Anthu Ongodzipereka Akugwiradi Ntchito
Anthu Ongodzipereka Akugwiradi Ntchito
MADZULO a Lachisanu lililonse Sirley yemwe ndi mphunzitsi wamkazi wachikulirepo wa ku Brazil, amasandutsa balaza la nyumba yake kukhala kalasi. Amélia yemwe ali nawo m’gulu la ophunzirawo amafika cha m’ma 2 koloko. Sajomba paphunziro lililonse ndipo akutha kuŵerenga bwino kuposa achinyamata ambiri omwe amaphunzira ku sekondale. Amélia ali ndi zaka 82.
Amélia akutsanzira anthu ena okalamba oposa 60 amene anamaliza maphunziro aulere a kulemba ndi kuŵerenga amene Sirley anawaphunzitsa m’dera limene akukhala. Posachedwapa nkhani ina yam’nyuzipepala ya ku Brazil yotchedwa Jornal do Sudoeste inafotokoza za ntchito yongodzipereka imene Sirley amachita. Nkhani ya m’nyuzipepalayo inanena kuti ntchito yake yongodziperekayo “yathandiza anthu a m’deralo kwambiri.” Ndipo kenaka inati Sirley amaphunzitsa anthu okalambawo m’njira yochititsa chidwi kwambiri moti “pakangotha maola 120 akuwaphunzitsa, okalambawo amakhala akutha kulemba makalata, kuŵerenga nyuzipepala, kuwonkhetsa masamu ndi kuchita zinthu zina zofunika masiku onse.” Nkhaniyo inawonjeza kunena kuti, buku limene Sirley amagwiritsa ntchito pophunzitsa, n’lakuti Phunzirani Kuŵerenga ndi Kulemba lopangidwa ndi Mboni za Yehova. *
Munthu Wamanyazi Anasanduka Munthu Waulemu Wake
Mayi Luzia a zaka 68 anaphunzitsidwanso ndi Sirley. Iwo anati asanaphunzire kuŵerenga ndi kulemba, ankachita manyazi kulankhula ndi ena. Ngakhale kugula zinthu kunkawavuta. “Pano ndimalembera makalata abale anga omwe ali m’madera ena, ndipo ndimatha kusunga ndalama zanga. Palibenso munthu amene amandibera chenje,”
anatero akumwetulira. Maria yemwenso ali ndi zaka 68 amakumbukira mmene ankachitira manyazi akamadinda chala papepala akafuna kulandira malipiro ake a penshoni. Ananena kuti, “Ndinkadziona ngati wopunduka.” Koma chifukwa cha maphunziro a kuŵerenga ndi kulemba, tsopano Maria amadzisainira dzina lake mokondwa.Anthu amene akuphunzirabe ndiponso amene anamaliza akamaitama ntchito yosalipiritsa imene Sirley amachita, amaitchukitsa moti balaza lake layamba kuchepa chifukwa chochuluka anthu. Posachedwapa kalasilo lisamukira m’nyumba yaikuluko.
Ntchito Imene Inalandira Mphoto
Sirley ali m’gulu la Mboni za Yehova. Sitikukayikira kuti mukudziŵa bwino ntchito yophunzitsa anthu Baibulo imene Mboni za Yehova zimachita mongodzipereka. Komabe si Sirley yekha amene akuphunzitsa anthu bwino choncho. Maphunziro a kuŵerenga ndi kulemba amene akuchitika m’Nyumba za Ufumu zambirimbiri ku Brazil konseko athandiza kale anthu oposa 22,000 m’dzikolo kuti adziŵe kuŵerenga ndi kulemba.
Ntchito zina zotere za Mboni za Yehova zathandizanso m’mayiko ena padziko lonse. Mwachitsanzo, m’dziko la Burundi mu Africa, bungwe la National Office for Adult Literacy (dipatimenti ina ya Unduna wa Zamaphunziro) linasangalala kwambiri ndi mapindu a ntchito ya Mboni yophunzitsa anthu kuŵerenga ndi kulemba, moti bungwelo linapereka mphoto kwa aphunzitsi ake anayi chifukwa cha “kulimbikira kuphunzitsa ena kuŵerenga.” Makamaka chimene chinakondweretsa akuluakulu aboma n’chakuti mwa anthu 100 amene anaphunzira kuŵerenga ndi kulemba, 75 mwa iwo anali amayi, koma kaŵirikaŵiri amayi amazengereza kuchita nawo zinthu ngati zimenezi.
