Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kulira Maliro N’kulakwa?

Kodi Kulira Maliro N’kulakwa?

Lingaliro Labaibulo

Kodi Kulira Maliro N’kulakwa?

“KOMA SITIFUNA, ABALE, KUTI MUKHALE OSADZIŴA ZA IWO AKUGONA; KUTI MUNGALIRE MONGANSO OTSALAWO, AMENE ALIBE CHIYEMBEKEZO.”—1 ATESALONIKA 4:13.

BAIBULO limati pali chiyembekezo kwa anthu amene anamwalira. Kuukitsa anthu kumene Yesu anachita komanso zinthu zimene anaphunzitsa, zimasonyeza nthaŵi imene akufa adzaukitsidwe. (Mateyu 22:23-33; Marko 5:35, 36, 41, 42; Luka 7:12-16) Kodi chiyembekezo chimenechi chiyenera kutikhudza bwanji? Mawu a mtumwi Paulo amene ali pamwambapo amasonyeza kuti chiyembekezo chimenechi chingatilimbitse mtima wokondedwa wathu akamwalira.

Ngati wokondedwa wanu anafa, n’zosakayikitsa kuti monga mmene zimakhalira wina akamwalira munavutika maganizo kwambiri. Anthu ena zimawatengera miyezi kapena zaka kuti aiŵale za imfayo. Theresa, yemwe mwamuna wake amene anakhala naye m’banja kwa zaka 42 anamwalira atangochitidwa kumene opaleshoni ya mtima, ananena kuti: “Zinali zosokoneza maganizo kwambiri! Poyamba ndinachita mantha kwambiri. Kenaka mtima wanga unayamba kundipweteka kwambiri. Ndinalira kwambiri.” Kodi kuteroko ndiye kuti mulibe chikhulupiriro cha lonjezo la Yehova la kuukitsa akufa? Kodi mawu a Paulo akutanthauza kuti kulira maliro n’kulakwa?

Zitsanzo za Kulira Maliro za M’Baibulo

Mayankho amafunso amenewo timawapeza pofufuza zitsanzo za kulira maliro zimene zili m’Baibulo. M’nkhani zambiri wina akamwalira m’banja panali nthaŵi yakulira. (Genesis 27:41; 50:7-10; Salmo 35:14) Nthaŵi zambiri anthu akamalira chonchi maganizo ankawapweteka kwambiri.

Taganizani mmene amuna ena achikhulupiriro analilira maliro a wokondedwa wawo. Mwachitsanzo, Abrahamu anali ndi chikhulupiriro champhamvu kuti Mulungu angaukitse akufa. (Ahebri 11:19) Ngakhale anali ndi chikhulupiriro champhamvu chimenecho, mkazi wake atamwalira, iye “anadza ku maliro a Sara, kuti am’lire.” (Genesis 23:1, 2) Pamene ana aamuna a Yakobo anam’namiza kuti mwana wake wapamtima Yosefe wamwalira, iye “anang’amba malaya ake . . . ndipo anam’lirira.” (Genesis 37:34, 35) Ndipotu zaka zambiri zitapita, Yakobo anadandaulabe kwambiri poganizira imfa ya mwana wake wapamtimayo! (Genesis 42:36-38) Mfumu Davide naye analira kwambiri pamaso pa anthu, ana ake aamuna Amnoni ndi Abisalomu atamwalira. Ngakhale kuti ana akewo anali atavutitsa kwambiri Davide ndi banja lake, iwo anali ana akebe ndipo imfa yawo inam’dandaulitsa kwambiri.—2 Samueli 13:28-39; 18:33.

Nthaŵi zina mtundu wonse wa Aisrayeli unkalira monga mmene anachitira pa imfa ya Mose. Deuteronomo 34:8 amatiuza kuti Aisrayeli anam’lira masiku makumi atatu.

