Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Zipembedzo Zinapulumukira

Mmene Zipembedzo Zinapulumukira

Mmene Zipembedzo Zinapulumukira

PAMENE dziko la Germany lolamulidwa ndi chipani cha Nazi linaloŵerera m’dziko la Russia mu June 1941, boma la Soviet Union linali litachotseratu tchalitchi cha Russian Orthodox. Koma a Nazi atachoka, boma la Soviet Union linayamba kusintha maganizo ake pa zachipembedzo. Kodi n’chiyani chinalichititsa kutero?

Richard Overy, pulofesa wa mbiri yamakono pa King’s College ku London, analongosola chifukwa chake m’buku lake lakuti Russia’s War—Blood Upon the Snow. Iye anati: “Bishopu Sergei, amene anali mtsogoleri wa Tchalitchichi, anapempha okhulupirira onse tsiku limene asilikali a Germany analoŵa m’dzikomo kuti ayesetse kuchita chilichonse kuti apambane. M’zaka ziŵiri zotsatira iye anafalitsa makalata pafupifupi makumi aŵiri ndi atatu, olimbikitsa nkhosa zake kuti zimenyere nkhondo dziko lawo lokana Mulungu.” Motero, malinga ndi kunena kwa Overy, ‘Stalin analola kuti zipembedzo zipitirire.’

Mu 1943, Stalin anafika mpaka pololeza tchalitchi cha Orthodox mwa kusankha Sergius kuti akhale mtsogoleri wake watsopano. Overy anati: “Zimenezi zinachititsa akuluakulu a Tchalitchicho kupemphetsa ndalama kwa okhulupirira awo kuti alipirire gulu la asilikali a Soviet Union omenya nkhondo pagalimoto za zida. Abusa ndi mabishopu analimbikitsa mipingo yawo kuti izitsatira chikhulupiriro cha Mulungu komanso cha Stalin.”

Polongosola nyengo imeneyi m’mbiri ya Russia, katswiri wa zachipembedzo wa ku Russia, Sergei Ivanenko analemba kuti: ‘Buku lofalitsidwa ndi tchalitchi cha Russian Orthodox, lakuti The Journal of the Moscow Patriarchate, linatama Stalin pomutcha mtsogoleri ndi mphunzitsi woposa onse m’mbiri yonse, ndiponso m’mayiko onse, wotumidwa ndi Mulungu kuti apulumutse dzikolo kwa anthu otsendereza, enimalo, ndiponso enichuma. Linalimbikitsa okhulupirira kufera kunkhondo poteteza USSR kwa adani ake ndi kuti achite zonse zotheka kuti alimbikitse ndale za Chikomyunizimu.’

“Amene a KGB Anawakonda Kwambiri”

Ngakhale nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse itatha mu 1945, tchalitchi cha Orthodox chinali kuthandizabe Chikomyunizimu. Buku lakuti The Soviet Union: The Fifty Years, lolembedwa ndi Harrison Salisbury, linavumbula mmene zinachitikira ponena kuti: “Nkhondoyo itatha, atsogoleri a matchalitchi anagwirizana ndi mfundo zonse za Stalin zokhudza mayiko akunja okangana ndi dziko lawo.”

Buku laposachedwapa la The Sword and the Shield linalongosola mmene atsogoleri a matchalitchi anatsatirira zofuna za boma la Soviet Union. Limati mtsogoleri Alexis I, amene analoŵa m’malo mwa Sergius mu 1945, “analoŵa nawo m’bungwe la World Peace Council logwirira ntchito boma la Soviet Union limene anakhazikitsa mu 1949.” Bukulo limanenanso kuti iyeyu pamodzi ndi bishopu Nikolai “a KGB [Gulu Loona za Chitetezo cha Boma la Soviet Union] anawakonda kwambiri monga anthu olimbikitsa ena kumvera boma.”