M’dziko la Mozambique, ophunzira 4,000 alembetsa m’makalasi ophunzira kuŵerenga ndi kulemba a Mboni, ndipo m’zaka zinayi zapitazo, ophunzira oposa 5,000 anadziŵa kuŵerenga ndi kulemba. Wophunzira wina wakale analemba kuti: “Ndikufuna nditchule mmene ndikukondwera kuchokera pansi pamtima. Chifukwa cha sukulu imeneyi, ndikutha kuŵerenga ndi kulemba.”
Kuthandiza Kogwira Mtima Osati Kongodzionetsera
Mtundu wina wa ntchito yongodzipereka imene Mboni za Yehova zimachita n’njothandiza komwe kwagwa tsoka. Posachedwapa nyumba yosungiramo katundu kufupi ndi mzinda wa Paris ku France, inadzaza kwambiri ndi anthu amene anali jijirijijiri kugwira ntchito. Kuyambira Loŵeruka mpakana Lamlungu, anthu ongodzipereka 400 anakhala akupakira zakudya, zovala ndi mankhwala m’makatoni. Pofika madzulo a tsiku Lamlungulo, n’kuti makontena 9 onyamulidwa pa magalimoto akuluakulu odzaza ndi katundu wokwana pafupifupi madola miliyoni imodzi ali chire kuti anyamulidwe. Kenaka posakhalitsa, katunduyo anafika m’chigawo cha pakati pa Africa chimene kunali nkhondo, ndipo mboni zongodzipereka za kumeneko zinam’gaŵa bwinobwino. Katundu wambiri mwa katunduyo anaperekedwanso ndi Mboni.
Nyuzipepala ina ku Congo (Kinshasa) inayamika ntchito yothandizayi ya Mboni za Yehova ponena kuti “n’njogwira mtima osati yongodzionetsera.” Nawo akuluakulu a bungwe la United Nations High Commissioner for Refugees (UNHCR) asonyeza kuti akuyamikira. Mayi wina yemwe ndi wamkulu m’bungwe la UNHCR m’dziko la Democratic Republic of Congo anachita chidwi kwambiri poona mmene Mboni zimachitira zinthu mwadongosolo pothandiza moti anapereka galimoto lake kuti ongodziperekawo aziigwiritsa ntchito. Anthu a kumeneko anachitanso chidwi kwambiri. Anthu ena amene ankaona anthu ovutikawo akulandira zinthuzo mwamsanga, anafunsa modabwa kuti: “Mumagwirizana bwanji kuti muzitha kugaŵira wina aliyense wofuna thandizo?”
Kuthandiza anthu amene tsoka lawagwera ndiponso kuphunzitsa anthu kuŵerenga ndi kulemba, ndi zitsanzo ziŵiri zokha za ntchito zimene Mboni za Yehova zakhala zikuchita padziko lonse kwa zaka zambiri. Komabe, Mbonizo zimachitanso mtundu wina wa ntchito yongodzipereka. Ntchitoyi n’njothandiza mokhalitsa. Nkhani yotsatira ikamba zimenezi.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Buku lakuti Phunzirani Kuŵerenga ndi Kulemba (lomwe lili m’zinenero 6) ndiponso buku lina latsopano kwambiri lakuti Dziperekeni pa Kuŵerenga ndi Kulemba (lomwe lili m’zinenero 29) n’ngofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Funsani ku Nyumba ya Ufumu yakwanuko kapena olemba magazini ino kuti mupeze buku lanulanu kwaulere.
