutatsala makilomita 25 kuti tikafike ku Aldeia da Barragem.”

Gululo linafika usiku komwe limapita. Wina pagululi akukumbukira kuti: “Tinaima ndipo tinangoti zii, kusoŵa chochita.” Kenako anthu anatulukira, akukuwa kuti: “Abale!” ndipo panali phokoso la chisangalalo. Ataona magetsi a galimoto ziŵiri, Mboni kumeneko zinadziŵiratu kuti ayenera kukhala abale awo, ndipo anauzako anzawo. Amene anaona izi anachita chidwi kwambiri, akumati: ‘Anthu aŵa amakondanadi. Amabweretsa chakudya komanso amabwera kudzawaona!’

Apitiriza Kuwasamalira

Abale a ku Aldeia da Barragem anawapititsa ku msasa wa ku Macia, kumene analandira chakudya, malo ogona ndi mankhwala. Nthaŵi imeneyi, ku Macia zinthu zinali kuipiraipira. Zinthu monga chakudya, mankhwala, ndi zophikira zinali zosoŵa, popeza zinkachita kubwera pandege. Pankafunika kwambiri kukonza msewu wa ku Maputo. Mmene March 8 imafika anali atachita zimenezi.

Mzinda waukulu wa Xai-Xai unali utasefukiriratu ndi madzi. Malo ena ku likulu la mzindawu kunali kodzaza madzi mpaka mamita atatu! Mboni zinakhazikitsa komiti yopereka chithandizo kuti isamalire abale awo kumeneko. Kuphatikiza apo, anakhazikitsa makomiti kuti asamalire anthu ovutika a kuchigawo cha Sofala ndi Manica.

Mboni za m’mayiko ena zinapereka chithandizo. Mwachitsanzo, nthambi ya South Africa inatumizako matani a zovala, mabulangete ndi zinthu zina. Ndipo kulikulu la padziko lonse la Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York, anapereka ndalama zothandizira anthu okhudzidwa ndi tsokalo.

Madzi ataphwa mokwanira ndiponso ataŵerenga anthu amene nyumba zawo zinawonongeka, anayamba ntchito yomanganso nyumba ndi Nyumba za Ufumu. Anakhazikitsa komiti yomanga imene inathandizidwa ndi anthu ambiri odzifunira, amene anayamba kugwira ntchito nthaŵi yomweyo. Kuyambira nthaŵi imeneyi nyumba zoposa 270 ndi Nyumba za Ufumu zosachepera zisanu zatha kukonza.

Nyumba zoyambirira kumangidwa ndi antchito odzifunira a Mboni zitayamba kukwera, anthu anachita chidwi. Wachinansi wina anati: ‘Mumalambira Mulungu wamoyo. Apasitala athu sazikumbukira nkhosa zawo zimene zikuvutika. Koma inu akukumangirani nyumba zabwino ngati zimenezi.’ M’madera ameneŵa anthu ambiri alabadira uthenga wa Ufumu umene Mboni za Yehova zimalalikira, ndipo ayambitsa maphunziro a Baibulo angapo.—Mateyu 24:14; Chivumbulutso 21:3, 4.

Ngakhale Mboni zambiri zinataya katundu wawo wochuluka, palibe anataya chikhulupiriro. M’malo mwake, chikhulupiriro chawo mwa Yehova Mulungu ndi mwa gulu lonse la okhulupirira anzawo padziko lonse chinalimba. Akuthokoza abale awo achikondi padziko lonse, amene anathandiza mwachangu vutoli litawagwera. Aona okha chisamaliro, chitetezo ndi chikondi cha Yehova, ndipo amakumbukira nthaŵi zonse mawu a m’Baibulo akuti: “Yehova ndiye wamkulu.”—Salmo 48:1.

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Madzi amatope anadzaza mzinda wa Xai-Xai

[Chithunzi patsamba 25]

Anatumiza chithandizo pandege

[Chithunzi patsamba 26]

Gulu la Mboni lopereka chithandizo linatsegula kachipatala

[Chithunzi patsamba 26]

Akupitiriza kumanga nyumba zatsopano

[Chithunzi patsamba 26]

Msasa waukulu wa anthu othaŵa kwawo unali ndi anthu 100,000