Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Thanzi Labwino kwa Onse—Lifika Posachedwapa!

Thanzi Labwino kwa Onse—Lifika Posachedwapa!

Thanzi Labwino kwa Onse—Lifika Posachedwapa!

“AMBIRI lerolino . . . amakhulupirira kuti anthu sadzadwalanso,” inatero magazini ya ku Germany ya Focus. Komatu sikoyamba kuganiza zimenezi. Pamene Mlengi anapanga munthu woyamba, sanafune kuti anthu azidwala. Cholinga chake sichinali kungopatsa ‘anthu onse padziko lapansi thanzi labwino’ ayi. Mlengi wathu anafuna kuti aliyense akhale ndi thanzi langwiro.

Nangano n’chifukwa chiyani timadwala? Baibulo limatiuza kuti Yehova Mulungu anapanga makolo a anthu onse , Adamu ndi Hava, angwiro. Atamaliza kulenga, “anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.” Mlengi wathu wachikondi sanafune kuti anthufe tizidwala ndi kufa. Koma Adamu ndi Hava anachimwa pamene anakana moyo umene iye anawaikira. Tchimo la Adamu linabweretsa imfa, imene ikukhudza anthu onse.—Genesis 1:31; Aroma 5:12.

Yehova sanawasiye choncho anthu ayi. Ndiponso sanasinthe cholinga chake choyamba kwa anthu ndi dziko lapansi. M’Baibulo lonse, amadziŵikitsa cholinga chake chowapatsanso thanzi labwino anthu omvera. Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu, ali padziko lapansi anaonetsa mphamvu za Mulungu pochiritsa matenda. Mwachitsanzo, Yesu anachiritsa akhungu, akhate, ogontha, ambulu, akhunyu, ndi amanjenje.—Mateyu 4:23, 24; Luka 5:12, 13; 7:22; 14:1-4; Yohane 9:1-7.

Posachedwapa Mulungu adzauza Mfumu yake Yaumesiya, Yesu Kristu, kuti ayambe kulamulira anthu onse padziko lapansi. Mu ulamuliro wake, ulosi wa Yesaya udzakwaniritsidwa: “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala; anthu okhala mmenemo, adzakhululukidwa mphulupulu zawo.” (Yesaya 33:24) Kodi zidzatheka bwanji?

Tikuona kuti mneneriyo akuti anthu “adzakhululukidwa mphulupulu zawo.” Choncho, uchimo wobadwa nawo umene unayambitsa matenda, udzachotsedwa. Motani? Mtengo wa nsembe ya dipo ya Yesu udzagwira ntchito kwa anthu omvera, ndipo udzachotsa matenda ndi imfa. Kulikonse padziko lapansi, anthu adzasangalala ndi paradaiso. Mtumwi wachikristu Yohane analemba kuti: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.” Zimenezi zichitika posachedwapa!—Chivumbulutso 21:3, 4; Mateyu chaputala 24; 2 Timoteo 3:1-5.

Kukhala Odekha

Padakali pano, anthu miyandamiyanda akuvutika ndi matenda. Choncho, n’zomveka kuti munthu adere nkhaŵa thanzi lake ndi la anthu amene amawakonda.

Akristu lerolino amayamikira kwambiri ntchito ya madokotala. Amatsatira njira zoyenera kuti akhale ndi thanzi labwino. Komabe, lonjezo la Baibulo la tsogolo lopanda matenda limatithandiza kudekha pa nkhaniyi. Thanzi langwiro silingatheke kufikira pamene Mfumu Yaumesiya idzayamba kulamulira mtundu wonse wa anthu. Ngakhale kuti atulukira mankhwala amphamvu koposa, monga momwe taonera, asayansi ya zamankhwala alephera kuthyola apulo labwino kwambiri pamwamba pa mtengo—thanzi labwino la aliyense.

Cholinga chopatsa “anthu onse padziko lapansi thanzi labwino” chikwaniritsidwa posachedwapa. Koma lidzachita zimenezi si bungwe la UN kapena la World Health Organization kapena akatswiri oona za malo okhala, kapena okonza chikhalidwe cha anthu, kapena madokotala. Yesu Kristu ndi amene adzakwaniritsa zimenezi. Padzakhalatu chimwemwe chachikulu pamene anthu onse ‘adzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu’!—Aroma 8:21.

[Zithunzi patsamba 10]

Anthu onse adzakhala ndi thanzi labwino m’dziko latsopano la Mulungu