[Bokosi/Chithunzi pamasamba 16, 17]
Ntchito Yogwira Mongodzipereka Ikusintha
Julie akamayenda kuzungulira dziko lonse poyendera zantchito, nthaŵi zonse amayesetsa kupeza nthaŵi ina yochita ntchito yongodzipereka kwa maola angapo. Posachedwapa ali ku South America anakhala madzulo onse akuthandiza m’nyumba yosamalira ana amasiye yomwe ili kufupi ndi mzinda wa Santiago, m’dziko la Chile. Ananena kuti kuyendayenda kumapereka “mipata yabwino kwambiri” yogwira ntchito zongodzipereka.
Anthu ambiri akungodzipereka monga mmene amachitira Julie, koma amatero mwa apo ndi apo. Sara Meléndez yemwe ndi pulezidenti wa gulu lofufuza lomwe limasunga zomwe apeza zokhudza ntchito yongodzipereka anati, “Zimenezi zangoyamba posachedwapa. Anthu akumadzipereka, koma akatero, kudziperekako kumangokhala kwa apo ndi apo.” Pa chifukwa chimenechi, akuluakulu okonza ntchito zotere akusoŵa anthu ongodzipereka ndipo akuvutika kupeza antchito oti agwire ntchito zimene akukonza.”
“Ntchito Yongodzipereka Mosakhazikika”
Akuluakulu ena okonza ntchitozi akuganiza kuti zimene zayamba kuchitikazi, zomagwira ntchito yongodzipereka kwa nthaŵi yochepa, zikuchitika chifukwa chakuti ongodziperekawo ayamba kusintha maganizo. Susan Ellis, amene amalangiza pa nkhani zokhudza magulu aanthu ongodzipereka anati, “Masiku ano simungamvenso odzipereka akunena kuti: ‘Ndizigwirabe ntchito pano malinga ngati ndikufunika. Anthu salonjezanso kuti adzipereka mokhazikika.’” Mtolankhani wina dzina lake Eileen Daspin akugwirizana ndi mfundo imeneyo. Atafunsa akuluakulu angapo oyang’anira magulu aanthu ongodzipereka, iye anati “ntchito yodalira anthu ongodzipereka sikuyenda bwino chifukwa anthu akuopa kudzipereka mokhazikika.”
Komabe woyang’anira bungwe la New York Cares, Kathleen Behrens uja tam’tchula poyamba paja, akuona kuti anthu amene amangodzipereka kwa nthaŵi yochepa uku akuchita ntchito zina, amatero chifukwa chosoŵa nthaŵi, osati chifukwa satha kudzipereka mokhazikika ayi. Anthu amene mlungu wonse amagwira ntchito zotangwanitsa ndiponso okhala ndi ana kapena makolo okalamba sangadzipereke n’komwe mokhazikika. Iye ananena kuti, “Komabe chokhacho chakuti anthu otangwanika ameneŵa amakhudzidwabe ndi ntchito zagulu, zimasonyeza kuti n’ngofunitsitsadi kuthandiza ena.”
Kwa anthu ongodzipereka omwe alibe nthaŵiŵa, njira yowathandiza n’kugwira “ntchito yongodzipereka mosakhazikika,” anatero Behrens. Masiku ano, mabungwe ambiri aanthu ogwira ntchito mongodzipereka akupereka ntchito zoyenera kugwira ngakhale tsiku limodzi lokha. “Zimenezi zimapereka mpata woti anthu adzipereke m’njira zaphindu ndiponso kuti akhalebe ndi ufulu umene akufuna woti agwire ntchitoyo nthaŵi zonse akapeza nthaŵi.”
Kuwonjezera apo, anthu ambiri akudzipereka ali kunyumba pogwiritsa ntchito makompyuta awo, polemba zinthu zofunika m’makompyuta ndiponso pofufuza zinthu zina. Magazini otchedwa The Wall Street Journal akuti, “Mwina ntchito yongodzipereka pogwiritsa ntchito kompyuta ndiyo ili ntchito yodabwitsadi, ndipo ena akuti ndiyo ikuoneka ngati idzathandize kwambiri pochita ntchito imene tsopano ikutchedwa kuti ‘ntchito yongodzipereka mosakhazikika.’”
[Bokosi/Zithunzi patsamba 18]
Kuthandiza Anthu Omwe Tsoka Linawagwera ku Kobe!
