Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Vuto la Mankhwala Osokoneza Bongo Lingathetsedwe!

Vuto la Mankhwala Osokoneza Bongo Lingathetsedwe!

Vuto la Mankhwala Osokoneza Bongo Lingathetsedwe!

“APOLISI Agwira Mankhwala Osokoneza Bongo Ambiri M’mabotolo a Vinyo.” Uwu unali mutu wa nkhani ya m’nyuzipepala, ndipo nkhani yake inalongosola mmene apolisi a mumzinda wa Johannesburg, ku South Africa, anagwirira kontena ya galimoto yaikulu itanyamula mabotolo 11,600 a vinyo wopangidwa ku South America. Vinyoyo anam’phatikiza ndi mankhwala osokoneza bongo a cocaine olemera makilogalamu pafupifupi 150 kapena 180. Akuti sakukayika kuti m’dzikolo munali musanaloweko cocaine wochuluka chonchi mwakatangale.

Ngakhale kuti apolisi akamagwira akatangaleŵa amatilimbikitsa, zoona zake n’zakuti padziko lonse iwo amangogwira mankhwala ochepa kwambiri otereŵa okwana maperesenti 10 kapena 15 okha. Zimenezi n’zomvetsa chisoni chifukwa zili ngati munthu wolima dimba amene wathothola masamba ochepa atchire lomwe lamera m’dimbamo, koma n’kusiya mizu yake yonse.

Phindu lalikulu limene limapezeka pogulitsa mankhwalaŵa limalepheretsa boma kuthetsa ntchito yopanga ndiponso yogulitsa mankhwalaŵa. Ku United States kokha, ndalama zimene zimapezeka pamalonda a mankhwalaŵa pachaka zimakwana madola mabiliyoni ambiri zedi. Chifukwa cha ndalama zochuluka chonchi, n’zosadabwitsa kuti apolisi ndiponso akuluakulu ena aboma, ngakhalenso mabwana ena amachita nawo katangaleyu.

Alex Bellos yemwe amagwira ntchito ku nyuzipepala yotchedwa The Guardian Weekly ku Brazil analemba kuti malingana n’kufufuza kwa am’nyumba yamalamulo, akuti “anthu atatu ogwira ntchito m’nyumbayo, andale 12, ndi mameya atatu anatchulidwa . . . m’gulu la anthu oposa 800 amene akuwaganizira kuti ankachita umbanda ndiponso katangale wa mankhwala osokoneza bongo ku Brazil.” Ena mwa anthuwo analinso “apolisi, maloya, amalonda ndi alimi ochokera m’maboma 17 mwa maboma 27 a m’dzikolo.” Pulofesa wa nkhani zandale pa yunivesite ya Brazil ananena kuti: “Zimenezi zikusonyeza kuti gulu lililonse la anthu a ku Brazil lili ndi mlandu.” Zimenezi zikhoza kukhalanso choncho m’madera ambiri m’mene mankhwalaŵa ali ofala. Chimawonjezera vutoli n’kupezeka kwa mankhwalaŵa anthu akawafuna.

Chifukwa chakuti malamulo ambiri akulephera kutsatiridwa, anthu ena amati ndibwino kungololeza mankhwala ena osokoneza bongo. Ambiri amati boma lizilola anthu kukhala ndi mankhwala otere pang’ono kuti azigwiritsa ntchito akafuna. Akuti potero boma silizivutika n’kulimbana ndi akatangale ndiponso lingachepetse ndalama zambiri zimene akuluakulu akatangalewo amapeza.

Ena Anakwanitsa

Mankhwalaŵa amatheka kuwachotsa m’thupi mwa anthu amene amangokhalira kuwagwiritsa ntchito ndipo zikatero thanzi lawo limakhala bwinopo. Tsoka ilo, anthu otere akangobwerera mwakale, mtima umangoti dyokodyoko kufuna kuti ayambenso kugwiritsa ntchito mankhwalaŵa. Wolemba wina wotchedwa Luigi Zoja akutchula chifukwa chochititsa zimenezo kuti: “N’zosatheka kungosintha khalidwe la munthu popanda kumuthandiza kusinthiratu maganizo ake.”