Motero, mu 1955, mtsogoleri Alexis I anati: “Tchalitchi cha Russian Orthodox chimavomereza mfundo zamtendere za boma lathu zokhudza mayiko akunja, osati chifukwa chakuti tchalitchichi chikusoŵa ufulu, koma chifukwa chakuti mfundo za Soviet Union n’zachilungamo ndiponso n’zogwirizana ndi mfundo zachikristu zimene tchalitchi chathu chimalalikira.”

Magazini ya ku London, England yotchedwa The Guardian ya pa January 22, 2000, inati wansembe wina wopanduka wa tchalitchichi, Georgi Edelshtein ananena kuti: “Mabishopu onse anasankhidwa mosamala zedi kuti azithandizana ndi boma la Soviet Union pantchito zake. Mabishopu onse anali akazitape a bungwe la KGB. N’zodziŵika ndithu kuti mtsogoleri Alexy anaikidwa pa udindowu ndi gulu la KGB, ndipo anam’patsa dzina lakuti Drozdov. Masiku ano, mabishopuwa sanasiyebe ndale zimene ankachita zaka 20 kapena 30 zapitazo.”

Wotumikira Boma la Soviet Union

Posimba za ubwenzi wa tchalitchi cha Orthodox ndi boma la Soviet Union, magazini ya Life ya pa September 14, 1959, inanena mawu akuti: “Stalin anapereka ufulu ku zipembedzo, ndipo matchalitchi anam’patsa ulemu ngati wa mfumu. Anaika unduna wapadera wa boma umene umaonetsetsa kuti tchalitchi cha Orthodox chikugwirizanabe ndi boma ndipo kuchokera pamenepo chipani cha Chikomyunizimu chagwiritsa ntchito tchalitchichi monga mbali ina ya boma la Soviet Union.”

M’buku lake la mu 1956, lotchedwa The Church in Soviet Russia, Matthew Spinka, wodziŵa bwino nkhani za matchalitchi a ku Russia, anavomereza kuti n’zoona kuti tchalitchichi ndi boma anali paubwenzi wa ponda apa m’pondepo. Iye analemba kuti: “Mtsogoleri watsopanoyu Alexei, wasandutsira dala tchalitchichi kukhala mbali ya boma.” Inde, tchalitchi cha Orthodox chinapulumuka chifukwa chotumikira boma. Koma mwina mungafunse kuti, ‘Kodi kutero n’kulakwa?’ Chabwino, taganizirani mmene Mulungu ndiponso Kristu amaonera nkhaniyi.

Yesu Kristu ananena izi kwa ophunzira ake oona: “Simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi.” Ndipo Mawu a Mulungu amafunsa funso mosapita m’mbali kuti: “Akazi achigololo inu, kodi simudziŵa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu?” (Yohane 15:19; Yakobo 4:4) Motero, malingana ndi mmene Baibulo limanenera, tchalitchichi chinadzipangitsa kukhala mkazi wachigololo wa chipembedzo amene “mafumu a dziko anachita chigololo naye.” Chasonyeza kuti chili mbali ya amene Baibulo limamutcha kuti ‘Babulo Wamkulu, amayi wa achigololo ndi wa zonyansitsa za dziko.’—Chivumbulutso 17:1-6.

Mmene Mboni Zinapulumukira

Mosiyana ndi zimenezi, Yesu Kristu anavumbula mmene otsatira ake oona adzadziŵikire, ponena kuti: ‘Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.’ (Yohane 13:35) Chikondi chimenechi chinathandiza kwambiri kupulumutsa Mboni m’dziko lakale la Soviet Union, monga mmene nkhani yotsatirayi yolembedwa m’buku lakuti The Sword and the Shield ikusonyezera. “M’njira zosiyanasiyana anthu a Yehovawa amathandiza anzawo okhala m’misasa [ya ukaidi], ndipo amawapatsa ndalama, chakudya ndi zovala.”