Mu January 1995, pamene chivomezi chinagwedeza mzinda wotchuka wa Kobe ku Japan womwenso uli ndi doko, chinawononga mochititsa mantha kwambiri. Chinapha anthu oposa 5,000 ndipo chiyambireni 1923 mpaka nthaŵiyi, ku Japan kunali kusanachitike chivomezi choopsa chotero. Mboni za Yehova ku Japan ndiponso padziko lonse zinayamba mwamsanga kuthandiza anthu onse okhudzidwa ndi tsokalo. Atapempha kuti pakhale thumba la ndalama zachithandizo, ndalama zoposa madola miliyoni imodzi zinaperekedwa m’masiku atatu okha. Katundu wosiyanasiyana wachithandizo ankafika ku Kobe mosaleka.
Mkristu wina, yemwe ndi mkulu ndipo ankathandiza nawo ntchito yogaŵa zinthu anaona kuti Nyumba yawo ya Ufumu yadzaza ndi katundu wochuluka mwakuti sangathe kumugwiritsa ntchito yenseyo. Kodi akanatani naye katundu yenseyo? Anagwirizana zoti apereke katundu wina ku chipatala chimene ali nacho pafupi monga mphatso. Mbonizo zinapakira katunduyu m’galimoto ya vani n’kuyamba ulendo wodutsa mumzinda wophwasukawu. Ulendowo unatenga maola ambiri m’malo moyenda kwa mphindi zochepa chabe monga mwa nthaŵi zonse. Atafika ku chipatalako, anapereka katunduyo kwa dokotala wamkulu. Katunduyo anali mabulangete, matilesi, matewera, zipatso ndiponso mankhwala ambiri. Dokotalayo anakondwera n’kunena kuti chipatalacho chilandira ndi manja aŵiri katundu aliyense amene Mboni zingapereke. Makamaka anakondwera chifukwa cha zipatsozo popeza kuti panalibe zipatso zokwanira odwala onse.
Pamene Mbonizo zinkatsitsa katunduyo, dokotalayo anangoima poteropo ali duu n’kumangoyang’ana, ngakhale kuti anafunikira kuchita ntchito yake mwachangu kwambiri. Kenaka anaŵeramitsa mutu wake modzichepetsa n’kuthokoza. Mbonizo pochoka, dokotalayo anangoimabe pomwepo pofuna kusonyeza kuti anathokozadi kuchokera pansi pamtima. Mkulu amene anapititsa thandizo uja anati pambuyo pake chipatala chimenechi chinayamba kumvetsa kwambiri zofuna za odwala omwe ali Mboni za Yehova.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 19]
Ntchito Yongodzipereka N’njopindulitsa
Gulu la anthu ogwira ntchito yongodzipereka m’kamudzi kena kotchedwa Kabezi m’dziko la Burundi linkafuna kuti limange Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova, koma mkulu wina woimira boma kumeneko anawapempha chinthu chosayembekezeka. Anapempha Mbonizo kuti zikonze msewu wodutsa kumene ankafuna kumanga Nyumba ya Ufumuyo. Mokondwa Mbonizo zinavomera kuti zikonza msewu wowonongekawo, ndipo zinachita ntchito yonseyo ndi manja okha basi. Ongodziperekawo anagwiradi bwino kwambiri ntchitoyo moti akuluakulu akumeneko anakondwera kwambiri chifukwa cha khama lawo ndiponso mzimu wofunitsitsa. Atamaliza, anthu ogwira ntchito yongodziperekawo anapitiriza kumanga Nyumba yawo ya Ufumu imene yajambulidwa pamwambayi. Tsopano ali ndi nyumba yokongola kwambiri imene ithandize kulimbikitsa maphunziro a Baibulo kwa zaka zambiri. Zoonadi, ntchito zonse zongodzipereka zingakhale ndi mapindu osasimbika.
[Zithunzi pamasamba 16, 17]
Sirley amasangalala akamaphunzitsa ena kuŵerenga
[Mawu a Chithunzi]
Nelson P. Duarte-Jornal do Sudoeste