Darren, amene tam’tchula poyamba uja, “anasinthiratu maganizo ake” m’moyo. Iye analongosola kuti: “Sindinkakhulupirira n’komwe zakuti kuli Mulungu. Koma patapita nthaŵi, ndinazindikira kuti kuyenera kukhala Mulungu, ngakhale kuti ndinkagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kuyambira m’maŵa mpaka usiku. Kwa miyezi iŵiri kapena itatu, ndinayesetsa kuti ndisiyane nawo mankhwala osokoneza bongo, koma anzanga sankandilola kutero. Ngakhale kuti ndinali kugwiritsabe ntchito mankhwalaŵa, ndinayamba kuŵerenga Baibulo mokhazikika ndisanakagone. Ndinaleka kukonda kucheza ndi anzangawo. Tsiku lina madzulo ine ndi mnzanga amene ndinkagona naye tinaledzeleratu ndi mankhwala osokoneza bongo. Kenaka ndinamuuza za Baibulo. M’maŵa wake iye anaimba telefoni kwa mkulu wake amene anali m’gulu la Mboni za Yehova. Iye anatiuza kuti tikakumane ndi Mboni ina imene inkakhala mumzinda wathu womwewo, ndipo ndinakakumana naye.

“Tinacheza mpaka 11 koloko yausiku, ndipo ndinachoka atandipatsa mabuku angapo othandiza kuphunzirira Baibulo. Anayamba kuphunzira nane Baibulo ndipo ndinasiya kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndi kusuta komwe. Pafupifupi miyezi isanu ndi inayi itatha, ndinabatizidwa n’kukhala m’gulu la Mboni za Yehova.”

Kusiya chizoloŵezi chogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo n’kovuta. Michael amene tam’tchula m’nkhani yam’mbuyoyi, anagwiritsa ntchito mankhwalaŵa kwa zaka 11 ndipo atasiya analongosola mavuto amene anakumana nawo motere: “Kudya kunkandivuta kwambiri choncho ndinawonda. Komanso ndinkamva kubayabaya m’thupi, ndinkatuluka thukuta, ndipo anthu ankaoneka ngati akunyezimira. Chilakolako chofuna kuyambiranso kugwiritsa ntchito mankhwalaŵa chinandikulira kwambiri, koma kuyandikira kwa Yehova m’pemphero ndiponso kuphunzira Baibulo zinandithandiza kuti ndisadzidetsenso.” Anthu omwe anagwiritsapo ntchito mankhwala osokoneza bongo ameneŵa amavomereza kuti anayenera kulekeratu kuyenda ndi anzawo akale.

Chifukwa Chimene Anthu Zimawakanikira

Kugwiritsa ntchito mankhwala oletsedwaŵa ndi mbali imodzi chabe ya vuto lalikulu la padziko lonse. Dziko lonse lakutidwa ndi mzimu wochititsa kuipa, chiwawa, ndiponso nkhanza. Baibulo limanena kuti “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Mtumwi Yohane anatchula “woipayo” pa Chivumbulutso 12:9: “Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.”

Kuphatikiza pa zofooka zawo, anthu akhala akulimbana ndi mdani wamphamvu ameneyu. Satana ndiye anachititsa kuti anthu agwe m’vuto pachiyambi pomwe. Iye akufunitsitsa kuti asokonezebe anthu ndi kuwachotsa kwa Mulungu. Zikuoneka kuti njira yake ina yokwaniritsira zimenezi ndiyo kuchititsa anthu kuti azigwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Akuchita zimenezi mokalipa kwambiri chifukwa akudziŵa kuti ‘kam’tsalira kanthaŵi.’—Chivumbulutso 12:12.

Kodi Mulungu Adzatani Kuti Athetse Vutoli?

Baibulo limavumbula cholinga chachikondi cha Mlengi chodzawombola anthu ku uchimo wawo. Pa 1 Akorinto 15:22, timauzidwa kuti: “Monga mwa Adamu onse amwalira, choteronso mwa Kristu onse akhalitsidwa ndi moyo.” Yesu anabwera padziko lapansi mofunitsitsa monga munthu wangwiro ndipo anapereka moyo wake wapadziko lapansi kuti awombole anthu ku uchimo ndi imfa.

Kudziŵa chifukwa chimene timafera ndiponso njira yothetsera mavuto a anthu kwalimbikitsa anthu ambiri kusiya mankhwala osokoneza bongo. Koma sikuti Baibulo limangothandiza anthu kuthana ndi vuto lawo la kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo panopo. Limanenanso zimene zidzachitike m’tsogolo muno, Satana akadzalandidwa mphamvu, pamene mavuto onse apadziko, kuphatikizapo kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo adzatheretu.