China mwa “chakudya” chimene ankapereka kwa okhala m’makampu a ndende chinali chauzimu, mabaibulo ndi mabuku olongosola Baibulo. M’Baibulo muli ‘mawu a Mulungu,’ amene Yesu anati timafunikira kuti tisunge moyo wathu wauzimu. (Mateyu 4:4) Mabukuwa anali kuwaloŵetsa m’kampu chozemba ndipo anali kuika moyo pachiswe, chifukwa munthu aliyense akangogwidwa akutero ankalangidwa moopsa.

Helene Celmina, wa ku Latvia, anamangidwa m’ndende ya Potma ku Russia kuchokera mu 1962 mpaka mu 1966. Iye analemba buku lotchedwa Women in Soviet Prisons, mmene analongosolamo kuti: “Mboni za Yehova zambiri ankazilamula kukhala m’ndende kwa zaka khumi zikugwira ntchito yakalavula gaga chifukwa chakuti m’nyumba zawo munali magazini ochepa chabe a Nsanja ya Olonda. Popeza anthu ankamangidwa chifukwa chokhala ndi mabuku ameneŵa, m’pomveka kuti akuluakulu a kampu ankada nkhaŵa ndiponso kupsa mtima mabuku oterewa akapezeka m’kampumo.”

N’zoonadi kuti kudziika pamavuto ndiponso kuika moyo pachiswe n’cholinga chothandiza anthu mwauzimu kunali umboni wa chikondi chachikristu! Koma ngakhale kuti chikondichi chinathandiza kwambiri kuti Mboni zipulumuke, panali chinthu china chothandiza kuposa apa. Helene Celmina anati: “Palibe munthu amene anamvetsa mmene mabuku oletsedwawa analoŵera m’malo ngati amenewa, otetezeka kwambiri ndiponso osati n’kuchezerana.” Zinaoneka ngati zosatheka, chifukwa aliyense woloŵa m’ndende ankam’fufuza paliponse. Wolemba mabukuyu analembanso kuti: “Zinali ngati kuti usiku angelo ankauluka n’kumaponya mabukuwo.”

N’zoona kuti Mulungu analonjeza kuti sadzasiya anthu ake, ngakhale kuwataya. Motero Mboni za Yehova m’dziko lakale la Soviet Union zimavomerezana ndi wamasalmo m’Baibulo amene anati: “Taonani, Mulungu ndiye mthandizi wanga.” (Salmo 54:4; Yoswa 1:5) N’zoona, iye anathandiza kwambiri kuti Mbonizo m’dziko lakale la Soviet Union zipulumuke!

Mmene Zinthu Zinasinthira

Pa March 27, 1991, Mboni za Yehova zinakhala gulu lololedwa mwalamulo ku Soviet Union zitasaina chikalata cha boma choikira umboni chokhala ndi mawu akuti: “Cholinga cha Gulu la Chipembedzoli ndicho kuyendetsa ntchito yachipembedzo yodziŵikitsa dzina la Yehova Mulungu ndiponso zimene iye mwachikondi wakonzera mtundu wa anthu kudzera mu Ufumu wake wakumwamba umene uli m’manja mwa Yesu Kristu.”

Zina mwa njira zolembedwa m’chikalatacho zochitira ntchito ya chipembedzoyi ndizo kulalikira poyera ndiponso kuyendera anthu m’nyumba zawo, kuphunzitsa anthu ofuna kumvetsera choonadi cha Baibulo, kuchititsa maphunziro aulere a Baibulo mothandizidwa ndi mabuku ophunzirira Baibulo, ndiponso kugaŵira mabaibulo.

Tsopano patha zaka khumi atasaina chikalata chimenecho, ndipo dziko la Soviet Union kulibenso, ndiponso nkhani yachipembedzo yasintha kwambiri m’mayiko 15 amene kale anali a Soviet Union. Kodi tinganenepo chiyani za tsogolo la chipembedzo kumeneku ndiponso padziko lonse lapansi?

