Tikulandirani ku Msonkhano Wachigawo wa “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu”!
Tikulandirani ku Msonkhano Wachigawo wa “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu”!
ANTHU MAMILIYONI AMBIRI ADZAPEZEKA pamisonkhano mazanamazana imene idzachitika padziko lonse. Misonkhano yokwana 26 idzachitika m’Malaŵi. Woyamba udzachitika pa August 10-12, ndipo womaliza udzachitika pa September 7-9. Mosakayikira, umodzi mwa misonkhano ya masiku atatu imeneyi—Lachisanu mpaka Lamlungu—udzachitika m’dera lapafupi ndi kwanu.
M’madera onse, pulogalamu idzayamba ndi nyimbo zamalimba pa 8:30 a.m. tsiku lililonse. Pambuyo pa nkhani ya malonje Lachisanu, padzatsatira nkhani zozikidwa pa Baibulo zakuti “Kuphunzitsa za Ufumu Kumabala Zipatso Zabwino,” “Talimbikitsidwa ndi ‘Zinthu Zazikulu za Mulungu’” ndi “Sangalalani ndi Chilungamo cha Yehova.” Nkhani yaikulu yakuti “Okonzeka Mokwanira Monga Aphunzitsi a Mawu a Mulungu” idzamaliza chigawo cha m’maŵa.
Nkhani yoyamba masana yakuti “Anatiyeretsa Monga Anthu Kuti Tichite Ntchito Zokoma” itatha, nkhani yosiyirana ya mbali zitatu yakuti “Kudziphunzitsa Tokha Pamene Tikuphunzitsa Ena” idzatsatira. Idzatsindika kufunika kochita zimene timalalikira pa nkhani za makhalidwe abwino, phunziro la Baibulo laumwini, ndiponso kukaniza zoyesayesa za Mdyerekezi zofuna kutisocheretsa. Kenako padzatsatira nkhani yakuti “Danani ndi Mliri wa Dzikoli wa Nkhani Zolaula.” Ndiyeno nkhani yakuti “Yehova Akometsera Anthu Ake ndi Kuunika,” yozikidwa pa Yesaya chaputala 60, idzamaliza pulogalamu ya tsikuli.
Nkhani za Loŵeruka zakuti “Kupeza Mpumulo M’goli la Kristu,” “Tsanzirani Mphunzitsi Wamkulu,” ndi “Kodi Ndinu Wofunitsitsa Kutumikira Ena?” zidzatsindika kufunika kotsatira chitsanzo cha Kristu. Loŵeruka lomweli, padzakhalanso nkhani zosiyirana za maola aŵiri za mitu yakuti “Atumiki Amene Kudzera mwa Iwo Ena Amakhala Okhulupirira” ndi “Pindulani Mokwanira ndi Maphunziro Ateokalase.” Nkhani yosiyirana ya m’maŵa idzafotokoza njira zopangira ophunzira, ndipo yamasana idzafotokoza mmene tingapindulire mokwanira ndi phunziro la Baibulo ndiponso kupezeka pamisonkhano yachikristu. Nkhani ya ubatizo idzamaliza pulogalamu ya m’maŵa ndipo oyenerera ubatizo adzakhala ndi mwayi wobatizidwa. Ambiri adzafunitsitsa kumvetsera nkhani yomaliza ya Loŵeruka masana yakuti “Zinthu Zatsopano Zothandiza Kuti Tipite Patsogolo Mwauzimu.”
Imodzi mwa nkhani za Lamlungu m’maŵa ndi nkhani yosiyirana ya mbali zitatu imene idzafotokoza buku la Malaki ndi kusonyeza bwino mmene likutithandizira lerolino. Ndiyeno padzatsatira seŵero la m’nthaŵi zakale la Kora, Datani, ndi Abiramu amene anapandukira ulamuliro wa Mose umene Mulungu anam’patsa. Nkhani yotsatira idzafotokoza bwinobwino mfundo zazikulu za uthenga wa m’seŵeroli. Pulogalamu yamasana idzakhala ndi nkhani ya poyera yakuti “Kodi Ndani Amene Akuphunzitsa Mitundu Yonse Choonadi?”
Ndithudi, mudzapindula kwambiri mwauzimu ngati mudzapezekapo kwa masiku onse atatu. Kuti mudziŵe kumene kudzachitikira msonkhanowu pafupi ndi kwanu, funsani pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ya m’dera lanu kapena lemberani ofalitsa magazini ino.