Kodi Mulungu Angamve Mapemphero Anga?
Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Mulungu Angamve Mapemphero Anga?
“Ndimapempherera nkhani iliyonse chifukwa Yehova ndi bwenzi langa, ndipo ndikudziŵa kuti adzandithandiza ngati ndili ndi vuto.”—Andrea.
MTSIKANA ameneyu, Andrea, amakhulupirira kuti Mulungu amamva mapemphero ake. Komabe achinyamata ambiri sakhulupirira zimenezo. Ena amaganiza kuti Mulungu ali kutali kwakuti sangam’peze. Mwinanso amakayika ngati Mulungu amawasamaladi mpaka poti angamve mapemphero awo.
Kodi chinsinsi cha pemphero n’chiyani? Kunena mwachidule, chinsinsi chake n’kukhala ndi ubwenzi weniweni ndi Mulungu. Wamasalmo anapemphera kuti: “Iwo akudziŵa dzina lanu adzakhulupirira Inu.” (Salmo 9:10) Bwanji inuyo? Kodi mukum’dziŵa bwino kwambiri Mulungu mwakuti mutha kupemphera ndi kukhulupirira kuti adzamva mapemphero anu? Musanapitirize kuŵerenga nkhaniyi, yesani kuyankha mafunso amene ali m’bokosi lakuti “Kodi Mukum’dziŵa Bwino Mulungu?” Kodi mungayankhe mafunso angati?
KODI MUKUM’DZIŴA BWINO MULUNGU? Mayankho ali patsamba 14
1. Kodi dzina la Mulungu ndani, ndipo limatanthauzanji?
2. Kodi mikhalidwe yaikulu inayi ya Mulungu imene Baibulo limafotokoza ndi iti?
3. Kodi Mulungu anasonyeza motani chikondi chake chachikulu kwa anthu?
4. Kodi tingatani kuti tikhale paubwenzi ndi Mulungu?
5. Kodi tiyenera kukhala ndi maganizo otani popemphera?
Kodi mwayankhapo mafunso ena, ngakhale kuti simunamalize kuŵerenga nkhani yonseyi? Ngati ndi choncho, ndiye kuti mukum’dziŵa bwinopo Mulungu kuposa anthu ena ambiri. Komabe mwina mayankho anu avumbula kuti mufunika kuphunzira zochuluka za iye, kuti mum’dziŵe bwino kwambiri monga bwenzi la ponda apa nane mpondepo. (Yohane 17:3) Muli n’cholinga chimenechi, lingalirani zinthu zingapo zimene Baibulo limatiphunzitsa za “Wakumva pemphero” ameneyu.—Salmo 65:2.
Mulungu Ndi Munthu Weniweni
Choyamba, Baibulo limatithandiza kuzindikira kuti Mulungu sali mphamvu yopanda umunthu. Iye ndi munthu ndipo ali ndi dzina lake, Yehova. (Salmo 83:18) M’Chihebri dzina limeneli limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhalako.” Amakhala amene akufuna kuti akwaniritse cholinga chake. Mphamvu chabe yopanda umunthu singachite zimenezo! Choncho popemphera, dziŵani kuti simukulankhula ndi mphamvu yopanda umunthu kapena kubwebweta nokha. Mukulankhula ndi munthu amene angamve ndiponso kuyankha mapemphero anu.—Aefeso 3:20.
Mtsikana wina dzina lake Diana akuti: “Ndikudziŵa kuti kulikonse kumene ndingakhale, Yehova adzandimva.” Kuti mukhale ndi chidaliro chimenecho, onani Mulungu kukhala weniweni! Baibulo limati: “Iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo.”—Ahebri 11:6.
Gwero la Nzeru ndi Mphamvu
Mulungu angatithandizedi chifukwa ali ndi mphamvu zodabwitsa. Kukula ndi kusamvetsetseka kwa chilengedwe chonse kumachitira umboni kuti mphamvu zimenezo zilibe malire. Baibulo limati Yehova amadziŵa dzina la nyenyezi iliyonse—ngakhale kuti pali nyenyezi mabiliyoni osaŵerengeka! Ndiponso, iye ndiye gwero la mphamvu zonse zimene zili m’kati mwa nyenyezizo. (Yesaya 40:25, 26) Kodi si zodabwitsa zimenezi? Komabe ngakhale kuti n’zodabwitsa choncho, Baibulo likutiuza kuti “zimenezi ndi kachigawo kochepa chabe ka mphamvu zake”!—Yobu 26:14, Today’s English Version.
Talingaliraninso nzeru za Yehova zopanda malire. Baibulo limati zolingalira zake “n’zozama ndithu.” (Salmo 92:5) Anapanga anthu, ndipo amatidziŵa bwino kwambiri kuposa mmene timadzidziŵira ife eni. (Salmo 100:3) Popeza kuti iye alipo “kuyambira nthaŵi yosayamba kufikira nthaŵi yosatha,” ali ndi nzeru zopanda malire. (Salmo 90:1, 2) Amadziŵa zonse.—Yesaya 40:13, 14.
Kodi Yehova amazigwiritsa ntchito bwanji mphamvu ndi nzeru zonsezi? Lemba la 2 Mbiri 16:9 limati: “Maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.” Mulungu angathetse vuto lililonse limene mungakhale nalo kapena kukuthandizani kuti mupirire. Mtsikana wina dzina lake Kayla akukumbukira kuti: “Posachedwapa, ine ndi achibale anga titakhala m’mavuto, ndinapemphera kwa Yehova, ndipo ndikukhulupirira kuti anatithandiza kupirira mavuto ndiponso kusweka mtima zimene sitikanapirira mwa ife tokha.” Mukamalankhula ndi Mulungu ndiye kuti mukulankhula ndi gwero la nzeru. Kodi pangakhalenso zabwino kuposa zimenezi ngati?
Mulungu wa Chilungamo ndi Chikondi
Koma kodi mungadziŵe bwanji kuti Mulungu akufuna kukuthandizani? Yehova sanasankhe kudzidziŵikitsa ndi mphamvu zake zazikulu kapena nzeru zake zakuya, ngakhalenso chilungamo chake chosasunthika. M’malo mwake, Yehova amadziŵika makamaka ndi mkhalidwe wake wa chikondi. ‘Mulungu ndiye chikondi,’ amatero 1 Yohane 4:8. Mkhalidwe waukulu umenewu wa chikondi umatipatsa chidaliro chakuti adzayankha mapemphero athu. Anasonyeza chikondi chake chachikulu popereka Mwana wake nsembe ya dipo kuti tidzapeze moyo wosatha.—Yohane 3:16; 1 Yohane 4:9, 10.
Popeza Mulungu ndiye chikondi, musaope kuti adzakunyalanyazani kapena kusakuchitirani chilungamo. Deuteronomo 32:4 amati: “Njira zake zonse ndi chiweruzo [“chilungamo,” NW].” Chikondi cha Mulungu chimakupatsani chikhulupiriro chakuti adzakumverani. Zimenezi zimatithandiza kukhala omasuka kum’fotokozera za pansi pa mtima.—Afilipi 4:6, 7.
Ubwenzi ndi Mulungu
Yehova akufuna kuti tizilankhula naye. Safuna kukhala ngati mlendo kwa ife. M’malo mwake, iye m’mbiri yonse ya anthu anafuna kuti anthu akhale mabwenzi ake. Amuna ndi akazi, ana ndi akulu omwe amene iye anawakonda zedi anali mabwenzi ake. Ena mwa iwo ndi Abrahamu, Mfumu Davide, ndi Mariya, mayi ake a Yesu.—Yesaya 41:8; Luka 1:26-38; Machitidwe 13:22.
