Kodi Zipembedzo Zonse ndi Misewu Yopita kwa Mulungu?
Lingaliro la Baibulo
Kodi Zipembedzo Zonse ndi Misewu Yopita kwa Mulungu?
“ZIMANDIVUTA kwambiri kukhulupirira kuti Mulungu wachilengedwe chonsechi anasankha kudziŵika ndi chikhulupiriro chimodzi chachipembedzo,” anatero wolemba wina Marcus Borg. Munthu wina amene anapambana mphoto ya zamtendere ya Nobel Peace Prize, dzina lake Desmond Tutu ananena kuti: “Palibe chipembedzo chimene chinganene kuti chili ndi choonadi chonse chokhudza chinsinsi” cha chikhulupiriro. Malingaliro otchuka kwambiri a chihindu ndi akuti “Jotto moth, totto poth,” potembenuza mwachisawawa zikutanthauza kuti zipembedzo zonse ndi misewu yosiyanasiyana yopita kumalo amodzi. Abuda nawo amagwirizana ndi malingaliro ameneŵa. N’zoona kuti anthu mamiliyoni ambiri amakhulupirira kuti zipembedzo zonse ndi misewu yopita kwa Mulungu.
Wolemba mbiri wina Geoffrey Parrinder anati: “Nthaŵi zina anthu amati zipembedzo zonse zili ndi cholinga chofanana kapena kuti ndi misewu yofanana yopezera choonadi, kapenanso mpaka kunena kuti zipembedzo zonse zili ndi chiphunzitso chimodzi.” N’zoonadi kuti ziphunzitso, miyambo, ndiponso milungu yazipembedzo ndi yofanana. Zipembedzo zambiri zimaphunzitsa za chikondi ndipo zimaphunzitsa kuti kupha anthu, kuba, ndiponso kunama n’zolakwa. M’zipembedzo zambiri anthu ena amayesetsa moona mtima kuti athandize anzawo. Motero, ngati munthu amatsatira zikhulupiriro zake moona mtima ndipo amayesetsa kukhala ndi khalidwe labwino, kodi pali vuto ngati atakhala m’chipembedzo chinachake? Kapena kodi zipembedzo zonse zangokhala chabe misewu yopita kwa Mulungu?
Kodi Kuona Mtima Pakokha N’kokwanira?
Taganizirani nkhani ya munthu wachiyuda wam’zaka za zana loyamba Sauli, amene anadzakhala Mkristu, mtumwi Paulo. Iye anali wotsatira Chiyuda wachangu chachikulu, ndipo zimenezi zinam’chititsa kuyesa kuthetsa kulambira kwa otsatira Kristu, kulambira kumene ankaona ngati kunali kosayenera. (Machitidwe 8:1-3; 9:1, 2) Komatu mwachifundo cha Mulungu Sauli anazindikira kuti anthu opembedza kwambiri ngati iyeyo angathe kukhala ndi changu cha kwa Mulungu, koma, chifukwa alibe mfundo zokwanira, angakhale akulakwitsa. (Aroma 10:2) Sauli atadziŵa bwino zofuna ndiponso zochita za Mulungu, anasintha n’kuyamba kulambirira pamodzi ndi anthu amene ankawazunza aja, otsatira Yesu Kristu.—1 Timoteo 1:12-16.
Kodi Baibulo limati pali zikhulupiriro zambirimbiri zimene tingasankhe ndipo kuti chilichonse Mulungu amachivomereza? Yesu Kristu atauka anauza mtumwi Paulo malangizo osiyana kwambiri ndi zimenezi. Yesu anam’tumiza iye kwa anthu amitundu “kukawatsegulira maso awo, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kuchokera ulamuliro wa satana kulinga kwa Mulungu.” (Machitidwe 26:17, 18) N’zoonekeratu kuti kusankha kwathu chipembedzo n’kofunika. Anthu ambiri amene Paulo anatumidwako anali kale ndi zipembedzo. Koma anali “mumdima.” Kunena zoona, zipembedzo zonse zikanakhala chabe misewu yopita kumoyo wosatha ndiponso kuchiyanjo cha Mulungu, Yesu sakanafunikira kuphunzitsa om’tsatira kuchita ntchito yopanga ophunzira imene anawapatsa kuti aichite.—Mateyu 28:19, 20.
Pa Ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri, Yesu anati: “Loŵani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuwonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene aloŵa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.” (Mateyu 7:13, 14) Baibulo limanena mwatchutchutchu kuti pali “chikhulupiriro chimodzi.” (Aefeso 4:5) N’zoonekeratu kuti ambiri amene ali pamsewu “wotakata” ali ndi chipembedzo. Koma alibe “chikhulupiriro chimodzi.” Chifukwa chakuti pali mtundu umodzi wokha wakulambira koonadi, anthu amene amafuna kupeza chikhulupiriro chenichenichi ayenera kuufunafuna mtunduwu.
Funafunani Mulungu Woona
Kuyambira pachiyambi penipeni pa anthu onse, Mulungu wakhala akuuza anthuwo zimene iye amafuna kuti iwo azichita. (Genesis 1:28; 2:15-17; 4:3-5) Masiku ano zimene amafuna zalongosoledwa momveka bwino m’Baibulo. Choncho timatha kusiyanitsa kulambira kovomerezeka ndi kulambira kosavomerezeka. (Mateyu 15:3-9) Anthu ena chipembedzo chawo n’chakum’tundu, koma ena amangoonera zimene anthu ena onse akuchita kumene amakhalako. Anthu ambiri analoŵa chipembedzo chinachake chifukwa chanthaŵi ndiponso malo amene anabadwira. Komabe, kodi muyenera kusankha chipembedzo chanu mwamwayi kapena kungosiyira ena kuti akusankhireni?
Muyenera kusankha chipembedzo chanu modziŵa bwino malingana ndi mfundo zimene zimapezeka pophunzira Malemba mosamalitsa. M’zaka za zana loyamba, anthu ena ophunzira si kuti anangovomereza mawu a mtumwi Paulo. Iwo ‘anasanthula m’malembo masiku onse, ngati zinthuzo zinali zoterodi.’ (Machitidwe 17:11; 1 Yohane 4:1) Bwanji inuyo osachita zomwezo?
Baibulo limalongosola kuti Mulungu wachilengedwechi amafuna anthu oti azimulambira m’choonadi. Malingana ndi zimene zinalembedwa pa Yohane 4:23, 24, Yesu analongosola kuti: “Koma ikudza nthaŵi, ndipo tsopano ilipo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m’choonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake. Mulungu ndiye mzimu; ndipo om’lambira iye ayenera kum’lambira mumzimu ndi m’choonadi.” Ndi “mapembedzedwe [okha] oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate” amene ali ovomerezeka kwa iye. (Yakobo 1:27) Mulungu wadalitsa ntchito ya anthu mamiliyoni ambiri yofufuza msewu wopapatiza wopita kumoyo. Iye sadzapereka moyo wosatha kwa anthu amene alibe nawo chidwi nkhaniyi koma kwa anthu amene amayesetsa kupeza njira yopapatiza imene iye waika ndipo akaipeza amaitsatira.—Malaki 3:18.