[Bokosi patsamba 19]

Kugwirizana kwa Tchalitchichi ndi Boma la Soviet Union

M’buku lake la mu 1945 lakuti Russia Is No Riddle, Edmund Stevens analemba kuti: “Tchalitchichi chinayesetsa kuti chisatsekereze mafulufute kudzenje. Atsogoleri ake anadziŵa bwino kuti Boma linkafuna kuti abwezere ufulu umene linawapatsa mwa kulithandiza ndi mtima wonse ndiponso kuchita zinthu mosapyola malire ake.”

Stevens anapitiriza kunena kuti: “Kuyambira kale tchalitchi cha Orthodox chakhala tchalitchi cha boma ndipo sikunali kovuta kuti chichite ntchito yake yatsopanoyi yogwirizana kwambiri ndi boma la Soviet Union.”

Bungwe loyang’ana za ufulu wa chipembedzo la Keston Institute linafufuza kwambiri mgwirizano umene unalipo kale pakati pa mtsogoleri wapano wa tchalitchi cha Russian Orthodox, Alexis II ndi atsogoleri a Soviet Union. Lipoti lake linapeza kuti: “Sikuti Aleksi anali yekha amene anagwirizanapo ndi bomali, chifukwa pafupifupi akuluakulu onse a zipembedzo zovomerezeka ndi boma, monga za Katolika, Baptist, Adventist, Chisilamu, ndi Chibuda, anali akazitape a bungwe la KGB. N’zoonadi lipoti lapachaka limene limasimba za ukazitape wa Aleksi limatchulanso akazitape ena ambiri, ndipo ena ndi atchalitchi cha Estonian Lutheran.”

[Bokosi/Chithunzi patsamba 20]

Kufikira Anthu M’makampu

Viktor Kalnins, mtolankhani wa ku Latvia, anakhala kwambiri m’kampu ya ku Mordovia pazaka khumi zimene anamangidwa. Kampuyi ili pa mtunda wa makilomita 400 kumwera chakum’maŵa kwa mzinda wa Moscow. Wolemba Galamukani! wina mu March 1979, anam’funsa Kalnins kuti: “Kodi Mboni zomangidwa zikudziŵa zimene zikuchitika kuno ku United States kapenanso mayiko ena zokhudza gulu la Mboni za Yehova?”

Iye anayankha kuti: “Inde akudziŵa, ndipo akudziŵira m’mabuku amene akulandira. . . . Moti ineyo anandisonyezako magazini awo ena. Sindinadziŵe kumene ankabisa mabuku awo chifukwa ankasinthasintha. Koma aliyense anadziŵa kuti mabukuwa anali m’kampu momwemo. Mboni za Yehova zinkayesetsa kubisa mabuku awo kwinaku asilikali olondera anali pakalapakala kufunafuna mabukuwo!”

Poyankha funso lakuti “Kodi Mboni za Yehova zinayesa kukuuzani zimene zimakhulupirira?” Kalnins anati: “Inde kwabasi! Zimene amakhulupirira n’zodziŵika bwino kwambiri. Tikudziŵa zonse zokhudza Armagedo . . . Ankatchulaponso kwambiri zakuti matenda adzatha.”

[Chithunzi]

Mboni za ku kampu ya ku Mordovia zinapitiriza kuuza ena choonadi cha m’Baibulo molimba mtima

[Chithunzi patsamba 16, 17]

Banja la a Vovchuk analithamangitsira ku mzinda wa Irkutsk, ku Siberia, chaka cha 1951 ndipo mpaka pano akali Akristu okhulupirika

[Chithunzi patsamba 18]

Pothandizidwa ndi matchalitchi pa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, Stalin analola kuti zipembedzo zikhale paufulu kwakanthaŵi

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi cha U.S. Army

[Chithunzi patsamba 18]

Mtsogoleri Alexis I (1945 mpaka 1970) anati: ‘Mfundo za boma la Soviet Union n’zogwirizana ndi mfundo zachikristu zimene tchalitchi chathu chimalalikira’

[Mawu a Chithunzi]

Central State Archive regarding the film/photo/phono documents of Saint-Petersburg