Inunso mungakhale bwenzi la Yehova. Zoonadi, ubwenzi umenewu sutanthauza kuti muzimuona Mulungu ngati mzimu winawake umene mungalankhule nawo kokha ngati pali zimene mukufuna kapena ngati muli ndi vuto lina. Popemphera tisamangoganiza zofuna zathu zokha. Ngati tikufuna kuti Mulungu akhale bwenzi lathu, tiziganizanso za chifuno chake—osati chathu chokha—ndipo tiyeneradi kuchita zimene Mulungu amafuna. (Mateyu 7:21) Choncho, Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kupempherera zinthu zofunika pamaso pa Mulungu. Anati: “Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Tizitamandanso ndi kuyamika Mulungu m’mapemphero athu!—Salmo 56:12; 150:6.
Komabe, tisaganize kuti zofuna zathu kapena nkhaŵa zathu n’zazing’ono zosafunika kuzipempherera. Mnyamata wina dzina lake Steve akuti: “Ngakhale kuti ndimayesetsa kukhala womasuka kwa Mulungu, nthaŵi zina ndimaganiza kuti ndisamam’vutitse ndi nkhani wamba.” Mukayamba kulingalira motero, yesani kukumbukira zimene Yesu anaphunzitsa ophunzira ake: “Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiŵiri? ndipo palibe imodzi ya izo iiŵalika pamaso pa Mulungu. . . . Musaopa, muposa mtengo wake wa mpheta zambiri.” (Luka 12:6, 7) Kodi si zolimbikitsa zimenezo?
Choncho, n’zosavuta kumvetsa kuti mukam’dziŵa bwino kwambiri Yehova, muzim’fikiranso mosavuta m’pemphero ndipo mudzakhala ndi chikhulupiriro chakuti Yehova akuthandizani. Nanga kodi mufunika kukhala ndi maganizo otani pamene mukupemphera kwa Mulungu? Khalani waulemu, wodzichepetsa, ndiponso wopanda dyera. Kodi pali munthu waulamuliro padziko lapansi lino amene angakumvetsereni ngati mukum’pempha monyada kapena mopanda ulemu? Ndiyetu musadabwe kuti Yehova amafunanso kuti mum’lemekeze ndiponso kulemekeza miyezo yake kuti ayankhe mapemphero anu.—Miyambo 15:29.
Achinyamata oopa Mulungu zikwizikwi aphunzira kuululira Mulungu za mumtima mwawo. (Salmo 62:8) Mnyamata wina dzina lake Brett akuti: “Yehova akayankha mapemphero anga, zimandilimbikitsa kuti iye ndi bwenzi langa nthaŵi zonse.” Bwanji inuyo? Kodi mungatani kuti mukhale pa ubwenzi ngati umenewu ndi Mulungu? Atsikana aŵiri achikristu anapereka ndemanga zotsatirazi:
Rachel: “Kuti ndim’konde kwambiri Yehova, ndikuganiza kuti ndiyenera kuphunzira Mawu ake mozama, ndipo ndikuyesetsa kukulitsa chilakolako chophunzira motero.”—1 Petro 2:2.
Jenny: “Ndikuganiza kuti ukamatumikira kwambiri Yehova, umam’kondanso kwambiri.”—Yakobo 4:8.
Kodi mukudziŵa phindu la pemphero? Mtsikana wina wachikristu akuti: “Ndikanam’konda kwambiri Mulungu ngati akanalankhula nane kapena kunditumizira uthenga.” Popeza Yehova samatiyankha mwapakamwa tikapemphera, kodi pemphero limatithandizadi motani? Tidzakambirana funsoli m’kope la m’tsogolo.
[Bokosi patsamba 14]
Mayankho a mafunso a patsamba 12
1. Yehova. Limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhalako.”
2. Chikondi, mphamvu, chilungamo, ndi nzeru.
3. Anatumiza Mwana wake wobadwa yekha, Yesu, kuti atifere.
4. Tisamangoganiza za ife tokha koma tizilingaliranso chifuno cha Mulungu ndi kuchita zimene iye amafuna.
5. Tikhale odzichepetsa, aulemu, ndiponso opanda dyera.
[Zithunzi patsamba 13]
Kuphunzira Baibulo ndi kuphunzira poona zimene Mulungu analenga zidzakuthandizani kum’dziŵa bwino Mulungu