Buku la Chivumbulutso limalongosolapo za “mtsinje wa madzi a moyo wonyezimira ngati krustalo, otuluka ku mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 22:1) Mtsinje wophiphiritsira umenewu ukuimira zimene Mulungu wapereka kudzera mwa Yesu Kristu kuti anthu apezenso moyo wangwiro padziko lapansi la paradaiso. Buku la Chivumbulutso limalongosola za mitengo ya moyo yomera motakasuka m’mphepete mwa mtsinjewo kuti: “Masamba a mtengo ndiwo akuchiritsa nawo amitundu.” (Chivumbulutso 22:2) Masamba ophiphiritsira amenewo akuimira zimene Yehova wapereka kuti achiritse anthu powabwezeretsa ku ungwiro wauzimu ndiponso wakuthupi.

Pamapeto pake, anthu adzasiyana nawo mankhwala osokoneza bongo ndiponso mavuto onse amene amawasoŵetsa mtendere m’dziko lopanda pakeli!

[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]

Kodi Chamba N’Chosaopsa?

Mayiko ambiri akuganiza zololeza chamba, makamaka kuti chikhale mankhwala ochizira odwala. Akuti chamba chimathandiza odwala kuti asamachite nseru akalandira mankhwala ochiza matenda ena, ndiponso akuti pali umboni wakuti chimathandiza odwala AIDS kuti azifuna kudya. Chakhalanso chikugwiritsidwa ntchito poziziritsa ululu.

Ngakhale kuti ofufuza sagwirizana pa mfundo imodzi, zofufuza zimene zinalembedwa m’nyuzipepala ya New Scientist zikutsimikizira kuopsa kwa chamba.

Ofufuza a ku Yunivesite ya Harvard anayesa gulu la anthu amene ankasuta chamba tsiku lililonse ndi gulu lina limene silinkasutasuta. Atawayesa m’mutu pogwiritsa ntchito njira ya nthaŵi zonse sanaone kusiyana kulikonse. Komabe, atawayesa kuti adziŵe amene angathe kuzoloŵera msanga zinthu zatsopano, anapeza kuti amene ankasuta chamba kwambiri aja analephera zedi.

Kwa zaka 15 Yunivesite ina inayesa gulu la anthu osuta chamba ndi gulu la anthu osuta fodya wamba. Nthaŵi zambiri achamba aja ankasuta ndudu zitatu kapena zinayi patsiku, pamene osuta fodya wamba ankasuta ndudu 20 kapenanso kuposa apo patsiku. M’magulu aŵiriŵa anthu ochuluka mofanana ankatsokomola ndiponso anali ndi matenda am’chifuwa. Atawayeza ziŵindi anaonanso kuti anthu onsewo anali ndi maselo owonongeka.

Ngakhale kuti achambawo sankasutasuta, anapeza kuti ndudu imodzi yokha imatulutsa phula limene limatulutsidwa ndi ndudu zitatu zafodya. Kuphatikizanso apo, magazini ya New Scientist inati: “Osuta chamba amakoka kwambiri utsi wake ndipo satulutsa mpweya msanga.”

Ndiponso maselo oteteza thupi a m’mapapo a anthu osuta chamba anapezeka kuti anali ofooka kwambiri ndi 35 peresenti kuti alimbane ndi mabakiteriya poyerekezera ndi maselo a anthu osuta fodya wamba.

[Mawu a Chithunzi]

U.S. Navy photo

[Bokosi patsamba 11]

Mlandu Wowawa” wa Makolo

Nkhani ina yolembedwa ndi mkonzi wa nyuzipepala ya ku South Africa yotchedwa Saturday Star inalongosola za kuchuluka kwa achinyamata ogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kodetsa nkhaŵa kwambiri ku South Africa ponena kuti:

“Zoti ana athu amatero [kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo] ndi mlandu wowawa kwambiri kwa ife makolo komanso kwa anthu ena onse. Nthaŵi zonse timakhala otanganidwa kwambiri kufunafuna ndalama kuti tipeze chuma chambiri. Ana athu amatithetsa nzeru ndipo amatifoola nkhongono. Kodi timakhala nawo mokwanira? N’kosavuta kungowapatsa ndalama kuti asativutenso kusiyana ndi kumvetsera zimene akunena, zimene amaopa, zimene amayembekeza, ndiponso zimene zimawavuta m’maganizo awo. Madzulo ano, tikapita kulesitilanti kapena tikamapuma n’kumangoonerera wailesi yakanema, kodi tingadziŵe zimene akuchita?”

Kapena tingafunsenso kuti kodi tingadziŵe zimene akuganiza?

[Chithunzi patsamba 10]

Anthu ambiri alimbikitsidwa ndipo asiya kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo