Lingakuthandizeni Wokondedwa Wanu Akamwalira
Lingakuthandizeni Wokondedwa Wanu Akamwalira
Zaka zingapo zapitazo Mboni za Yehova zinafalitsa bulosha limene linafotokoza mavuto amene mumalimbana nawo munthu amene mumam’konda akamwalira. Posachedwapa, munthu wina wa m’dziko la Federal Republic of Yugoslavia anayamikira polemba kalata. Iye analemba kuti: “Ndikufuna ndikuthokozeni kuchokera pansi pamtima polemba bulosha lakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Limanenadi nkhani zonse zokhudza kuferedwa.”
Wolembayo anafotokoza kuti: “Mkulu wanga atamwalira pangozi yagalimoto, buloshali linandithandiza n’tasoŵeratu chochita. Kamutu kakuti ‘Malingaliro Ena Othandiza’ kamene kali patsamba 18 kanandilimbitsadi mtima. Koma patapita miyezi inayi ndinayamba kuvutika m’maganizo kwambiri ndi kusungulumwa. Ndinali ndi nkhaŵa yoti ndidwala nthenda yamaganizo.
“Ndiye ndinaŵerenganso bulosha lija. Ndipo patsamba 9 m’kabokosi kakuti ‘Mchitidwe Wakumva Chisoni,’ ndinazindikira kuti usanaiŵale kwenikweni, umayambanso kuchita chisoni ndi kusungulumwa. Zinandithandizadi kwambiri. Zikomo chifukwa cha chifundo chanu chimene munasonyeza m’bulosha limeneli.”
N’kutheka kuti inuyo kapena munthu wina yemwe mumam’dziŵa angathandizidwenso poŵerenga bulosha limeneli la masamba 32. Mungapemphe buloshali polemba zofunika m’mizere ili pamunsiyi n’kutumiza ku adiresi yoyenera imene yalembedwa patsamba 5 la magazini ino.
□ Nditumizireni bulosha lakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira.
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.