Chitsanzo chomaliza ndicho cha Yesu Kristu. Mnzake wapamtima Lazaro anamwalira. Ndipo Yesu ataona mmene achemwali a Lazaro, Marita ndi Mariya pamodzi ndi anzawo anali kulirira, “anadzuma mumzimu, navutika mwini.” Ngakhale kuti anali kudziŵa kuti sipatenga nthaŵi asanamuukitse mnzakeyo, iye “analira.” Yesu ankawakonda anzake apamtimawo Marita ndi Mariya. Motero zinam’khudza kwambiri poona akudandaula kwambiri ndi imfa ya mchimwene wawo.—Yohane 11:33-36.

Onsewo, Abrahamu, Yakobo, Davide ndi Yesu anali kukhulupirira kwambiri Yehova ndi malonjezo ake, koma analirabe. Kodi ndiye kuti kulira maliro kumeneku kunali chizindikiro cha kufooka kwauzimu? Kodi chisoni chawo chinkatanthauza kuti sanali kukhulupirira kwambiri za chiukiriro? Ayi ndithu! Kulira maliro n’chinthu chimene chimachitika mwachibadwa wokondedwa akamwalira.

Chifukwa Chake Timalira Maliro

Sichinali cholinga cha Mulungu kuti anthu azifa. Cholinga cha Yehova choyambirira chimene Adamu ndi Hava anauzidwa chinali chakuti dziko lapansi lisandutsidwe paradaiso wokongola, wokhala ndi anthu achimwemwe okhaokha. Imfa ikanabwera kokha ngati anthu aŵiri oyambawo akanasankha kusamvera Yehova. (Genesis 1:28; 2:17) N’zachisoni kuti Adamu ndi Hava anasankha zoti asamveredi ndipo chifukwa cha kusamverako, “imfa inafikira anthu onse.” (Aroma 5:12; 6:23) Choncho imfa ndiyo mdani wankhanza yemwe sanafunikire kuti akhalepo.—1 Akorinto 15:26.

Ndiye n’zomvekadi kuti imfa poti n’njosazoloŵereka ikatenga wina wapamtima imadandaulitsa kwambiri anthu omwe afedwa. Imawapangitsa kukhala osungulumwa kwambiri m’moyo wawo. Theresa yemwe ndi mkazi wamasiye amene tam’tchula pamwambapo, poganizira mwamuna wake anati: “Ndikukhulupirira kuti ndidzamuonanso pa chiukiriro, komabe ndimam’soŵa kwambiri tsopano. Zimenezi n’zimene zimandipwetekadi kwambiri.” Imfa ya kholo ingatikumbutse zoti ifenso tidzafa. Imfa ya mwana wamng’ono imatipwetekanso kwambiri chifukwa amakhala asanadyerere m’moyo.—Yesaya 38:10.

Inde, imfa ndi yosazoloŵereka. Kudandaula kumene kumakhalapo sikupeŵeka, ndipo Yehova saona kulira maliro monga kusoŵa chikhulupiriro cha chiukiriro. Monga mmene taonera zitsanzo za Abrahamu, Yakobo, Davide, mtundu wa Aisrayeli ndi Yesu, sikuti kusonyeza poyera mmene mtima wathu ukuŵaŵira ndi kufooka mwauzimu. *

Komabe ngakhale kuti ife Akristu timalira chifukwa cha imfa, sitilira “monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.” (1 Atesalonika 4:13) Sitidzivutitsa ndi kulira kochita kunyanyira chifukwa timadziŵa mmene anthu akufa alili. Timadziŵa kuti sakumva kuŵaŵa kapena kuvutika maganizo, koma kuti amangokhala ngati ali m’tulo tabwino tofa nato. (Mlaliki 9:5; Marko 5:39; Yohane 11:11-14) Timakhulupiriranso kwambiri kuti Yesu yemwe ali “kuuka ndi moyo,” adzakwaniritsa lonjezo lake la kuukitsa “onse ali m’manda.”—Yohane 5:28, 29; 11:24, 25.

Choncho ngati mukulira maliro pakali pano, limbani mtima podziŵa kuti Yehova amamvetsa chisoni chanu. Kudziŵa zimenezi ndiponso chiyembekezo chanu cha chiukiriro zikutonthozeni ndipo zikuthandizeni kupirira pamene mwafedwa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Kuti muthandizidwe pothetsa chisoni, onani masamba 14-19 a bulosha lakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.